MUTU 48
Yesu Anachita Zozizwitsa Koma Anakanidwa Ngakhale Kwawo ku Nazareti
MATEYU 9:27-34; 13:54-58 MALIKO 6:1-6
YESU ANACHIRITSA ANTHU OSAONA NDI WINA WOSALANKHULA
ANTHU A KU NAZARETI ANAKANA YESU
Yesu atachoka m’dera la Dekapole, anapita ku Kaperenao komwe anachiritsa mzimayi amene ankadwala matenda otaya magazi komanso anaukitsa mwana wamkazi wa Yairo. Yesu anachita zinthu zonsezi tsiku limodzi. Komabe pamene ankachoka kunyumba kwa Yairo, anthu awiri osaona anayamba kumutsatira n’kumakuwa kuti: “Mutichitire chifundo, Mwana wa Davide.”—Mateyu 9:27.
Chifukwa choti anthuwo anatchula Yesu kuti “Mwana wa Davide,” anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Yesu ndiye woyenera kulowa Ufumu wa Davide ndiponso kuti anali Mesiya. Poyamba Yesu anaoneka ngati sanamve zimene anthuwo ankanena koma n’kutheka kuti anachita dala zimenezi kuti aone ngati anthuwo ankafunitsitsa kuti Yesuyo awathandize. Ndipo anthuwo anachitadi zimenezo. Yesu atalowa m’nyumba, anthu awiri aja anamutsatira. Kenako anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi chikhulupiriro kuti ndingachite zimenezi?” Iwo anamuyankha motsimikiza kuti: “Inde, Ambuye.” Pamenepo Yesu anawagwira m’maso n’kuwauza kuti: “Malinga ndi chikhulupiriro chanu zichitike momwemo kwa inu.”—Mateyu 9:28, 29.
Nthawi yomweyo anthu aja anayamba kuona. Yesu anauzanso anthuwa ngati mmene anachitira ndi anthu oyambirira aja kuti asauze aliyense zimene anawachitira. Koma chifukwa chakuti anali osangalala, patapita nthawi anayamba kufotokozera anthu a m’madera apafupi komanso akutali zimene Yesu anawachitira.
Pa nthawi imene anthu awiriwa ankachoka, anthu anabweretsa munthu wina amene sankalankhula chifukwa chakuti anali wogwidwa ndi chiwanda. Yesu atangotulutsa chiwandacho, munthuyo anayamba kulankhula. Anthu ambiri ataona zimenezi anadabwa kwambiri ndipo ananena kuti: “Zinthu zoterezi sizinaonekepo n’kale lonse mu Isiraeli.” Pamene zimenezi zinkachitika panalinso Afarisi. Afarisi sakanatha kutsutsa zozizwitsa zimene Yesu anachitazi, koma anayambanso kunena kuti Yesu “amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”—Mateyu 9:33, 34.
Kenako pasanapite nthawi yaitali, Yesu anabwerera ku tauni ya kwawo ku Nazareti ali ndi ophunzira ake. Pa nthawiyi n’kuti patadutsa pafupifupi chaka kuchokera pamene anaphunzitsa m’sunagoge wa ku Nazaretiko. Ngakhale kuti pa nthawi imeneyo anthu anagoma ndi uthenga wake, koma anakwiya kwambiri ndipo ankafuna kumupha. Komabe Yesu anapanganso ulendowu ndi cholinga choti akathandize anthu akwawo.
Pa tsiku la Sabata Yesu analowa m’kachisi kukaphunzitsa. Anthu ambiri anadabwa ndi mmene ankaphunzitsira ndipo anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu, nzeru ndi ntchito zamphamvu zoterezi anazitenga kuti? Kodi si mwana wa mmisiri wamatabwa uyu? Kodi mayi ake si Mariya, ndipo abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi? Alongo ake onse sitili nawo konkuno? Nanga iyeyu zinthu zonsezi anazitenga kuti?”—Mateyu 13:54-56.
Anthuwo ankaona Yesu ngati munthu wamba, moti ankaganiza kuti: ‘Tamuona akukula uyu ndiye angakhale bwanji Mesiya?’ Choncho ngakhale kuti panali umboni wokwanira wosonyeza kuti Yesu anali Mesiya komanso anamuona akuchita zinthu zamphamvu ndiponso zosonyeza kuti anali wanzeru kwambiri, anthuwo anamukana. Anachita zimenezi chifukwa ankamudziwa bwino ndipo ngakhale achibale ake anakhumudwa naye. Zimenezi zinachititsa Yesu kunena kuti: “Mneneri salemekezedwa kwawo kapena m’nyumba mwake, koma kwina.”—Mateyu 13:57.
Mosakayikira Yesu anadabwa ndi kupanda chikhulupiriro kwa anthuwa. Choncho sanachite zozizwitsa zilizonse kumeneko kupatulako ‘kungoika manja pa odwala owerengeka ndi kuwachiritsa.’—Maliko 6:5, 6.