“Chizindikiro cha Kumwamba”
NYIMBO yakale imati: “Kukakhala mtambo wofiira usiku, amalinyero amasangalala kuti kudzacha bwino,/Kukakhala mtambo wofiira m’maŵa, amalinyero amadziŵa kuti sikudzacha bwino.” Lerolino, masatelaiti, maphunziro a zanyengo ochilikizidwa ndi makompyuta, chiŵiya chotchedwa Doppler radar, ndi njira zina zasayansi zimagwiritsiridwa ntchito kuneneratu za nyengo. Kaŵirikaŵiri kuloserako kumagwirizana ndi nyimbo yomwe yangogwidwa mawuyo.
Panthaŵi ina adani achipembedzo a Yesu Kristu anapempha kuti iye awapatse “chizindikiro cha kumwamba,” chisonyezero chachilendo chotsimikizira kuti iye anali Mesiya. Iye anati: “Madzulo munena, Kudzakhala ngwe; popeza thambo lili lacheza. Ndipo m’maŵa, Lero nkwa mphepo: popeza thambo lili la cheza chodera. Mudziŵa kuzindikira za pankhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo ino, simungathe kuzindikira. Obadwa oipa ndi achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona.”—Mateyu 16:1-4.
Adani a Yesu anakhoza kuneneratu za nyengo koma sanakhoze kuzindikira zinthu zauzimu. Mwachitsanzo, bwanji ponena za “chizindikiro cha Yona”? Pambuyo pokhala pafupifupi masiku atatu m’mimba mwa nsomba yaikulu, Yona mneneri wa Mulungu analalikira m’Nineve ndipo motero anakhala chizindikiro kwa mzinda waukulu wa Asuri umenewo. Mbadwo wa Yesu unali ndi “chizindikiro cha Yona” pamene Kristu anathera mbali za masiku atatu m’manda ndipo anaukitsidwa. Ophunzira ake analengeza umboni wa chochitika chimenecho, ndipo motero Yesu anali chizindikiro kwa mbadwo umenewo.—Mateyu 12:39-41.
Panthaŵi ina, ophunzira a Yesu anampempha “chizindikiro” cha “kukhalapo” (NW) kwake kwamtsogolo m’mphamvu Yaufumu. Poyankha, iye anapereka chizindikiro chachiungwe chopangidwa ndi mbali zosiyanasiyana, kuphatikizapo nkhondo zosayerekezereka, zivomezi zazikulu, njala, ndi kulalikira kwapadziko lonse konena za Ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwa kumwamba.—Mateyu 24:3-14.
Kodi mukuzindikira chizindikiro cha kukhalapo kwa Kristu monga Mfumu yosawoneka yakumwamba? Mbali zake zikukwaniritsidwa pambadwo uno. (Mateyu 24:34) Ndipo bwanji ponena za mtsogolo? Baibulo silimangovumbula kokha kuti mapeto a dongosolo lino la zinthu ali pafupi komanso limaneneratu za dziko latsopano lolonjezedwa ndi Mulungu lomwe lidzafika posachedwapa kwa mtundu wa anthu.—2 Petro 3:13.