Ndife Anthu a Yehova
“Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kukhala cholowa chake.”—SAL. 33:12.
1. N’chifukwa chiyani n’zomveka kunena kuti Yehova ndi mwini wa zinthu zonse? (Onani chithunzi choyambirira.)
YEHOVA ndi mwini wa zinthu zonse. Baibulo limanena kuti: “Kumwamba ndi kwa Yehova Mulungu wanu. Kumwambamwamba ndi zonse zili kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo ndi zake zonsezo.” (Deut. 10:14; Chiv. 4:11) Choncho munthu aliyense ndi wa Yehova chifukwa iye ndi amene anatilenga. (Sal. 100:3) Koma kuyambira kale, Mulungu wakhala akusankha magulu osiyanasiyana a anthu kuti akhale anthu ake apadera.
2. Kodi ndi anthu ati amene Baibulo limasonyeza kuti ndi apadera kwa Yehova?
2 Mwachitsanzo, lemba la Salimo 135 limanena kuti Aisiraeli amene ankatumikira Yehova mokhulupirika anali “chuma chake chapadera.” (Sal. 135:4) Buku la Hoseya linaloseranso kuti anthu ena omwe si Aisiraeli adzakhala anthu a Yehova. (Hos. 2:23) Ulosi wa Hoseya unakwaniritsidwa pamene Yehova analola kuti anthu omwe sanali Ayuda akhale m’gulu la anthu amene akalamulire ndi Khristu. (Mac. 10:45; Aroma 9:23-26) Gulu limeneli limatchedwa “mtundu woyera” komanso “chuma chapadera” cha Yehova chifukwa choti amadzozedwa ndi mzimu woyera komanso amasankhidwa kukakhala ndi moyo kumwamba. (1 Pet. 2:9, 10) Nanga bwanji za Akhristu ambirimbiri okhulupirika amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli? Yehova amanenanso kuti amenewa ndi ‘anthu ake osankhidwa mwapadera.’—Yes. 65:22.
3. (a) Kodi ndi anthu ati amene ali pa ubwenzi wapadera ndi Yehova masiku ano? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Masiku ano, “kagulu ka nkhosa” komwe kakuyembekezera kupita kumwamba komanso a “nkhosa zina” amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli, amapanga “gulu limodzi” la nkhosa. Ndipo Yehova amawaona kuti onsewa ndi anthu ake apadera. (Luka 12:32; Yoh. 10:16) Tiyenera kusonyeza kuti timayamikira kwambiri zimene Yehova wachita potilola kuti tikhale naye pa ubwenzi wapadera. Munkhaniyi, tikambirana njira zimene tingasonyezere kuti timayamikira zimene Yehova watichitirazi.
TIMADZIPEREKA KWA YEHOVA
4. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zimene Mulungu anachita potithandiza kukhala naye pa ubwenzi? (b) Kodi Yesu anachita chiyani pamene anabatizidwa?
4 Njira imodzi imene timasonyezera kuti timayamikira zimene Yehova watichitira ndi kudzipereka kwa iye ndi mtima wonse. Munthu akabatizidwa, amasonyeza poyera kuti iyeyo ndi wa Yehova ndipo ndi wokonzeka kumugonjera. (Aheb. 12:9) Izi n’zimene Yesu anachita pamene anabatizidwa, chifukwa zinali ngati ankauza Yehova kuti: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.” (Sal. 40:7, 8) Ngakhale kuti Yesu anabadwa komanso kukulira mumtundu wodzipereka kwa Mulungu, iye payekha anadzipereka kuti achite chifuniro cha Yehova.
5, 6. (a) Kodi Yehova anamva bwanji pamene Yesu anabatizidwa? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova amayamikira tikadzipereka kwa iye ngakhale kuti zinthu zonse ndi zake.
5 Kodi Yehova anatani pamene Yesu anabatizidwa? Baibulo limanena kuti: “Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo. Pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzamutera. Panamvekanso mawu ochokera kumwamba onena kuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.’” (Mat. 3:16, 17) Ngakhale kuti Yesu anali kale Mwana wake, Yehova anasangalala kumuona akudzipereka ndi mtima wonse kuti achite chifuniro chake. Yehova amasangalalanso akaona tikudzipereka kwa iye ndipo amatidalitsa.—Sal. 149:4.
6 Kuti timvetse mfundoyi, tiyerekeze kuti bambo anadzala mtengo wa mango. Ndiye mangowo atayamba kubereka, mwana wake wamkazi wapita kukathyola limodzi n’kupatsa bambo akewo kuti adye. Popeza mangowo anadzala ndi bambowo, ndipo tingati ndi awo kale, kodi iwo angaone kuti sayenera kuthokoza mwanayo? Bambo achikondi sangaganize zoti mangowo ndi awo kale koma angayamikire ndipo angaone kuti mwanayo amawakonda. Angaonenso kuti bango limene mwanayo wawapatsa ndi lamtengo wapatali kuposa mango onse amene ali mumtengomo. Nayenso Yehova amayamikira kwambiri tikadzipereka ndi mtima wonse kuti tizimutumikira.—Eks. 34:14.
7. Kodi Malaki anasonyeza bwanji mmene Yehova amamvera akaona anthu amene amamutumikira ndi mtima wonse?
7 Werengani Malaki 3:16. Ngati panopa simunadzipereke kwa Yehova n’kubatizidwa, ndi bwino kuganizira kwambiri ubwino wochita zimenezi. N’zoona kuti kuyambira pamene munabadwa, munakhala munthu wa Yehova mofanana ndi anthu ena onse. Koma Yehova angasangalale kwambiri ngati mwadzipereka kwa iye komanso kuchita zimene amafuna chifukwa chozindikira kuti iye ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. (Miy. 23:15) Yehova amazindikira anthu amene amamutumikira ndi mtima wonse ndipo amalemba mayina awo ‘m’buku la chikumbutso.’
8, 9. Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene alembedwa ‘m’buku la chikumbutso’ azichita chiyani?
8 Komabe anthu amene mayina awo alembedwa ‘m’buku la chikumbutso’ la Yehova amayenera kuchita zinthu zina. Paja Malaki anasonyeza kuti tiyenera ‘kuopa Yehova komanso kuganizira za dzina lake.’ Ngati titayamba kudzipereka kwa munthu wina kapena chinthu china ndiye kuti dzina lathu likhoza kuchotsedwa m’buku la moyo lophiphiritsali.—Eks. 32:33; Sal. 69:28.
9 Choncho pamafunika zambiri kuti munthu adzipereke kwa Yehova osati kungolonjeza kuti achita zimene Yehovayo amafuna ndiponso kubatizidwa basi. Tikutero chifukwa chakuti kulonjeza ndiponso kubatizidwa sizitenga nthawi yaitali ndipo zikhoza kuiwalika. Koma munthu amafunika kusonyeza kuti amamvera Yehova ndipo ali kumbali ya ulamuliro wake kwa moyo wake wonse.—1 Pet. 4:1, 2.
TIZIPEWA KULAKALAKA ZINTHU ZA M’DZIKOLI
10. Kodi munthu amene amatumikira Mulungu amasiyana bwanji ndi amene samutumikira?
10 Munkhani yapita ija tinakambirana za Kaini, Solomo ndi Aisiraeli. Onsewa ankaona kuti akulambira Yehova koma zochita zawo zinasonyeza kuti sanadzipereke kwa iye ndi mtima wonse. Izi zikusonyeza kuti munthu aliyense amene wadzipereka kwa Yehova ayenera kuchita chilungamo n’kumapeweratu zinthu zoipa. (Aroma 12:9) M’pake kuti Malaki atangotchula za “buku la chikumbutso,” Yehova ananena za “kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sanatumikirepo Mulungu.”—Mal. 3:18.
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti anthu onse azioneratu kuti ndife odzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse?
11 Apa tsopano tikuona chinthu chachiwiri chimene tingachite posonyeza kuti timayamikira zimene Yehova watichitira. ‘Anthu onse ayenera kuona’ kuti tikupita patsogolo mwauzimu. (1 Tim. 4:15; Mat. 5:16) Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi anthu onse amaona kuti ndine wodzipereka kwa Mulungu ndi mtima wonse? Kodi mpata ukapezeka ndimaugwiritsa ntchito kuti anthu adziwe zoti ndine wa Mboni za Yehova?’ Popeza Yehova anatisankha kuti tikhale m’gulu la anthu ake, angakhumudwe kwambiri ngati ataona kuti sitikufuna kudziwika kuti ndife Mboni zake.—Sal. 119:46; werengani Maliko 8:38.
12, 13. Kodi anthu ena amachita zotani zomwe siziwasiyanitsa kwenikweni ndi anthu omwe si Mboni?
12 N’zomvetsa chisoni kuti atumiki a Yehova ena amayamba kutengera “mzimu wa dziko” moti zochita zawo siziwasiyanitsa kwenikweni ndi anthu amene satumikira Mulungu. (1 Akor. 2:12) Mzimu wa dzikoli umalimbikitsa anthu kuti azichita “zofuna za thupi.” (Aef. 2:3) Mwachitsanzo, ngakhale kuti gulu lakhala likupereka malangizo pa nkhani ya kavalidwe ndi kudzikongoletsa, anthu ena amachitabe zinthu motayirira. Amavala zovala zothina kapena zoonetsa mkati ngakhale kumisonkhano yathu. Apo ayi amameta kapena kupesa m’njira yachilendo kwambiri. (1 Tim. 2:9, 10) Chifukwa cha zimenezi, anthu oterewa akakhala ndi anthu ena munthu sangasiyanitse pakati pa atumiki a Yehova ndi ‘mabwenzi a dzikoli.’—Yak. 4:4.
13 Pali zinthu zinanso zimene a Mboni ena amachita potsanzira anthu a m’dzikoli. Mwachitsanzo, amavina komanso kuchita zinthu zina pamapwando zomwe si zoyenera Akhristu. Komanso amaika zithunzi zawo ndiponso kulemba zinthu zina pa intaneti zomwe n’zosayenera kwa Akhristu enieni. N’kutheka kuti amakhala asanachite tchimo lalikulu koma akhoza kusokoneza kwambiri anthu amene amafuna kukhala ndi khalidwe labwino potumikira Yehova.—Werengani 1 Petulo 2:11, 12.
14. Kodi tingateteze bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?
14 Dzikoli limalimbikitsa kwambiri “chilakolako cha thupi, chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” (1 Yoh. 2:16) Koma popeza tinadzipereka kwa Yehova, timalimbikitsidwa kuti tizikana “moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma kukhala amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu m’nthawi ino.” (Tito 2:12) Choncho mawu athu komanso zimene timachita pa nkhani ya kudya, kumwa, kuvala ndi kudzikongoletsa ziyenera kusonyezeratu anthu ena kuti tinadzipereka kwa Mulungu ndi mtima wonse.—Werengani 1 Akorinto 10:31, 32.
‘TIZIKONDANA KWAMBIRI’
15. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala achikondi komanso okoma mtima kwa Akhristu anzathu?
15 Zimene timachitira abale ndi alongo athu zingasonyeze ngati timayamikira ubwenzi wathu ndi Yehova kapena ayi. Tizikumbukira kuti anzathuwo ndi a Yehovanso. Tikamakumbukira mfundo imeneyi, nthawi zonse tidzakhala okoma mtima komanso achikondi kwa abale ndi alongo athu. (1 Ates. 5:15) Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”—Yoh. 13:35.
16. Kodi zimene Yehova ankachita poteteza ziwiya za m’kachisi zikutiphunzitsa chiyani?
16 Kuti tione mmene tingachitire zimenezi mumpingo, tiyeni tikambirane chitsanzo ichi. Kale, ziwiya zokhala m’kachisi wa Yehova zinkakhala zogwiritsa ntchito polambira Mulungu basi. M’Chilamulo cha Mose munali malangizo a mmene anthu angazigwiritsire ntchito ndipo munthu wosatsatira malamulowo ankaphedwa. (Num. 1:50, 51) Ndiye ngati Yehova ankateteza chonchi zipangizo zopanda moyo zimene zinkagwiritsidwa ntchito pomulambira, kodi angamve bwanji ngati wina akusokoneza anthu amene anawasankha omwe amamulambira mokhulupirika? Paja ponena za anthu ake Yehova ananena kuti: “Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.”—Zek. 2:8.
17. Kodi Yehova ‘amatchera khutu n’kumamvetsera’ tikamachita chiyani?
17 Chochititsa chidwi n’chakuti Malaki ananena kuti Yehova ‘amatchera khutu n’kumamvetsera’ zimene anthu ake akukambirana. (Mal. 3:16) Izi zikusonyezeratu kuti Yehova “amadziwa anthu ake.” (2 Tim. 2:19) Iye amadziwa chinthu chilichonse chimene timachita komanso kulankhula. (Aheb. 4:13) Tikamachita kapena kulankhula zinthu zopweteka kwa Akhristu anzathu, Yehova ‘amatchera khutu n’kumamvetsera.’ Koma tikamachereza alendo, kupereka zinthu mowolowa manja, kukhululukira anthu komanso kuwakomera mtima, Yehova amaonanso.—Aheb. 13:16; 1 Pet. 4:8, 9.
“YEHOVA SADZATAYA ANTHU AKE”
18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mwayi wokhala anthu a Yehova?
18 Kunena zoona, tiyenera kuyesetsa kusonyeza kuti timayamikira Yehova chifukwa chotipatsa mwayi wokhala anthu ake. Tiyeneranso kuona kuti popeza ndife anthu ake, ndi nzeru kudzipereka kwa iye. Ngakhale kuti timakhala “pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota,” timafuna kuti anthu aziona kuti ndife ‘opanda chifukwa chotineneza nacho ndiponso osalakwa.’ Timafunanso kuti ‘tiziwala pakati pawo monga zounikira m’dzikoli.’ (Afil. 2:15) Choncho tiyenera kukaniratu kuchita zinthu zoipa. (Yak. 4:7) Tiyeneranso kukonda ndiponso kulemekeza Akhristu anzathu podziwa kuti nawonso ndi anthu a Yehova.—Aroma 12:10.
19. Kodi Yehova amadalitsa bwanji anthu ake?
19 Baibulo limalonjeza kuti: “Yehova sadzataya anthu ake.” (Sal. 94:14) Lonjezoli lidzakwaniritsidwa ngakhale titakumana ndi mavuto aakulu kwambiri. Ngakhale imfa singatisiyanitse ndi chikondi cha Yehova. (Aroma 8:38, 39) Paja Baibulo limanena kuti: “Tikakhala ndi moyo, timakhalira moyo Yehova, ndipo tikafa, timafera Yehova. Chotero kaya tikhale ndi moyo kapena tife, ndife a Yehova.” (Aroma 14:8) Tonsefe timalakalaka nthawi imene Yehova adzaukitse anthu onse amene anamwalira omwe anali anzake okhulupirika. (Mat. 22:32) Koma ngakhale panopa timapeza madalitso ambiri. Baibulo limanena kuti: “Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kukhala cholowa chake.”—Sal. 33:12.