Khalani ndi Chikhulupiriro Cholimba
“Limbani m’chikhulupiriro, . . . khalani amphamvu.”—1 AKOR. 16:13.
1. (a) N’chiyani chinachitikira Petulo panyanja ya Galileya? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) N’chifukwa chiyani Petulo anayamba kumira?
TSIKU lina usiku kunali mphepo yamkuntho moti mtumwi Petulo ndi ophunzira ena ankavutika kuyendetsa ngalawa yawo panyanja ya Galileya. Kenako, mwadzidzidzi anaona Yesu akuyenda panyanjayo. Ndiyeno Petulo anafunsa Yesu ngati nayenso angayende pamadzi n’kupita kumene kunali Yesuyo. Atamuuza kuti abwere, Petulo anatsika m’ngalawayo n’kuyamba kuyenda pamadzipo. Koma patangopita nthawi yochepa, anayamba kumira. Izi zinachitika chifukwa chakuti anayang’ana mphepo yamkunthoyo n’kuyamba kuchita mantha. Kenako Petulo anafuula n’kupempha Yesu kuti amuthandize ndipo Yesuyo anamugwira n’kunena kuti: “Wachikhulupiriro chochepa iwe, n’chifukwa chiyani wakayikira?”—Mat. 14:24-32.
2. Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?
2 Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zokhudza chikhulupiriro zimene tingaphunzire pa nkhaniyi. Tikambirana (1) zimene Petulo anachita poyamba posonyeza kuti ankakhulupirira zoti Mulungu amuthandiza, (2) zimene zinachititsa kuti chikhulupiriro cha Petulo chiyambe kuchepa, ndiponso (3) zimene zinamuthandiza kuti alimbitsenso chikhulupiriro chake. Kukambirana mfundozi kungatithandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.—1 Akor. 16:13.
TIZIKHULUPIRIRA KUTI MULUNGU AZITITHANDIZA
3. N’chiyani chinathandiza Petulo kutsika m’ngalawa, nanga ife tikufanana naye bwanji?
3 Petulo anali ndi chikhulupiriro cholimba ndipo Yesu atamuitana anatsika m’ngalawa n’kuyamba kuyenda panyanja koma osamira. Iye ankakhulupirira kuti Mulungu amuthandiza kuyenda pamadzi ngati mmene anathandizira Yesu. Ifenso tingati Yesu anatiitana kuti tikhale otsatira ake. Choncho tinadzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. Tinachita zimenezi chifukwa chokhulupirira kuti Yesu ndiponso Mulungu azitithandiza m’njira zosiyanasiyana.—Yoh. 14:11; werengani 1 Petulo 2:21.
4, 5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri?
4 Chikhulupiriro n’chofunika kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti chinathandiza Petulo kuyenda panyanja ndipo chingatithandizenso kuchita zinthu zimene zingaoneke kuti n’zosatheka. (Mat. 21:21, 22) Mwachitsanzo, enafe tinasintha kwambiri makhalidwe athu moti anthu amene ankatidziwa kale amadabwa kwambiri. Yehova anatithandiza kusintha chifukwa chakuti tinasonyeza kuti timamukhulupirira. (Werengani Akolose 3:5-10.) Chikhulupiriro chinatithandizanso kuti tidzipereke kwa Mulungu n’kukhala anzake. Sitikanatha kuchita zimenezi patokha.—Aef. 2:8.
5 Chikhulupiriro n’chofunikabe masiku ano. Mwachitsanzo, chimatithandiza kupewa misampha ya Mdyerekezi yemwe ndi mdani wathu wamphamvu. (Aef. 6:16) Chimatithandizanso kuti tisamade nkhawa kwambiri tikakumana ndi mavuto. Yehova amanena kuti tikakhala ndi chikhulupiriro n’kumaika patsogolo Ufumu wake, iye adzatipatsa zinthu zina zofunika pa moyo. (Mat. 6:30-34) Tikakhalanso ndi chikhulupiriro tidzapeza moyo wosatha ndipo imeneyi ndi mphatso yamtengo wapatali yomwe sitingaipeze patokha.—Yoh. 3:16.
TISALOLE KUTI CHIKHULUPIRIRO CHATHU CHICHEPE
6, 7. (a) Kodi mphepo ndi mafunde tingaziyerekezere ndi chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala pa nkhani ya chikhulupiriro chathu?
6 Petulo anayenda pang’ono koma kenako anayamba kuchita mantha chifukwa cha mphepo ndi mafunde. Mavuto amene timakumana nawo potumikira Yehova tingawayerekezerenso ndi mphepo kapena mafunde. Koma kaya mavutowo akule bwanji, Yehova akhoza kutithandiza kupirira. Kumbukirani kuti Petulo sanamire chifukwa chogwetsedwa ndi mphepo kapena mafunde. Tikutero chifukwa chakuti nkhaniyi imati: “Ataona mphepo yamkuntho, anachita mantha.” (Mat. 14:30) Chikhulupiriro cha Petulo chinayamba kuchepa atasiya kuyang’ana Yesu. Ifenso chikhulupiriro chathu chingachepe ngati titayamba kuganizira kwambiri mavuto athu. Tikhoza kuona kuti mavutowo ndi aakulu kwambiri n’kuyamba kukayikira zoti Yehova atithandiza.
7 Popeza kuti chikhulupiriro chathu chikhoza kuchepa, tiyenera kukhala osamala kwambiri. Paja Baibulo limanena kuti kuchepa kwa chikhulupiriro kuli ngati “tchimo limene limatikola mosavuta.” (Aheb. 12:1) Nkhani ya Petuloyi ikusonyeza kuti chikhulupiriro chathu chingachepe ngati titayamba kuganizira kwambiri zinthu zolakwika. Kodi tingadziwe bwanji ngati chikhulupiriro chathu chayamba kuchepa? Tiyeni tione mafunso amene angatithandize podzifufuza.
8. N’chiyani chingatichititse kusiya kukhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu?
8 Kodi ndasiya kukhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu? Mwachitsanzo, Mulungu walonjeza kuti adzawononga dziko loipali. Koma ngati tingatanganidwe ndi zosangalatsa za m’dzikoli, chikhulupiriro chathu chikhoza kuchepa ndipo tingayambe kukayikira zoti mapeto ali pafupi. (Hab. 2:3) Mulungu analonjezanso kuti azitikhululukira machimo athu pogwiritsa ntchito dipo. Koma tikamaganizira kwambiri zinthu zimene tinalakwitsa m’mbuyomu, tikhoza kuyamba kukayikira zoti Yehova ‘wafafaniza’ machimo athu. (Mac. 3:19) Izi zingachititse kuti tisiye kusangalala komanso kutumikira Mulungu mwakhama.
9. Kodi chingachitike n’chiyani ngati titayamba kuganizira kwambiri zofuna zathu?
9 Kodi ndimachitabe khama potumikira Mulungu? Mtumwi Paulo ananena kuti tikamachita khama potumikira Yehova ‘chiyembekezo chathu chimakhala chotsimikizika mpaka mapeto.’ Ndiyeno kodi chingachitike n’chiyani ngati tayamba kuganizira kwambiri zofuna zathu? Tiyerekeze kuti tayamba kugwira ntchito ya malipiro abwino koma imene ikutilepheretsa kuchita zinthu zina zokhudza kulambira. Kodi zotsatira zake zingakhale zotani? Izi zingachititse kuti chikhulupiriro chathu chichepe ndipo tingayambe ‘kuchita ulesi’ potumikira Mulungu.—Aheb. 6:10-12.
10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kukhululukira ena kumasonyeza kuti timakhulupirira Yehova?
10 Kodi ndimavutika kukhululukira anthu? Anthu ena akatikhumudwitsa ndiyeno ife n’kumaganizira kwambiri mmene tikumvera mumtima, tikhoza kuwakalipira kapena kusiya kuwalankhula. Koma tikawakhululukira timasonyeza kuti timakhulupirira kwambiri Yehova. Tikutero chifukwa chakuti munthu akatilakwira zili ngati ali nafe ngongole. Ifenso timakhala ndi ngongole kwa Yehova chifukwa cha machimo athu. (Luka 11:4) Choncho tikakhululukira munthu wina timasonyeza kuti timakhulupirira zoti Yehova adzatidalitsa ndipo timaona kuti kumusangalatsa n’kofunika kwambiri kuposa kubwezera munthuyo. Ophunzira a Yesu ankadziwa kuti kukhululukira ena kumafuna chikhulupiriro. Paja Yesu anawauza kuti azikhululukira anthu ngakhale amene awalakwira mobwerezabwereza. Ndiyeno iwo anamupempha kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.”—Luka 17:1-5.
11. N’chiyani chingatichititse kuvutika kulandira malangizo?
11 Kodi ndimavutika kulandira malangizo? Nthawi zina anthufe tikapatsidwa malangizo sitiganizira ubwino wake koma timayamba kupezera zifukwa malangizowo kapena amene akuwapereka. (Miy. 19:20) Mtima umenewu ungatilepheretse kuphunzira kuona zinthu mmene Yehova amazionera.
12. Kodi munthu akamakonda kudandaula za anthu amene Yehova akuwagwiritsa ntchito amasonyeza chiyani?
12 Kodi ndimadandaula za abale amene akutsogolera mumpingo? Aisiraeli ataganizira kwambiri zinthu zoipa zimene amuna 10 amene anakazonda dziko lolonjezedwa ananena, anayamba kutsutsa Mose ndi Aroni. Zimene Aisiraeli ankachitazi zinasonyeza kuti sankakhulupirira Mulungu amene anasankha Mose ndi Aroni kuti aziwatsogolera. Tikutero chifukwa chakuti Yehova anafunsa Mose kuti: “Kodi adzayamba liti kundikhulupirira?” (Num. 14:2-4, 11) Ifenso tikamakonda kudandaula za abale amene Yehova akuwagwiritsa ntchito, zimasonyeza kuti sitikhulupirira kwambiri Yehovayo.
13. N’chifukwa chiyani sitiyenera kutaya mtima ngati taona kuti chikhulupiriro chathu chayamba kuchepa?
13 Tisataye mtima ngati pambuyo podzifunsa mafunso amene ali m’ndime zapitazi, taona kuti chikhulupiriro chathu chayamba kuchepa. Tizikumbukira kuti nayenso mtumwi Petulo anachita mantha n’kuyamba kukayika. Nthawi zina Yesu ankadzudzulanso atumwi onse chifukwa chokhala ndi ‘chikhulupiriro chochepa.’ (Mat. 16:8) Phunziro lofunika pa nkhani ya Petuloyi ndi lokhudza zimene anachita pambuyo poti wayamba kumira chifukwa cha kuchepa kwa chikhulupiriro.
TIZITSATIRA YESU KUTI TILIMBITSE CHIKHULUPIRIRO
14, 15. (a) Kodi Petulo anachita chiyani atayamba kumira? (b) Popeza Yesu sitingamuone, kodi ‘tingamuyang’anitsitse’ bwanji?
14 Kodi Petulo anachita chiyani atayamba kumira? Iye ankadziwa kusambira koma sanadzidalire n’kuyesetsa kuti abwerere yekha mungalawayo. (Yoh. 21:7) M’malomwake anayang’ananso Yesu n’kulola kuti amuthandize. Tiyenera kutsatira chitsanzo cha Petulo tikaona kuti chikhulupiriro chathu chayamba kuchepa. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?
15 Mofanana ndi Petulo, ifenso tiyenera ‘kuyang’anitsitsa Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu, Yesu’ kuti atithandize. (Werengani Aheberi 12:2, 3.) N’zoona kuti sitingaone Yesu ngati mmene Petulo anachitira. Koma ‘timamuyang’anitsitsa’ tikamaphunzira ndiponso kutsatira zimene iye ankaphunzitsa ndi kuchita. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Tiyeni tsopano tikambirane zinthu zina zimene tingachite potsatira chitsanzo cha Yesu.
16. Kodi kuphunzira Baibulo kungalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu?
16 Tizikhulupirira kwambiri Baibulo. Yesu ankakhulupirira kwambiri kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu ndiponso kuti malangizo ake ndi othandiza. (Yoh. 17:17) Ifenso tiyenera kuwerenga Baibulo tsiku lililonse, kuliphunzira ndiponso kusinkhasinkha zimene taphunzirazo. Tiyeneranso kufufuza mozama m’Baibulo kuti tipeze mayankho a mafunso amene tingakhale nawo. Mwachitsanzo, tikhoza kuphunzira mwatsatanetsatane umboni wa m’Baibulo wakuti tikukhala m’masiku otsiriza. Kuchita zimenezi kungatithandize kukhulupirira kwambiri kuti mapeto ayandikira. Tikhozanso kuphunzira maulosi amene akwaniritsidwa kale n’cholinga choti tizikhulupirira kwambiri malonjezo amene adzakwaniritsidwe m’tsogolo. Kuwerenga za anthu amene anasintha moyo wawo ataphunzira za Yehova kungatithandizenso kukhulupirira zoti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza kwambiri.a—1 Ates. 2:13.
17. (a) N’chiyani chinathandiza Yesu kupirira mavuto aakulu? (b) Nanga ife tingamutsanzire bwanji?
17 Tiziganizira kwambiri malonjezo a Yehova. Yesu anatha kupirira mavuto aakulu chifukwa ankaganizira zinthu zabwino zimene ankayembekezera. (Aheb. 12:2) Iye sankasokonezedwa ndi zinthu za m’dzikoli. (Mat. 4:8-10) Tingatsanzire Yesu tikamaganizira zinthu zabwino zimene Yehova watilonjeza. Kulemba kapena kujambula zimene tikufuna kudzachita m’dziko latsopano kungatithandize kwambiri. Tingalembenso mayina a anthu amene tikufunitsitsa kudzacheza nawo akadzaukitsidwa ndiponso zimene tikufuna kudzakambirana nawo. Aliyense ayenera kuona kuti zinthu zimene tikuyembekezera n’zimene Mulungu wamulonjeza iyeyo payekha osati gulu la anthu.
18. Kodi kupemphera kungatithandize bwanji kulimbitsa chikhulupiriro chathu?
18 Tizipemphera kuti tikhale ndi chikhulupiriro. Yesu anauza ophunzira ake kuti azipempha Yehova kuti awapatse mzimu woyera. (Luka 11:9, 13) Ifenso tikamapempha mzimu woyera tiyenera kupemphanso kuti tikhale ndi chikhulupiriro. Paja chikhulupiriro ndi khalidwe lina limene mzimu woyera umatulutsa. Tikamapemphera tiyenera kutchula vuto lenileni limene likusonyeza kuti chikhulupiriro chathu n’chochepa. Mwachitsanzo, ngati timavutika kukhululukira ena tingapemphe Yehova kulimbitsa chikhulupiriro chathu kuti tizitha kuchita zimenezi.
19. Kodi tiyenera kusankha anthu otani kuti akhale anzathu?
19 Tizicheza ndi anthu okhulupirika. Yesu ankasankha mwanzeru anthu ocheza nawo, makamaka anzake apamtima. Anthu amene anasankha kuti akhale atumwi ake ankamumvera mokhulupirika. (Werengani Yohane 15:14, 15.) Ifenso tizisankha anzathu amene ali ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso amene amamvera Yesu. Tizikumbukiranso kuti anzathu abwino ndi amene timalankhulana nawo moona mtima ngakhale pamene tikupatsana malangizo.—Miy. 27:9.
20. Kodi kuthandiza ena kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kumatithandizanso bwanji?
20 Tizithandiza ena kukhala ndi chikhulupiriro. Zimene Yesu ankalankhula ndiponso kuchita zinkalimbitsa chikhulupiriro cha ophunzira ake. (Maliko 11:20-24) Nafenso tizilimbitsa chikhulupiriro cha anthu ena chifukwa tikamatero timalimbitsanso chikhulupiriro chathu. (Miy. 11:25) Tikamaphunzitsa anthu tiziwauza umboni wakuti kuli Mulungu ndiponso kuti amatikonda. Tiziwathandiza kudziwa kuti Baibulo ndi Mawu ake. Tizithandizanso abale ndi alongo athu kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Mwachitsanzo, ngati taona kuti ena akudandaula za abale amene akutsogolera mumpingo, si bwino kufulumira kuwapewa. Koma tiziyesetsa kuwathandiza n’kulimbitsa chikhulupiriro chawo. (Yuda 22, 23) Kapena ngati muli kusukulu ndipo anthu akukambirana nkhani yosemphana ndi zimene mumakhulupirira, muzifotokoza molimba mtima zimene Baibulo limanena. Izi zikhoza kuthandiza anzanuwo kuchita chidwi ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.
21. Kodi Yehova walonjeza kuchita chiyani?
21 Mulungu ndiponso Yesu anathandiza Petulo kuti asiye kuchita mantha komanso kukayikira. Ndiyeno iye anadzakhala ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri ndipo ankalimbikitsa Akhristu anzake. Yehova amatithandizanso kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Werengani 1 Petulo 5:9, 10.) Choncho tikamachita khama kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu tidzadalitsidwa kwambiri.
a Mwachitsanzo, tingawerenge nkhani za mutu wakuti, “Baibulo Limasintha Anthu” m’magazini ogawira a Nsanja ya Olonda.