MUTU 56
Kodi Chimaipitsa Munthu N’chiyani?
MATEYU 15:1-20 MALIKO 7:1-23 YOHANE 7:1
YESU ANATCHULA MIYAMBO YOIPA IMENE ANTHU ANKATSATIRA
Pamene mwambo wa Pasika wa mu 32 C.E. unkayandikira, Yesu anali akuphunzitsa ku Galileya. Potsatira Chilamulo cha Mulungu, Yesu ananyamuka n’kulowera ku Yerusalemu kuti akachite nawo mwambo wa Pasika. Pa ulendowu, Yesu anachita zinthu mosamala kwambiri chifukwa Ayuda ankafuna kumupha. (Yohane 7:1) Mwambowu utatha anabwereranso ku Galileya.
Zikuoneka kuti Yesu anali ku Kaperenao pamene anakumana ndi Afarisi ndi alembi omwe anachokera ku Yerusalemu. N’chifukwa chiyani Afarisiwa anapanga ulendowu? Ankafuna kupezera Yesu zifukwa kuti amuimbe mlandu wosokoneza chipembedzo. Iwo anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya miyambo ya makolo? Mwachitsanzo, sasamba m’manja akafuna kudya chakudya.” (Mateyu 15:2) Mulungu sanauze anthu ake kuti azitsatira mwambo umenewu woti azisamba “m’manja mpaka m’zigongono.” (Maliko 7:3) Koma Afarisi ankaona kuti ngati munthu sanachite zimenezi ndiye kuti wapalamula mlandu waukulu.
M’malo moyankha mlandu umene ankamuimbawo, Yesu anawasonyeza mmene iwowo ankaphwanyira Malamulo a Mulungu mwadala. Anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani inunso mumaphwanya malamulo a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu? Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’ Komanso anati, ‘Aliyense wonenera bambo ake kapena mayi ake zachipongwe afe ndithu.’ Koma inu mumanena kuti, ‘Aliyense wouza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ine ndili nacho, chimene ndikanakuthandizirani, ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,” asalemekeze bambo ake.’”—Mateyu 15:3-6; Ekisodo 20:12; 21:17.
Afarisiwo ankanena kuti ndalama, katundu kapena chilichonse chomwe munthu wasankha kuti adzapereke kwa Mulungu monga mphatso, chinkayenera kugwiritsidwa ntchito pakachisi moti sankafunika kusintha kuti achigwiritse ntchito pa zinthu zina. Koma zomwe zinkachitika n’zakuti munthu ankasungabe mphatsoyo. Mwachitsanzo, munthu ankanena kuti ndalama kapena katundu wake ndi “khobani,” kutanthauza mphatso imene adzaipereke kwa Mulungu kapena kukachisi, ngati kuti zinthuzo zili kale m’manja mwa kachisi. Ngakhale kuti munthuyo ankagwiritsa ntchito ndalama kapena katunduyo pa zofuna zake, ankakana kugwiritsa ntchito zinthu zomwezo pothandizira makolo ake okalamba komanso osauka. Pochita zimenezi ankathawa udindo wosamalira makolo ake.—Maliko 7:11.
Yesu anakwiya kuti Afarisi ankapotoza Chilamulo cha Mulungu ndipo anati: “Mwasandutsa mawu a Mulungu kukhala opanda pake chifukwa cha miyambo yanu. Onyenga inu! Yesaya analosera moyenera za inu muja anati, ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mtima wawo uli kutali ndi ine. Amandipembedza pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.’” Afarisiwo anasowa chonena atawadzudzula mwamphamvu. Ndiyeno Yesu anauza gulu la anthu kuti limuyandikire n’kunena kuti: “Mvetserani ndipo muzindikire tanthauzo lake: Chimene chimalowa m’kamwa sichiipitsa munthu, koma chotuluka m’kamwa mwake n’chimene chimaipitsa munthu.”—Mateyu 15:6-11; Yesaya 29:13.
Kenako Yesu anapita kunyumba ina ndipo ali kumeneko ophunzira ake anamufunsa kuti: “Kodi mukudziwa kuti Afarisi akhumudwa ndi zimene mwanena zija?” Iye anawayankha kuti: “Mbewu iliyonse imene sinabzalidwe ndi Atate wanga wakumwamba idzazulidwa. Alekeni amenewo. Iwo ndi atsogoleri akhungu. Chotero ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera m’dzenje.”—Mateyu 15:12-14.
Yesu anadabwa kumva Petulo akufuna kudziwa chimene chimaipitsa munthu. Petulo ankafunsa zimenezi m’malo mwa ophunzirawo. Yesu anamuyankha kuti: “Inunso simudziwa kodi kuti chilichonse cholowa m’kamwa chimadutsa m’matumbo ndipo chimakatayidwa kuchimbudzi? Koma zotuluka m’kamwa zimachokera mumtima, ndipo zimenezo zimaipitsa munthu. Mwachitsanzo, maganizo oipa, za kupha anthu, za chigololo, za dama, za kuba, maumboni onama, ndi zonyoza Mulungu, zimachokera mumtima. Izi n’zimene zimaipitsa munthu, koma kudya chakudya osasamba m’manja sikuipitsa munthu.”—Mateyu 15:17-20.
Sikuti Yesu ankaletsa anthu kukhala aukhondo kapena ankawaletsa kuti asamasambe m’manja asanayambe kukonza kapena kudya chakudya. M’malomwake ankadzudzula atsogolera achipembedzo omwe ankachita zinthu mwachinyengo pophwanya malamulo olungama a Mulungu n’kumatsatira miyambo ya anthu. Choncho mfundo ya Yesu inali yakuti zinthu zoipa zimene munthu amachita, zomwe zimayambira mumtima, ndi zimene zimaipitsa munthu.