Nthawi ya Kuyesedwa ndi Kusefedwa
“Ndipo Ambuye yemwe mumfuna adzadza ku kachisi wake modzidzimutsa; [ndiponso ndi NW] mthenga wa chipangano . . . ndipo adzakhala ndi kuyenga ndi kuyeretsa.”—MALAKI 3:1, 3.
1, 2. (a) Kodi ndi mikhalidwe yotani imene inalipo pakati pa anthu a Mulungu mu zana la chisanu B. C.E.? (b) Kodi nchifukwa ninji ulosi wa Malaki uyenera kukhala wosangalatsa kwa ife?
“ALI KUTI Mulungu wachiweruzo?” Awo amene anadzutsa funso lachitokoso limenelo kubwerera m’mbuyomo zana la chisanu B. C.E. anadandaulanso: “Chiri chopanda phindu kutumikira Mulungu.” Kuwonongedwa kwa chipembedzo ndi makhalidwe abwino pakati pa anthu a Mulungu, Ayuda, kunadzutsa mkangano ponena za chiweruzo chaumulungu. Koma maso a Mulungu wowona amene sagona, anali pa iwo. Ndipo iye anatumiza mneneri wa Chihebri Malaki kuwadziwitsa iwo kuti ntchito yoyeretsa, nthawi ya kuyesa ndi kusefa, inali kutsogolo. Iwo akanadziwa kumene “Mulungu wa chiweruzo” anali pamene anabwera mwadzidzidzi kaamba ka chiweruzo!—Malaki 2:17; 3:1, 14, 15.
2 Ulosi wa Malaki uyenera kukhala wosangalatsa koposa mbiri chabe kwa ife. Chifukwa ninji? Popeza iwo mwachiwonekere uli ndi kukwaniritsidwa mu tsiku lathu. (Aroma 15:4) Inde, anthu a Yehova lerolino akhala akupita mkati mwa nthawi ya kuyesedwa ndi kusefedwa! Motani? Kuyang’anitsitsa kosamalitsa paulosi wa Malaki kudzatithandiza ife kuyankha.
3. Kodi nchiyani chimene chinaphatikizidwamo mu ntchito ya kuyenga ya makedzana?
3 Koma, choyamba, kodi nchifukwa ninji Yehova amaika anthu ake pa kuyesedwa ndi kusefedwa? Monga “wosanthula mitima,” iye anakonzekera kuyenga anthu ake olinganizidwa. (Miyambo 17:3; Masalmo 66:10) Mu nthawi za Baibulo ntchito ya kuyenga inaphatikizapo kutentha chitsulo ku mlingo wakusungunuka ndipo kenaka kuchotsa zoipa kapena mphala. Timawerenga: “Woyenga amayang’ana kachitidweko, kaya ataimilira kapena kukhala pansi, ndi kuyang’anitsitsa kosamalitsa, kufikira. . . chitsulo [chamadzi] chikhala ndi kawonekedwe ka kalilole wopukutidwa bwino, kuunikira chinthu chirichonse chozungulira icho; ngakhale woyenga, pamene akuyang’ana pa chitsulo, angadziwone iye mwini ngati kuti akuyang’ana pa kalilole, ndipo chotero iye angapange chiweruzo cholondola kwambiri ponena za kuyera kwa chitsulocho. Ngati iye wakhutiritsidwa, moto umachotsedwa, ndipo chitsulo chimachotsedwa m’ng’anjo; koma ngati sichinalingaliridwe kukhala choyera, ntovu wowonjezereka umaikidwa ndipo ntchitoyo imabwerezedwa.”(Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature, yolembedwa ndi J. McClintock ndi J. Strong) Golide kapena siliva woyengedwa motero anali wamtengo wapatali.—Yerekezani ndi Chivumbulutso 3:18.
4. Kodi nchifukwa ninji Yehova walola kuyesedwa ndi kusefedwa pakati pa anthu ake?
4 Yehova amalola kuyesedwa ndi kusefedwa kotero kuti ayenge, kapena kuyeretsa, anthu ake, kuwathandiza iwo kuunikira molongosoka chifaniziro chake. (Aefeso 5:1) Muntchito ya kuyenga, iye amachotsa mphala mwa kuyeretsa ziphunzitso zonyansa ndi machitachita. (Yesaya 1:25) Iye amasefanso kuchokera pakati pa anthu ake awo amene amakana kugonjera ku ntchito yoyenga ndi iwo amene “amakhala chokhumudwitsa ndi anthu amene amachita kusayeruzika.” Ichi chimayeretsa njira kaamba ka “ana a ufumu,” Israyeli wauzimu, kuti awale ndi kunyezimira kotero kuti gulu la padziko lapansi lingasonkhanitsidwe ndi kumamatira kwa iwo mwa gulu kaamba ka kupulumuka.—Mateyu 13:38, 41, 43; Afilipi 2:15.
Ntchito ya Malaki
5, 6. (a) Ndani, mwapadera, amene anali ndi thayo la mkhalidwe wotsika wauzimu wa Aisrayeli mu tsiku la Malaki? Nchifukwa ninji? (b) Kodi ndi chiyambukiro choipa chotani chimene ichi chinakhala nacho pa Aisrayeli onse?
5 Malaki analosera pambuyo pa 443 B. C.E., chifupifupi zana limodzi pambuyo pa kubwerera kwa Ayuda omangidwa ukapolo kuchokera ku Babulo. Zaka zoposa 70 zinali zitapita kuyambira pamene makhazikitsidwe a kumanganso kachisi anapangidwa ndi Zerubabele. Mkhalidwe wauzimu wa Aisrayeli unali utasweka kumalo otsika. Ndani, mwachindunji, amene anali ndi thayo? Ansembe! Motani? Iwo anali “kunyazitsa” dzina la Yehova mwakulandira nsembe zodwala ndi zopuwala. (Malaki 1:6-8) Iwo anapangitsa “ambiri kukhumudwa ndi lamulo” mwakulephera kulangiza anthu ndi kusonyeza tsankho mu chiweruzo.—Malaki 2:6-9; Yakobo 3:1.
6 Monga chotulukapo chake, Aisrayeli anayamba kukaikira kufunika kwa kutumikira Mulungu, ngakhale kukana kupereka chachikhumi chofunidwa ndi lamulo. (Malaki 3:610, 14, 15; Levitiko 27:30) Kufikira pamenepo iwo anali atagwa mu kudzipereka kwawo ku Lamulo la Mulungu kotero kuti ena anachita “mwambanda” ndi akazi awo, mwachidziwikire mwakuwaleka iwo ndi cholinga chofuna kukwatira akazi achikunja. Nkulekelanji, popeza machitachita onyansa amenewo monga kubwebweta, chigololo, kulumbira monama, ndi kunyenga zinali zofala pakati pa anthu a Mulungu!—Malaki 2:10-16; 3:5.
7, 8. Kodi nchiyani chomwe chinali ntchito ya mneneri Malaki?
7 Ntchito ya Malaki inali yachiwonekere. Mumkhalidwe wosabisira iye anavumbulutsa ansembe osasamalawo, ndipo iye anapanga anthu kuzindikira mkhalidwe wawo weniweni wauzimu. Komabe, iye anasonyeza kuti Mulungu wa chifundo chachikondi anali wokonzekera kukhululukira. “Bwererani kudza kwa ine, ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,” anadandaula tero Yehova. (Malaki 3:7) Malaki ananeneratu kuti KAmbuye wowona,” anali kudza ku kachisi wake kaamba ka chiweruzo. Ansembe anali ofunikira kuyeretsedwa ndi cholinga cha kufuna kukhala “opereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo.” (Malaki 3: 1-3) Mu kuwonjezerapo, anthuwo anaikidwa pa chidziwitso kuti “Ambuye wowona” adzakhala “mboni yofulumira” motsutsana ndi awo amene anapitirizabe mu machitachita onyansa.—Malaki 3:5.
8 Malaki anali wowona ku ntchito yake; iye anapereka chenjezo. Zomwe iye ananena zinali zaphindu kwa ansembe ndi anthu a m’tsiku lake. Komabe, mazana ambiri anapita ulosi wake usanawone zina za mbali zake zikukhala zowona mu kukwaniritsidwa kwake koyamba.
Kukwaniritsidwa Kwa Mu Zana Loyamba
9. Mkukwaniritsa ulosi wa Malaki, kodi ndani amene anali “mthenga”? Nchifukwa ninji mwayankha tero?
9 Akumalankhula kuchokera ku mpando wake wachifumu wokwezeka kumwamba, Woweruza Wamkulu anati: “Tawonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga.” (Malaki 3:1a) Kodi ndani amene anali “mthenga’’? Mlembi wa Baibulo Marko akuphatikiza maulosi a Malaki 3:1 ndi Yesaya 40:3 ndi kuwagwiritsira aŵiri onse kwa Yohane Mbatizi. (Marko 1:1-4) Yesu Kristu, nayenso, pambuyo pake anazindikiritsa Yohane monga “mthenga’’ ameneyo. (Mateyu 11:10-14) Chotero kunali kuti mu ngululu ya 29 C.E., Yohane Mbatizi anayamba ntchito yake monga “mthenga,” kalambula bwalo. Iye anayenera kukonzekera njira kaamba ka chiweruzo chakudza cha Yehova mwakukonzekeretsa Aisrayeli kaamba ka kudza kwa Woimira Wamkulu wa Mulungu, Yesu Kristu.
10. Kodi ndimotani mmene Yohane Mbatizi anatumikirira “kukonzekeretsa kaamba ka Yehova anthu okonzekera”? (Luka 1:17)
10 Kutumizidwa kwa Yohane nthaŵi isanakwane chinali chisonyezero cha Mulungu chachikondi kulinga kwa Ayuda. Mu unansi wa pangano ndi Yehova, iwo anafunikira kulapa machimo awo motsutsana ndi lamulo. Yohane anakonzanso nkhani za chipembedzo ndi kuvumbulutsa kunyenga kwa chipembedzo. (Mateyu 3:1-3, 7-12) Iye anadzutsa Ayuda owona mtima kudikirira Kristu kuti adzamutsate iye.—Yohane 1:35-37.
11. Kodi ndimotani mmene tingazindikirire “Ambuye wowona” amene akabwera ku kachisi modzidzimutsa
11 Ulosi wa Malaki ukupitiriza: “’Ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku kachisi wake modzidzimutsa; [ndiponso ndi NW] mthenga wa chipangano amene mukondwera naye,’ tawonani akudza ati Yehova wa makamu.” (Malaki 3:1b) Kodi ndani amene anali“Ambuye wowona” amene akafika ku kachisi wake “modzidzimutsa,” kapena mosayembekezeredwa? Liwu la Chihebri logwiritsidwa ntchito liri ha·’A·dhohnʹ. Kugwiritsira ntchito kwa liwu lotsimikiza ha (“a”) Kutsogolo kwa dzina laulemu lakuti ‘A·dhohnʹ (“Ambuye; Mbuye”) limaika malire ku kugwiritsira ntchito kwake kwa dzina laulemu limeneli kokha kwa Yehova Mulungu. Indedi, kunali ku “kachisi Wake” kumene Yehova akabwera.—Habakuku 2:20; Masalmo 11:4.
12. Kodi ndani yemwe ali “mthenga wa chipangano,” ndipo kodi “mthenga” ameneyo ali wa “pangano” liti?
12 Pambuyo pa kutchula mthenga mmodzi, Malaki anasonyeza kuti “Ambuye wowona” akafika ku “kachisi Wake” atatsagana ndi wina, mthenga wosiyana, “mthenga wa chipangano.” Kodi ameneyo akakhala ndani? Chabwino, m’chiyang’aniro cha mmene zinthu zinachitidwira, chiri chanzeru kumaliza kuti “mthenga wa chipangano” ali Yesu Kristu, amene Yohane Mbatizi anamudziwikitsa kwa ophunzira ake monga “Mwanawakhosa wa Mulungu.” (Yohane 1:29-34) Kodi Mesiya ali “mthenga” wa “Chipangano” chiti? Chitsimikiziro cha Luka 1:69-75 ndi Machitidwe 3:12, 19-26 chimapereka. lingaliro lakuti liri pangano la Abrahamu, pa maziko amene Ayuda anali oyambirira kupatsidwa mwawi wa kukhala olowa m’malo a Ufumu.
13. Kodi ndi mlingaliro lotani mmene “Ambuye wowona” Yehova adzabwerera ku kachisi?
13 “Mbuye wowona” Yehova sanabwere mwaumwini ku kachisi weniweniyo mu Yerusalemu. (1 Mafumu 8:27) Iye anabwera moimiridwa, kunena kuti, kupyolera mwa “mthenga wake wa chipangano,” Yesu Kristu, yemwe anabwera mu dzina la Yehova ndi chirikizo la mzimu woyera wa Mulungu.a
14. (a) Kodi nchifukwa ninji kuyeretsa kachisi kwa Yesu mu 30 C.E. mwachiwonekere kunali kokha mbali ya chimene chidzachitika? (b) Ndimotani ndipo ndi liti pamene kachisi anayeretsedwa mkukwaniritsa Malaki 3:1?
14 Mu ngululu ya 30 C.E., Yesu anabwera ku kachisi wa Yehova mu Yerusalemu ndi kutulutsa awo amene anali kuipanga iyo “nyumba ya malonda.” (Yohane 2:13-16) Koma iyi inali kokha mbali ya chomwe chinayenera kudza mu kukwaniritsa ulosi wa Malaki. Kutsatira chochitika chimenechi, Yohane, monga “mthenga,” anapitiriza kubatiza ndi kutsogoza ophunzira ake kwa Yesu. (Yohane 3:23-30) Komabe, pa Nisani 9, 33 C.E., Yesu anapanga kulowa kwake kwa chipambano mu Yerusalemu, kumadzipereka iyemwini monga Mfumu. (Mateyu 21:1-9; Zekariya 9:9) Yohane anamaliza ntchito yake, pamene anadulidwa mutu ndi Herode chifupifupi chaka chimodzi pambuyo pake. Chotero pamene Yesu anabwera ku kachisi pa Nisani 10, iye anabwera mwalamulo monga “mthenga wa chipangano,” woimira walamulo wa “Ambuye wowona” Yehova, mkukwaniritsa Malaki 3:1. Yesu anayeretsa kachisi, kutulutsira kunja awo amene anasandutsa iyo kukhala nyumba ya malonda, kugwetsa magome a anthu osintha ndalama. Iye anapitiriza kunena kuti:“Kodi sichinalembedwe [pa Yesaya 56:7],‘kuti nyumba ya [Yehova] idzatchedwa nyumba ya mapemphero a mitundu yonse’? Koma inu mwaiyesa iyo phanga la achifwamba.”—Marko 11:15-18.
15. Monga gulu, kodi ndimotani mmene atsogoleri achipembedzo a Chiyuda anavomerezera ku ntchito ya kuyenga, koma kodi nchiyani chimene chinali chowona ponena za ansembe ena?
15 Mwakutero chidziwitso chinatumikiridwa pa atsogoleri a chipembedzo a Aisrayeli kuti tsiku lawo linali litafika. Monga gulu, iwo anakana kulandira “mthenga wa chipangano” wa Yehova. Iwo ‘sanadikire tsiku la kudza kwake,’ popeza iwo anakana kugonjera modzichepetsa ku ntchito ya kuyenga ya Woyenga Wamkulu. (Malaki 3:2, 3) Iwo anayenera kusefedwa monga oyenera kaamba ka chiwonongeko. Mwachidziwikire, ngakhale kuli tero, panali “ana a Levi” ena amitima yabwino, popeza osati kale kwambiri pambuyo pa imfa ya Yesu “khamu lalikulu la ansembe [a Levi] anayamba kukhala omvera ku chikhulupiriro.”—Machitidwe 6:7.
16. Ndimotani ndipo ndi liti pamene “tsiku lalikulu ndi lowopsya la Yehova” linagwera mtundu wa Ayuda umenewo?
16 Pa Nisani 11, tsiku limodzi pambuyo pa kuyeretsa kachisi, Yesu mwamphamvu anavumbulutsa kunyenga kwa chipembedzo ndi kuneneratu za kuwonongedwa kwa kachisi ndi dongosolo la kachitidwe kazinthu la Chiyuda. (Mateyu, mutu 23, 24) Indedi, “Mulungu wa chiweruzo” anafika monga “mboni yofulumira” pa mtundu wa Chiyudawo zaka 37 pambuyo pake mu 70 C.E., pamene “tsiku lalikulu ndi lowopsya la Yehova” linawagwera iwo. (Malaki 2:17; 3:5; 4:5, 6) Panthawi imeneyo, Aisrayeli onse pamodzi, monga gulu lofanana ndi mtengo womwe unalephera kubereka zipatso zokoma, “anadulidwa ndi kutenthedwa” mwa chiwonongeko pa manja a Aroma. (Luka 3:3-14) Zonsezi ‘popeza sanazindikira nyengo ya mayang’aniridwe awo.’—Luka 19:44.
Kukwaniritsidwa Kwa Makono
17. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti ulosi wa Malaki udzapeza kukwaniritsidwa kowonjezereka mu nthawi za makono?
17 Koma bwanji ponena za kukwaniritsidwa kwachiwiri, kapena kwa makono, kwa ulosi wa Malaki? Mu zana loyamba, kukwaniritsidwa koyamba kunatsatira kudzozedwa kwa Yesu ndi mzimu woyera kudzakhala Mfumu yokhazikitsidwa ya Ufumu wa Mulungu. Mwanzeru, payenera kukhala kukwaniritsidwa kowonjezereka kwa ulosi wa pambuyo pa kukhazikitsidwa monga Mfumu kwa Yesu Kristu kumwamba mu 1914. Ulosi weniweniwo unasonyeza kuti ukapeza kukwaniritsidwa “lisanadze tsiku lalikulu ndi lowopsya la Yehova.” (Malaki 4:5) Pamene “tsiku la Yehova” linafika pa kachitidwe kazinthu ka Ayuda mu 70 C.E., Malemba amaloza kutsogolo ku “tsiku la Yehova” lamtsogolo mkati mwanthawi ino ya “kukhalapo” kwa Kristu—Mateyu 24:3; 2 Atesalonika 2:1, 2; 2 Petro 3: 10-13.
18. Mu 1922, ndimotani mmene anthu a Mulungu anakhalitsidwira maso kuti anali mu nthawi ya chiweruzo?
18 Kumayambiriro mu 1922, anthu a Yehova anachenjeza kuti iwo anali mu nthawi ya chiweruzo mkukwaniritsa ulosi wa Malaki. Nsanja ya Olonda (m’Chingelezi) ya September 1 inati: “Koma ulosi wa Malaki umayang’ana kupyola kukwaniritsidwa kwa mbali imodzi mu kuwoneka koyamba kwa Ambuye wathu, ndi kutsogolo ku nthawi pamene Mesiya adzabwera mu ulemerero ndi mphamvu, ndi pamene iye adzaweruza pakati pa anthu ake . . . Tsopano, kachiwirinso, nthawi ya chiweruzo yafika; kachiwirinso anthu ake odzinenera akuyesedwa ndi moto, ndipo ana owona mtima a Levi akusonkhanitsidwa pamodzi kaamba ka ntchito.”
19. Mkukwaniritsidwa kwa makono, ndi mwanjira yotani mmene “mthenga” anatumizidwira pasadakhale?
19 Monga kwasonyezedwa pa Malaki 3:1, mthenga wapadera anatumizidwa pasadakhale. Ichi chinatsimikizira kukhala, osati munthu mmodzi, koma monga gulu lotumikira monga Yohane Mbatizi. Kuyambira 1881 gulu limeneli lagwiritsira ntchito chomwe tsopano chikudziwika monga Watch Tower Bible and Tract Society mu ntchito yophunzitsa Baibulo yozindikirika. Ichi chinatulukapo m’kukhazikitsanso maziko a chowonadi chochuluka mu mitima ya anthu okonda Baibulo. Kwina kwakumveketsedwa kumeneku kuli: Munthu alibe moyo wosakhoza kufa, koma iye mwini ali moyo; kulibe helo wotentha; Yesu Kristu sadzabweranso m’thupi; Yehova ali Mulungu mmodzi, osati Utatu. Indedi, inali ntchito yomwe ‘inayeretsa njira pamaso pa Yehova’ kaamba ka ntchito yake ya chiweruzo.
20. (a) Ndi liti, mwachiwonekere, pamene Yehova anabwera ku kachisi? (b) Kodi ndi mafunsootani amene ichi chimadzutsa?
20 Modzidzimutsa, Yehova, monga “Ambuye wowona,” anabwera ku kachisi wake wauzimu. Liti? Njira ya kachitidwe kazinthu inakhazikitsidwa mu kukwaniritsidwa kwa zana loyamba. Kubwerera mu nthawi imeneyo Yesu anabwera ndi kuyeretsa kachisi zaka zitatu ndi theka pambuyo pa kudzozedwa monga Mfumu pa Yordano. Mowona kukachitidwe kameneko, kuyambira pamene Yesu anakhazikitsidwa monga mfumu mu ngululu ya 1914, chikuwoneka kukhala chanzeru kuti zaka zitatu ndi theka pambuyo pake iye akayenera kuyembekezeredwa kutsagana ndi “Ambuye wowona” Yehova ku kachisi wauzimu. Molingana ndi ulosi, kodi nchiyani chimene chikachitika kuyambira panthawi imeneyo kunka mtsogolo? Kuyesedwa ndi kusefedwa. Koma ichi chimadzutsa mafunso ena ofunika kwambiri: Kodi ndi zizindikiro zotani zimene ziripo za kuyeretsa kumeneku? Kodi
Mawu a m’munsi
a Pazochitika zingapo, athenga aungelo analankhula monga ngati kuti anali Yehova Mulungu, popeza iwo anali kuchita monga oimira a Yehova.—Genesis 31: 11-13; Oweruza 2:1-3; yerekezani ndi Genesis 16:11, 13.
Kodi Mungakumbukire?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova amalola anthu ake kupita pansi pa kuyesedwa ndi kusefedwa?
◻ Kodi ndimotani mmene Yohane Mbatizi anatumikirira monga “mthenga,” kalambula bwalo?
◻ Mu zana loyamba, kodi ndimotani mmene Yesu anabwerera ku kachisi monga “mthenga wa chipangano”?
◻ Kodi ndimotani mmene timadziwira kuti ulosi wa Malaki udzakhala ndi kukwaniritsidwa kwa mu nthawi za makono?
[Chithunzi patsamba 13]
Monga mthenga, Yohane Mbatizi anakonzekeretsa anthu kaamba ka “mthenga wa chipangano” wakudzayo