‘Kupeza Mpumulo wa Miyoyo Yanu’
“Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, . . . ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”—MATEYU 11:28-30.
1, 2. Nchiyani chomwe chakhala mkhalidwe wa banja la anthu kwa zaka mazana angapo, ndipo ndimotani mmene ichi chimasiyanirana ndi chimene Mulungu anafuna poyambirira?
“TIDZIŴA kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.” Chimenecho ndi chimene munthu analemba kwa mabwenzi ake mu Roma zaka mazana angapo zapita. (Aroma 8:22) M’zaka zapita chiyambire pamenepo, kubuula ndi kuwawa kwa banja la munthu monga lonse kwangowonjezeka. Kunyada, umphaŵi, chiwawa, ndi njala zatenga mlingo wochititsa ngozi kulikonse. Dongosolo la zachuma lopanda chilungamo limakakamiza mamiliyoni kuchoka ntchito ndipo ngakhale kuchoka m’nyumba zawo, ndipo zisonkhezero za usatana zimachepsya zoyesayesa za kulera ana m’njira imene iwo ayenera kupitamo.
2 Koma mwinamwake ngozi yaikulu koposa imawoneka pamene kudwala, matenda, kapena ukalamba zichotsera anthu nyonga yawo ndi kuwalanda iwo ulemu wawo pamene akunyonyotsoka kufikira ku mkhalidwe wochepera wakale wa iwo eni. Kuwawa ndi kuvutika kowopsya, kaŵirikaŵiri komatha milungu ingapo, miyezi, ndipo nthaŵi zina ngakhale zaka, kumapangitsa kuwawidwa mtima ndi kupangitsa kugwetsa misozi. Ndi ndemanga yomvetsa chisoni chotani nanga pa moyo! Ponena za tsoka la munthu, mfumu yanzeru ya nthaŵi zakale inanena kuti: “Pakuti masiku ake onse ndi zisoni, vuto lake ndi kumliritsa.” (Mlaliki 2:23; 4:1) Moyo lerolino ndithudi suli monga mmene Mulungu poyambirira anafunira iwo kukhala!—Genesis 2:8, 9.
3. Kodi chiri ndi kuthekera kotani kumene Mulungu analenga munthu, ndipo ndimotani mmene pa nthaŵi ino kukuzindikiridwa ku ukulu wokhala ndi polekezera?
3 Yehova Mulungu analenga munthu wangwiro, ndi kuthekera kwa kusangalaladi ndi moyo. (Deuteronomo 32:4, 5) Tangolingalirani za chisangalatso cha kulaŵa chakudya chabwino, kupuma mpweya woyera, kapena kupenyerera kuloŵa kwa dzuŵa kosangalatsa! “Ndawona vuto limene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti avutidwe nalo,” inawona tero mfumu yanzeru imodzimodziyo ya nthaŵi zakale. “Ndidziŵa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe nawone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.”—Mlaliki 3:10-13.
4. (a) Monga momwe kwasonyezedwera ndi zokumana nazo za Yesu, ndi uti womwe uli mkhalidwe womvetsa chisoni wa ambiri? (b) Ndi chiitano chotenthetsa mtima chotani chimene Yesu akufutukula, ndipo kodi ndi mafunso otani amene ichi chikudzutsa?
4 Komabe, ndi ochepera chotani nanga omwe ali okhoza kusangalala ndi zinthu zabwino zimene Mulungu anakonzekeretsa kaamba ka ife! Yesu Kristu anali wozindikira za mkhalidwe wokanthidwa, womvetsa chifundo wa mtundu wa anthu. “Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa iye,” likunena tero Baibulo, “ali nawo opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziŵalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake.” Ndimotani nanga mmene Yesu anamverera chifundo anthu opanda mwaŵi oterowo! (Mateyu 9:36; 15:30) Pa chochitika china, iye anapereka chiitano chotenthetsa mtima ichi: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.” (Mateyu 11:28, 29) Ndithudi, awa ali mawu opereka chiyembekezo! Koma kodi ndi mpumulo wotani umene Yesu anali kulankhula ponena za iwo? Ndipo ndimotani mmene tingaupezere iwo?
Chowonadi Chimene Chimadzetsa Mpumulo
5. Ndimotani mmene Yesu analozera njira ku ufulu wowona ndi mpumulo wa miyoyo yathu?
5 Pamene Yesu anapezeka pa Phwando la Misasa chifupifupi miyezi isanu ndi umodzi imfa yake isanafike, iye analoza ku njira ya kukhalira womasuka ndipo mwakutero kulandira mpumulo wowona. Akumalankhula kwa awo omwe anaika chikhulupiriro mwa iye, iye ananena kuti: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:31, 32) Kodi nchowonadi chotani chomwe Yesu anali kulankhula za icho? Kodi icho chikatimasula kuchokera ku chiyani? Ndi m’njira yotani mmene amvetseri ake analiri akapolo?
6. (a) Ndi chitsutso chotani chimene otsutsa a chipembedzo anadzutsa, ndipo nchifukwa ninji? (b) Ndi m’njira yotani mmene tonsefe tiriri akapolo?
6 Otsutsa a chipembedzo anasokoneza Yesu, akumatsutsa kuti: “Tiri mbewu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthaŵi iriyonse; munena bwanji, Mudzayesedwa aufulu?” Otsutsa Achiyuda amenewo anali onyanda ponena za choloŵa chawo. Ngakhale kuti mtunduwo kaŵirikaŵiri unabwera pansi pa ulamuliro wakunja, Ayudawo anakana kutchedwa akapolo. Koma Yesu anasonyeza njira mu imene iwo analiri akapolo, akumanena kuti: “Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita chimo ali kapolo wa chimolo.” Inde, amvetseri ake onse anali ‘akuchita chimo,’ mongadi mmene tonsefe tiriri lerolino. Ichi chiri chifukwa chakuti tonsefe tinapeza choloŵa cha chimo kuchokera kwa makolo athu oyambirira. Koma Yesu analonjeza kuti: “Ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.”—Yohane 8:33-36; Aroma 5:12.
7. Ndimotani mmene ufulu wowona ungazindikiridwire, ndipo nchiyani chomwe chiri chowonadi chomwe chimatimasula ife?
7 Ufulu wowona mwakutero ungazindikiridwe kokha kupyolera mwa Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, yemwe anapereka moyo wake waumunthu wangwiro monga nsembe ya dipo. Iri nsembe imeneyi yomwe imatimasula ife kuchokera ku chimo lodzetsa imfa ndi kuchipangitsa icho kukhala chothekera kwa ife kusangalala ndi moyo wosatha mu umoyo wangwiro ndi chimwemwe m’dziko latsopano lolungama la Mulungu. (Yohane 3:16; 1 Yohane 4:10) Chotero, chowonadi chomwe chimatimasula ife chiri chowonadi ponena za Yesu Kristu ndi mbali yake m’kukwaniritsidwa kwa zifuno za Mulungu. Ufumu, ndi Kristu monga Mfumu, uli umene udzakwaniritsa chifuniro cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi, ndipo Yesu mosalekeza anachitira umboni ponena za chowonadi chimenechi.—Yohane 18:37.
Mmene Chowonadi Chimadzetsera Mpumulo
8. Ndimotani mmene njira mu imene chowonadi chimaperekera mpumulo ingachitidwire fanizo?
8 Njira mu imene chowonadi chimadzetsera mpumulo ingachitiridwe fanizo ndi mkazi yemwe wawuzidwa kuti ali ndi mtundu wina wa kansa yomwe imafalikira mofulumira. Kulemetsa kwa chidziŵitso choterocho kumamukhwethemula iye pamene iye akulingalira zotulukapo zowawa, zosakaza mothekera. M’kupita kwa nthaŵi, ngakhale kuli tero, iye amalankhula ndi dokotala wina ndi kupita m’kufufuzidwa kowonjezereka. Pamene zotulukapo za kufufuza kumeneko zivumbula kuti mwinamwake kusanthula koyambirirako kunali kolakwika kapena kuti iye anali ndi kuchira kozizwitsa, mungalingalire kudzimva kosangalatsa kwa mpumulo kumene amakumana nako. Ndi chodzetsa mpumulo chotani nanga ku moyo wake!
9. Ndimotani mmene Yesu anaperekera mpumulo mwa kuphunzitsa anthu chowonadi?
9 Mofananamo, pamene Yesu anabwera ku dziko lapansi, anthuwo anali olemedwa ndi madongosolo a mwambo opanda phindu a tsikulo. Ponena za alembi ndi Afarisi omwe anali ndi thayo, Yesu ananena kuti: “Amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo.” (Mateyu 23:4; Marko 7:2-5) Ndi mpumulo wotani nanga womwe iwo unali pamene Yesu anapereka kwa anthuwo chowonadi chomwe chinawamasula iwo kuchoka ku miyambo yoika mu ukapolo yoteroyo! (Mateyu 15:1-9) Sichosiyana lerolino.
10. Ndi katundu wochotsa chimwemwe wotani yemwe ambiri akhala naye, ndipo ndimotani mmene munthu angamverere pamene izi zachotsedwa monga chotulukapo cha kuphunzira kwake chowonadi?
10 Mwinamwake inu munali mmodzi amene, chifukwa cha katundu wolemetsa wa ziphunzitso za chipembedzo chonyenga, munakhala m’mantha a kuvutika ndi chizunzo m’moto wa helo kapena mu purigatoriyo pambuyo pa imfa. Kapena pamene wokondedwa wanu anafa, mungakhale munakhwethemulidwa pamene mtsogoleri wachipembedzo anakuwuzani kuti Mulungu watenga mwana wanu wokondedwa chifukwa Iye anafunikira mngelo wina—ngati kuti Mulungu anafuna mwana wanu kuposa mmene munamfunira. Pa nthaŵi zina atsogoleri a chipembedzo amawuzanso anthu omwe akuvutika ndi matenda ena kuti liri temberero lochokera kwa Mulungu. Kodi ndithudi sichiri chodzetsa mpumulo kuphunzira zowonadi za Baibulo zomwe zimamasula munthu kuchokera ku zinyengo za chipembedzo zolemetsa zoterozo? Chimenechi chimabweretsa kudzimva kwa mpumulo kotani nanga!—Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4; Yohane 9:2, 3.
11. (a) Ndi uti yemwe ali mmodzi wa katundu wamkulu koposa, ndipo ndimotani mmene angachotsedwere? (b) Ndi mpumulo wotani umene Yesu anabweretsa kwa ochimwa pamene anali pa dziko lapansi?
11 Mmodzi wa katundu wamkulu koposa woyenera kunyamulidwa ali uja wa liwongo chifukwa cha machimo omwe tapanga. Uli mpumulo kudziŵa kuti chifukwa cha mphoto ya nsembe ya dipo ya Kristu, machimo amenewa angachotsedwe. ‘Mwazi wa Yesu utisambitsa kutichotsera machimo onse,’ likutitsimikizira tero Baibulo. (1 Yohane 1:7) Mosasamala kanthu za zinthu zowopsya zomwe tingakhale tinazichita, ngati ife mowonadi talapa ndi kuwongolera njira zathu, tingasangalale ndi chimasuko chodzetsa mpumulo cha chikumbumtima choyera ndi chitsimikizo chakuti Mulungu sadzakumbukiranso machimo athu. (Salmo 103:8-14; 1 Akorinto 6:9-11; Ahebri 10:21, 22) Ndi mpumulo wotani nanga umene Kristu anabweretsa kwa awo olemedwa ndi machimo, monga ngati akazi achigololo ndi a msonkho monga Zakeyu! Yesu anawatonthoza iwo ndi zowonadi za Baibulo pamene anadya nawo.—Luka 5:27-32; 7:36-50; 19:1-10.
12. (a) Kodi kunali kwa anthu a mikhalidwe yodzetsa chipsyinjo yotani imene Yesu anabweretsa mpumulo? (b) M’zana loyamba, ndi kwa ndani kumene Yesu anasonyeza m’njira yowonekera kuti iye anali “njira, ndi chowonadi, ndi moyo”?
12 Anthu ena ambiri amatenga katundu wolemetsa wa kudwala ndi matenda, kupsyinjika kokulira, ndi chisoni chachikulu chomwe chimabwera ndi imfa ya wokondedwa. Yesu, ngakhale kuli tero, anabweretsa mpumulo kwa onse oterowo omwe anali “akulema ndi akuthodwa.” (Mateyu 4:24; 11:28, 29) Iye anachiritsa mkazi wina yemwe mopanda chipambano anafuna thandizo kuchokera kwa asing’anga kwa zaka 18. Yesu anachiritsanso mwamuna yemwe anali wodwala kwa zaka 38, ndi wina yemwe anabadwa wakhungu. Kodi mungalingalire kumasulidwa kwawo pamene Yesu anawachiritsa iwo? (Luka 13:10-17; Yohane 5:5-9; 9:1-7) Chenicheni chiri chakuti awo onse omwe anabwera kwa Yesu m’chikhulupiriro anabwera ku magwero a chowonadi, mpumulo wowona, ndi moyo. Kwa mkazi wamasiye yemwe analandira mwana wake yekha kuchokera kwa akufa ndi makolo amene mwana wawo wamkazi wakufa wa zaka 12 zakubadwa anabwezedwa wamoyo kwa iwo, Yesu ndithudi anatsimikizira m’njira yowonekera kuti iye anali “njira, ndi chowonadi, ndi moyo.”—Yohane 14:6; 17:3; Luka 7:11-17; 8:49-56.
13. Kodi ndi kwa ndani kumene Yesu anatiphunzitsa ife kutembenukirako kaamba ka thandizo, ndipo nchiyani chomwe chimachitika pamene tigwiritsira ntchito uphungu wake?
13 Mosakaikira pali nthaŵi zimene inu mumayang’anizana ndi mavuto omwe ali okulira kuposa ndi mmene mungathe kuwasamalira mwaumwini. Yesu anatiphunzitsa ife kutembenukira kwa Yehova kaamba ka thandizo, mongadi mmene iyemwini anachitira. (Luka 22:41-44; Ahebri 5:7) Pamene ife mokhazikika titembenukira kwa Mulungu m’pemphero, timafikira m’kugawana malingaliro a wamasalmo yemwe analemba kuti: “Wolemekezeka [Yehova, NW], tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.” (Salmo 55:22; 68:19) Inde, kudziŵa chowonadi kumabweretsadi mpumulo. Kumatikokera ife kufupi ndi Yehova ndi kutithandiza ife kuyamikira kuti ndi thandizo lake kuli kothekera kusamalira mwachipambano ngakhale mikhalidwe yovuta koposa m’moyo.
Kupatsidwa Mpumulo ndi Chiyembekezo Chaufumu
14. Kodi nchiyani chomwe chinachirikiza Yesu m’mayeso ake, ndipo nchiyani chomwe chiri chofunikira ngati titi tipeze mpumulo wa miyoyo yathu?
14 Kuti tipeze mpumulo wowona wa miyoyo yathu, tiyenera kukhala ndi chiyembekezo champhamvu. Chinali chiyembekezo chomwe chinachirikiza Yesu. Baibulo limanena kuti: “Chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo, NW] nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” (Ahebri 12:2) Chiyembekezo cha chimwemwe chomwe chinachirikiza Yesu chinali chija cha kuthandizira ku kuyeretsedwa kwa dzina la Atate wake mwa kusunga umphumphu, limodzinso ndi kutsimikizira woyenerera kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Kusungirira masomphenya owonekera a chiyembekezo chathu, kaya monga wolamulira mnzake wa Kristu m’mwamba kapena monga mmodzi wa nzika zake zokhala ndi moyo pa dziko lapansi la Paradaiso, kudzatichirikizanso ife mu utumiki wa Mulungu. Ndithudi, chiyembekezo chimenecho chiri chofunikira ku kupeza mpumulo wa miyoyo yathu.—Aroma 12:12.
15. Kodi ndi ziti zomwe ziri ziyembekezo zathu za moyo popanda chiyembekezo cha Ufumu?
15 Lingalirani ziyembekezo zathu za moyo popanda chiyembekezo cha Ufumu. Utali wa moyo wofala uli kokha zaka 70 kapena mothekera 80. Ndipo masiku amenewo amapita mofulumira, monga mmene aliyense amene akukula adzakuuzirani! Inde, Baibulo mowonadi limanena za moyo kuti: “Pakuti kumapitako msanga ndipo tithaŵa ife tomwe.” (Salmo 90:10) Komabe, timafuna masiku athu kupitirizabe. Timafuna kukhala ndi moyo. Pali zofunikira kuchita zambiri kwenikweni ndi kusangalala nazo.
16. Kuti tipeze mpumulo wa miyoyo yathu, nchiyani chomwe tifunikira kuchita?
16 Chotero, ndi choyenerera chotani nanga, kuti ife tibwere m’chikhulupiriro kwa “Kristu Yesu, chiyembekezo chathu”! (1 Timoteo 1:1) Monga mmene iye ananenera kuti: “Chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang’ana Mwana, ndi kukhulupirira iye, akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 6:40, 51) Kodi timakhulupirira chimenecho? Kuti tipeze mpumulo kaamba ka miyoyo yathu, ife motsimikizirika tiyenera kutero. Sitingathe kuchita popanda icho. Ndithudi, tiyenera kuvala “chisoti chiri chiyembekezo cha chipulumutso.” (1 Atesalonika 5:8; yerekezani ndi Ahebri 6:19.) Chiyembekezo chimenecho chiyenera kuchinjiriza maganizo athu, kulingalira kwathu. Kupanda apo, tidzakhala olemetsedwa ndi katundu ndi mavuto kotero kuti tidzaleka ndi kulephera kupeza moyo wosatha. Chotero, ndi cholinga chofuna kupeza mpumulo wa moyo wanu, khalani otsimikizira kusunga chiyembekezo chanu cha Ufumu kukhala champhamvu.
Mpumulo Wochokera ku Kuchita Ntchito ya Mulungu
17. (a) Kuti tipeze mpumulo, nchiyani chomwe chikufunikira, ndipo nchifukwa ninji ichi sichiri chokulira kwa ife? (b) Kodi kulandira goli la Kristu kumaphatikizapo chiyani?
17 Koma kuti tipeze mpumulo, zambiri zikufunikira kuposa kokha kubwera kwa Yesu. Iye anawonjezera kuti: “Tengani goli langa [kapena, “Bwerani pansi pa goli langa limodzi nane”] ndipo phunzirani kwa ine, chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofeŵa ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:29, 30, New World Translation Reference Bible, mawu a m’munsi) Kutenga goli kumasonyeza ntchito. Koma zindikirani kuti Yesu sakutifunsa ife kutenga goli pa ife eni ndi kuchita ntchito yonseyo tokha. Tiyenera kukoloweka goli limodzi naye. M’nkhani imeneyi, kulandira goli limene Kristu akupereka kumaphatikizapo kupanga kudzipereka kwa Mulungu, kuchitira chithunzi uku mwa ubatizo wa m’madzi, ndipo kenaka kutenga thayo la kukhala wophunzira wa Kristu. Koma ndimotani mmene goli la kukhala wophunzira limeneli lingabweretsere mpumulo?
18. (a) Kodi nchifukwa ninji kulandira goli la Kristu kumabweretsa mpumulo? (b) Ndimotani mmene ntchito yolalikira imatibweretsera ife chimwemwe ndi mpumulo?
18 Kulandira goli la Kristu kumabweretsa mpumulo chifukwa chakuti Yesu ali wofatsa ndi wodzichepetsa mtima. Popeza kuti iye sali wosalingalira, chiri chodzetsa mpumulo kugwira ntchito limodzi naye pansi pa goli limodzimodzilo. Iye amalingalira kukhala kwathu ndi polekezera ndi zifooko. Monga mmene iye ananenera kuti, “Goli langa liri lofeŵa.” Zowonadi, goli la kukhala wophunzira limaphatikizapo ntchito, ntchito yolalikira ndi yophunzitsa imodzimodziyo imene Yesu anachita ndi kaamba ka imene iye anaphunzitsa atsatiri ake oyambirira. (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8) Komabe, iyo iri ntchito yodzetsa mpumulo chotani nanga kuwuza ena ponena za Mulungu wathu wachikondi, Mwana wake, ndi Ufumu! Chiri chodzetsa mpumulo chotani nanga kuwuza anthu mmene iwo angakhalire ndi moyo kosatha m’Paradaiso! Ndipo pamene iwo avomereza ku uthenga wopatsa moyo wa Ufumu ndi kugwirizana nafe m’kutumikira Yehova Mulungu, ndi chokulira chotani nanga mmene chimwemwe chathu chimakhalira!—1 Timoteo 4:16.
19. Kodi nchifukwa ninji uphungu wa apongozi a Mose uli wofunikira kaamba ka akulu a mu mpingo lerolino?
19 M’zaka zaposachedwapa, mamiliyoni abwera ku gulu la Yehova omwe akufuna thandizo m’kulandira goli la Kristu, ndipo ichi chimawonjezera thayo la ntchito ya olengeza Ufumu ndi awo omwe akuwaŵeta iwo. Kwa abusa auzimu oterowo, uphungu womwe mneneri Mose analandira kuchokera kwa apongozi ake uli woyenerera. Iye anapatsa Mose chilangizo ichi: “Chinthu uchitachi sichiri chabwino ayi. Udzalema konse, iwe ndi anthu omwe uli nawo; pakuti chikulaka chinthu ichi; sungathe kuchichita pa wekha.” Chotero iye analangiza Mose kusankha amuna ena othekera kuti agawane ntchito ya kuŵeta anthuwo. Kutsatira chilangizo chimenechi kunatsimikizira kukhala kwa chipambano. (Eksodo 18:17-27) Lerolino, kuphunzitsa kopitirizabe kudzatulutsa amuna ambiri othekera, “mphatso mwa anthu,” omwe angagawanemo m’kuŵeta gulu kotero kuti akulu a mu mpingo asatope.—Aefeso 4:8, 16.
20. Kodi nchiyani chimene Yesu Kristu ndi Atate wake amafuna kuchokera kwa ife?
20 Ngakhale kuti Kristu anachenjeza otsatira ake kudziikizako iwo eni mwamphamvu, iye osatinso Atate ake samafuna kuti aliyense wa ife achite zochulukira kuposa zomwe ziri zolingalirika. Pa nthaŵi imodzi, pamene ena anasuliza Mariya mlongo wa Lazaro kaamba ka zoyesayesa zake m’malo mwa Yesu, iye anawadzudzula iwo, akumanena kuti: “Mlekeni. . . . Iye wachita chimene wakhoza.” (Marko 14:6-8; Luka 13:24) Ndipo izi ndi zonse zomwe zikuyembekezeredwa kwa ife—kuchita zimene tikhoza. Ntchito Yachikristu yoteroyo siiri katundu wolemetsa koma mpumulo. Nchifukwa ninji? Chifukwa imabweretsa chikhutiritso chowona tsopano ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha mapindu osatha mtsogolo.
21. (a) Kodi nchiyani chomwe chiri katundu wopepuka wa Kristu, ndipo nchiyani chimene kaŵirikaŵiri chimapangitsa ntchito yolalikira kukhala yovuta? (b) Nchiyani chomwe chiyenera kukhala chigamulo chathu champhamvu, ndipo ndi chiyembekezo chotsimikizirika chotani?
21 Zowona, Satana adzawona ku icho kuti tikuzunzidwa, mongadi mmene mnzathu wosenza naye goli, Yesu Kristu, anachitira. (Yohane 15:20; 2 Timoteo 3:12) Koma kumbukirani kuti sikatundu wopepuka wa Kristu amene ali wolemetsa. M’malomwake, chiri chitsutso cha Satana ndi nthumwi zake chimene kaŵirikaŵiri chimapangitsa ntchito yathu kukhala yovuta chotero. Katundu wa Kristu amapangidwa kokha ndi kukhala mogwirizana ndi zifuno za Mulungu, ndipo izi siziri zolemetsa. (1 Yohane 5:3) Lolani kuti ife, chotero, tipitirize kukhala pansi pa goli la Yesu Kristu limodzi naye, kudziikizako ife eni m’ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa, mongadi mmene iye anachitira. Mwa kuchita tero ife, monga mmene analonjezera, ‘tidzapeza mpumulo wa miyoyo yathu.’
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Mogwirizana ndi Aroma 8:22, nchiyani chomwe chakhala mkhalidwe wa mtundu wa anthu?
◻ Kodi ndi m’njira zotani mmene kudziŵa chowonadi kumabweretsera mpumulo?
◻ Nchifukwa ninji chiyembekezo cha Ufumu chiri chodzetsa mpumulo motero?
◻ Nchiyani chomwe chiri goli la Yesu, ndipo nchifukwa ninji liri lofeŵa?
◻ Kodi ndi kunyamula katundu wotani komwe kungatibweretsere mpumulo?