Sungani Kuwopa Kwanu Yehova
“‘Ine ndine mfumu yaikulu,’ ati Yehova wa makamu; ‘ndipo dzina langa ndi lowopsa pakati pa amitundu.’”—MALAKI 1:14.
1, 2. (a) Ndi uthenga wamphamvu wotani umene uli mu bukhu la Malaki? (b) Ndi phunziro lotani limene likuperekedwa ndi mawu otsegulira a uthenga wa Yehova?
“KUGAMULA: Kwa mawu a Yehova ponena za Israyeli mwa Malaki.” (Malaki 1:1, NW) Ganizo lachidule, lodzutsa maganizo limeneli limayamba bukhu la Baibulo la Malaki. Mu Baibulo [kugamula, NW] kaŵirikaŵiri kumaimira kuwononga kwa zoipa. Ichi mowonadi chiri chowona m’nkhani ya bukhu la Malaki lokhala ndi uthenga wake wachindunji ndi wamphamvu ku mtundu wa Israyeli. Kulingalira kwathu ilo kudzawunikira kufunika kwa kusunga kuwopa kwathu Yehova ndi chikondi chathu kaamba ka iye.
2 Maversi oyambirira aŵiri a bukhuli amapereka phunziro m’kupereka uphungu. Yehova akutsimikizira amvetseri ake za chikhumbo chake cha kuwathandiza iwo: “‘Ndakukondani [anthu inu, NW],’ ati Yehova.” Ndi chiyambi chotsimikizira, chodzutsa maganizo chotani nanga kwa owona mtima a Israyeli wopanduka. Uthengawu ukupitiriza kunena kuti: “Koma inu mukuti: ‘Mwatikonda motani?’ ‘Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi?’ ati Yehova. ‘Ndipo ndinakonda Yakobo; koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ake abwinja, ndi kupereka cholowa chake kwa ankhandwe a m’chipululu.’”—Malaki 1:2, 3.
3. Ndi ziti zomwe zinali zifukwa za malingaliro a Yehova kulinga kwa Yakobo ndi Esau?
3 Nchifukwa ninji Yehova anakonda Yakobo ndipo, pambuyo pake, mbadwa za Yakobo, Aisrayeli? Chinali chifukwa chakuti Yakobo anali munthu wowopa Mulungu ndipo analemekeza makolo ake owopa Mulungu. Esau, kumbali ina, anali munthu wadyera, wosawopa Yehova. Ndiponso, iye analibe ulemu kaamba ka makolo ake, omwe anali ndi kuyenera kopatsidwa ndi Mulungu, kwa kuyembekezera kumvera kwake. Molondola, Yehova anakonda Yakobo koma anada Esau. Iri ndi chenjezo kwa ife. Tiyenera nthaŵi zonse kupewa kutaya kuwopa Mulungu ndi kukhala wokondetsa zinthu zakuthupi monga Esau, yemwe anasankha kokha kukhutiritsa zikhumbo zake zakuthupi.—Genesis 26:34, 35; 27:41; Ahebri 12:16.
4, 5. (a) Njira ya moyo ya Yakobo ndi Esau inali ndi chiyambukiro chotani pa mbadwa zawo? (b) Ndimotani mmene ichi chinayambukirira Aisrayeli?
4 Monga mmene njira ya Yakobo inatsimikizira kukhala dalitso kwa mbadwa zake, Aisrayeli, choteronso njira ya Esau inatsimikizira kukhala yosiyanako kwa mbadwa zake, a Edomu. A Edomu sanasangalale ndi dalitso la Yehova. M’malomwake, mwakutsutsa kwawo kwa ukali ku anthu a pangano ake, iwo anadzipezera mkwiyo wa Yehova. Iwo anapitikitsidwa ndi magulu ankhondo a Nebukadinezara ndipo pambuyo pake ndi a Arabu. Potsirizira pake, monga mmene kunaloseredwera ndi Yehova, A Edomu anazimiririka monga mtundu.—Obadiya 18.
5 Ziweruzo za Mulungu pa Edomu zinayamba kale kwambiri lisanafike tsiku la Malaki. Ndimotani mmene ichi chiyenera kuyambukirira Aisrayeli? Yehova akuwauza iwo kuti: “Ndipo maso anu adzawona, nimudzati: ‘Yehova anali wamkulu kupitirira malire a Israyeli.’” (Malaki 1:5) Kupyola m’zaka mazana angapo, Israyeli anawona “ndi maso ake” chikondi chimene Yehova ali nacho kaamba ka iwo monga mtundu.
Zochita Zathu Zidzasonyeza Ngati Timawopa Yehova
6. Ndi chidzudzulo chotani chimene Yehova anapanga motsutsana ndi Aisrayeli?
6 Chigamulocho chikupitirizabe: “‘Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake, ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiwopa kuli kuti?’ ati Yehova wa makamu kwa inu, ansembe akupeputsa dzina langa. (Malaki 1:6; Eksodo 4:22, 23; Deuteronomo 32:6) Yehova anawongolera, Aisrayeli kuwapatsa, ndi kuwachinjiriza, monga mmene atate amachitira kwa mwana wake. Nchiyani chimene iye moyenerera anayembekezera kumubwezera? Kuti alemekezedwe ndi kuwopedwa. Mtunduwo, kuphatikizapo ansembe, analephera kuchita ichi koma, m’malomwake, anasonyeza kupanda ulemu ku dzina la Yehova ndi kulinyoza ilo. Iwo anakhala “ana obwerera.”—Yeremiya 3:14, 22; Deuteronomo 32:18-20; Yesaya 1:2, 3.
7. Ndimotani mmene Aisrayeli anamverera ponena za chidzudzulo chimenechi, ndipo nchiyani chimene chinali yankho la Yehova kwa iwo?
7 Aisrayeli anafunsa kuti: “Tapeputsa dzina lanu motani?” Yehova mwamphamvu anayankha kuti: “‘[Mwa kupereka, NW] mkate wodetsa pa guwa langa la nsembe.’ Ndipo mukuti: ‘Tapeputsa dzina lanu motani?’ Mmenemo, mwakuti munena: ‘Gome la Yehova nlonyozeka.’ Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe mukuti: ‘Palibe choipa!’ Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala: ‘Palibe choipa.’ ‘Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi?’ ati Yehova wa makamu.”—Malaki 1:6-8.
8. Nchiyani chimene Aisrayeli anali kusonyeza mwa machitidwe awo?
8 Wina angalingalire m’Israyeli akuyang’ana pa zoweta zake ndipo mwadala akusankha yakhungu kapena nyama yotsimphina kupereka nsembe kwa Yehova. M’njira imeneyi iye angapite m’makonzedwe onse akupanga nsembe komabe mwadyera akusunga zoweta zabwino koposa kwa iyemwini. Iye sangayerekeze kuchita chinthu chotero kwa kazembe! Koma Aisrayeli anachita chimenecho kwa Yehova—ngati kuti iye sanali kuwona makonzedwe awo ndi kunyenga. Molondola Yehova anawafunsa iwo kuti, “Kundiwopa kuli kuti?” Ndi mawu awo, iwo angakhale anadzinenera kuti amawopa Yehova, koma zochita zawo mwachiwonekere zinasonyeza zosiyana.—Deuteronomo 15:21.
9. Ndimotani mmene ansembe anavomerezera ku zimene anthu anali kuchita?
9 Nchiyani chomwe chinali chivomerezo cha ansembe ku nsembe zonyodola zimenezi? Iwo anati: “Palibe choipa.” Iwo analungamitsa njira yolakwa ya Israyeli. Chotero ngakhale kuti okhala mu ukapolo omwe anabwerera kuchokera ku Babulo anapanga chiyambi cha changu cha kukhazikitsanso kulambira kowona, iwo pambuyo pake anakhala osasamala, onyada, ndi odzilungamitsa. Iwo anataya kuwopa kwawo Yehova. Chotero, utumiki wawo wa pa kachisi unakhala choseketsa, ndipo iwo anasunga madyerero mu mkhalidwe wa chosangulutsa.—Malaki 2:1-3; 3:8-10.
10. (a) Ndi nsembe yotani imene Yehova amafuna lerolino? (b) Ndimotani mokha mmene nsembe yathu ingakumanirane ndi chivomerezo cha Yehova?
10 Ena angatsutse kuti: ‘Ichi sichigwira ntchito kwa ife; ife sitipereka nkomwe nsembe zanyama.’ Koma tiri ndi mtundu wina wa nsembe yopereka. Zindikirani dandaulo la changu la Paulo: “Chifukwa chake ndikupemphani inu abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.” (Aroma 12:1) Nsembe imene Yehova akuifuna lerolino iri inu! Uko ndiko kuti, mphamvu zanu, chuma, ndi kuthekera. Nsembe zathu zidzakumana ndi chivomerezo chake kokha ngati iri yabwino koposa kwa ife. Kupereka kwa Yehova zotsalira, monga ngati nsembe zotsimphina, nsembe zodwala, motsimikizirika kudzayambukira unansi wathu ndi iye.
11. Ndi kudzisanthula kotani kumene mtumiki aliyense wodzipereka wa Yehova ayenera kuchita?
11 Ngakhale kuti ena anganene kuti, m’chenicheni, “Palibe choipa,” tikudziŵa mmene Yehova amadzimverera ponena za icho. Chotero, tiyeni ife, mosamalitsa tisanthulenso “nsembe” za “utumiki wopatulika” zimene tikupereka, umene umaphatikiza gawo limene timalitenga m’kulalikira, phunziro laumwini, pemphero, ndi kupezeka pa misonkhano. Kodi muli okhutiritsidwa kuti mukupereka kwa Yehova zinthu zanu zabwino koposa, kapena kodi ziri kokha zotsalira? Pali ngozi ya kudziloŵetsa kwambiri mu zosangulutsa kapena maseŵera kothera kwa mlungu kotero kuti wina samakhala ndi nthaŵi kapena mphamvu ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu ndi kupezeka pa misonkhano. Njira yathu yonse ya moyo, kukhala kwathu kwa tsiku ndi tsiku, kuphatikizapo mikhalidwe ndi zisonkhezero, ziyenera kugwirizana ndi nsembe imene timapereka kwa Yehova. Iloleni iyo isakhale china chirichonse koma yabwino koposa!
Kuzindikira Owopa Mulungu Enieni
12. Ndi uphungu wotani umene ukuperekedwa tsopano?
12 “Ndipo tsopano,” ukutero ulosiwo, “mupepese Mulungu, kuti atichitire chifundo.” (Malaki 1:9) Yehova anafulumiza Aisrayeli kuchita chomwe chinali cholondola, kusonyeza kuwopa koyenera kwa Mulungu, ndi kupereka kwa iye chimene amayenerera. Tiyenera kuchita chofananacho lerolino. Kokha mwakukhala mogwirizana ndi zifuno za Mulungu ndi pamene tingapeze ndi kusunga chiyanjo chake.
13. (a) Popanda kuwopa Mulungu, ndi mu msampha wotani mmene tingagweremo? (b) Ndimotani mmene dyera linayambukirira ansembe Achiisrayeli?
13 Popanda kuwopa koyenera kwa Mulungu, utumiki wathu kwa iye ungapangidwe kokha monga chinthu cha chizoloŵezi ndi kaamba ka phindu ladyera. Onani mmene Yehova anafunsira ansembe a Israyeli ponena za utumiki wawo pa kachisi: “‘[Ndani alipo pakati pa inu adzatseka zitseko? NW] Kuti musasonkhe moto chabe pa guwa langa la nsembe. Sindikondwera nanu,’ ati Yehova wa makamu, ‘ndipo sindidzalandira chopereka m’dzanja lanu.’” (Malaki 1:10) Aha, inde, ansembe anali pamenepo kugwira ntchito pa kachisi, akumatseka zitseko za kumalo opatulika, kusonkha moto pa maguwa a nsembe. Koma iwo sanachite ichi kwachabe. Iwo anali kuyang’ana kaamba ka ndalama ndi ziphuphu kuchokera kwa Aisrayeli omwe anabwera kudzapereka nsembe pa kachisi. Yehova sanapeze chisangalalo pa nthaŵiyo, ndipo iye sapeza chisangalalo tsopano, mu utumiki umene umachitika kokha kaamba ka phindu ladyera. Iwo uli wonyansa kwa iye.
14. Nchifukwa ninji pali kufunika kosatha kwa kudzichinjiriza motsutsana ndi dyera?
14 Kufunika kwa kukhala ogalamuka motsutsana ndi kudzikonda ndi dyera sizinazimiririke m’tsiku lathu. Mobwerezabwereza Malemba amatichenjeza ife molimbana ndi dyera, akumanena kuti anthu adyera sayanjidwa ndi Yehova. (1 Akorinto 6:10; Aefeso 5:5) M’kukwaniritsa utumiki wathu, lolani chikondi chathu ndi kuwopa Yehova zitisunge ife omasuka kuchoka ku kuchita iwo kaamba ka phindu ladyera. Tiyenera kukhala achangu kuchotsa zikhoterero zirizonse zoterozo zomwe zingabuke m’mitima yathu. Akulu ndi atumiki otumikira akuchenjezedwa mwapadera kusakhala “achisiriro chonyansa.” (Tito 1:7; 1 Timoteo 3:8; 1 Petro 5:2) Ena mwadala angakulitse maunansi kokha ndi abale omwe angawathandize iwo mwakuthupi, kutulukapo mu kukondwera ndi kusinkhasinkha kupereka uphungu kwa oterowo. Sitifunikira mpang’ono pomwe kukhala monga ansembe adyera a Israyeli omwe anali kuyang’ana kaamba ka zopereka ndi ziphuphu kuchokera kwa Aisrayeli anzawo.
15. (a) Ndimotani mmene Malaki anasonyezera kuti padzakhala owopa Yehova m’mbali zonse za dziko lapansi? (b) Ndi Malemba ena ati amene amachirikiza chimenechi?
15 Lerolino, ngati Yehova atafunsa funso lakuti, “Kuli kuti kundiwopa ine?” Kodi anthu alionse angayankhe kuti, ‘Ndife pano, amene timakuwopani’? Motsimikizirikadi! Ndani? Mboni zokhulupirika za Yehova, zomwe zikupezeka m’mbali zonse za dziko lapansi. Gulu la anthu amitundu yonse limeneli ndi ntchito imene amachita inanenedweratu pa Malaki 1:11: “‘Pakuti kuyambira kotulukira dzuŵa’ kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo . . . adzapereka dzina langa chofukiza ndi chopereka chowona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu,’ ati Yehova wa makamu.”—Onaninso Masalmo 67:7; Yesaya 33:5, 6; 41:5; 59:19; Yeremiya 32:39, 40.
16. Kuchokera kotulukira dzuŵa kufikira kolowera dzuŵa kungakhale ndi matanthauzo osiyana otani, ndipo ndimotani mmene ichi chikukwaniritsidwira?
16 Ndi moyenerera chotani nanga mmene Malaki pano akunenera za ntchito yaikulu imene ikuchitidwa m’tsiku lathu mwa kulalikira mbiri yabwino m’dziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14; Chivumbulutso 14:6, 7) Kuchokera kotulukira dzuŵa kufikira kolowera dzuŵa, m’lingaliro la chikhalidwe chadziko, kumatanthauza kuchokera kum’mawa kufikira kumadzulo. Mosasamala kanthu ndi kumene tingayang’ane m’dziko lapansi lerolino, timapeza owopa Yehova akuchita chifuniro chake. Kuchokera kotulukira dzuŵa kufikira kolowera dzuŵa kumatanthauzanso tsiku lonse lathunthu. Inde, chilemekezo chikuperekedwa mokhazikika ndi atumiki owopa Mulungu. Monga mmene Yehova analonjezera, dzina lake likulalikidwa m’dziko lonse lapansi ndi awo amene mowonadi amamuwopa iye.—Eksodo 9:16; 1 Mbiri 16:23, 24; Masalmo 113:3.
Sungani Kuwopa Mulungu Koyenera
17. Nchiyani chimene chingakhale chotulukapo cha kutaya kwathu ulemu kaamba ka Yehova ndi kumuwopa kwathu iye?
17 Kwa awo amene amalephera kulemekeza ndi kuwopa Yehova, kulambira ndi utumiki zimakhala cholemetsa. Yehova ananena kwa Aisrayeli kuti: “Koma inu muliipsa [dzina langa, NW] pakunena kuti, ‘Gome la Yehova laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, ‘chonyozeka.’ Mukutinso, Tawonani! ncholemetsa ichi!’” (Malaki 1:12, 13) Chofananacho chingakhale chowona m’nthaŵi zamakono. Kwa awo amene amataya kuwopa Yehova, misonkhano, utumiki wa m’munda, ndi machitachita ena a Chikristu angakhale cholemetsa.
18. Kuchokera kunthaŵi ndi nthaŵi, nchiyani chomwe chakhala chikuchitika kwa ena a atumiki a Mulungu amakono?
18 Zindikirani mmene oterowo analongosoledwera mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1937, Chingelezi: “Kwa awo osakhulupirika mwaŵi wa kutumikira Mulungu mwa kubweretsa zipatso zaufumu pamaso pa ena, monga mmene Ambuye analamulira, wakhala kokha phwando lotopetsa ndi lachizoloŵezi, limene silimapereka kwa iwo mwaŵi uliwonse wa kuwala m’maso mwa anthu. Kunyamula kwa uthenga wa ufumu kuchokera kunyumba ndi nyumba mu mtundu wosindikizidwa, ndi kupereka uwu kwa anthu, kulinso konyazitsa kwa anthu odzimva apamwamba oterewa. Iwo sapeza chimwemwe chirichonse mu icho . . . Chotero iwo amanena kuti, ndipo akupitiriza kunena kuti: ‘Kunyamula mabukhu uku kumazungulirazungulira kuli chabe makonzedwe ogulitsa mabukhu. Ndi ntchito yotopetsa chotani nanga mmene iyo iliri!’” Ngakhale lerolino pali awo amene, kuchokera ku nthaŵi ndi nthaŵi, amapeza utumiki wa m’munda kukhala wogwetsa ulesi ndi kupezeka pa misonkhano kotopetsa. Ichi ndi chimene chingachitike pamene titaya kuwopa kwathu Yehova ndipo, limodzi ndi iko, chikondi chathu kaamba ka iye.
19. Ndimotani mmene tingapitirizire kusonyeza chiyamikiro chathu kaamba ka makonzedwe a Yehova?
19 Kusunga kuwopa Yehova kudzatisunga ife kukhala odzichepetsa pamaso pake ndiponso oyamikira nthaŵi zonse za zonse zimene iye akuchita kaamba ka ife. Kaya tiri pa msonkhano wa kagulu kochepa m’nyumba kapena pa msonkhano waukulu wa makumi a zikwi mu bwalo la maseŵera, tiri oyamikira kwa Yehova kaamba ka mwaŵi wa kukhala limodzi ndi abale athu Achikristu. Tidzasonyeza kuyamikira kwathu mwakukhalapo pamenepo ndi mwa kufulumiza ena kupezeka ku “chikondano ndi ntchito zabwino” mwa kukambitsirana kwathu komangilira ndi ndemanga zimene timapanga mkati mwa misonkhano. (Ahebri 10:24, 25) Ngati uli mwaŵi wathu wa kusamalira mbali pa misonkhano, tidzapewa kusakonzekera kufikira pa mphindi yomalizira, kumasonkhanitsa malingaliro pamodzi mwaliŵiro. Musachite nkomwe ndi magawo oterowo monga chinachake chofala. Iwo uli mwaŵi wopatulika, ndipo njira imene timasamalira iwo iri chisonyezero china cha mmene timalemekezera ndi kuwopa Yehova.
20. (a) Nchiyani chimene sitiyenera kuiwala? (b) Ndi kumapeto otani kumene tingafike?
20 Ndi chotulukapo chomvetsa chisoni chotani nanga chimene chiripo kwa awo amene amataya kuwopa Mulungu! Iwo amasowa chiyamikiro kaamba ka mwaŵi wapadera wa kukhala ndi unansi ndi Wolamulira wa chilengedwe. “‘Ndine Mfumu yaikulu,’ ati Yehova wa makamu, ‘ndipo dzina langa ndi lowopsa pakati pa amitundu.’” (Malaki 1:14; Chivumbulutso 15:4) Lolani kuti tisaiwale chimenecho. Lolani kuti aliyense wa ife akhale monga wamasalmo amene ananena kuti: “Ine ndine wakuyanjana nawo onse akukuwopani.” (Masalmo 119:63) Pambuyo pa kulingalira nkhani imeneyi, tingabwere ku mapeto amodzimodziwo amene Solomo anachita pamene iye ananena kuti: “[Opani Mulungu wowona ndi kusunga malamulo ake. NW] Pakuti choyenera anthu onse ndi ichi. Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.”—Mlaliki 12:13, 14.
Maphunziro Kuchokera ku Bukhu la Malaki—
◻ Nchifukwa ninji Aisrayeli anali ndi mangawa a kuwopa Yehova?
◻ Ndimotani mmene machitidwe athu amasonyezera kuti kaya mowonadi timawopa Yehova?
◻ Nchiyani chimene chimatsimikizira kuti pali owopa Yehova kuzungulira pa dziko lonse lapansi lerolino?
◻ Nchifukwa ninji tiyenera kusunga kuwopa Mulungu koyenera?
[Mawu Otsindika patsamba 18]
Aisrayeli ananyoza Yehova mwa kupereka nyama za khungu, zotsimphina, kapena zodwala monga nsembe
[Chithunzi patsamba 17]
Kuchokera kotulukira dzuŵa kufikira kolowera dzuŵa, dzina la Yehova lidzapangidwa kukhala lalikulu