Chiitano Chachikondi kwa Otopa
“Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu.”—MATEYU 11:28.
1. Kodi Yesu anaonanji mu Galileya paulendo wake wolalikira wachitatu?
CHAKA cha 32 C.E. chitatsala pang’ono kuyamba, Yesu anali paulendo wake wachitatu wokalalikira m’chigawo cha Galileya. Anapyola m’mizinda ndi midzi, “namaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.” Pochita zimenezi, anaona makamu a anthu, ndipo “anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.”—Mateyu 9:35, 36.
2. Kodi Yesu anawathandiza motani anthu?
2 Komabe, Yesu anachita zoposa kumvera chifundo chabe makamuwo. Atalangiza ophunzira ake kupemphera kwa “Mwini zotuta,” Yehova Mulungu, anawatumiza kukathandiza anthu. (Mateyu 9:38; 10:1) Ndiyeno anapatsa anthu chitsimikizo chake cha njira yopezera mpumulo ndi chitonthozo chenicheni. Anawapatsa chiitano chotonthoza mtima chakuti: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.”—Mateyu 11:28, 29.
3. Kodi nchifukwa ninji chiitano cha Yesu chili chokopa ngakhale lerolino?
3 Lerolino, tikukhala m’nthaŵi imene anthu ambiri ali othodwa ndi olema. (Aroma 8:22; 2 Timoteo 3:1) Kwa ena, kungochita ntchito yochirikizira moyo kumawatengera nthaŵi ndi nyonga yochuluka kwakuti amatsala ndi yochepa kwambiri yokhala ndi banja lawo, mabwenzi, kapena kuchita kanthu kena. Ambiri ali othodwa ndi matenda aakulu, zopweteka, tondovi, ndi mavuto ena athupi ndi a maganizo. Povutika ndi zimenezo, ena amayesa kupeza mpumulo mwa kudziloŵetsa kwambiri m’zokondweretsa, zakudya, zakumwa, ndipo ngakhale anamgoneka. Ndithudi, zimenezi zimangoipitsiratu zinthu, zikumawonjezera mavuto ndi zipsinjo. (Aroma 8:6) Mwachionekere, chiitano cha Yesu chachikondicho chikumveka chokopa lerolino mofanana ndi kale lija.
4. Kodi ndi mafunso otani omwe tiyenera kuwalingalira kuti tipindule ndi chiitano cha Yesu chachikondi?
4 Komabe, kodi anthu a m’tsiku la Yesu anavutika ndi chiyani, moti nkuoneka “okambululudwa ndi omwazikana,” akumachititsa Yesu kuwamvera chifundo? Kodi mitolo ndi akatundu amene ananyamula anali chiyani, ndipo kodi chiitano cha Yesu chinawathandiza motani? Mayankho a mafunso ameneŵa angatithandize kwambiri kupindula ndi chiitano chachikondi cha Yesu kwa otopa.
“Akulema ndi Akuthodwa”
5. Kodi nchifukwa ninji kunali koyenera kuti mtumwi Mateyu alembe za chochitika chimenechi cha mu utumiki wa Yesu?
5 Nkosangalatsa kuona kuti ndi Mateyu yekha amene analemba za chochitika chimenechi cha mu utumiki wa Yesu. Pakuti anakhalapo wokhometsa msonkho, Mateyu, wotchedwanso Levi, anadziŵa bwino lomwe mtolo winawake umene anthu anausenza. (Mateyu 9:9; Marko 2:14) Buku lakuti Daily Life in the Time of Jesus limati: “Misonkho imene [Ayuda anayenera] kukhoma monga ndalama ndi zinthu kapena mautumiki inali yaikulu kwambiri, ndipo inakulirapo kwenikweni chifukwa chakuti panali mitundu iŵiri ya msonkho panthaŵi imodzimodzi, misonkho ya boma ndi misonkho ya chipembedzo; ndipo panalibe waung’ono.”
6. (a) Kodi ndi njira yotani yokhometsera msonkho imene anagwiritsira ntchito m’nthaŵi ya Yesu? (b) Kodi nchifukwa ninji okhometsa msonkho anali ndi mbiri yoipa? (c) Kodi Paulo anaona kukhala kofunika kukumbutsa Akristu anzake za chiyani?
6 Chimene chinachititsa zonsezi kukhala zothodwetsa kwambiri chinali njira yapanthaŵiyo yokhometsera msonkho. Akulu a boma Achiroma anapatsa mphamvu yokhometsa misonkho m’zigawozo kwa awo amene anagula mphamvuyo ndi ndalama zochuluka kwambiri. Iwonso analemba ntchito anthu a m’midzimo ya kuyendetsa ntchito yeniyeniyo yokhometsa msonkho. Aliyense pantchito yake anakuona kukhala kololeka kuwonjezera msonkho kuti apezerepo phindu lake. Mwachitsanzo, Luka anasimba kuti panali “mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyu; ndipo iye anali mkulu wa amisonkho, nali wachuma.” (Luka 19:1, 2) “Mkulu wa amisonkho” Zakeyu ndi antchito ake mwachionekere anadzilemeretsa mwa kudyera anthu masuku pamutu. Nkhanza yake ndi chinyengo cha njira yoteroyo zinachititsa anthu kuika okhometsa msonkho pakati pa ochimwa ndi akazi achigololo, ndipo zikuoneka kuti nthaŵi zambiri anayeneradi kuonedwa motero. (Mateyu 9:10; 21:31, 32; Marko 2:15; Luka 7:34) Popeza kuti anthu anamva kukhala ndi mtolo wosapiririka, mposadabwitsa kuti mtumwi Paulo anakuona kukhala koyenera kukumbutsa Akristu anzake kusataya mtima pokhala m’goli la Aroma koma kuti ‘apereke kwa anthu onse mangawa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa.’—Aroma 13:7a; yerekezerani ndi Luka 23:2.
7. Kodi malamulo achilango ankhalwe Achiroma anawonjezera motani mtolo wa anthu?
7 Paulo anakumbutsanso Akristu za kupereka “kuwopa kwa eni ake a kuwawopa; ulemu kwa eni ake a ulemu.” (Aroma 13:7b) Aroma anadziŵika ndi nkhanza ndi malamulo awo achilango ankhalwe. Kaŵirikaŵiri anagwiritsira ntchito kumenya, kukwapula, zilango zoipa za m’ndende, ndi kunyonga, kuti achititse anthu kukhala ogonjera. (Luka 23:32, 33; Machitidwe 22:24, 25) Ngakhale atsogoleri Achiyuda anapatsidwa mphamvu ya kupereka zilango zimenezo pamene anakuona kukhala koyenera. (Mateyu 10:17; Machitidwe 5:40) Njira yoteroyo inali yopondereza kwambiri, kapena yodidikiza, kwa aliyense wokhala pansi pake.
8. Kodi atsogoleri achipembedzo anaika motani mtolo pa anthu?
8 Komabe, choipa kuposa ngakhale misonkho ndi malamulo a Aroma chinali mtolo umene atsogoleri achipembedzo anaika pa anthu wamba a panthaŵiyo. Kwenikweni, kukuoneka kuti chimenechi ndicho chinali nkhaŵa yaikulu ya Yesu pamene ananena za anthuwo kukhala “akulema ndi akuthodwa.” Yesu ananena kuti m’malo mopatsa anthu oponderezedwawo chiyembekezo ndi chitonthozo, atsogoleri achipembedzo “amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapeŵa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo.” (Mateyu 23:4; Luka 11:46) Munthu sangalephere kuona m’Mauthenga Abwino mkhalidwe woonekera poyera wa atsogoleri achipembedzo—makamaka alembi ndi Afarisi—monga gulu lodzikuza, lopanda chifundo, ndi lonyenga. Iwo anaona anthu wamba kukhala otsika, abuluthu ndi odetsedwa, ndipo ananyansidwa ndi alendo okhala pakati pawo. Ndemanga ina yonena za mkhalidwe wawo ikuti: “Munthu amene asenzetsa kavalo katundu wolemera kwambiri masiku ano amapatsidwa mlandu ndi lamulo. Bwanji ponena za munthu amene anasenzetsa katundu wa malamulo okwanira 613 pa ‘anthu apansi’ amene sanaphunzitsidwe za chipembedzo; ndiyeno, popanda kuwathandiza mwa njira iliyonse, anawasuliza kukhala opanda umulungu?” Ndithudi, mtolo weniweni sunali Chilamulo cha Mose, koma miyambo yochuluka younjikidwa pa anthu.
Chochititsa Vuto Chenicheni
9. Kodi mikhalidwe ya anthu a m’nthaŵi ya Yesu inali motani poyerekezera ndi ija ya m’tsiku la Mfumu Solomo?
9 Nthaŵi zina mtolo wa zandalama unali waukulu kwambiri pa anthuwo, kwakuti umphaŵi unali wofalikira. Aisrayeli anayenera kupereka msonkho woyenera malinga ndi Chilamulo cha Mose. Ndiyeno, mkati mwa ulamuliro wa Solomo, anthu anapereka ndalama zochirikiza ntchito zomanga za mtunduwo zofuna ndalama zambiri, monga kumanga kachisi ndi nyumba zina. (1 Mafumu 7:1-8; 9:17-19) Komabe, Baibulo limatiuza kuti anthu anali ‘kudya ndi kumwa namakondwera. . . . Ndipo Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.’ (1 Mafumu 4:20, 25) Kodi chinachititsa kusiyana nchiyani?
10. Kodi nchiyani chinachititsa mkhalidwe wa Israyeli kukhala wotero pofika m’zaka za zana loyamba?
10 Malinga ngati mtunduwo unaimabe nji pa kulambira koona, uwo unakhala ndi chiyanjo cha Yehova ndipo unadalitsidwa ndi chisungiko ndi chitukuko mosasamala kanthu za ndalama zochuluka zowonongedwa pantchito za mtunduwo. Komabe, Yehova anachenjeza kuti ‘akadzabwerera pang’ono pokha osatsata [iye], kapena osasunga malamulo [ake],’ adzaona zotulukapo zatsoka. Kwenikweni, “Israyeli adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.” (1 Mafumu 9:6, 7) Zinthu zinadzakhaladi motero. Israyeli anadzakhala pansi pa ulamuliro wachilendo, ndipo ufumu umene panthaŵi ina unali waulemerero unadzatsika kukhala wolamuliridwa ndi ena. Ha, ndi mphotho yotani nanga ya kunyalanyaza mathayo awo auzimu!
11. Kodi nchifukwa ninji Yesu anaona kuti anthu anali “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa”?
11 Zonsezi zimatithandiza kuzindikira chifukwa chake Yesu anaona kuti anthu omwe anaonawo “anali okambululudwa ndi omwazikana.” Iwo anali Aisrayeli, anthu a Yehova, amene kwakukulukulu anali kuyesa kutsatira malamulo a Mulungu ndi kulambira mwa njira yovomerezeka. Komabe, iwo analimidwa pamsana ndi kuponderezedwa osati chabe ndi magulu a ndale ndi a malonda komanso ndi atsogoleri achipembedzo ampatuko pakati pawo. ‘Ananga nkhosa zopanda mbusa’ chifukwa chakuti analibe wowasamalira kapena wowatetezera. Anafunikira chilimbikitso chakuti apirire nacho mikhalidwe yankhalwe. Ha, chiitano cha Yesu chachikondi ndi chachifundo chinali chapanthaŵi yake chotani nanga!
Chiitano cha Yesu Lerolino
12. Kodi ndi zovuta zotani zimene atumiki a Mulungu pamodzi ndi anthu ena oona mtima amakhala nazo lerolino?
12 Zinthu lerolino nzofanana ndi zimenezo m’njira zambiri. Anthu oona mtima amene amayesa kukhala oona mtima pantchito zawo amapeza kuti zitsenderezo ndi zofuna za dziko loipali nzovuta kuchita nazo. Ngakhale aja amene anapatulira miyoyo yawo kwa Yehova amakhudzidwa. Malipoti amasonyeza kuti ena pakati pa atumiki a Yehova amakuona kukhala kovutirapo nthaŵi zonse kukwaniritsa mathayo awo onse, ngakhale kuti amafuna kutero. Amamva kukhala olema, otopa, olefuka. Ena amafika ngakhale pakuganiza kuti mwina angapeze mpumulo ngati angaiŵale zonse ndi kupita kwinakwake kuti akalingalirenso bwino. Kodi zinakuchitikiranipo zimenezo? Kodi mumadziŵa munthu wina amene ali mumkhalidwe umenewo? Inde, chiitano chotonthoza mtima cha Yesu chimatanthauza zochuluka kwa ife lerolino.
13. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikiza kuti Yesu akhoza kutithandiza kupeza mpumulo ndi chitonthozo?
13 Yesu asanapereke chiitano chake chachikondicho, anati: “Zinthu zonse zinaperekedwa kwa ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziŵa Mwana, koma Atate yekha; ndi palibe wina adziŵa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.” (Mateyu 11:27) Chifukwa cha chikondi chachikulu chimenechi pakati pa Yesu ndi Atate wake, tili otsimikiza kuti mwa kulandira chiitano cha Yesu ndi kukhala ophunzira ake, tingakhale ndi ubwenzi ndi Yehova, “Mulungu wa chitonthozo chonse.” (2 Akorinto 1:3; yerekezerani ndi Yohane 14:6.) Ndiponso, popeza kuti ‘zinthu zonse zaperekedwa kwa iye,’ Yesu Kristu yekhayo ndiye ali ndi mphamvu ndi ulamuliro wa kupeputsa mitolo yathu. Mitolo iti? Ija yoikidwa pa ife ndi andale, amalonda, ndi zipembedzo, limodzinso ndi mtolo wa uchimo wathu wa choloŵa ndi kupanda ungwiro kwathu. Ha, limenelo ndi lingaliro losonkhezera ndi lolimbikitsa chotani nanga kuyambira pachiyambi penipeni!
14. Kodi ndi kulema kotani kumene Yesu anaperekapo mpumulo?
14 Yesu anapitiriza kunena kuti: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu.” (Mateyu 11:28) Ndithudi, Yesu sanali kutsutsa kugwira ntchito zolimba, pakuti kaŵirikaŵiri analangiza ophunzira ake kulimbikira pantchito imene anali nayo. (Luka 13:24) Koma “kulema” (“kugwira ntchito yotopetsa,” Kingdom Interlinear) konenedwa pano kumatanthauza kugwira ntchito yolimba kwa nthaŵi yaitali ndipo kofooketsa, kaŵirikaŵiri popanda phindu lililonse. Ndipo “kuthodwa” kuli ndi lingaliro la kutopa kopambanitsa. Kusiyana kumene kulipo kungafaniziridwe ndi kuja kwa munthu wokumba chuma chobisika ndi uja wokumba maenje mumsasa wachibalo. Onse akuchita ntchito yolimba yofanana. Wina amachita ntchitoyo mofunitsitsa, koma winayo, imakhala yotopetsa nthaŵi zonse. Kusiyana kumakhala pa cholinga chake cha ntchitoyo kapena kupanda kwake cholinga.
15. (a) Kodi ndi mafunso otani amene tiyenera kudzifunsa ngati timva kuti tasenza mtolo wolemera? (b) Kodi tinganenenji za zimene zimachititsa mitolo yathu?
15 Kodi mumamva kuti muli “akulema ndi akuthodwa,” kuti pali zinthu zochuluka kwambiri zofuna nthaŵi ndi nyonga yanu? Kodi mitolo imene mwanyamula ikuoneka kukhala yokulemerani kwambiri? Ngati ikutero, kungakhale kothandiza kudzifunsa nokha kuti, ‘Kodi ndikulema kaamba ka chiyani? Kodi ndanyamula katundu wa mtundu wanji?’ Ponena za zimenezi, wothirira ndemanga pa Baibulo, zaka zoposa 80 zapitapo anati: “Ngati tipenda mitolo ya moyo tipeza kuti imagwa m’magulu aŵiri; tingatche magulu ameneŵa kukhala a [mitolo] yodziikira ndi yosapeŵeka: yochititsidwa ndi zochita zathu, ndi yosachititsidwa ndi zochita zathu.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Titapenda mosamalitsa, ambiri tingadabwe ndi kuchuluka kwa mitolo imene timadziikira tokha.”
16. Kodi ndi mitolo yotani imene tingadziikire tokha mopanda nzeru?
16 Kodi mitolo ina imene tingadziikire tokha ndi yotani? Lerolino, tikukhala m’dziko lokonda chuma, lokondetsa zokondweretsa, ndi lachisembwere. (2 Timoteo 3:1-5) Ngakhale Akristu odzipatulira amasonkhezeredwa nthaŵi zonse kuti atsatire mafashoni ndi masitayelo a dzikoli. Mtumwi Yohane analemba za “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo.” (1 Yohane 2:16) Zimenezi ndi zisonkhezero zamphamvu zimene zingatiyambukire mosavuta. Anthu ena adziloŵetsa m’ngongole zochuluka kotero kuti asangalale ndi zokondweretsa zambiri za dziko kapena kuti akhalebe ndi mtundu winawake wa moyo. Ndiyeno amapeza kuti ayenera kuwonongera nthaŵi yochuluka pantchito, kapena kuchita ntchito zosiyanasiyana kuti apeze ndalama zobwezera ngongole zawo.
17. Kodi ndi mkhalidwe wotani umene ungachititse kusenza katundu kukhala kovutirapo, ndipo kodi thandizo lake lingakhale lotani?
17 Ngakhale kuti munthu angaganize kuti sikulakwa kukhala ndi zinthu zina kapena kuchita zinthu zina zimene ena amachita, kuli kofunika kwambiri kupenda ndi kuona kuti mwina akuwonjezera katundu wosafunikira. (1 Akorinto 10:23) Pakuti munthu ali ndi mlingo wa zimene anganyamule, ayenera kutula chinthu china kuti awonjezerepo katundu wina. Kaŵirikaŵiri, ndi zinthu zofunika kwambiri pa mkhalidwe wathu wauzimu—phunziro laumwini la Baibulo, kupezeka pamisonkhano, ndi utumiki wakumunda—zimene zimayamba kutulidwa pansi. Chotsatirapo chimakhala kutaya nyonga yauzimu, kumene kumachititsanso kusenza katunduyo kukhala kovutirapo. Yesu Kristu anachenjeza za ngozi imeneyo pamene anati: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha.” (Luka 21:34; Ahebri 12:1) Ndi kovuta kuti munthu wonyamula katundu wolemera ndi wotopa aone msampha ndi kuupeŵa.
Chitonthozo ndi Mpumulo
18. Kodi Yesu amalonjezanji kwa aja amene adza kwa iye?
18 Chotero, Yesu mwachikondi anapereka chithandizo: “Idzani kuno kwa ine . . . ndipo ine ndidzakupumulitsani inu.” (Mateyu 11:28) Mawu akuti “kupumulitsa” panopa ndiponso akuti “mpumulo” pa vesi 29 amachokera ku mawu Achigiriki ofanana ndi liwu limene matembenuzidwe a Septuagint amagwiritsira ntchito pomasulira liwu Lachihebri lakuti “sabata” kapena “kusunga sabata.” (Eksodo 16:23) Motero, Yesu sanalonjeze kuti aja amene adza kwa iye sadzakhalanso ndi ntchito, koma analonjeza kuti adzawapumulitsa kuti akhale okonzeka kaamba ka ntchito imene anayenera kuchita mogwirizana ndi chifuno cha Mulungu.
19. Kodi munthu ‘amadza motani kwa Yesu’?
19 Tsopano kodi munthu ‘amadza motani kwa Yesu’? Kwa ophunzira ake, Yesu anati: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge [mtengo wake wozunzirapo, NW], nanditsate ine.” (Mateyu 16:24) Motero, kudza kwa Yesu kumatanthauza kusiya chifuniro chathu ndi kutenga cha Mulungu ndi cha Kristu, tikumalandira katundu wa thayo, ndi kuchita zimenezo mopitirizabe. Kodi zonsezi zimafuna zochuluka mopambanitsa? Kodi zimafuna nsembe yaikulu kwambiri? Tiyeni tipende zimene Yesu ananena atapereka chiitano chachikondi kwa otopa.
Kodi Mungakumbukire?
◻ Kodi anthu a m’tsiku la Yesu analemetsedwa motani?
◻ Kodi nchiyani kwenikweni chinachititsa vuto la anthuwo?
◻ Kodi tiyenera kudzipenda motani ngati timva kuti tasenza zolemera kwambiri?
◻ Kodi ndi mitolo iti imene tingadziikire tokha mopanda nzeru?
◻ Kodi tingalandire motani chitonthozo chimene Yesu analonjeza?
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi ina ya mitolo imene tingadziikire tokha ndi yotani?
[Mawu a Chithunzi patsamba 15]
Chilolezo cha Bahamas Ministry of Tourism