Malo Kuchokera ku Dziko Lolonjezedwa
“Tsoka kwa Iwe, Korazini!”—Chifukwa Ninji?
INU motsimikizirika simukafuna Mulungu kulengeza tsoka pa inu, kodi mukatero? Talingalirani, kenaka, mmene Ayuda a mizinda itatu ya Galileya ayenera kukhala anadzimverera pamene Mwana wa Mulungu ndi Woweruza analengeza kuti:
“Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa m’Turo ndi m’Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m’ziguduli ndi m’phulusa. Komanso ndinena kwa inu kuti dzuŵa la kuweruza mlandu wawo wa Turo ndi Sidoni udzachepa ndi wanu. Ndipo iwe, Kapernao, . . . udzatsika kufikira ku dziko la akufa!”—Mateyu 11:21-23.
Malo ali pamwambapo amasumika pa umodzi wa mizinda imeneyo—Korazini. Chithunzithunzi chimenechi chinawonekeranso kaamba ka Julayi/Ogasiti mu 1989 Kalenda ya Mboni za Yehova. Mokondweretsa, mawu a Yesu pa Mateyu 11:21-23 ali mu programu ya kuŵerenga Baibulo ya Mboni za Yehova mkati mwa August. Nchiyani, kenaka, chimene tiyenera kudziŵa ponena za Korazini?
Chabwino, yang’anani pamene Korazini wakale anakhazikitsidwa. Inu mungawone mabwinja ake m’malo apatsogolo a chithunzi ichi. Chotsatira, onani mitengo pa malire a gombe la kumpoto kwa Nyanja ya Galileya. Pamenepo ndi pomwe Kapernao anali, chifupifupi makilomita atatu kutali. Kawonedwe ka chithunzithunzi cha m’mlengalenga chimenechi kangalingalire malo otsika otambalala, komabe Korazini m’chenicheni iri m’mapiri mamita 270 pamwamba pa gombe.
Chimathandizanso kudziŵa kuti pa chifupifupi mtunda umodzimodziwo kuchokera ku Kapernao, mphepete mwa malire a gombelo, panali Betsaida. Chotero, mwa kudzudzula mizinda itatu imeneyi, Yesu anali kusumika kwambiri pa malo aang’ono mozungulira malo ake a pakati a ntchito yake mu Galileya. (Mateyu 4:13; Marko 2:1; Luka 4:31) Nchifukwa ninji Yesu analengeza tsoka pa iwo?
Yesu anathera nthaŵi yochulukira ndi atumwi m’malo amenewa, ndipo anachita ntchito zamphamvu zambiri. Pafupi ndi Betsaida iye mozizwitsa anadyetsa anthu oposa 5,000, ndipo anabwezeretsa kuwona kwa mwamuna wakhungu. (Marko 8:22-25; Luka 9:10-17) Pakati pa zozizwitsa zake mkati kapena pafupi ndi Kapernao panali kuchiritsa kwake mnyamata wodwala wochokera kutali, kuchiritsa mwamuna wokhala ndi ziwanda, ndi kukhozetsa mwamuna wamanjenje kuyenda, ndi kuwukitsa mwana wamkazi wa mkulu wa sunagoge. (Marko 2:1-12; 5:21-43; Luka 4:31-37; Yohane 4:46-54) Pamene kuli kwakuti Baibulo silimanena molunjika kaamba ka ife “ntchito zamphamvu” zimene zikugwirizanitsidwa ndi Korazini, Mateyu 11:21 imasonyeza kuti Yesu anachita zozizwitsa mkati kapena pafupi ndi kumeneko. Komabe, anthu sakalapa ndi kuika chikhulupiriro mwa iye monga Mesiya yemwe anali ndi chirikizo la Mulungu.
Kuyang’ana pa malo omwe aikidwa muno a Yesu akuchita ntchito zoterozo, inu mungafunse kuti, ‘Kodi ndimotani mmene anthu a ku Korazini anakhalira osavomereza chotero?’ Mwinamwake mfungulo idzapezedwa pakati pa miyala ya black basalt imene akatswiri a zinthu zofotseredwa pansi anafukula pakati pa mabwinja amenewa, zokhala ndi deti kuchokera zana lachitatu C.E. Zotsalira zimenezi zimaphatikizapo sunagoge m’malo apakati pa mzindawo ndi malo okhalamo anthu apafupipo. Ina ya miyala imeneyo yochokera ku sunagoge inali ndi zithunzi zozokotedwa zachilendo. Za chiyani? Zolembedwa kuchokera ku nthanthi ya Chigriki, zonga ngati Medusa (Nsomba yaubweya) yonga njoka ndi chirombo, mbali ina munthu ndi mbali ina kavalo. Popeza kuti Chiyuda chiyenera kukhala chinatsutsa mwamphamvu zosemedwa za mafano zoterozo, nchifukwa ninji atsogoleri Achiyuda mu Korazini akazilola izo pa sunagoge yawo?
Nthanthi imodzi iri yakuti “mkhalidwe wa kuwoloŵa manja uyenera kukhala unali wa mwambo m’malo amenewo,” kupatsa Yesu chifukwa cha kuyembekezera kaamba ka chivomerezo chabwino mumzindawo.a Koma ngati zizindikiro za sunagoge zimenezi zimalingalira chirichonse ponena za mkhalidwe m’tsiku la Yesu, chiyenera kukhala kuti unyinji wa anthu mu Korazini mwapadera sanali odera nkhaŵa ndi kulambira “Atate mu mzimu ndi m’chowonadi.” (Yohane 4:23) Iwo anasonyeza chimenecho mwa kusalandira kwawo Mesiya wochita ntchito zozizwitsa.
Pamene Yesu anatumiza ophunzira 70, iye kachiŵirinso anagwiritsira ntchito kalongosoledwe kosinjirira koloŵetsamo kusavomereza kwa Korazini, Betsaida, ndi Kapernao. Ngati Agalileya anzake a Yesu a ku Korazini omwe anali ozoloŵerana ndi ntchito zake zamphamvu sanavomereze mokomera, ophunzirawo sayenera kudabwa ngati nzika za mizinda ina mu imene iwo analalikira sanawalandire iwo.—Luka 10:10-15.
Chotero pamene tikupenda mabwinja akuda opanda moyo a Korazini, tiyenera kukumbukira chenjezo lotanthauzidwa mu “tsoka” la Yesu. Kulephera kulapa, kuyankha ku ntchito ya Mulungu yomwe ikuchitidwa ndi anthu ake, kungatsogolere ku chitonzo ndi mtsogolo mosweka.
[Mawu a M’munsi]
a The World of the Bible, Volyumu 5, tsamba 44, yofalitsidwa ndi Educational Heritage, Inc., New York, 1959.
[Mapu patsamba 16]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Chorazin
Bethsaida
Capernaum
Sea of Galilee
Tiberias
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel
[Chithunzi patsamba 17]
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.