Khalani Olimba Mtima!
“Khalani olimba mtima ndi kunena kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga.’”—AHEBRI 13:6, NW.
1. Kodi ndikulimba mtima kotani kumene kunasonyezedwa ndi awo amene anaphunzira chowonadi cha Mulungu m’zaka za zana loyamba C.E.?
MUNALI m’zaka za zana loyamba la Nyengo Yathu. Mesiya woyembekezeredwa kwanthaŵi yaitaliyo anali atadza. Iye anali ataphunzitsa ophunzira ake bwino lomwe ndipo anali atayambitsa ntchito yofunika ya kulalikira. Inali nthaŵi yakuti anthu amve mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Chifukwa chake, amuna ndi akazi amene anali ataphunzira chowonadi molimba mtima analengeza uthenga wabwino kwambiri umenewo.—Mateyu 28:19, 20.
2. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimafunikira kulimba mtima lerolino?
2 Ufumuwo unali usanakhazikitsidwe m’masiku amenewo. Koma Mfumu Yosankhidwiratu, Yesu Kristu, inali italosera ponena za kukhalapo kwake kosaoneka kwamtsogolo mumphamvu ya Ufumu. Kukasonyezedwa ndi zinthu zonga nkhondo zosayerekezeredwa ndi zina, njala, miliri, zivomezi, ndi kulalikidwa kwa mbiri yabwino padziko lonse. (Mateyu 24:3-14; Luka 21:10, 11) Monga Mboni za Yehova, timafunikira kulimba mtima kuti tilimbane ndi mikhalidwe imeneyi ndi chizunzo chimene timakumana nacho. Chifukwa chake kudzakhala kopindulitsa kulingalira nkhani za m’Baibulo zonena za olengeza a Ufumu olimba mtima a m’zaka za zana loyamba C.E.
Kulimba Mtima kwa Kutsanzira Kristu
3. Kodi ndani amene amapereka chitsanzo chabwino koposa cha kulimba mtima, ndipo kodi kunanenedwanji za iye pa Ahebri 12:1-3?
3 Yesu Kristu amatipatsa chitsanzo chabwino koposa cha kulimba mtima. Atatchula za “mtambo waukulu” wa mboni za Yehova zolimba mtima zokhalako Chikristu chisanadze, mtumwi Paulo anafotokoza za Yesu mwa kunena kuti: “Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo, NW], nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu. Pakuti talingirirani iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.”—Ahebri 12:1-3.
4. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kulimba mtima poyesedwa ndi Satana?
4 Pambuyo pa ubatizo wake ndi masiku 40 a kusinkhasinkha, kupemphera, ndi kusala kudya m’chipululu, Yesu anatsutsa Satana molimba mtima. Poyesedwa ndi Mdyerekezi kuti asandutse miyala kukhala mkate, Yesu anakana chifukwa chakuti kuchita chozizwitsa kuti akhutiritse chikhumbo chaumwini kunali kolakwa. “Kwalembedwa,” Yesu anatero, “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa [Yehova, NW].” Pamene Satana anamtokosa kudumpha pamwamba pa chimbudzi cha kachisi, Yesu anakana chifukwa chakuti kuchita zimenezo kukanakhala kuyesa Mulungu kuti ampulumutse pakudzipha mwadala. “Ndiponso kwalembedwa,” anatero Kristu, “Usamuyese [Yehova, NW] Mulungu wako.” Satana anamlonjeza kuti akampatsa maufumu onse a dziko ngati ‘atamlambira’ (NW), koma Yesu sakanatha kupatuka ndi kuchirikiza chitonzo cha Mdyerekezi chakuti anthu sangakhale okhulupirika kwa Mulungu pansi pa chiyeso. Chotero Yesu analengeza kuti: “Choka Satana, pakuti kwalembedwa, [Yehova, NW] Mulungu wako udzimgwadira, ndipo iye yekhayekha udzamlambira.” Pomwepo, Woyesayo “analekana naye kufikira nthaŵi ina.”—Mateyu 4:1-11; Luka 4:13.
5. Kodi nchiyani chimene chingatithandize kuchilimika m’mayesero?
5 Yesu anali wogonjera kwa Yehova ndipo anali wotsutsana ndi Satana. Ngati ife mofananamo ‘tigonjera Mulungu ndi kutsutsa Mdyerekezi, adzatithaŵa.’ (Yakobo 4:7, NW) Mofanana ndi Yesu, tingachilimike m’mayesero molimba mtima ngati tigwiritsira ntchito Malemba, mwinamwake ngakhale kugwira mawu ake panthaŵi imene tikuyesedwa kuchita chinthu cholakwa. Kodi tingagonjere chiyeso cha kuba ngati panthaŵiyo tibwereza kunena lamulo la Mulungu lakuti: “Usabe”? Kodi Akristu aŵiri angagonjere pakuchita chisembwere ngati ngakhale mmodzi wa iwo molimba mtima agwira mawu akuti: “Usachite chigololo”?—Aroma 13:8-10; Eksodo 20:14, 15.
6. Kodi ndimotani mmene Yesu analiri wolaka dziko wolimba mtima?
6 Monga Akristu odedwa ndi dzikoli, tikhoza kupeŵa mzimu wake ndi makhalidwe ake auchimo. Yesu anauza otsatira ake kuti: “M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi ine.” (Yohane 16:33) Analaka dziko mwa kusakhala wofanana nalo. Chitsanzo chake monga wolaka ndi chotulukapo cha njira yake ya kusunga umphumphu zingatichititse kukhala olimba mtima kumtsanzira mwa kukhala olekana ndi dzikoli ndi osadetsedwa nalo.—Yohane 17:16.
Kulimba Mtima kwa Kupitirizabe Kulalikira
7, 8. Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kupitirizabe kulalikira mosasamala kanthu za chizunzo?
7 Yesu ndi ophunzira ake anadalira Mulungu kaamba ka kulimba mtima kuti apitirizebe kulalikira mosasamala kanthu za chizunzo. Kristu anakwaniritsa utumiki wake molimba mtima mosasamala kanthu za chizunzo, ndipo pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E., otsatira ake ozunzidwa anapitirizabe kulengeza mbiri yabwino ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo Achiyuda anayesa kuwaletsa. (Machitidwe 4:18-20; 5:29) Ophunzirawo anapemphera kuti: “[Yehova, NW] penyani mawu awo akuwopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse.” Ndipo chinachitika nchiyani? “Mmene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo,” cholembedwacho chimatero, “ndipo anadzazidwa onse ndi mzimu woyera, nalankhula mawu a Mulungu molimbika mtima.”—Machitidwe 4:24-31.
8 Popeza kuti anthu ambiri lerolino samakondweretsedwa ndi mbiri yabwino, kaŵirikaŵiri kulimba mtima kumafunika kuti tipitirizebe kuwalalikira. Makamaka pamene atumiki a Yehova azunzidwa, amafunikira kulimbika mtima kopatsidwa ndi Mulungu kotero kuti apereke umboni wokwanira. (Machitidwe 2:40; 20:24) Nchifukwa chake Paulo wolengeza wa Ufumu wolimba mtimayo anauza wantchito mnzake wachichepere ndi wachidziŵitso chochepa kuti: “Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso. Potero usachite manyazi paumboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wake; komatu umve masautso ndi uthenga wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu.” (2 Timoteo 1:7, 8) Ngati tipempherera kulimba mtima, tidzakhala okhoza kupitirizabe kulalikira, ndipo ngakhale chizunzo sichidzatichotsera chisangalalo chathu monga olengeza Ufumu.—Mateyu 5:10-12.
Kulimba Mtima kwa Kuima Kumbali ya Yehova
9, 10. (a) Kodi nchiyani chimene Ayuda ndi Akunja a m’zaka za zana loyamba anachita kuti akhale otsatira a Kristu obatizidwa? (b) Kodi nchifukwa ninji kulimba mtima kunali kofunika kuti akhale Akristu?
9 Ayuda ndi Akunja ambiri a m’zaka za zana loyamba analeka miyambo yosachokera m’malemba kuti akhale otsatira Kristu obatizidwa. Mwamsanga pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E., “chiŵerengero cha akuphunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.” (Machitidwe 6:7) Ayuda amenewo analimbika mtima kuti adule maunansi awo ndi chipembedzo ndi kuvomereza Yesu monga Mesiya.
10 Kuyambira mu 36 C.E., Akunja ambiri anakhala okhulupirira. Pamene Korneliyo, ziŵalo za banja lake, ndi Akunja ena anamva mbiri yabwino, anailandira nthaŵi yomweyo, analandira mzimu woyera, ndipo ‘anabatizidwa m’dzina la Yesu Kristu.’ (Machitidwe 10:1-48) Ku Filipi mdindo wandende Wachikunja ndi banja lake analandira Chikristu mofulumira, “nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake.” (Machitidwe 16:25-34) Kulimba mtima kunafunika kuti atenge njira zotero chifukwa chakuti Akristu anali kagulu kozunzidwa ndi kodedwa. Ndipo adakali otero. Koma ngati inu simunadzipatulire kwa Mulungu ndi kubatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova, kodi ino sinthaŵi yanu ya kutenga njira zimenezi za kulimba mtima?
Kulimba Mtima m’Mabanja Ogaŵanika
11. Kodi nzitsanzo zabwino zotani za kulimba mtima zimene Yunike ndi Timoteo anapereka?
11 Yunike ndi mwana wake Timoteo amapereka zitsanzo zabwino za chikhulupiriro cha kulimba mtima m’banja logaŵanika mwachipembedzo. Ngakhale kuti Yunike anali ndi mwamuna wachikunja, iye anaphunzitsa mwana wake “malembo opatulika” kuyambira ukhanda wake. (2 Timoteo 3:14-17) Atakhala Mkristu, anasonyeza “chikhulupiriro chosanyenga.” (2 Timoteo 1:5) Iye analinso ndi kulimba mtima kwa kukhomereza chiphunzitso cha Chikristu mwa Timoteo pamene anali kupereka ulemu wa umutu kwa mwamuna wake wosakhulupirirayo. Ndithudi, chikhulupiriro chake ndi kulimba mtima zinafupidwa pamene mwana wake wophunzitsidwa bwinoyo anasankhidwa kutsagana ndi Paulo pamaulendo aumishonale. Ha, mmene zimenezi zingalimbitsire mtima makolo Achikristu amene ali mumkhalidwe wofananawo nanga!
12. Kodi Timoteo anakhala munthu wotani, ndipo kodi ndani amene tsopano akutsimikiza kukhala ofanana naye?
12 Ngakhale kuti Timoteo anakulira m’banja logaŵanika mwachipembedzo, iye analandira Chikristu molimba mtima nakhala munthu wauzimu amene Paulo anatha kunena za iye kuti: “Ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu [Afilipi] msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu. Pakuti ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima wowona. . . . Muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine uthenga wabwino.” (Afilipi 2:19-22) Lerolino, anyamata ndi asungwana ambiri okhala m’mabanja ogaŵanika mwachipembedzo amalandira molimba mtima Chikristu chowona. Mofanana ndi Timoteo amatsimikiza mtima, ndipo tikusangalala chotani nanga kuti iwo ali mbali ya gulu la Yehova!
Kulimba Mtima kwa ‘Kupereka Makosi Athu’
13. Kodi Akula ndi Priskila anasonyeza kulimba mtima m’njira yotani?
13 Akula ndi mkazi wake, Priskila (Priska), amapereka chitsanzo mwa ‘kupereka makosi awo’ molimba mtima chifukwa cha wokhulupirira mnzawo. Iwo analandira Paulo m’nyumba yawo, anagwira naye ntchito yopanga mahema, ndipo anamthandiza kuumba mpingo watsopano mu Korinto. (Machitidwe 18:1-4) Muubwenzi wawo wa zaka 15 umenewo, anaikadi miyoyo yawo pangozi chifukwa cha iye m’njira imene sinatchulidwe. Iwo anali kukhala ku Roma pamene iye anauza Akristu a kumeneko kuti: “[Mundiperekere moni kwa, NW] Priska ndi Akula, antchito anzanga m’Kristu Yesu, amene anapereka khosi lawo chifukwa cha moyo wanga; amene ndiwayamika, siine ndekha, komanso mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu.”—Aroma 16:3, 4.
14. Mwa kupereka makosi awo chifukwa cha Paulo, kodi Akula ndi Priskila anali kuchita mogwirizana ndi lamulo liti?
14 Mwa kupereka makosi awo chifukwa cha Paulo, Akula ndi Priska anachita mogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34) Lamulo limeneli linali “latsopano” m’chakuti linaposa chofunika cha Chilamulo cha Mose kuti munthu akonde mnansi wake monga momwe anadzikondera. (Levitiko 19:18) Linafunikiritsa chikondi chodzimana chimene chikanachita zambiri kufikira pa kuchititsa munthu kupereka moyo wake kaamba ka ena, monga momwe Yesu anachitira. Tertullian, wolemba wa m’zaka za zana lachiŵiri ndi lachitatu C.E., anagwira mawu a anthu akudziko onena za Akristu pamene analemba kuti: “‘Taonani,’ iwo akutero, ‘mmene amakonderana . . . ndi mmene aliri okonzekera kuferana.’” (Apology, mutu XXXIX, 7) Makamaka pakati pa chizunzo tikhaletu otsimikiza kusonyeza chikondi chaubale mwa kuika miyoyo yathu pachiswe molimba mtima kuti tisachititse okhulupirira anzathu kuchitiridwa nkhanza kapena kuphedwa ndi adani.—1 Yohane 3:16.
Kulimba Mtima Kumadzetsa Chisangalalo
15, 16. Monga momwe kwasonyezedwera m’buku la Machitidwe chaputala 16, kodi ndimotani mmene kulimba mtima ndi chisangalalo zingagwirizanitsidwire?
15 Paulo ndi Sila amapereka umboni wakuti kusonyeza kulimba mtima pakati pa mayesero kungabweretse chisangalalo. Molamulidwa ndi oweruza a mzinda wa Filipi, iwo anakwapulidwa poyera naikidwa m’ndende. Komabe, iwo sanachite mantha mwachisoni. Mosasamala kanthu za mikhalidwe yawo yoyesayo, iwo anakhalabe ndi kulimba mtima kopatsidwa ndi Mulungu ndi chisangalalo chimene kumadzetsa kwa Akristu okhulupirika.
16 Chapakati pausiku, Paulo ndi Sila anali kupemphera ndi kutamanda Mulungu ndi nyimbo. Mwadzidzidzi, chivomezi chinagwedeza ndendeyo, ndi kuchititsa maunyolo awo kumasuka, ndipo chinachititsa makomo ake kutseguka. Mdindo wandende wamantha ndi banja lake anapatsidwa umboni wamphamvu umene unawachititsa kubatizidwa kukhala atumiki a Yehova. Iye mwiniyo “anasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pake, atakhulupirira Mulungu.” (Machitidwe 16:16-34) Nchisangalalo chotani nanga chimene zimenezi ziyenera kukhala zitadzetsera Paulo ndi Sila! Pokhala titalingalira chitsanzo chimenechi ndi zitsanzo zina za m’Malemba za kulimba mtima, kodi ndimotani mmene tingakhalirebe olimba mtima monga atumiki a Yehova?
Pitirizanibe Kukhala Olimba Mtima
17. Monga momwe kwasonyezedwera m’Salmo 27, kodi ndimotani mmene kuyembekezera Yehova kuliri kogwirizana ndi kulimba mtima?
17 Kuyembekezera Yehova kudzatithandiza kukhalabe olimba mtima. Davide anaimba kuti: “Yembekeza Yehova: Limbika, ndipo iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.” (Salmo 27:14) Salmo 27 limasonyeza kuti Davide anadalira Yehova monga “mphamvu” ya moyo wake. (Vesi 1) Kukhala ataona mmene Mulungu anachitira ndi adani a Davide m’nthaŵi zakale kunamlimbitsa mtima. (Mavesi 2, 3) Chiyamikiro kaamba ka malo olambirira apakati a Yehova chinali chifukwa china chochititsa. (Vesi 4) Kudalira chithandizo cha Yehova, chitetezero, ndi chilanditso kunalimbikitsanso kulimba mtima kwa Davide. (Mavesi 5-10) Chinthu chinanso chothandiza chinali malangizo opitirizabe a m’malamulo a mkhalidwe a njira zachilungamo za Yehova. (Vesi 11) Pemphero lachidaliro la kupulumutsidwa kwa adani ake, limodzi ndi chikhulupiriro ndi chiyembekezo, zinathandiza Davide kukhala wolimba mtima. (Mavesi 12-14) Tingakulitse kulimba mtima kwathu m’njira zofananazo, motero tikumasonyeza kuti ‘timayembekezadi Yehova.’
18. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti mayanjano okhazikika ndi olambira Yehova anzathu angatithandize kukhalabe olimba mtima? (b) Kodi misonkhano Yachikristu imachita mbali yotani m’kukulitsa kulimba mtima?
18 Kuyanjana ndi olambira Yehova anzathu kokhazikika kungatithandize kukhalabe olimba mtima. Pamene Paulo anachitira apilo mlandu wake kwa Kaisara ndipo ali paulendo wake wa ku Roma, olambira anzake anakomana naye ku Bwalo la Apiyo ndi Kunyumba za Alendo Zitatu. “Pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima,” cholembedwacho chimatero. (Machitidwe 28:15) Pamene tifika pamisonkhano Yachikristu mokhazikika, timalabadira uphungu wa Paulo wakuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu [tilimbikitsane, NW], ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Kodi kulimbikitsa kumatanthauzanji? Kulimbikitsa kumatanthauza “kusonkhezera kulimba mtima, mzimu, kapena chiyembekezo.” (Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary) Tingachite zambiri kusonkhezera Akristu ena molimba mtima, ndipo chilimbikitso chawo mofananamo chingakulitse mkhalidwe umenewu mwa ife.
19. Kodi ndimotani mmene Malemba ndi zofalitsidwa Zachikristu ziliri zogwirizana ndi kukhala kwathu olimba mtima?
19 Kuti tikhalebe olimba mtima, tiyenera kuphunzira Mawu a Mulungu mokhazikika ndi kugwiritsira ntchito uphungu wake m’miyoyo yathu. (Deuteronomo 31:9-12; Yoswa 1:8) Phunziro lathu lokhazikika liyenera kuphatikizapo zofalitsidwa Zachikristu zozikidwa m’Malemba, pakuti uphungu wabwino umene umaperekedwa udzatithandiza kuyang’anizana ndi ziyeso za chikhulupiriro ndi kulimba mtima kopatsidwa ndi Mulungu. Kuchokera m’zolembedwa za Baibulo, taona mmene atumiki a Yehova akhalira olimba mtima m’mikhalidwe yosiyanasiyana. Pakali pano, sitingadziŵe mmene chidziŵitso chotero chingatithandizire, koma Mawu a Mulungu ngamphamvu, ndipo zimene timaphunziramo zingatipindulitse nthaŵi zonse. (Ahebri 4:12) Mwachitsanzo, ngati kuwopa anthu kuyamba kuyambukira utumiki wathu, tingakumbukire mmene Enoke analiri wolimba mtima popereka uthenga wa Mulungu kwa anthu opanda umulungu.—Yuda 14, 15.
20. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti pemphero nlofunika ngati titi tikhalebe olimba mtima monga atumiki a Yehova?
20 Kuti tikhalebe olimba mtima monga atumiki a Yehova, tiyenera kulimbikira m’pemphero. (Aroma 12:12) Yesu anapirira mayeso ake molimba mtima chifukwa chakuti “anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa, ndipo anamveka popeza anawopa Mulungu.” (Ahebri 5:7) Mwa kuyandikirabe Mulungu m’pemphero, sitidzakhala monga anthu adziko amantha oyembekezera “imfa yachiŵiri” imene ilibe chiukiriro. (Chivumbulutso 21:8) Chitetezero chaumulungu ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu nza atumiki ake olimba mtima.
21. Kodi nchifukwa ninji Mboni zokhulupirika za Yehova zingakhale zolimba mtima?
21 Monga Mboni za Yehova zokhulupirika, sitiyenera kuwopa ziŵanda ndi adani aumunthu, pakuti tili ndi chichirikizo cha Mulungu ndi chitsanzo cha kulimba mtima cha Yesu monga wolaka dziko. Mayanjano omangirira mwauzimu ndi anthu a Yehova nawonso amatithandiza kukhala olimba mtima. Kulimba mtima kwathu kumakulitsidwanso kupyolera m’chitsogozo ndi uphungu wa m’Malemba ndi zofalitsidwa Zachikristu. Ndipo zolembedwa za m’Baibulo za atumiki a Mulungu akale zimatithandiza kuyenda m’njira zake molimba mtima. Chifukwa chake, m’masiku otsiriza ano, tiyeni tipite patsogolo molimba mtima muutumiki wopatulika. Inde, anthu a Yehova onse akhaletu olimba mtima!
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene chitsanzo cha Yesu chingatilimbitsire mtima?
◻ Kodi nchiyani chimene chinalimbitsa mtima Yesu ndi ophunzira ake kupitirizabe kulalikira?
◻ Kodi nchifukwa ninji Ayuda ndi Akunja anafunikira kulimba mtima kuti aime kumbali ya Yehova?
◻ Kodi nzitsanzo zotani za kulimba mtima zimene zinaperekedwa ndi Yunike ndi Timoteo?
◻ Kodi ndiumboni wotani umene ulipo wakuti kulimba mtima kumadzetsa chisangalalo ngakhale pozunzidwa?
[Chithunzi patsamba 18]
Mofanana ndi Yesu, tingachilimike m’mayesero ngati tigwiritsira ntchito ndi kugwira mawu Malemba