‘Kodi Inali Nthaŵi Yanji?’
‘KODI ndinthaŵi yanji?’ Kodi ndikangati pamene mwafunsa funso limenelo? M’nyengo yathu yamakono yofulumira, nthaŵi zonse timasamalira nthaŵi. Zochita zathu zambiri zatsiku ndi tsiku—kudzuka m’mawa, kupita kuntchito, kudya chakudya chathu, kukumana ndi mabwenzi, ndi zina zotero—zimalamulidwa ndi nthaŵi kotheratu. Ndipo kuti tidziŵe nthaŵi, timadalira pa zipangizo zamitundumitundu—makoloko, mawatch, maalarm, mawailesi.
Bwanji ponena za m’nthaŵi Zabaibulo pamene anthu analibe zipangizo zodziŵitsa nthaŵi monga zathu? Kodi ndimotani mmene anaŵerengera nthaŵi? Kodi cholembedwa cha Baibulo chimapereka chizindikiro chirichonse ponena za izi? Kudziŵa nthaŵi ya tsiku pamene chochitika chakutichakuti cha m’Baibulo chinachitika kukhoza kukupatsani chidziŵitso chatsopano cha Mawu a Mulungu ndi kuwonjezera chisangalalo ku phunziro lanu Labaibulo.
Zodziŵitsa Nthaŵi Zoperekedwa ndi Mulungu
M’masiku akale nthaŵi ya chochitika inazindikiridwa mwakuwona dzuŵa kapena mwezi, ‘zounikira zazikulu ziŵiri’ zimene Mlengi anaika kumwamba ‘kulekanitsa usana ndi usiku.’ (Genesis 1:14-16) Mwachitsanzo, kunali ‘pamene kunacha’ pomwe angelo aŵiri anafulumiza Loti ndi banja lake kuthaŵa kuchoka m’mzinda woyembekezera kuwonongedwa wa Sodomu. (Genesis 19:15, 16) Ndipo kunali ‘nthaŵi yamadzulo’ pamene kapolo wokhulupirika wa Abrahamu anafika pa chitsime pamene anakumana ndi Rebeka.—Genesis 24:11, 15.
Nthaŵi zina, matchulidwe achindunji kwenikweni anthaŵi anaperekedwa. Mwachitsanzo, Abimeleki, mwana wamwamuna wachiwawa wa Woweruza Gideoni, analangizidwa kuukira mzinda wa Sekemu ‘m’maŵa, pakutuluka dzuŵa.’ (Oweruza 9:33) Mwachiwonekere panali chifukwa chamachenjera kumbuyo kwa zimenezi. Chizimezime cha dzuŵa lomatuluka kumbuyo kwa magulu ankhondo a Abimeleki chinakupangitsa kukhala kovuta kwambiri kwa alonda a Sekemu kuwona magulu oukirawo mu “mthunzi wa mapiri.”—Oweruza 9:36-41.
Mawu Okuluwika Anthaŵi
Ahebri anagwiritsira ntchito mawu otchulira nthaŵi amene ali ponse paŵiri omvekera bwino ndi osangalatsa. Iwo samangotipatsa lingaliro la mkhalidwe wa ku malo akutiakuti ndi miyambo yake koma amavumbulanso zinazake ponena za mikhalidwe ya chochitikacho.
Mwachitsanzo, Genesis 3:8, (NW) amatiuza kuti kunali “pafupi ndi nthaŵi yamphepo ya tsiku” pamene Yehova analankhula kwa Adamu ndi Hava patsiku limene anachimwa. Zimenezi zimamvedwa kukhala pafupi ndi kuloŵa kwa dzuŵa pamene mphepo yozizira iyambika, ikumadzetsa mpumulo ku kutentha kwa tsikulo. Kaŵirikaŵiri, pamene tsiku liyandikira mapeto ake, imakhala nthaŵi yomasuka ndi kupuma. Komabe, Yehova sanalole nkhani yaikulu yachiweruzo kuyembekezera mpaka tsiku lotsatira pamene padakali nthaŵi yoisamalira.
Kumbali ina, Genesis 18:1, 2 amasonyeza kuti angelo a Yehova anabwera ku hema wa Abrahamu ku Mamre ‘pakutentha dzuŵa.’ Tapenyani ndi diso lanu lamaganizo dzuŵa lamasana likuswa mtengo m’mapiri a Yudeya. Kutenthako kungakale kotopetsa. Inali nthaŵi yachizoloŵezi yakudya chakudya chamasana ndi kupuma. (Onani Genesis 43:16, 25; 2 Samueli 4:5.) Chotero, Abrahamu ‘anakhala pakhomo la hema wake,’ pamene pangakhale mphepo yowomba pang’ono, mwinamwake akupuma pambuyo podya chakudya chake. Tikhoza kuzindikira kwambiri kuchereza kwa mwamuna wachikulireyu pamene tiŵerenga kuti “anawathamangira . . . kukakomana” ndi alendowo ndiyeno ‘analoŵa msanga m’hema’ kukauza Sara kukonzekeretsa mkate, pambuyo pake ‘anafulumira kumka kuzoŵeta’ ndipo ‘anafulumira kuphika.’ Zonsezi m’kutentha kwa tsikulo!—Genesis 18:2-8.
Maola Ausiku a Ahebri
Mwachiwonekere Ahebri anagaŵa usiku m’nyengo zitatu, zotchedwa “maulonda.” Nyengo iriyonse inakuta chigawo chimodzi mwazitatu cha nthaŵi yapakati pa kuloŵa ndi kutuluka kwa dzuŵa, kapena pafupifupi maola anayi, kudalira pa nyengo. (Salmo 63:6) Kunali “poyambira ulonda wa pakati,” umene unayambira pafupifupi 10 koloko usiku mpaka pafupifupi 2 koloko m’mawa, pamene Gideoni anaukira msasa wa Amidyani. Kuukira panthaŵiyi mwachiwonekere kunawadzidzimutsa kotheratu alondawo. Ndithudi, Gideoni wochenjerayo sakanasankha nthaŵi ina yoyenerera youkira koposa imeneyo!—Oweruza 7:19.
Panthaŵi ya ulendo wotchedwa Eksodo, Yehova “anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum’mawa usiku wonse,” akumalola Aisrayeli kuwoloka panthaka youma. Podzafika nthaŵi imene Aigupto anawapeza, inali kale “ulonda wa mamawa,” ndipo Yehova anawasokoneza Aigupto, ndikuwawononga pomalizira pake mwakubweza madzi ‘m’mayendedwe ake mbanda kucha.’ (Eksodo 14:21-27) Chotero kunatenga pafupifupi usiku wonse kuti nyanja igaŵikane ndikuti Aisrayeli awoloke.
M’Zaka za Zana Loyamba
Podzafika zaka za zana loyamba, Ayuda anayamba kuŵerengera kwa maola 12 patsiku. Ndicho chifukwa chake m’limodzi la mafanizo ake, Yesu ananena kuti: ‘Kodi sikuli maola khumi ndi aŵiri usana?’ (Yohane 11:9) Aŵa anaŵerengedwa kuchokera pakutuluka kwa dzuŵa mpaka pakuloŵa kwake, kapena pafupifupi 6 koloko m’mawa mpaka 6 koloko m’madzulo. Chotero, ‘ola lachitatu’ likakhala pafupifupi 9 koloko m’mawa. Kunali panthaŵi imeneyi patsiku la Pentekoste pamene mzimu woyera unatsanulidwa. Pamene anthu anaimba ophunzira mlandu ‘wokhuta vinyo walero,’ Petro mofulumira anathetsa chinenezocho. Ndithudi palibe aliyense angaledzere pa ola la m’mawa loterolo!—Machitidwe 2:13, 15.
Mofananamo, mawu a Yesu akuti ‘chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha amene anandituma ine’ amakhala ndi tanthauzo lowonjezereka pamene tilingalira nthaŵi yoloŵetsedwamo. Mogwirizana ndi Yohane 4:7, linali ‘ola lachisanu ndi chimodzi,’ kapena pafupifupi nthaŵi yamasana. Pambuyo poyenda kupyola dera lamapiri la Samariya m’mawa monse, Yesu ndi ophunzira ake anali ndi njala ndi ludzu. Ndicho chifukwa chake ophunzirawo anamfulumiza kudya pamene anabwera ndi chakudya. Iwo sanaidziŵe nyonga ndi chichirikizo zimene Yesu anapeza mwakuchita ntchito ya Yehova. Mosakaikira mawu a Yesu sanali mwambi. Iye m’lingaliro lenileni anachirikizidwa mwakuchita ntchito ya Mulungu ngakhale kuti panali patapita maola ambiri kuyambira pamene anadyera chakudya.—Yohane 4:31-34.
Popeza kuti kutuluka ndi kuloŵa kwa dzuŵa kunasiyana malinga ndi nyengo ya chaka, kaŵirikaŵiri kokha nthaŵi yongoyerekezera ya chochitika inaperekedwa. Chotero, nthaŵi zambiri timaŵerenga za zinthu zochitika pa ola lachitatu, lachisanu ndi chimodzi, kapena lachisanu ndi chinayi—kaŵirikaŵiri kutanthauza mongoyerekezera panthaŵizo. (Mateyu 20:3, 5; 27:45, 46; Marko 15:25, 33, 34; Luka 23:44; Yohane 19:14; Machitidwe 10:3, 9, 30) Komabe, pamene nthaŵi inali yofunika m’nkhaniyo, mawu achindunji koposa anagwiritsiridwa ntchito. Mwachitsanzo, kwa mwamuna yemwe anafunitsitsa kudziŵa ngati mwana wake anachiradi mwa mphamvu ya Yesu, akapolo anayankha kuti: ‘Dzulo ola lachisanu ndi chiŵiri [pafupifupi 1 koloko masana] malungo anamsiya.’—Yohane 4:49-54.
Zigawo Zausiku
Podzafika nthaŵi ya ulamuliro Wachiroma, Ayuda awonekera kuti anatengera kugaŵa kwa Agiriki ndi Aroma kwa usiku m’maulonda anayi mmalo mwa atatu amene ankagwiritsira ntchito kalelo. Pa Marko 13:35, Yesu mwachiwonekere analoza ku zigawo zinayizo. Ulonda wa “madzulo” unayambira pakuloŵa kwa dzuŵa mpaka pafupifupi 9 koloko madzulowo. Ulonda wachiŵiri, wa “pakati pausiku,” unayambira pafupifupi 9 koloko ndi kuthera pakati pausiku. Ulonda wa “pakulira tambala” unayambira pakati pausiku mpaka pafupifupi 3 koloko. Ndipo ulonda womalizira wa, “mamawa,” unatha mbanda kucha, kapena pafupifupi 6 koloko.
Ulonda wa “pakulira tambala” ngwofunika koposa chifukwa cha mawu a Yesu kwa Petro pa Marko 14:30 akuti: ‘Tambala asanalire kaŵiri, udzandikana ine katatu.’ Pamene kuli kwakuti othirira ndemanga ambiri amanena kuti mawuwo ‘kaŵiri’ amaloza mwachindunji ku nthaŵi zakutizakuti—pakati pausiku ndi mbanda kucha—A Dictionary of Christ and the Gospels, lokonzedwa ndi James Hastings, limasonyeza kuti “kunena zowona atambala amalira usiku, Kum’maŵa monga kwina kulikonse, panthaŵi zosiyanasiyana kuchokera pakati pausiku kumka kutsogolo.” Mwachiwonekere, Yesu sanali kuloza ku nthaŵi yakutiyakuti pamene Petro akamkana. Mmalomwake, ankapereka chizindikiro kutsimikiziritsa mawu ake kwa Petro, omwe anakwaniritsidwa molondola usiku womwewo.—Marko 14:72.
Kunali ‘paulonda wachinayi wa usiku’—pakati pa 3 ndi 6 koloko m’mawa—pamene Yesu, ali kuyenda pamadzi a Nyanja ya Galileya, anadza kwa ophunzira ake, omwe anali m’ngalawa “pakati pa nyanja.” Mwinamwake, kuli kosavuta kumvetsetsa chifukwa chake ophunzira “ananthunthumira, nati, Ndi mzukwa! Ndipo anafuula ndi mantha.” (Mateyu 14:23-26) Kumbali ina, chimenechi chimasonyeza kuti Yesu anathera nthaŵi yaikulu akupemphera payekha m’phiri. Popeza kuti zimenezi zinali mwamsanga pambuyo pakuti Yohane Mbatizi wadulidwa mutu ndi Herode Antipa ndipo kutatsala pang’ono Paskha isanachitike, imene inazindikiritsa kuyambika kwa chaka chomalizira cha uminisitala wa Yesu wapadziko lapansi, Yesu analidi nzambiri zoti asinkhesinkhe m’pemphero lake laumwini kwa Atate.
Limodzi ndi maulonda anayi, kuŵerenga kwa maola 12 ausiku kunkagwiritsiridwanso ntchito. Kuti aperekeze Paulo ku Kaisareya mwachisungiko, kazembe wankhondo Klaudiyo Lusiya anauza nduna zake kukonzekera gulu la asirikali 470 pa ‘ola lachitatu la usiku.’ (Machitidwe 23:23, 24) Chotero Paulo anatengedwa usiku mwachisungiko kuchoka ku Yerusalemu.
Dziŵani Nthaŵi ya Tsikulo
Kuŵerenga ndi kusinkhasinkha pa zolembedwa za zimene zinachitikira anthu a Mulungu akale kuli magwero a chisangalalo ndi nyonga yauzimu. Ngati mukhoza kuphatikizapo nthaŵi m’kusanthula kwanu, kudzawonjezeradi chimwemwe cha phunziro lanu Labaibulo. Kodi nchifukwa ninji kuli tero? Chifukwa chakuti mwanjirayi mukhoza kuwadziŵa bwino Mawu a Mulungu. Mabuku onga Insight on the Scriptures ndi New World Translation of the Holy Scriptures With References ndiothandiza amtengo wake pa nkhaniyi (onse aŵiri ngofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.). Adzakuthandizani kupeza yankho pamene mudzifunsa kuti: ‘Kodi inali nthaŵi yanji?’