MUTU 41
Kodi Yesu Ankazitenga Kuti Mphamvu Zochitira Zozizwitsa?
MATEYU 12:22-32 MALIKO 3:19-30 LUKA 8:1-3
YESU ANAYAMBA ULENDO WACHIWIRI WOPITA KOKALALIKIRA
ANATULUTSA ZIWANDA KOMANSO ANAWACHENJEZA ZA TCHIMO LIMENE MUNTHU SANGAKHULULUKIDWE
Atangomaliza kufotokoza za kukhululuka kunyumba ya Simoni, yemwe anali Mfarisi, Yesu anayamba ulendo wake wachiwiri wolalikira m’dera la Galileya. Chimenechi chinali chaka chake chachiwiri kuchokera pamene anayamba utumiki wake ndipo pa ulendowu sanali yekha. Anali ndi atumwi ake 12 aja komanso anali ndi azimayi ena amene “anawatulutsa mizimu yoipa ndi kuwachiritsa matenda awo.” (Luka 8:2) Ena mwa azimayiwa anali Mariya Mmagadala, Suzana komanso Jowana, yemwe mwamuna wake anali kapitawo wa Mfumu Herode Antipa.
Anthu ambiri atayamba kudziwa zimene Yesu ankachita, anayamba kutsutsa kwambiri ntchito zake. Zimenezi zinaonekera pamene anthu anabweretsa munthu wogwidwa ndi chiwanda, yemwe anali wakhungu komanso wosalankhula, kuti Yesu amuchiritse. Yesu anatulutsadi chiwanda mwa munthuyo komanso anayamba kuona ndi kulankhula. Anthu ataona zimenezi anadabwa kwambiri ndipo ananena kuti: “Kodi ameneyu sangakhale Mwana wa Davide uja?”—Mateyu 12:23.
Anthu amene anasonkhana kunyumba imene Yesu ankakhala anali ambiri moti Yesu ndi atumwi ake sanapeze nthawi yoti adye. Koma sikuti anthu onse ankakhulupirira kuti Yesu ndi “Mwana wa Davide.” Pagulupo panalinso alembi ndi Afarisi amene anachokera ku Yerusalemu. Cholinga cha alembi ndi Afarisiwa si chinali kudzaphunzira zimene Yesu ankaphunzitsa kapena kudzamuthandiza. Iwo ankauza anthu kuti: “Ali ndi Belezebule,” kutanthauza kuti ankachita zinthu mogwirizana ndi “wolamulira ziwanda.” (Maliko 3:22) Abale ake a Yesu atamva zimene zinkachitikazi, anabwera kuti adzamugwire n’kumutenga. N’chifukwa chiyani ankafuna kuchita zimenezi?
Pa nthawiyi, ngakhale abale ake a Yesu sankakhulupirira kuti Yesuyo ndi Mwana wa Mulungu. (Yohane 7:5) Abale ake sankakhulupirira kuti Yesu yemwe ankamudziwa komanso amene anakulira naye limodzi ku Nazareti ndi amene ankachita zinthu zodabwitsa ndipo nkhani yake inali m’kamwam’kamwa. Iwo ankaganiza kuti mutu wake sukuyenda bwinobwino ndipo ananena kuti: “Wachita misala.”—Maliko 3:21.
Koma zimene Yesu ankachita zinali zosiyana ndi zimene abale akewo ankaganiza. Yesu anali atangochiritsa munthu amene anali ndi chiwanda komanso kumuthandiza kuti ayambenso kuona ndi kulankhula. Palibe amene akanatsutsa zimenezi. Koma alembi ndi Afarisi ankafuna kuchititsa Yesu manyazi moti anayamba kumuimba milandu yabodza. Iwo ankanena kuti: “Ameneyutu sikuti amatulutsa ziwanda ndi mphamvu zake ayi. Amatero ndi mphamvu ya Belezebule, wolamulira ziwanda.”—Mateyu 12:24.
Yesu ankadziwa zimene alembi ndi Afarisi ankaganiza, choncho ananena kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha, ndipo mzinda uliwonse kapena nyumba yogawanika siikhalitsa. Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana amatulutsa Satana, ndiye kuti wagawanika. Nanga tsopano ufumu wake ungakhalepo bwanji?”—Mateyu 12:25, 26.
Zimenezitu zinali zomveka chifukwa Afarisi ankadziwa kuti Ayuda ena ankatulutsanso ziwanda. (Machitidwe 19:13) Choncho Yesu anawafunsa kuti: “Ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule, nanga otsatira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani?” Pamenepatu Yesu ankatanthauza kuti Ayuda enawonso ankayenera kuimbidwa mlandu umene Yesu ankaimbawo. Ndiyeno Yesu anapitiriza kuti: “Koma ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya mzimu wa Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wakufikani modzidzimutsa.”—Mateyu 12:27, 28.
Yesu ankatulutsa ziwanda pofuna kusonyeza kuti ali ndi mphamvu zoposa za Satana. Choncho kuti anthuwa amvetse mfundo imeneyi, anawafotokozera fanizo lakuti: “Munthu angalowe bwanji m’nyumba ya munthu wamphamvu ndi kulanda katundu wake, ngati sangamange munthu wamphamvuyo choyamba? Atam’manga, m’pamene angathe kutenga katundu m’nyumbamo. Amene sali kumbali yanga ndi wotsutsana ndi ine, ndipo amene sagwira limodzi ndi ine ntchito yosonkhanitsa anthu kwa ine amawabalalitsa.” (Mateyu 12:29, 30) Alembi ndi Afarisi ankadana ndi Yesu zomwe zinkasonyeza kuti ankatumikira Satana. Iwo ankathamangitsa anthu kuti asayandikire Mwana wa Mulungu, yemwe ankachita zinthu mothandizidwa ndi Yehova.
Yesu anachenjeza anthu otsutsa, omwe ankatumikira Satanawa, kuti: “Ana a anthu adzakhululukidwa zinthu zonse, kaya ndi machimo otani amene anachita kapena mawu onyoza otani amene analankhula. Komabe, aliyense amene wanyoza mzimu woyera sadzakhululukidwa kwamuyaya, koma adzakhala ndi mlandu wa tchimo losatha.” (Maliko 3:28, 29) Choncho anthu amene amapereka ulemu kwa Satana pa zinthu zimene zikuonekeratu kuti zikuchitika chifukwa cha mzimu wa Mulungu, anthu amenewo adzakumana ndi tsoka lalikulu.