Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kuchokera pa Mateyu 11:11, kodi tinganene kuti Yesu anadziŵa pasadakhale kuti Yohane Mbatizi akafa Yesu asanafe?
Inde, Yesu mwachiwonekere anadziŵadi kuti Yohane sakakhalabe ndi moyo kufikira kukhala Mkristu wodzozedwa, pakuti Yesu anati: ‘Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu ufumu wa kumwamba amkulira iye.’—Mateyu 11:11.
Pamene mngelo Gabriyeli analengeza kubadwa kwa Yohane, ananeneratu za Yohane kuti ‘ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, . . . akakonzeratu [Yehova, NW] anthu okonzeka.’ Yohane anali kudzakhala kalambula bwalo, wokonzekeretsa anthu kudza kwa Mesiya wa Yehova. Koma chilengezo cha Mulungu chimenecho sichinasonyeze konse kuti Yohane mwiniyo akakhala wophunzira wa Mesiya wakudzayo, ndipo ngakhale m’mawu aulosi onenedwa ndi Zekariya, atate ŵa Yohane, munalibe lingaliro lililonse lokhudza zimenezo.—Luka 1:17, 67-79.
Chifukwa chake, pambuyo pakubatiza Yesu, Yohane anapitiriza kulalikira ndi kubatiza, kupitiriza ndi ntchito yake yakukonzekeretsa anthu. Mozizwitsa Yohane anadziŵa kuti Yesu akachita ubatizo ndi mzimu woyera, koma Yohane sananene kuti iyemwini akalandira mzimu woyera, ndi kukhala Mkristu wodzozedwa. (Mateyu 3:11) Yohane anazindikiranso kuti akacheperabe, pamene Yesu akawonjezerekabe.—Yohane 3:22-30.
Pamene Yesu ananena zimene tiŵerenga pa Mateyu 11:11, Yohane anali kale m’ndende. Yesu ananena pasadakhale kuti mneneri woponyedwa m’ndendeyo anali wamng’ono kwa wochepa amene mtsogolo akatumikira monga mfumu ndi wansembe kumwamba. Komabe, zikuwoneka kuti Yesu anadziŵanso kuti Yohane akamwalira posachedwa, kuchoka padziko lapansi njira “yatsopano” ya kumoyo wakumwamba isanatsegulidwe. (Ahebri 10:19, 20) Zimenezo zinatanthauza kuti Yohane sakakhalabe ndi moyo kufikira pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene kudzozedwa ndi mzimu woyera kwa ophunzira a Yesu kunayamba. Chifukwa chake, ndemanga ya Yesu pa Mateyu 11:11 ingawonedwenso kukhala chisonyezero chakuti iye anadziŵa kuti Yohane sakapita kumwamba.