Madalitso a Yehova Alemeretsa
“Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.” —MIYAMBO 10:22.
1-3. Ngakhale kuti ambiri akudera nkhaŵa zinthu zakuthupi, kodi nchiyani ponena za chuma chakuthupi chimene onse ayenera kuzindikira?
ANTHU ena samaleka kulankhula za ndalama—kapena kusoŵeka kwake. Mwachisoni, m’zaka zaposachedwapa akhala nzambiri zokambitsirana. Mu 1992 ngakhale maiko a Kumadzulo olemerawo akanthidwa ndi vuto lazachuma, ndipo mamanijala limodzi ndi antchito wamba anachotsedwa ntchito. Ambiri anakaikira ngati akawonanso nthaŵi ya kulemerera kokhazikika.
2 Kodi nkulakwa kudera nkhaŵa za mkhalidwe wathu wachuma chakuthupi? Ayi, kumlingo wina iko nkwachibadwa. Panthaŵi imodzimodzi, pali chowonadi chachikulu chimene tiyenera kudziŵa ponena za chuma. Kwakukulukulu, zinthu zonse zakuthupi zimachokera kwa Mlengi. Iye ndiye “Mulungu Yehova, iye amene . . . [a]nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka m’menemo, iye amene amapatsa anthu a m’menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m’menemo.”—Yesaya 42:5.
3 Ngakhale kuti Yehova samaikiratu amene adzakhala wolemera ndi amene adzakhala mmphaŵi, tonsefe tiyenera kudziyankhira za njira imene timagwiritsira ntchito mbali iriyonse imene tiri nayo ya “dziko lapansi, ndi chimene chituluka m’menemo.” Ngati tigwiritsira ntchito chuma chathu kuchita umbuye pa ena, Yehova adzatiimba mlandu. Ndipo alionse amene akutumikira chuma mmalo mwa kutumikira Yehova adzapeza kuti “wokhulupirira chuma chake adzagwa.” (Miyambo 11:28; Mateyu 6:24; 1 Timoteo 6:9) Kulemera kwakuthupi kopanda mtima wogonjera kwa Yehova potsirizira pake kumakhala kosapindulitsa.—Mlaliki 2:3-11, 18, 19; Luka 16:9.
Kulemera Kofunika Koposa
4. Kodi nchifukwa ninji kulemera kwauzimu kuli kwabwino koposa chuma chambiri chakuthupi?
4 Kuwonjezera pa kulemera kwakuthupi, Baibulo limalankhulanso za kulemera kwauzimu. Kumeneku mwachiwonekere ndiko kwabwino koposerapo. (Mateyu 6:19-21) Kulemera kwauzimu kumaphatikizapo unansi wokhutiritsa ndi Yehova umene ungakhaleko kuumuyaya wonse. (Mlaliki 7:12) Ndiponso, atumiki a Mulungu olemera mwauzimu sakuphonya madalitso a zinthu zabwino zakuthupi. M’dziko latsopano, chuma chauzimu chidzayendera limodzi ndi kulemera kwakuthupi. Okhulupirika adzasangalala ndi chisungiko cha zinthu zakuthupi zosapezedwa mwa mpikisano wa mtima bii kapena moika thanzi ndi chimwemwe pachiswe, monga momwe kaŵirikaŵiri ziliri lerolino. (Salmo 72:16; Miyambo 10:28; Yesaya 25:6-8) Iwo adzapeza kuti m’njira iriyonse “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”—Miyambo 10:22.
5. Kodi ndilonjezo lotani limene Yesu anapereka ponena za zinthu zakuthupi?
5 Ngakhale lerolino, awo amene amalemekeza zinthu zauzimu ali ndi mtendere wamaganizo kumlingo winawake ponena za zinthu zakuthupi. Zowona, iwo amagwira ntchito kuti alipilire ngongole ndi kudyetsa mabanja awo. Kapena ena angataikiridwedi ndi ntchito zawo m’nthaŵi za mavuto azachuma. Koma iwo samada nkhaŵa mopambanitsa ndi zinthu zoterozo. Mmalo mwake, amakhulupirira lonjezo la Yesu pamene anati: “Chifukwa chake musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzabvala chiyani? . . . Pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:31-33.
Chuma Chauzimu Lerolino
6, 7. (a) Fotokozani mbali zina za kulemera kwauzimu kwa anthu a Mulungu. (b) Kodi ndiulosi uti umene ukukwaniritsidwa lerolino, ndipo kodi ndimafunso ati amene umadzutsa?
6 Chotero, anthu a Yehova asankha kuika Ufumuwo patsogolo m’miyoyo yawo, ndipo adalitsidwa chotani nanga! Iwo akupeza chipambano chachikulu m’ntchito yawo yopanga ophunzira. (Yesaya 60:22) Akuphunzitsidwa ndi Yehova, akumasangalala ndi kuyenda kwatawatawa kosatha kwa zinthu zabwino zauzimu zoperekedwa kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47; Yesaya 54:13) Ndiponso, mzimu wa Yehova uli pa iwo, kuwagwirizanitsa kukhala gulu la abale losangalala la mitundu yonse.—Salmo 133:1; Marko 10:29, 30.
7 Kumeneku kulidi kulemera kwauzimu, kanthu kena kamene ndalama sizingagule. Ndiko kukwaniritsidwa kochititsa chidwi kwa lonjezo la Yehova lakuti: “Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.” (Malaki 3:10) Ife lerolino tawona lonjezo limeneli likukwaniritsidwa. Komabe, kodi nchifukwa ninji, Yehova, Magwero a chuma chonse, akupempha atumiki ake kubweretsa gawo limodzi lakhumi, kapena chakhumi? Kodi ndani amene amapindula ndi chakhumi? Kuyankha mafunso ameneŵa, talingalirani chifukwa chimene Yehova analankhulira mawuŵa kupyolera mwa Malaki m’zaka za zana lachisanu B.C.E.
Zakhumi ndi Nsembe
8. Malinga ndi lamulo Lachipangano, kodi kulemera kwa zinthu zakuthupi kwa Israyeli kunadalira pachiyani?
8 M’nthaŵi ya Malaki anthu a Mulungu sanali kulemerera? Chifukwa ninji? Chifukwa china chinali kaamba ka zopereka ndi zakhumi. Kalelo, Israyeli anali pansi pa pangano la Chilamulo cha Mose. Pamene Yehova anapanga pangano limenelo, analonjeza kuti ngati Aisrayeli akachita mbali yawo yapanganolo, iye akawadalitsa mwauzimu ndi mwakuthupi. M’chenicheni, kulemera kwa Israyeli kunadalira pa kukhulupirika kwawo.—Deuteronomo 28:1-19.
9. M’masiku a Israyeli wakale, kodi nchifukwa ninji Yehova anafuna Israyeli kupereka zakhumi ndi kubwera nazo nsembe?
9 Mbali ina ya thayo la Israyeli pansi pa Chilamulocho inali kubweretsa nsembe ku kachisi ndi kulipira zakhumi. Zina za nsembezo zinapserezedwa zathunthu paguwa lansembe la Yehova, pamene zinazo, ansembe anagaŵana pakati pawo ndi awo operekera nsembe, mbali zapadera zikumaperekedwa kwa Yehova. (Levitiko 1:3-9; 7:1-15) Ponena za zakhumi, Mose anauza Aisrayeli kuti: “Limodzi mwa magawo khumi la zonse m’dziko, la mbewu zake za dziko, la zipatso za mtengo, ndilo la Yehova; likhale lopatulikira Yehova.” (Levitiko 27:30) Chakhumi chinaperekedwa kwa antchito Achilevi pachihema ndipo pambuyo pake pakachisi. Nawonso, Alevi osakhala ansembe anali kupereka kwa ansembe a mzera wa Aroni mbali imodzi mwa khumi ya zimene analandira. (Numeri 18:21-29) Kodi nchifukwa ninji Yehova anafuna Israyeli kupereka zakhumi? Choyamba, kunali kuti asonyeze mwanjira yowoneka chiyamikiro chawo pa ubwino wa Yehova. Ndipo chachiŵiri, kuti athandize kuchirikiza Alevi, kotero kuti aike chisamaliro pamathayo awo, ophatikizapo kuphunzitsa Chilamulo. (2 Mbiri 17:7-9) Mwanjira imeneyi kulambira koyera kunachirikizidwanso, ndipo aliyense anapindula.
10. Kodi nchiyani chinachitika pamene Israyeli analephera kubwera nazo zakhumi ndi nsembe?
10 Ngakhale kuti zakhumi ndi nsembe zinadzagwiritsiridwa ntchito ndi Alevi, izo kwenikweni zinali mphatso kwa Yehova ndipo chotero zinayenera kukhala zabwino, zomyenera. (Levitiko 22:21-25) Kodi chinachitika nchiyani pamene Aisrayeli analephera kubweretsa zakhumi zawo kapena pamene anabweretsa nsembe zosayenera? Panalibe chilango cholembedwa m’Chilamulo, komabe panali zotulukapo zake. Yehova anachotsa dalitso lake, ndipo Aleviwo, posoŵa chichirikizo m’zinthu zakuthupi, anasiya ntchito zawo zapakachisi kuti akadzichirikize. Chotero, Israyeli yense anavutika.
“Mtima Wanu Usamalire Njira Zanu”
11, 12. (a) Kodi chinachitika nchiyani pamene Israyeli ananyalanyaza kusunga Chilamulo? (b) Kodi ndintchito yotani imene Yehova anapatsa Israyeli pamene anawabweza kuchokera ku Babulo?
11 M’nyengo yonse ya mbiri ya Israyeli, ena anali achitsanzo chabwino m’kuyesayesa kusunga Chilamulo, kuphatikizapo kupereka zakhumi. (2 Mbiri 31:2-16) Komabe, kaŵirikaŵiri, mtunduwo unali wonyalanyaza. Mobwerezabwereza iwo anaswa pangano lawo ndi Yehova, kufikira potsirizira pake iye anawalola kugonjetsedwa ndipo, mu 607 B.C.E., anatengeredwa kundende m’Babulo.—2 Mbiri 36:15-21.
12 Chimenecho chinali chilango champhamvu, koma pambuyo pazaka 70 Yehova anabwezeretsera anthu ake kudziko lakwawo. Ambiri a maulosi Aparadaiso mu Yesaya anali kudzakhala ndi kukwaniritsidwa kwawo koyamba pambuyo pa kubwerera kumeneko. (Yesaya 35:1, 2; 52:1-9; 65:17-19) Komabe, chifukwa chachikulu chimene Yehova anabwezeretsera anthu ake chinali, osati kumanga paradaiso wa padziko lapansi, koma kumanganso kachisi ndi kubwezeretsa kulambira kowona. (Ezara 1:2, 3) Ngati Israyeli akamvera Yehova, mapindu akuthupi akatsatira, ndipo dalitso la Yehova likawalemeretsa ponse paŵiri mwauzimu ndi mwakuthupi. Mogwirizana ndi zimenezo, mwamsanga atafika kudziko lakwawo mu 537 B.C.E., Ayudawo anamanga guwa lansembe m’Yerusalemu nayamba kumanga kachisi. Komabe, anakumana ndi chitsutso champhamvu naleka. (Ezara 4:1-4, 23) Monga chotulukapo, Israyeli sanakhale ndi dalitso la Yehova.
13, 14. (a) Kodi chinatsatira nchiyani pamene Israyeli analephera kumanganso kachisi? (b) Kodi ndimotani mmene potsirizira pake kachisi anamangidwira, koma kodi ndizolephera zina ziti za Israyeli zimene zikusimbidwa?
13 M’chaka cha 520 B.C.E., Yehova anautsa aneneri Hagai ndi Zekariya kuti alimbikitse Israyeli kuyambiranso ntchito yomanga kachisi. Hagai anasonyeza kuti mtunduwo unali ndi vuto la zinthu zakuthupi nasonyeza kuti zimenezi zinachititsidwa ndi kupanda kwawo changu cha pa nyumba ya Yehova. Iye anati: “Chifukwa chake tsono, atero Yehova wa makamu; Mtima wanu usamalire njira zanu. Mwabzala zambiri, koma mututa pang’ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudziveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa ntchito yakulipidwa alandirira kulipirako m’thumba lobooka. Atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu. Kwerani ku dziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa.”—Hagai 1:5-8.
14 Atalimbikitsidwa ndi Hagai ndi Zekariya, Aisrayeli anapenda njira zawo, ndipo kachisiyo anamangidwa. Komabe, pafupifupi zaka 60 pambuyo pake, Nehemiya anapitanso ku Yerusalemu napeza kuti Israyeli ananyalanyazanso Chilamulo cha Yehova. Anawongolera zimenezi. Koma paulendo wake wachiŵiri, anapeza kuti kachiŵirinso zinthu zaipirapo. Iye akusimba kuti: “Ndinazindikiranso kuti sanapereka kwa Alevi magawo awo; m’mwemo Alevi ndi oyimbira adathaŵira yense ku munda wake.” (Nehemiya 13:10) Vutoli linathetsedwa, ndipo “Ayuda onse anabwera nalo limodzi limodzi la magawo khumi a tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ku nyumba za chuma.”—Nehemiya 13:12.
Kulanda Yehova
15, 16. Kodi ndizolephera ziti zimene Yehova, kupyolera mwa Malaki, akudzudzulira Israyeli?
15 Mwachiwonekere, kulosera kwa Malaki kunachitika m’nyengo imodzimodziyi imeneyi, ndipo mneneriyo akutiuza zowonjezereka za kusakhulupirika kwa Israyeli. Iye akulemba mawu a Yehova kwa Israyeli kuti: “Ngati ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa.” Kodi chinalakwika nchiyani? Yehova akufotokoza kuti: “Pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa!”—Malaki 1:6-8.
16 Mwakalongosoledwe komvekera bwino kameneka, Malaki akusonyeza kuti ngakhale kuti Aisrayeli anali kubwera nazo nsembe, mkhalidwe woipa wa zimenezi unasonyeza kupanda ulemu kwakukulu. Malaki analembanso kuti: “Kuyambira masiku a makolo anu mwapambuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa ine, ndipo ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu.” Aisrayeli sanadziŵe chimene kwenikweni anafunikira kuchita, chotero anafunsa kuti: “Tibwerere motani?” Yehova anayankha kuti: “Kodi munthu adzalanda za Mulungu? ndipo inu mundilanda ine.” Kodi nchiyani chimene Israyeli analanda Yehova, Magwero a ulemerero wonse? Yehova anayankha kuti: “Limodzi limodzi la magawo khumi ndi zopereka.” (Malaki 3:7, 8) Inde, mwa kulephera kubweretsa zakhumi zawo ndi nsembe, Israyeli anali kulanda Yehova!
17. Kodi nchifuno chotani chimene zakhumi ndi nsembe zinatumikira mu Israyeli, ndipo kodi ndilonjezo lotani limene Yehova akupereka ponena za zakhumi?
17 Zochitika za m’mbiri yakale zimenezi zimasonyeza kufunika kwa zakhumi ndi nsembe mu Israyeli. Zinali chisonyezero cha chiyamikiro cha woperekayo. Ndipo zinathandizira kuchirikizira kulambira kowona m’njira yakuthupi. Chotero, Yehova anapitirizabe kulimbikitsa Israyeli kuti: “Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo.” Akumasonyeza zimene zikatsatira ngati anatero, Yehova analonjeza kuti: ‘Ndidzakutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.’ (Malaki 3:10) Dalitso la Yehova likanalemeretsa.
Kuweruzidwa ndi ‘Ambuye Wowona’
18. (a) Kodi Yehova akuchenjeza za kudza kwa yani? (b) Kodi ndiliti pamene kuzonda kachisi kunali kudzakhalako, kodi kunaphatikizapo yani, ndipo chotulukapo kwa Israyeli chinali chiyani?
18 Yehova kupyolera mwa Malaki anachenjezanso kuti akadza kudzaweruza anthu ake. “Tawonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye [wowona] amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; tawonani akudza.” (Malaki 3:1) Kodi kudza kukachisi kolonjezedwako kunachitika liti? Pa Mateyu 11:10, Yesu anagwira mawu ulosi wa Malaki wa mthenga amene akakonza njira naugwiritsira ntchito kwa Yohane Mbatizi. (Malaki 4:5; Mateyu 11:14) Chotero mu 29 C.E., nthaŵi ya chiweruzo inafika! Kodi ndani amene anali mthenga wachiŵiri, mthenga wa chipangano amene akatsagana ndi Yehova “Ambuye wowona,” kukachisi? Yesu iyemwiniyo, ndipo kaŵiri anadza kukachisi m’Yerusalemu nauyeretsa mwamphamvu, akumatulutsa osinthana ndalama osawona mtimawo. (Marko 11:15-17; Yohane 2:14-17) Ponena za nthaŵi ya m’zaka za zana loyamba imeneyi ya chiweruzo, Yehova mwaulosi akufunsa kuti: “Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka iye?” (Malaki 3:2) Kunena zowona, Israyeli sanaime. Anazondedwa, napezedwa kukhala wopereŵera, ndipo mu 33 C.E., ngakhale kuti anali mtundu wosankhidwa wa Yehova, iye anasadzidwa.—Mateyu 23:37-39.
19. Kodi ndimnjira yotani imene otsalira anabwerera kwa Yehova m’zaka za zana loyamba, ndipo kodi analandira dalitso lotani?
19 Komabe, Malaki analembanso kuti: “Ndipo [Yehova] adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golidi ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo.” (Malaki 3:3) Mogwirizana ndi zimenezi, ngakhale kuti ochulukitsitsa odzinenera kukhala otumikira Yehova m’zaka za zana loyamba anasadzidwa, ena anayengedwa nadza kwa Yehova, napereka nsembe zolandirika. Kodi anali ayani? Amene anali atalabadira Yesu, mthenga wa chipanganoyo. Pa Pentekoste wa 33 C.E., okwanira 120 a olabadira amenewa anasonkhana pamodzi m’chipinda chapamwamba m’Yerusalemu. Atalimbikitsidwa ndi mzimu woyera, anayamba kupereka zopereka m’chilungamo, ndipo ziŵerengero zawo zinakula mofulumira. Mwamsanga, anafalikira mu Ulamuliro wonse wa Roma. (Machitidwe 2:41; 4:4; 5:14) Chotero, otsalira anabwerera kwa Yehova.—Malaki 3:7.
20. Pamene Yerusalemu ndi kachisi zinawonongedwa, kodi nchiyani chimene chinachitikira Israyeli watsopano wa Mulungu?
20 Otsalira a Israyeli amenewa, amene anadzaphatikizapo Akunja omezanitsidwa, kunena kwake titero, patsinde la Israyeli, anali “Israyeli wa Mulungu” watsopano, mtundu wopangidwa ndi Akristu odzozedwa ndi mzimu. (Agalatiya 6:16; Aroma 11:17) Mu 70 C.E., “tsiku, lotentha ngati ng’anjo” linadzera Israyeli wakuthupi pamene Yerusalemu ndi kachisi wake zinawonongedwa ndi magulu ankhondo Achiroma. (Malaki 4:1; Luka 19:41-44) Kodi nchiyani chimene chinachitikira Israyeli wauzimu wa Mulungu? Yehova anasonyeza ‘chifundo pa iwo monga momwe munthu amasonyezera chifundo mwana wake womtumikira.’ (Malaki 3:17) Mpingo Wachikristu wodzozedwawo unalabadira chenjezo lolosera la Yesu. (Mateyu 24:15, 16) Anapulumuka, ndipo madalitso a Yehova anapitirizabe kuwalemeretsa mwauzimu.
21. Kodi ndimafunso otani amene atsalabe onena za Malaki 3:1 ndi 10?
21 Ndikulemekezedwa kwa Yehova kotani nanga! Komabe, kodi ndimotani nanga, mmene Malaki 3:1 akukwaniritsidwira lerolino? Ndipo kodi Mkristu ayenera kulabadira motani chilimbikitso cha Malaki 3:10 cha kubweretsa chakhumi chonse m’nkhokwe? Tidzakambitsirana zimenezi m’nkhani yotsatira.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kwakukulukulu, kodi ndani amene ali Magwero a chuma chonse?
◻ Kodi nchifukwa ninji kulemera kwauzimu kuli kwabwinopo kuposa chuma chakuthupi?
◻ Kodi zakhumi ndi nsembe zinatumikira chifuno chotani mu Israyeli?
◻ Kodi nliti pamene Yehova, ‘Ambuye wowona,’ anadza kukachisi kudzaweruza Israyeli, ndipo ndi chotulukapo chotani?
◻ Kodi ndani amene anabwerera kwa Yehova pambuyo pakudza kwake kukachisi wake m’zaka za zana loyamba C.E.?
[Chithunzi patsamba 10]
Mthenga wa chipangano, Yesu, woimira Yehova, anadza kukachisi kudzapereka chiweruzo m’zaka za zana loyamba C.E.