MUTU 12
“Nthawi Zonse Iye Ankalankhula Nawo Pogwiritsa Ntchito Mafanizo”
1-3. (a) Kodi ophunzira amene ankayenda ndi Yesu anali ndi mwayi wapadera kwambiri uti, nanga Yesu anawathandiza bwanji kuti azikumbukira mosavuta zimene ankaphunzitsa? (b) N’chifukwa chiyani mafanizo ogwira mtima amakhala osavuta kuwakumbukira?
OPHUNZIRA amene ankayenda ndi Yesu anali ndi mwayi wapadera kwambiri chifukwa ankaphunzira mwachindunji kuchokera kwa Mphunzitsi Waluso. Iwo ankamva iye akufotokoza tanthauzo la Mawu a Mulungu powaphunzitsa mfundo zosangalatsa za choonadi. Pa nthawiyi ophunzirawo ankafunika kusunga mawu ake amtengo wapataliwo m’maganizo ndi mumtima mwawo, chifukwa nthawi yoti mawu amenewo alembedwe inali isanakwane.a Komabe, Yesu anawathandiza kuti azikumbukira mosavuta zimene ankawaphunzitsazo. Kodi anachita bwanji zimenezi? Anachita zimenezi pogwiritsa ntchito mafanizo mwaluso kwambiri.
2 N’zoonadi, mafanizo ogwira mtima saiwalika msanga. Munthu wina wolemba mabuku ananena kuti mafanizo amathandiza munthu “kuona m’maganizo mwake zimene akumvazo” ndiponso “amathandiza omvera kuti azitha kuona zithunzi za zinthu zimene akumvazo m’maganizo mwawo.” Popeza kuti anthufe timamvetsa bwino nkhani tikamayerekezera kuti tikuona m’maganizo mwathu zimene tikumvazo, mafanizo amathandiza kwambiri kuti timvetse mfundo iliyonse ngakhale yovuta kumvetsa. Mafanizo amathandizanso kuti timvetse bwino nkhani ndipo zimene taphunzirazo siziiwalika.
3 Palibe mphunzitsi aliyense padziko lapansi amene anagwiritsa ntchito mafanizo mwaluso kuposa Yesu Khristu ndipo anthu amakumbukirabe mafanizo ake mpaka pano. N’chifukwa chiyani Yesu ankadalira kwambiri njira imeneyi pophunzitsa? Nanga n’chiyani chinapangitsa kuti mafanizo ake akhale ogwira mtima? Kodi tingaphunzire bwanji kugwiritsa ntchito njira imeneyi pophunzitsa?
N’chifukwa Chiyani Yesu Ankagwiritsa Ntchito Mafanizo Pophunzitsa?
4, 5. N’chifukwa chiyani Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa?
4 Baibulo limanena zifukwa ziwiri zofunika kwambiri zimene zinachititsa kuti Yesu azigwiritsa ntchito mafanizo. Chifukwa choyamba n’chakuti, anachita zimenezo kuti akwaniritse ulosi. Palemba la Mateyu 13:34, 35, timawerenga kuti: “Yesu analankhula zonsezi ndi gulu la anthulo pogwiritsa ntchito mafanizo. Ndithudi, nthawi zonse iye ankalankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo, kuti zimene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri zikwaniritsidwe. Mneneriyo anati: ‘Ndidzatsegula pakamwa panga n’kunena mafanizo.’” Mneneri amene Mateyu ankanena anali amene analemba Salimo 78:2. Mneneriyu anauziridwa ndi mzimu wa Mulungu kuti alembe Salimoli zaka zambirimbiri Yesu asanabadwe. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Kutatsala zaka zambiri kuti Yesu abadwe, Yehova ananeneratu kuti Mesiya adzagwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa. Izi zikusonyeza kuti Yehova amaona kuti njira yophunzitsira imeneyi ndi yofunika kwambiri.
5 Chifukwa chachiwiri n’chakuti, Yesu anafotokoza kuti ankagwiritsa ntchito mafanizo kuti asiyanitse anthu amene ‘anaumitsa mitima yawo’ ndi anthu amene ankafuna kudziwa choonadi. (Mateyu 13:10-15; Yesaya 6:9, 10) Kodi mafanizo ake ankawanena m’njira yotani kuti adziwe zimene anthu akuganiza? Nthawi zina, ankafuna kuti anthu amene akumumvetsera afunse kuti awafotokozere mfundo zimene sanamvetse bwino. Anthu odzichepetsa ankafunsa pamene anthu amene anali odzikuza kapena opanda chidwi sankafunsa. (Mateyu 13:36; Maliko 4:34) Choncho, mafanizo a Yesu ankathandiza kuti choonadi chidziwike kwa anthu odzichepetsa komanso kuti chibisike kwa anthu odzikuza.
6. Kodi mafanizo a Yesu anali ofunika kwambiri m’njira ziti?
6 Mafanizo a Yesu anali ogwira mtima pa zifukwa zinanso. Ankapangitsa anthu kukhala ndi chidwi choti amvetsere. Ankathandiza anthu kukhala ndi chithunzi m’maganizo chowathandiza kuti amvetse bwino nkhani. Monga mmene taonera kale, mafanizo a Yesu ankathandiza anthu kukumbukira zimene ankawaphunzitsa. Mwachitsanzo, ulaliki wa paphiri umene uli pa Mateyu 5:3 mpaka 7:27, ndi chitsanzo chabwino kwambiri chimene tingapezemo mafanizo ambirimbiri a Yesu. Munthu wina atawerenga anapeza kuti mu ulaliki umenewu muli mafanizo osiyanasiyana oposa 50. Kuti timvetse zimenezi, kumbukirani kuti munthu angawerenge ulalikiwu mokweza kwa maminitsi pafupifupi 20. Zimenezi zikutanthauza kuti munthu akamawerenga, pa masekondi 20 aliwonse angapeze fanizo. Pamenepa n’zoonekeratu kuti Yesu anaona kuti kugwiritsa ntchito mafanizo n’kofunika kwambiri.
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito mafanizo ngati mmene Yesu ankachitira?
7 Popeza ndife otsatira a Khristu, tiyenera kutsatira njira zimene iye ankagwiritsa ntchito pophunzitsa, monga kugwiritsa ntchito mafanizo. Mofanana ndi mchere umene umakometsa ndiwo, mafanizo oyenera angakometse zimene tikuphunzitsa ndipo zingakhale zogwira mtima. Mafanizo abwino angathandizenso munthu kuti amvetse mosavuta mfundo zofunika za choonadi. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zina zimene zinachititsa kuti mafanizo a Yesu akhale ogwira mtima. Kenako tiona mmene tingagwiritsire ntchito bwino njira yothandiza imeneyi pophunzitsa.
Mafanizo Osavuta Oyerekezera Zinthu
8, 9. (a) Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo osavuta kumva. (b) N’chifukwa chiyani mafanizo a Yesu anali ogwira mtima?
8 Nthawi zambiri, Yesu pophunzitsa ankagwiritsa ntchito mafanizo oyerekezera zinthu amene anali osavuta kumva ndipo ankawafotokoza m’mawu ochepa chabe. Koma mafanizo osavutawo ankathandiza anthu kumvetsa bwino mfundo za choonadi zimene ankawaphunzitsa. Mwachitsanzo, pamene Yesu ankauza ophunzira ake kuti asamade nkhawa ndi zofunika za tsiku ndi tsiku, iye anawapatsa chitsanzo cha “mbalame zamumlengalenga” ndiponso “maluwa akutchire.” N’zoona kuti mbalame sizifesa kapena kukolola mbewu ndipo maluwa sawomba nsalu, koma Mulungu amasamalira zonsezi. Pamenepa mfundo yake ndi yoonekeratu yakuti, ngati Mulungu amasamalira mbalame ndiponso maluwa, n’zosakayikitsa kuti adzasamalira anthu amene ‘amaika Ufumu pamalo oyamba pa moyo wawo.’—Mateyu 6:26, 28-33.
9 Yesu ankagwiritsanso ntchito kwambiri mafanizo ena ogwira mtima oyerekezera zinthu. Komabe ankayesetsa kuti mafanizowo akhale osavuta. Mwachitsanzo, pa nthawi ina iye anauza ophunzira ake kuti: “Inu ndinu kuwala kwa dziko.” Ophunzirawo sanavutike kumvetsa tanthauzo la fanizoli. Iwo anadziwa kuti zolankhula ndi zochita zawo zingathandize kuti choonadi chiwale ndiponso zingathandize kuti anthu ena azipereka ulemerero kwa Mulungu. (Mateyu 5:14-16) Onaninso mafanizo ena amene Yesu anagwiritsa ntchito. Mwachitsanzo iye anati: “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi” ndiponso “Ine ndine mtengo wa mpesa, inu ndinu nthambi zake.” (Mateyu 5:13; Yohane 15:5) Mafanizo oterewa ndi osavuta kumva koma ndi ogwira mtima kwambiri.
10. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza mmene mungagwiritsire ntchito mafanizo pophunzitsa?
10 Kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa? Simukufunikira kuchita kupeka kapena kufotokoza nkhani zazitali. Mukhoza kungoganizira fanizo lalifupi ndiponso losavuta. Tiyerekezere kuti mukukambirana nkhani yonena za kuuka kwa akufa ndipo mukufuna kugwiritsa ntchito fanizo losonyeza kuti Yehova sangavutike kuukitsa munthu. Kodi mungagwiritse ntchito fanizo lotani? Baibulo limayerekezera imfa ndi kugona tulo. Choncho munganene kuti, “Mulungu sangavutike kuukitsa anthu akufa ngati mmene munthu sangavutikire kudzutsa munthu amene akugona.” (Yohane 11:11-14) Yerekezerani kuti mukufuna kupereka fanizo losonyeza kuti ana amafunika kukondedwa kuti akule bwino. Kodi mungagwiritse ntchito fanizo liti? Baibulo limayerekezera chonchi: Ana ali ngati “mphukira za mtengo wa maolivi.” (Salimo 128:3) Mukhoza kunena kuti, “Chikondi n’chofunika kwambiri kwa ana ngati mmene dzuwa ndi madzi zilili zofunika kuti mtengo ukule bwino.” Fanizo likakhala losavuta kumva, zimakhalanso zosavuta kuti anthu amvetse bwino mfundo yake.
Yesu Ankagwiritsa Ntchito Mafanizo Ogwirizana ndi Zimene Zinkachitika Tsiku ndi Tsiku
11. Perekani zitsanzo za mmene Yesu ankagwiritsira ntchito mafanizo a zinthu zimene ankaona ku Galileya kuyambira ali mwana.
11 Yesu anali katswiri pogwiritsa ntchito mafanizo ogwirizana ndi zimene anthu ankachita pa moyo wawo. Mafanizo ake ambiri anali ogwirizana ndi zimene zinkachitika tsiku ndi tsiku zimene iye ankaona ku Galileya kuyambira ali mwana. Mwachitsanzo, taganizirani zimene anaphunzira kuyambira ali wamng’ono. Nthawi zambiri ankaona mayi ake akupera ufa, akuthira zofufumitsa mu ufa pophika mikate, akuyatsa nyale kapenanso akusesa m’nyumba. (Mateyu 13:33; 24:41; Luka 15:8) Nthawi zambiri ankaonanso asodzi akuponya makoka awo m’nyanja ya Galileya. (Mateyu 13:47) Ndiponso ankaona ana akusewera m’misika. (Mateyu 11:16) N’zosakayikitsa kuti Yesu anaonanso zinthu zina zimene zinkachitika tsiku ndi tsiku zimene anazitchula m’mafanizo ake ambiri. Zina mwa zinthu zimenezi ndi kudzala mbewu, mapwando a ukwati ndiponso mbewu zitacha m’minda.—Mateyu 13:3-8; 25:1-12; Maliko 4:26-29.
12, 13. N’chifukwa chiyani zinali zomveka kuti Yesu anatchula msewu ‘wochokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko’ pofuna kuti anthu amvetse mfundo ya m’fanizo la Msamariya wachifundo?
12 M’mafanizo ake, Yesu ankatchula zinthu zimene omvera ake ankazidziwa bwino. Mwachitsanzo, pofotokoza fanizo la Msamariya wachifundo, iye anayamba ndi mawu akuti: “Munthu wina ankayenda kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko ndipo anakumana ndi achifwamba amene anamuvula n’kumumenya koopsa. Kenako anachoka, n’kumusiya atatsala pang’ono kufa.” (Luka 10:30) Zikuoneka kuti Yesu anatchula msewu ‘wochokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko’ kuti anthu amvetse bwino mfundo yake. Pamene ankafotokoza fanizo limeneli iye anali ku Yudeya, pafupi ndi Yerusalemu, choncho omvera akewo mosakayikira ankaudziwa bwino msewu umenewu. Anthu ankadziwa kuti msewu umenewu unali woopsa makamaka ngati munthu akuyenda yekha. Msewu umenewu unkadutsa kutali ndi midzi ndiponso unali wokhotakhota. Zimenezi zinachititsa kuti ukhale ndi malo ambiri omwe mungabisale achifwamba.
13 Yesu ananenanso zinthu zina zodziwika bwino zokhudza msewu ‘wochokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko.’ Fanizoli limafotokoza kuti, choyamba mumsewumo munadutsa wansembe kenako Mlevi koma palibe amene anaima kuti athandize munthu wovulalayo. (Luka 10:31, 32) Ansembe ankatumikira pakachisi ku Yerusalemu ndipo Alevi ankawathandiza. Akakhala kuti sakugwira ntchito pakachisi, ansembe ndi Alevi ambiri ankakhala ku Yeriko, mzinda womwe unali pamtunda wa makilomita 23 okha kuchokera ku Yerusalemu. N’chifukwa chake ankadutsadutsa mumsewu umenewu.b N’zoonekeratu kuti pophunzitsa, Yesu ankaganizira omvera ake.
14. Tikamagwiritsa ntchito mafanizo, kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira omvera athu?
14 Nafenso timafunika kuganizira omvera athu tikamagwiritsa ntchito mafanizo. Kodi ndi zinthu zina ziti zokhudza omvera athu zimene zingatithandize kusankha mafanizo amene tingagwiritse ntchito? Mwina mungaganizire zinthu monga msinkhu, chikhalidwe kapena banja limene anthuwo anachokera ndiponso ntchito imene amagwira. Mwachitsanzo, fanizo limene likunena za ulimi lingamveke bwino kumidzi kuposa m’tawuni. Tingapange mafanizo abwino tikaganizira zimene omvera athu amachita tsiku ndi tsiku pa moyo wawo monga zimene amakonda kuchita, zakudya zawo, ana awo ndi nyumba zawo.
Yesu Ankagwiritsa Ntchito Mafanizo Okhudza Zinthu Zam’chilengedwe
15. N’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuti Yesu ankadziwa kwambiri zachilengedwe?
15 Mafanizo ambiri a Yesu amasonyeza kuti ankadziwa bwino zachilengedwe monga zomera, nyama ndi nyengo. (Mateyu 16:2, 3; Luka 12:24, 27) Kodi zinthu zimenezi anazidziwa bwanji? Kuyambira ali mwana ku Galileya, n’zosakayikitsa kuti anali ndi mpata wabwino woona ndi kuphunzira zachilengedwe. Kuposa zonsezi, Yesu ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse” ndipo polenga zinthu zonse, Yehova anamugwiritsira ntchito monga “mmisiri waluso.” (Akolose 1:15, 16; Miyambo 8:30, 31) Choncho n’zosadabwitsa kuti Yesu ankadziwa bwino kwambiri zinthu zam’chilengedwe. Tiyeni tione mmene anagwiritsira ntchito mwaluso zimene ankadziwazo.
16, 17. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankazidziwa bwino nkhosa? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti nkhosa zimadziwa bwino mawu a m’busa wawo.
16 Kumbukirani kuti Yesu anadzitchula kuti iye ndi “m’busa wabwino” ndipo otsatira ake ndi “nkhosa.” Zimene Yesu ananenazi zikusonyeza kuti nkhosa ankazidziwa bwino. Iye ankadziwanso kuti nkhosa zimamudziwa bwino kwambiri m’busa wawo. Ankadziwa kuti nyama zokhulupirika zimenezi zimalolera kuti m’busa wawo azizitsogolera ndipo nkhosazo zimatsatira m’busayo mokhulupirika. N’chifukwa chiyani nkhosa zimatsatira m’busa wawo? Yesu anati: “Chifukwa zimadziwa mawu ake.” (Yohane 10:2-4, 11) Kodi nkhosa zimadziwadi mawu a m’busa wawo?
17 Ataona zimene nkhosa zimachita, George A. Smith analemba m’buku lake kuti: “Nthawi zina masana tinkakonda kupuma pafupi ndi zitsime ku Yudeya, ndipo abusa atatu kapena 4 ankabwera aliyense ndi nkhosa zake. Nkhosazo zinkasakanikirana ndipo ife tinkadabwa kuti m’busa aliyense adziwa bwanji nkhosa zake. Koma nkhosazo zikamaliza kumwa madzi ndiponso kusewera, m’busa aliyense ankapita kwayekha n’kuitana nkhosa zake. Ndipo nkhosa za m’busa aliyense zinkachoka pagulupo mwadongosolo n’kutsatira m’busa wawo.” Pamenepa Yesu anagwiritsa ntchito fanizo labwino kwambiri potsindika mfundo yakuti, tikamatsatira ndi kumvera zimene iye amaphunzitsa, adzatisamalira, chifukwa iye ndi “m’busa wabwino.”
18. Kodi nkhani zokhudza zinthu zimene Yehova analenga tingazipeze kuti?
18 Kodi ifeyo tingatani kuti tizigwiritsa ntchito mafanizo okhudzana ndi zinthu zam’chilengedwe? Tingapange mafanizo osavuta koma ogwira mtima pogwiritsa ntchito zimene nyama zina zimachita. Kodi tingapeze kuti nkhani zokhudza zinthu zimene Yehova analenga? M’Baibulo tingapezemo nkhani zambiri zokhudza nyama zosiyanasiyana ndipo nthawi zina tingapezemo mafanizo ofotokoza mmene nyama zimakhalira. Mwachitsanzo Baibulo limanena za kuthamanga mwaliwiro ngati mbawala kapena kambuku, kukhala ochenjera ngati njoka komanso kukhala oona mtima ngati nkhunda.c (1 Mbiri 12:8; Habakuku 1:8; Mateyu 10:16) Tingapezenso nkhani zina m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! komanso m’nkhani ndi m’mavidiyo a mutu wakuti “Kodi Zinangochitika Zokha,” zomwe zikupezeka pa jw.org. Mungaphunzire zambiri poona mmene nkhani zimenezi zafotokozera mafanizo osavuta kuchokera ku zinthu zochititsa chidwi zimene Yehova analenga.
Yesu Ankagwiritsa Ntchito Mafanizo a Zinthu Zodziwika Bwino
19, 20. (a) Potsutsa bodza limene anthu ankakhulupirira, kodi Yesu anagwiritsa ntchito bwanji mwaluso nkhani imene inali itangochitika kumene? (b) Kodi tikamaphunzitsa, tingagwiritse ntchito bwanji nkhani ndiponso zinthu zimene zinachitikadi?
19 Tingapange mafanizo ogwira mtima pogwiritsa ntchito zochitika zenizeni pa moyo. Nthawi ina Yesu anagwiritsa ntchito nkhani imene inali itangochitika kumene pofuna kutsutsa bodza limene anthu ankakhulupirira lakuti munthu akakumana ndi tsoka ndiye kuti ndi wochimwa. Iye anati: “Nanga bwanji za anthu 18 aja, amene nsanja inawagwera ku Siloamu n’kuwapha? Kodi mukuganiza kuti anali ochimwa kwambiri kuposa anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu?” (Luka 13:4) Si kuti anthu 18 aja anafa chifukwa chakuti anali ochimwa kapena chifukwa chakuti Mulungu sankasangalala nawo. Koma anafa chifukwa chakuti anakumana ndi “nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezereka.” (Mlaliki 9:11) Choncho Yesu anafotokoza nkhani imene omvera ake ankaidziwa bwino potsutsa bodza limene anthu ankaphunzitsa.
20 Kodi pophunzitsa, tingagwiritse ntchito bwanji nkhani ndiponso zinthu zimene zinachitikadi? Yerekezerani kuti mukukambirana za kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu wonena za chizindikiro cha kukhalapo kwake. (Mateyu 24:3-14) Mungagwiritse ntchito nkhani zimene zangochitika kumene ngati za nkhondo, njala kapena zivomerezi, posonyeza kuti ulosi wa Yesu wonena za kukhalapo kwake ukukwaniritsidwa. Kapena tiyerekezere kuti mukufuna kufotokoza zimene munthu angafunike kuchita kuti asinthe khalidwe lake loipa n’kuvala umunthu watsopano. (Aefeso 4:20-24) Kodi nkhani ngati zimenezo mungazipeze kuti? Mungafotokoze nkhani zosiyanasiyana za Akhristu anzanu kapena mungafotokoze nkhani zimene zinalembedwa m’mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mungapezenso nkhani zofotokoza zimene zinachitikira anthu ena munkhani zimene zili pamutu wakuti “Baibulo Limasintha Anthu” pa jw.org.
21. Kodi timapeza madalitso otani tikamaphunzitsa Mawu a Mulungu mwaluso?
21 Ndithudi, Yesu anali Mphunzitsi Waluso kwambiri. Monga mmene taonera m’gawo lino, ntchito yaikulu pa moyo wa Yesu inali ‘yophunzitsa komanso kulalikira uthenga wabwino.’ (Mateyu 4:23) Ntchito imeneyi ndi yofunikanso kwambiri kwa ife ndipo timapeza madalitso ambiri tikamaphunzitsa mwaluso. Tikamaphunzitsa, timakhala tikupatsa ena choonadi ndipo kupatsa kotereku kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri. (Machitidwe 20:35) Timakhala osangalala chifukwa tikudziwa kuti tikuthandiza anthu kuti adziwe choonadi chonena za Yehova chomwe ndi chamtengo wapatali. Komanso timasangalala kudziwa kuti tikutsanzira Yesu, yemwe ndi Mphunzitsi waluso kuposa aliyense amene anakhalapo padziko lapansi.
a Zikuoneka kuti Uthenga Wabwino wa Mateyu ndi nkhani youziridwa yoyamba yonena za moyo wa Yesu padziko lapansi, ndipo unalembedwa patapita zaka pafupifupi 8 Yesu atamwalira.
b Yesu ananenanso kuti wansembe ndi Mleviyo ‘ankachokera ku Yerusalemu,’ zimene zikusonyeza kuti ankachokera kukachisi. Choncho palibe amene angawaikire kumbuyo ponena kuti iwo anapewa kukhudza wovulalayo chifukwa ankaoneka ngati wafa, ndipo akanakhala osayenerera kutumikira pakachisi kwa kanthawi.—Levitiko 21:1; Numeri 19:16.
c Kuti mupeze mndandanda wa mafanizo onena za nyama amene ali m’Baibulo onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 268, 270 ndi 271. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.