Miyambo ya Chipembedzo ndi Baibulo
“MUYESA achabe mawu a Mulungu mwa mwambo wanu.” Awa anali mawu osati a wina aliyense koma Yesu Kristu. (Marko 7:13) Mofanana ndi anthu ambiri lerolino, Ayuda m’tsiku la Yesu anamamatira mokhulupirika ku dongosolo locholowanacholowana la malingaliro ndi miyambo. Ndipo mofanana ndi atsogoleri ambiri a chipembedzo lerolino, atsogoleri awo achipembedzo amawona miyambo imeneyi kukhala yofunika kwambiri kuposa Baibulo.
Kuti tichitire chitsanzo: Mawu a Mulungu mwachindunji analamulira kuti ana alemekeze makolo awo. (Eksodo 20:12) Ichi mwachidziŵikire chinaphatikizapo kuthandiza makolo omwe anagwera m’kusowa kwakukulu kwa zachuma. Ngakhale kuli tero, mwambo wa Chiyuda unakulitsidwa womwe unapereka njira yoyenerera ya kuwukira thayo la Baibulo limeneli. Munthu wadyera anayenera kokha kulumbira kuti katundu wake wa iyemwini akayenera kuperekedwa ku kachisi pambuyo pake, akumaika katunduyo pambali mwa kunena kuti iye ali “korban.” Liwu limeneli linatanthauza “mphatso yoperekedwa kwa Mulungu.” Ngakhale kuti wolambira Wachiyuda anali mwachiwonekere waufulu kupitiriza kugwiritsira ntchito korban ameneyu kaamba ka phindu lake laumwini, iye mwachinyengo akaikaniza iyo kwa makolo ake.—Marko 7:9-12.
Yesu, ngakhale ndi tero, anatokosa ichi ndi ‘miyambo yopatulika’ ina ya Chiyuda, akumanena kuti: “Onyenga inu, koma Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, ‘Anthu awa andilemekeza ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo iri kutali ndi ine. Koma andilambira ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso ndi malangizo a anthu.’”—Mateyu 15:3-9.
M’chiyang’aniro cha chimene Yesu ananena, kodi Mkristu ndithudi angalingalire mwambo uliwonse wa chipembedzo kukhala wogwirizana ndi Baibulo? Kutalitali. Mosasamala kanthu ndi kukomeza kapena kulingalira kokulira komwe kungagwirizane ndi mwambowo, chodera nkhaŵa cha Mkristu chikakhala kuwona kaya ngati iwo umagwirizana ndi Mawu a Mulungu kapena ayi. Monga nkhani ya m’nsongayi, lingalirani machitidwe ena a mwambo a chipembedzo olongosoledwa m’bukhu la Chikatolika Liturgy—an Elementary Course, lolembedwa ndi María A. Lombillo Clark, T.D. Ndimotani mmene miyambo imeneyi imafananirani ndi chimene Baibulo kwenikweni limanena?
[Bokosi]
LITURGY MAWU A MULUNGU
“Timasonyeza kulambira kwathu “Tiana, dzisungireni nokha
kwa Mulungu kupyolera mu kupewa mafano.”—1 Yohane 5:21.
machitidwe a chipembedzo.” “Mulungu ndiye Mzimu, ndipo
omulambira iye ayenera
kumulambira iye mu mzimu ndi
m’chowonadi.”—Yohane 4:24.
“Pakuti tiyenda
mwachikhulupiriro, si mwa
ciwonekedwe.”—2 Akorinto 5:7.
“Ine ndine Yehova. Dzina langa
ndi lomweli; ndipo ulemerero
wanga sindidzapereka kwa wina,
ngakhale kunditamanda kwa
mafano osemedwa.”—Yesaya 42:8.
“Tiyenera kupereka machitidwe “Usadzipangire iwe wekha fano
a chipembedzo kwa Namwali losema kapena chifaniziro
Wopatulikitsa Mariya, kwa chirichonse cha zinthu za
angelo, ndi kwa oyera. Koma mthambo la kumwamba kapena
machitidwe a chipembedzo za m’dziko lapansi . . .
[oterowo] a kulemekeza . . . Usazipembedzere izo
potsirizira pake amabwera kwa usazitumikire izo.”—Eksodo
Mulungu, m’njira yofananayo 20:4, 5.
monga mmene mfumu “Ine Yohane . . . ndinagwa
imalemekezedwera pamene ulemu pansi kulambira pa mapazi
waperekedwa kwa nduna zake.” a mngelo . . . Ndipo ananena
ndi ine: ‘Tapenya! Usachite
[tero, NW]! . . . Lambira
Mulungu.’”—Chivumbulutso
22:8, 9.
“Pali Mulungu mmodzi, ndi
m’tetezi mmodzi pakati pa
Mulungu ndi anthu, ndiye
munthu, Kristu Yesu.”
“Mtanda uli wosasiyika “Mulungu amene analenga
pa guwa la nsembe; popanda dziko lapansi ndi zomwe
iwo Misa Yopatulika ziri momwemo, Iyeyo, ndiye
singasangalalidwe. Nsalu [Mbuye wa, NW] kumwamba ndi
zitatu za pa guwa la nsembe, dziko lapansi, sakhala
zoimikapo makandulo ziŵiri, m’nyumba za kachisi
ndi magome opatulika alinso zomangidwa ndi manja.”
ofunikira.” —Machitidwe 17:24.
“Sitipenyerera zinthu zowoneka,
koma zinthu zosawoneka.”
“November 1 . . . “Akufa salemekeza [Ya],
chikondwerero cha Tsiku la kapena yense wakutsikira kuli
Oyera Onse. Liri Tsiku chete.”—Salmo 115:17.
Lopatulika la miyoyo yonse “Akufa sadziŵa kanthu.”
yomwe imakhala yachimwemwe —Mlaliki 9:5, Revised Standard
kumwamba, ndi kuti tsiku Version Common Bible.
limodzi lidzakhala lathu.” “Moyo uliwonse wosamva mneneri
ameneyo udzawonongedwa.”
—Machitidwe 3:23, Douay Version.
“M’kuthandiza miyoyo imeneyi “Kulibe ntchito, kapena
[Tchalitchi] chinakhazikitsa kulingalira, kapena nzeru,
‘Chikumbukiro cha akufa kapena chidziŵitso, chomwe
okhulupirika’ pa November 2. chidzakhalako mu helo,
Pa tsiku limeneli ansembe kumene iwe ukufulumiza kupita.”
amakondwerera Misa nthaŵi —Mlaliki 9:10, Douay Version.
zitatu kuchepetsako zizunzo “Musaike chikhulupiriro chanu
za miyoyo yodalitsidwa imeneyi mwa [munthu;] . . . iye
ya purigatoriyo ndi kufulumiza adzabwerera ku dziko lake:
kulowa kwawo kumwamba.” tsiku lomwelo malingaliro awo
“M’kundandalitsa komalizira, adzatha.”—Salmo 145:2-4,
chiphunzitso cha Chikatolika Douay Version.
pa purigatoriyo chiri
chozikidwa pa mwambo, osati
Malemba Opatulika.”
New Catholic Encyclopedia,
Volyumu 11, tsamba 1034.
Kuwomboledwa Kuchokera ku Miyambo Yovulaza
Miyambo yambiri ya chipembedzo yofala iri chotero yosasangalatsa kwa Mulungu ndipo chotero iri yovulaza. Mosangalatsa, ngakhale ndi tero, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndipo ndikutamandani kuti m’zinthu zonse . . . musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.” (1 Akorinto 11:2) Miyambo imeneyi, ngakhale kuli tero, inali yabwino, machitachita opindulitsa ozikidwa pa Mawu a Mulungu—osati miyambo yopanda pake, yopangidwa ndi anthu. Iyo inalowa m’malo “makhalidwe achabe kuchokera kwa makolo” amene ambiri m’zana loyamba anachita asanakhale Akristu.—1 Petro 1:18.
Mofananamo lerolino, munthu wowopa Mulungu ayenera kusanthula mosamalitsa ndi kukana mwambo uliwonse womwe umatsimikizira kukhala wosakhala wa m’malemba. Ndithudi, unansi wa wina ndi Mulungu uli wa mtengo kwambiri koposa mtundu uliwonse wopangidwa ndi anthu wa kulambira! Ndithudi, kukana miyambo yosakhala ya m’malemba sikuli mwa njira iri yonse kopepuka. Iko kaŵirikaŵiri kumafunikira kusintha zikhoterero zamakhalidwe zokhazikitsidwa kwa nthaŵi yaitali. Mwamuna mmodzi wachichepere mu Colombia, mwachitsanzo, anamizidwa m’miyambo ya chipembedzo. Kuyambira ku ubwana iye anali ndi chikhumbo cha kukhala wansembe Wachikatolika. Iye kaŵirikaŵiri anali kuseŵera pa ‘akunena za Misa’ ndi alongo ake, ngakhale kulandira “kulapa” kuchokera kwa iwo. Zaka zingapo pambuyo pake iye anapeza chilolezo cha kulowa ku sukulu yotsogolera ku maphunziro a chipembedzo, potsirizira pake akumalembetsa ku yuniversite ya Chikatolika. Kumeneko, miyambo ya chipembedzo inamangiriridwa mozama m’moyo wake.
Tsiku lina, mmodzi wa Mboni za Yehova anachezera kunyumba kwake. Pamene makolo ake sakanalola Mboniyo kudzilongosolera, zochepera zomwe zinanenedwazo zinasangalatsa wachichepere wa malingaliro a chipembedzo ameneyu. Pambuyo pake iye anakonza kaamba ka kuphunzira Baibulo mwachinsinsi ndi Mboni imeneyi. “Chikhumbo changa chowona mtima,” iye akukumbukira tero, “chinali kufikira pa kudziŵa Baibulo kuchokera ku kawonedwe kosiyana popanda kusintha chipembedzo changa. Ndinali ndi chikhumbo champhamvu cha kutumikira Mulungu monga wansembe, kuyesera kupangitsa masinthidwe m’mitima ya anthu. Pambuyo pophunzira Baibulo kwa mwezi umodzi, kuwombana kunabuka mkati mwanga, mongadi mmene miyambo ndi machitachita ofala a chipembedzo changa anamenyana molimbana ndi miyezo yoyera ya Malemba.”
Banja lake linamudidikiza iye kuleka kuphunzira Baibulo, ndipo potsirizira pake iye anakakamizidwa kuchoka panyumba. Mosasamala kanthu za chimenecho, iye akunena kuti: “Pambuyo pa miyezi iŵiri ya kuphunzira Baibulo, ndinakhala wokhutiritsidwa kuti ndinali m’cholakwa chachikulu, ndipo ndinasiya yuniversite ndi ntchito yanga monga mphunzitsi mu koleji ya chipembedzo ndi kudzipereka ine mwini ku kulalikira kuchokera kunyumba ndi nyumba. Tsopano moyo wanga wasintha ndipo yateronso miyambo yanga. Ndinadzimva wachimwemwe mwapadera tsiku losaiwalika limenelo limene ndinachitira chithunzi kudzipereka kwanga kwa Yehova mu ubatizo.” Mwamuna wachichepere ameneyu tsopano akutumikira kwa nthaŵi zonse m’kuthandiza ena kudzimasula iwo eni kuchokera ku miyambo yosalemekeza Mulungu.
Ngati inu muli wodzipereka wokangalika wa miyambo ya chipembedzo, mungachipezenso icho kukhala choyenera kupanga masinthidwe ena. Kumbukiraninso chimene Yesu ananena ndi mkazi wa Chisamariya pa chitsime. Iye ndi anthu ake anali ndi mwambo wolemekezedwa kwa nthaŵi yaitali wa kulambira Mulungu pa Phiri la Gerizimu. Yesu, ngakhale kuli tero, anamusonyeza iye kuti uwu unali mwambo wopanda pake, akumanena kuti: “Tamvera ine, mkazi iwe kuti, Ikudza nthaŵi imene simudzalambira Atate kapena mu phiri iri kapena m’Yerusalemu. . . . Olambira owona adzalambira Atate mu mzimu ndi m’chowonadi, pakuti, Atate afuna otere akhale olambira ake.”—Yohane 4:19-23.
Kodi inu muli mmodzi amene “Atate afuna”? Kodi muli ndi chikhumbo chotentha cha kulambira Mulungu m’chowonadi? Choktero chenjezo la mtumwi Paulo pa Akolose 2:8 liri loyenerera koposa: “Samalirani kuti wina aliyense asakunyengeni inu ndi nthanthi zake, ndi malingaliro achabe otengedwa kuchokera ku miyambo ya umunthu.” (The Holy Bible, Ronald A. Knox) Tsatirani, m’malomwake, ziphunzitso za Chikristu chowona, zomwe zingakutsogozeni ku moyo wosatha!—Yohane 17:3.