Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kuchoka ku Nyumba ya Yairo ndi Kuchezeranso ku Nazarete
TSIKU lakhala lotanganitsa kwa Yesu—ulendo wa pa nyanja kuchokera ku Dekapoli, kuchiritsa mkazi wokukha mwazi, ndi kuukitsa mwana wamkazi wa Yairo. Koma tsiku silinathebe. Mwachiwonekere pamene Yesu akuchoka ku nyumba ya Yairo, amuna awiri akhungu akumutsatira pambuyo, akumafuula: “Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.”
Mwakumuitana Yesu monga “Mwana wa Davide,“ amuna amenewa akusonyeza chikhulupiriro kuti Yesu ali mlowa m’malo ku mpando wachifumu wa Davide, chotero kuti iye ali Mesiya wolonjezedwa. Komabe, Yesu, mwachiwonekere akunyalanyaza kufuula kwawo kaamba ka thandizo, mwinamwake kuti ayese kukakamira kwawo. Koma amunawo sakutaya chikhulupiriro. Iwo akumutsatira Yesu kumene iye akukhala, ndipo pamene iye alowa mnyumba, iwo akumutsatira mkatimo.
Kumeneko Yesu awafunsa: “Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi?“
“Inde, Ambuye,“ iwo akuyankha motsimikizika.
Chotero, akukhudza maso awo, Yesu akuti: “Chichitidwe kwa inu monga chikhulupiriro chanu.” Pomwepo iwo akuwona! Yesu kenaka awauzitsa iwo: “Yang’anirani asadziwe munthu aliyense.” Koma modzazidwa ndi chimwemwe, iwo akunyalanyaza lamulo la Yesu ndi kulankhula ponena za iye mu dziko lonselo.
Mwamsanga pamene amuna awa akuchoka, anthu abweretsa munthu wogwidwa ndi chiwanda amene chiwandacho chamulanda kulankhula kwake. Yesu atulutsa chiwandacho, ndipo panthawi yomweyo munthuyo ayamba kulankhula. Makamuwo azizwa pa zozizwitsa izi, akumati: “Kale lonse sichinawoneke chomwecho mwa Israyeli.”
Afarisi, nawonso, alipo. Iwo sangakane zozizwitsazo, koma mkusakhulupirira kwawo koipa iwo abweretsa mlandu wawo ponena za magwero a ntchito zamphamvu za Yesu akumati: “atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.”
Mwamsanga pambuyo pa zochitika izi, Yesu abwerera ku tauni ya kwawo ya Nazarete, panthawiyi atsagana ndi ophunzira ake. Chifupifupi chaka chimodzi poyambirira, iye anapita ku sunagoge ndi kuphunzitsa kumeneko. Ngakhale kuti anthu poyamba anazizwa ndi zonena zake zosangalatsa, iwo kenaka amupalamulitsa pa chiphunzitso chake ndi kuyesa kumupha iye. Tsopano mwachifundo, Yesu apanga kuyesera kwina kwakuthandiza anansi ake akale.
Pamene kuli kwakuti m’malo ena anthu amathamangira kwa Yesu, kuno mwachiwonekere iwo sakutero. Chotero, pa Sabata, iye apita ku sunagoge kukaphunzitsa. Ambiri a awo omvetsera iye adabwitsidwa. “Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi?“ Iwo akufunsa. “Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? Kodi dzina la amake si Mariya, ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda? Ndipo alongo ake sali ndife onsewa? Ndipo iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti?“
‘Yesu ali kokha munthu wamba monga ife,’ akupereka chifukwa. ‘Tinamuwona iye akukula, ndipo timadziwa banja lake. Ndimotani mmene iye angakhalire Mesiya?’ Chotero mosasamala kanthu za chitsimikizo chonsechi—nzeru yake yaikulu ndi zozizwitsa—akumukana iye. Ngakhale abale ake enieni, chifukwa cha kuzolowerana kwathithithi kwawo, akukhumudwitsidwa naye, kumupangitsa Yesu kumaliza: “Mneneri sakhala wopanda ulemu koma ku dziko la kwawo ndiko, ndi kubanja kwake.”
Ndithudi, Yesu akudabwa pa kusowa kwawo kwa chikhulupiriro. Chotero iye sakupanga chozizwitsa chirichonse kumeneko kusiyapo kokha kuika manja ake pa odwala ochepa ndi kuwachiritsa iwo. Mateyu 9:27-34; 13:54-58; Marko 6:1-6; Yesaya 9:7.
◆ Mwakumuitana Yesu monga “Mwana wa Davide,“ kodi nchiyani chimene amuna akhunguwo akusonyeza kuti amakhulupirira?
◆ Kodi ndi kulongosola kotani kwa zozizwitsa za Yesu kumene Afarisi akhazikitsa?
◆ Kodi nchifukwa ninji chiri chifundo kwa Yesu kubwerera kukathandiza awo a mu Nazarete?
◆ Kodi ndi kulandiridwa kotani kumene Yesu walandira mu Nazarete, ndipo nchifukwa ninji?