Mmene Akristu Amachitira ndi CHitonzo Chofalitsidwa
KODI mumamva bwanji pamene munthu wina akutonzani kapena kufalitsa mabodza onena za inu? Mwachibadwa zimenezi zimakupwetekani kwambiri. Mboni za Yehova zimamva chimodzimodzi pamene zinenezedwa monama kapena moipa m’nkhani zofalitsidwa. Koma monga momwe Yesu ananenera pa Mateyu 5:11, 12, izo zimakhalabe ndi chifukwa chokhalira zachimwemwe.
Mwachitsanzo, chofalitsa china Chachikatolika ku Germany chinanena kuti “Mboni iliyonse imafunikira kupereka pakati pa 17 ndi 28 peresenti ya malipiro ake ku malikulu a chipembedzo cha mpatukocho.” Komabe, Mboni za Yehova sizili mpatuko, ndipo ntchito yawo imalipiriridwa ndi zopereka zaufulu zokha. Aŵerengi ambiri anasochezedwa ndi bodza limeneli, ndipo Mboni za Yehova zimamvera chisoni oterowo. Koma kodi Akristu oona ayenera kuchita motani ndi chitonzo cha m’nkhani zofalitsidwa?
Chitsanzo Chimene Akristu Ayenera Kulondola
Mateyu chaputala 23 amafotokoza bwino lomwe mmene Yesu anadzudzulira omtsutsa achipembedzo kaamba ka chinyengo chawo ndi kusaona mtima. Kodi zimenezi zimapereka chitsanzo kwa Akristu lerolino cha mmene ayenera kuchitira ndi osuliza? Osati kwenikweni. Mwana wa Mulungu anadzudzula omtsutsa achipembedzo mwa ulamuliro wake wapadera ndi chidziŵitso chimene anali nacho, akumatero kaamba ka phindu la makamu omwe anali kumvetserawo.
Mateyu 15:1-11 amasimba kuti Yesu anatsutsidwa chifukwa chakuti ophunzira ake ananenedwa kuti analumpha mwambo wa Chiyuda. Kodi Yesu anachita motani? Anachirimika. Nthaŵi zina, Yesu anakangana mosapita m’mbali ndi omsuliza, akumatsutsa malingaliro awo olakwa. Kunena mwa chisawawa, Akristu lerolino sali olakwa pamene amayesa kuwongolera malingaliro olakwa onena za ntchito yawo kapena ziphunzitso, akumayesa kumveketsa bwino mkhalidwe mwa njira yolongosola zenizeni ndi ya nzeru. Iwo amachita zimenezi kuti athandize anthu oona mtima kuzindikira kuti chisulizo choikidwa pa Mboni za Yehova nchopanda maziko ndipo ndicho kuipitsa dzina.
Koma onani mmene Yesu anayankhira pambuyo pake pamene ophunzira ake anamfunsa kuti: “Mudziŵa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva chonenacho?” Afarisi ameneŵa “anakhumudwa”—iwo sanangokwiya chabe koma anakhala otsutsa osawongolereka amene Yesu anawakana. Chifukwa chake iye anayankha kuti: “Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu.” Kupitiriza kukambitsirana ndi otsutsa audani amenewo kunali kosaphula kanthu, kosaphindulitsa aliyense, ndipo kukanangochititsa mkangano wopanda pake. (Mateyu 7:6; 15:12-14; yerekezerani ndi 27:11-14.) Mayankho amene Yesu anapereka anasonyeza kuti pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi ya kulankhula.”—Mlaliki 3:7.
Mboni za Yehova sizimaganiza kuti munthu aliyense adzalankhula zabwino ponena za izo. Zimakumbukira mawu a Yesu: “Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo awo anawatero momwemo aneneri onama.” (Luka 6:26) C. T. Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, anafunsidwa nthaŵi ina kuti nchifukwa ninji sanayankhe pamene anatonzedwa. Iye anayankha kuti: “Ngati uima kuti ukanthe galu aliyense amene auŵa iwe, sufika patali.”
Chotero sitiyenera kulola mawu okambidwa ndi otsutsa ouma khosi kutidodometsa pa utumiki wathu kwa Mulungu. (Salmo 119:69) Tiyeni tisumike maganizo pa ntchito ya Akristu oona, ija yolalikira. Mwachibadwa, chotulukapo nchakuti tidzakhala ndi mipata ya kuyankha mafunso ndi kufotokoza cholinga cha ntchito yathu, monga kukulitsa makhalidwe abwino a munthu ndi kumphunzitsa Mawu a Mulungu.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Kodi Muyenera Kuyankha Mawu Osuliza?
Yesu anati za otsatira ake: “Simuli a dziko lapansi . . . chifukwa cha ichi likudani inu.” (Yohane 15:19) Malipoti ambiri a nkhani zofalitsidwa amene amaunjika chitonzo pa Mboni za Yehova ali chisonyezero cha udani umenewu, ndipo ayenera kunyalanyazidwa. Komabe, ofalitsa nkhani nthaŵi zina anganene zimene zimasonyeza kuti samazindikira bwino za Mboni kapena zimene zimapotoza mfundo zina kapena kuzinena molakwa. Atolankhani ena angalembe nkhani yotengedwa kwa anthu osinjirira. Kaya tiyenera kunyalanyaza nkhani zonama zofalitsidwa kapena kuchinjiriza choonadi mwa kutsatira njira yoyenera zimadalira pa mikhalidwe, pa wosonkhezera kusulizako, ndi pa cholinga chake.
Nthaŵi zina mfundozo zingawongoleredwe ndi kalata yolembedwa bwino kwa mkonzi ngati kuti kalatayo ifalitsidwa yonse. Koma kalata yoteroyo ikhozanso kuputa zosiyana ndi zimene tikufuna. Motani? Bodza loyamba lija lingangofalitsidwa mowonjezereka, kapena otsutsawo angapatsidwe mwaŵi wina wofalitsa mabodzawo kapena kusinjirira kwawo. Kaŵirikaŵiri, kumakhala kwanzeru kusiya nkhani ya kulemba kalata kwa mkonzi m’manja mwa akulu oloŵetsedwamo. Ngati lipoti loipa lofalitsidwa libutsa malingaliro olakwa, ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ingadziŵitse mipingo m’dzikolo zifukwa zenizeni, kotero kuti ofalitsa akhale okhoza kupereka mafotokozedwe okhutiritsa kwa ofunsa.
Kodi inu panokha muyenera kudziloŵetsa nkomwe m’zinenezo zopotoka zoterozo? Uphungu wa Yesu wakuti “kawalekeni iwo,” kuwanyalanyaza, umagwira ntchito moonekeratu kwa adani otere. Akristu okhulupirika ali ndi zifukwa za Baibulo zopeŵera ampatuko ndi malingaliro awo. (1 Akorinto 5:11-13; Tito 3:10, 11; 1 Yohane 2:19; 2 Yohane 10, 11) Ngati munthu wina akufuna kudziŵadi ngati kuti kusulizidwa kwa Mboniko nkoona kapena konama, chidziŵitso chanu chokhala ndi maziko abwino chimakhala chokwanira kupereka yankho.—Onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 1986, masamba 10 ndi 11.
Ngati mupeza nkhani yonama yofalitsidwa, kumbukirani uphungu wa pa Miyambo 14:15: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” Ku Switzerland anthu ambiri anakwiya pamene lipoti lovutitsa maganizo lofalitsidwa m’nyuzipepala linanena kuti Mboni ina yachitsikana inamwalira chifukwa chakuti achibale ake anakana kulola madokotala kumuika mwazi. Komabe kodi zimenezo ndizo zinali zifukwa zoona? Iyayi. Wodwalayo anakana kuthiridwa mwazi pa zifukwa za chipembedzo, koma anavomera machiritso ena osaphatikizapo mwazi. Zimenezi zikanachitidwa popanda zovuta ndipo mwina zikanapulumutsa moyo wake. Komabe, chipatala chinachedwetsa zinthu mosafunikira moti kunakhala kuchedwa. Lipoti lofalitsidwalo silinatchule mfundo zimenezi.
Chifukwa chake, pendani mosamalitsa kuona kuti malipotiwo ali oona motani. Tingafotokoze kwa ofunsa kuti akulu a kumaloko amasamalira nkhani zoterozo m’njira yachikondi ndipo mogwirizana ndi malangizo a Baibulo. Kutsatira malangizo pamene tikuyankha kumatiletsa kugamula mofulumira.—Miyambo 18:13.
Nkhani Yodzimverera Ndiyo Yofunika
M’zaka za zana loyamba, anthu anafalitsa mabodza onena za Yesu Kristu kuti amuipitse dzina, ndipo ena anamneneza kukhala woukira boma. (Luka 7:34; 23:2; yerekezerani ndi Mateyu 22:21.) Pambuyo pake, mpingo Wachikristu wanthete umenewo unayang’anizana ndi chitsutso chofalikira kwambiri cha achipembedzo ndi akunja. Popeza kuti “Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi,” ambiri anaona atumiki ake kukhala apansi. (1 Akorinto 1:22-29) Akristu oona lerolino ayenera kudziŵa kuti adzayang’anizana ndi chitonzo, chimene chili mtundu wina wa chizunzo.—Yohane 15:20.
Komabe, Mboni za Yehova zimayamikira ngati kuti munthu amene zikambitsirana naye ali wa maganizo abwino ndipo asonyeza mkhalidwe wofanana ndi wa ena a alendo a Paulo ku Roma, amene ananena kuti: “Tifuna kumva mutiuze muganiza chiyani; pakuti za mpatuko uwu, tidziŵa kuti aunenera ponseponse.”—Machitidwe 28:22.
Fotokozani zifukwa kwa anthu ouzidwa zonama, mukumatero ndi chifatso. (Aroma 12:14; yerekezerani ndi 2 Timoteo 2:25.) Apempheni kudzimverera okha zenizeni ponena za Mboni za Yehova, zimene zidzawakhozetsa kuona chinyengo cha zinenezo zonama. Mungagwiritsirenso ntchito malongosoledwe atsatanetsatane ofalitsidwa ndi Watch Tower Society onena za gululo, mbiri yake, ndi ziphunzitso zake.a Panthaŵi ina Filipo anayankha Nataniyeli mwa kungonena kuti: “Tiye ukaone.” (Yohane 1:46) Tingachite chimodzimodzi. Aliyense wofuna angafike pa Nyumba Yaufumu kuti adzionere yekha mtundu wa anthu amene Mboni za Yehova zili ndi zimene zimakhulupirira.
Musawopsezedwe ndi Otsutsa
Ndi kolimbikitsa chotani nanga kudziŵa kuti chitonzo sichimaletsa anthu kukhala Mboni! Pa programu ya kufunsa ya pa TV mu Germany, ampatuko ananena mabodza ambiri onena za Mboni. Wopenyerera wina anazindikira kuti kudzikometsera kwampatuko kumeneko kunali maloto okhaokha ndipo anasonkhezereka kuyambanso kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Inde, chitonzo chofalitsidwa nthaŵi zina chingakhale ndi zotulukapo zabwino!—Yerekezerani ndi Afilipi 1:12, 13.
Mtumwi Paulo anadziŵa kuti ena akasamalira kwambiri “nthano zachabe” m’malo mwa choonadi. Motero analemba kuti: “Khala maso m’zonse, imva zoŵaŵa, chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.” (2 Timoteo 4:3-5) Chotero musalole kuti akuchenjenekeni, ndipo ‘musawopsedwe konse’ ndi adani anu. (Afilipi 1:28) Khalani woleza mtima ndi wosatekeseka, nimulalikire uthenga wabwino mwa chisangalalo, ndipo mudzachirimika pa chitonzo chofalitsidwa. Inde, kumbukirani lonjezo la Yesu: “Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu m’Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.”—Mateyu 5:11, 12.
[Mawu a M’munsi]
a Onani zofalitsa zakuti Mboni za Yehova—Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi, Mboni za Yehova m’Zaka za Zana la Makumi Aŵiri, ndi Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom.
[Mawu Otsindika patsamba 27]
Poyang’anizana ndi otsutsa, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Kawalekeni iwo.” Kodi anatanthauzanji?
[Mawu Otsindika patsamba 29]
“Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha ine.”—Mateyu 5:11