“Yang’anirani Mupeŵe Chotupitsa Mkate cha Afarisi ndi Asaduki”
PAMENE Yesu Kristu analankhula mawuwo zaka zoposa mazana 19 zapitazo, anali kuchenjeza ophunzira ake za ziphunzitso zowononga za chipembedzo ndi machitachita ake. (Mateyu 16:6, 12) Nkhani ya pa Marko 8:15 imanena molunjika kuti: “Yang’anirani, penyani kuti mupeŵe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode.” Kodi Herode anatchulidwiranji? Chifukwa chakuti Asaduki ena anali Aherode, chipani cha ndale.
Kodi nchifukwa ninji chenjezo lapadera limenelo linali lofunika? Kodi Afarisi ndi Asaduki omwe sanali adani a Yesu odziŵikiratu? (Mateyu 16:21; Yohane 11:45-50) Inde, analidi. Komabe, ena a iwo pambuyo pake akalandira Chikristu ndiyeno akayesa kupereka malingaliro awo pa mpingo Wachikristu.—Machitidwe 15:5.
Panalinso ngozi yakuti ophunzira enieniwo akatsanzira atsogoleri achipembedzo amenewo chifukwa cha kukulira pansi pa chisonkhezero chawo. Nthaŵi zina, kungokhala ndi makulidwe oterowo kunakhala chopinga chowalepheretsa kuona mfundo za ziphunzitso za Yesu.
Kodi nchiyani chimene chinachititsa Ufarisi ndi Usaduki kukhala wowopsa? Kupenda pang’ono mikhalidwe ya chipembedzo m’nthaŵi ya Yesu kudzatithandiza kuzindikira.
Kusagwirizana kwa Chipembedzo
Ponena za chitaganya cha Ayuda a m’zaka za zana loyamba C.E., wolemba mbiri Max Radin analemba kuti: “Kudziimira kwa mipingo ya Ayuda uliwonse pawokha kunali kwenikweni, ndipo kunaumirizidwadi. . . . Kaŵirikaŵiri, pamene kulemekeza kachisi ndi mzinda wopatulika kunagogomezeredwa mwamphamvu, pangakhale panali kusonyeza udani waukulu kwa awo amene panthaŵiyo anali m’malo olamulira m’dziko lawolo.”
Umenewo unali mkhalidwe wauzimu womvetsa chisoni chotani nanga! Kodi ndi ziti zina zimene zinauchititsa? Si Ayuda onse amene ankakhala m’Palesitina. Chisokhezero cha mwambo wa Agiriki, amene kwawo ansembe sanali olamulira m’chitaganya, chinafooketsa ulemu wa makonzedwe a Yehova a unsembe. (Eksodo 28:29; 40:12-15) Ndiponso panali anthu wamba ophunzira ndi alembi.
Afarisi
Dzina lakuti Afarisi, kapena Peru·shimʹ, liyenera kuti linatanthauza “opatulidwa.” Afarisi anadziona kukhala atsatiri a Mose. Anapanga chigwirizano chawo, kapena ubale (m’Chihebri, chavu·rahʹ). Kuti munthu aloŵemo, anafunikira kuŵinda pamaso pa ziŵalo zitatu kuti adzasunga chiyero cha Ulevi mosalephera konse, kupeŵa mayanjano ndi ʽam-ha·ʼaʹrets (anthu osaphunzira), ndi kupereka zachikhumi mosaphonya. Marko 2:16 amalankhula za “alembi a kwa Afarisi.” Ena achipani chimenechi anali alembi aukatswiri ndi aphunzitsi, pamene ena anali anthu wamba.—Mateyu 23:1-7.
Afarisi anakhulupirira Mulungu wokhala paliponse. Analingalira kuti popeza kuti “Mulungu ali paliponse, Iye akhoza kulambiridwa mkati ndi kunja komwe kwa Kachisi, ndipo sanafunikire kupembedzeredwa ndi nsembe zokha. Motero iwo anachirikiza sunagoge kukhala malo olambirira, ophunzirira, ndi opempherera, ndipo anamkweza kukhala malo ofunika kwambiri m’moyo wa anthu mofanana ndi Kachisi.”—Encyclopaedia Judaica.
Afarisi anali osayamikira Kachisi wa Yehova. Zimenezi zingaonedwe m’mawu a Yesu akuti: “Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula Kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golidi wa Kachisi, wadzimangirira. Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golidi kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golidiyo? Ndiponso, Amene aliyense akalumbira kutchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula mtulo wa pamwamba pake wadzimangirira. Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo? Chifukwa chake wakulumbira kutchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pake.”—Mateyu 23:16-20.
Kodi ndimotani mmene kalingaliridwe ka Afarisi kanapotokera motero? Kodi iwo anali kunyalanyaza chiyani? Onani zimene Yesu akunena pambuyo pake. “Ndipo wakulumbira kutchula Kachisi, alumbira ameneyo ndi iye wakukhala momwemo.” (Mateyu 23:21) Ponena za vesi limeneli, katswiri wina E. P. Sanders ananena kuti: “Kachisiyo anali woyera osati chabe chifukwa chakuti Mulungu woyera anali kulambiridwa kumeneko, komanso chifukwa chakuti anali kumeneko.” (Judaism: Practice and Belief, 63 BCE—66 CE) Komabe, kukhalapo kwa Yehova kwapadera sikukanatanthauza kanthu kwenikweni kwa awo amene analingalira kuti iye anali paliponse.
Afarisi anakhulupiriranso za kuikiratu za mtsogolo pamodzi ndi ufulu wa kusankha. M’mawu ena, “chinthu chilichonse chimaikidwiratu, komabe ufulu wa kusankha umaperekedwa.” Ngakhale ndi choncho, iwo anakhulupirira kuti kunaikidwiratu kuti Adamu ndi Hava adzachimwe ndi kuti ngakhale kudzicheka pang’ono pachala kunaikidwiratu.
Yesu angakhale atakumbukira za malingaliro onama oterowo pamene analankhula za kugwa kwa nsanja imene inapha anthu 18. Iye anafunsa nati: “Kodi muyesa kuti iwo [ophedwawo] anali olakwa koposa anthu onse akukhala m’Yerusalemu?” (Luka 13:4) Monga momwe zimakhalira pa ngozi zambiri, izi zinachitika monga “zomgwera m’nthaŵi mwake,” osati choikidwiratu monga momwe Afarisi anaphunzitsira. (Mlaliki 9:11) Kodi ndimotani mmene olingaliridwa kukhala anzeru amenewo anachitira ndi malamulo a Malemba?
Anali Osintha Zinthu Achipembedzo
Afarisi anakhulupirira kuti malamulo a Malemba anayenera kumasuliridwa ndi arabi a mbadwo uliwonse mogwirizana ndi malingaliro awo opita patsogolo. Motero, Encyclopaedia Judaica imanena kuti iwo “sanakuone kukhala kovuta kugwirizanitsa ziphunzitso za Tora ndi malingaliro opita patsogolo, kapena kuona malingaliro awo kukhala otchulidwa kapena ochirikizidwa m’mawu a Tora.”
Ponena za Tsiku la Chitetezero la chaka ndi chaka, iwo anachotsa mphamvu ya kutetezera machimo pa mkulu wa nsembe ndi kuiika pa tsiku lenilenilo. (Levitiko 16:30, 33) Pa phwando la Paskha, anasamalira kwambiri za kunena moloŵeza pamtima maphunziro a m’mbiri ya kunyamuka Ulendo wawo pamene anali kumwa vinyo ndi kudya mkate wopanda chotupitsa m’malo mwa mwana wa nkhosa wa paskha.
M’kupita kwa nthaŵi, Afarisiwo anakhala ndi mphamvu pakachisi. Ndiyeno anayambitsa ligubo lonyamula madzi kuchokera ku dziŵe la Siloamu ndi kuwatsanulira paguwa lansembe pa Madyerero a Kututa, limodzinso ndi kuwombetsa nthambi za msondodzi pa guŵa la nsembe pakutha kwa phwandolo, ndi mapemphero a nthaŵi zonse a tsiku ndi tsiku amene analibe maziko m’Chilamulo.
“Chapadera kwambiri” chinali “kusintha zinthu kwa Afarisi zokhudza Sabata,” imatero The Jewish Encyclopedia. Mkazi anafunikira kuchingamira Sabata mwa kuyatsa nyali. Ngati kunaoneka kuti kuchita kanthu kena kungakhale kugwira ntchito koletsedwa ndi lamulo, Afarisi analetsa kuchita kanthuko. Iwo anafika ngakhale pa kulamulira za machiritsidwe ndi kusonyeza mkwiyo pa kuchiritsa kozizwitsa kwa Yesu pa Sabata. (Mateyu 12:9-14; Yohane 5:1-16) Komabe, osintha zinthu achipembedzo ameneŵa sanalekezere pa kuyambitsa malamulo atsopano kotero kuti aike chochinga, kapena chochinjiriza, kuti atetezere malamulo a Malemba.
Kufafaniza Malamulo
Afarisi anadzipatsa mphamvu ya kuletsa kapena kufafaniza malamulo a Malemba. Kalingaliridwe kawo kakusonyezedwa ndi mwambi wa mu Talmud wakuti: “Kuli bwinopo kuti lamulo limodzi lichotsedwe kuposa kuti Tora yonse iiŵalidwe.” Chitsanzo cha zimenezi chinali kulekedwa kwa phwando la Chaka Choliza Lipenga pa zifukwa zakuti, poopera kutha kwa ngongole zimene ena anali nazo kwa iwo pofika nyengoyo, palibe amene akafunanso kukongoza aumphaŵi.—Levitiko, chaputala 25.
Zitsanzo zina ndizo kufafanizidwa kwa mlandu wa mkazi wolingaliridwa kukhala atachita chigololo ndi wa mbanda yochitidwa ndi munthu wosadziŵika, kuchotsedwa kwa kachitidwe ka kuthetsa mlandu wosoŵa wouchita. (Numeri 5:11-31; Deuteronomo 21:1-9) M’kupita kwa nthaŵi, Afarisi anafafaniza chofunika cha Malemba cha kusamalira zosoŵa za makolo a munthu.—Eksodo 20:12; Mateyu 15:3-6.
Yesu anachenjeza kuti: “Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.” (Luka 12:1) Ufarisi, ndi makhalidwe ake osakhala a teokrase, unali zonyenga zokhazokha—zinthu zosafunika kuloŵetsedwa mumpingo Wachikristu. Komabe, mabuku a maumboni Achiyuda amasonyeza Afarisi mowayanja kwambiri kusiyana ndi Asaduki. Tsopano tiyeni tipende kagulu kameneka kosunga mwambo kwambiri.
Asaduki
Liwu lakuti Asaduki likuoneka kukhala lotengedwa kwa Zadoki, mkulu wansembe m’masiku a Solomo. (1 Mafumu 2:35, mawu amtsinde, NW) Asaduki anapanga chipani chosunga mwambo chochirikiza zinthu za kachisi ndi unsembe. Mosiyana ndi Afarisi, amene anadzipatsa ulamuliro chifukwa cha kuphunzira ndi kudzipereka, Asaduki anazika ulamuliro wawo pa mzera wobadwira ndi udindo. Iwo anatsutsa kusintha zinthu kwa Afarisi mpaka pa nthaŵi ya kuwonongedwa kwa kachisi mu 70 C.E.
Kuwonjezera pa kukana kwawo chiphunzitso cha kuikiratu za mtsogolo, Asaduki anakananso kuvomereza chiphunzitso chilichonse chosatchulidwa mwachindunji mu Pentatuke, ngakhale ngati chinatchulidwa penapake m’Mawu a Mulungu. Ndi iko komwe, kutsutsa nkhani zimenezi “anakuona kukhala ulemerero.” (The Jewish Encyclopedia) Zimenezi zimakumbutsa chochitika china pamene iwo anayesa Yesu ponena za chiukiriro.
Akumagwiritsira ntchito chitsanzo cha mkazi wamasiye wa amuna asanu ndi aŵiri, Asadukiwo anafunsa kuti: “M’kuuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wa yani wa asanu ndi aŵiriwo?” Ndithudi, mkazi wamasiye wongoyerekeza wawoyo akanakhala ngakhale ndi amuna 14 kapena 21. Yesu analongosola kuti: “M’kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa.”—Mateyu 22:23-30.
Podziŵa kuti Asaduki anali okana alembi ouziridwa kupatulapo Mose yekha, Yesu anatsimikiziritsa mfundo Yake mwa kugwira mawu mu Pentatuke. Iye anati: “Simunaŵerenga m’kalata wa Mose kodi, za Chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo? Sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo.”—Marko 12:26, 27.
Ozunza Yesu ndi Otsatira Ake
Asaduki anadalira pa kuchita mapangano a boma ndi mitundu ina m’malo moyembekezera Mesiya—ngati anakhulupirira nkomwe kubwera kwake. M’pangano lawo ndi Roma, iwo anafunikira kuyendetsa zinthu za kachisi ndipo sanafune kufika kwa Mesiya aliyense, kuti adzadodometse zinthu. Poona Yesu kukhala chiwopsezo pa udindo wawo, iwo anagwirizana ndi Afarisi kuti apangane za chiwembu cha imfa yake.—Mateyu 26:59-66; Yohane 11:45-50.
Pokhala a maganizo a ndale, Asadukiwo mochenjera anapanga nkhaniyo kukhala ya kukhulupirika kwawo kwa Roma nafuula: “Tilibe Mfumu koma Kaisara.” (Yohane 19:6, 12-15) Pambuyo pa imfa ya Yesu ndi kuuka kwake, anali Asaduki amene anatsogolera m’zoyesayesa za kuletsa kufalikira kwa Chikristu. (Machitidwe 4:1-23; 5:17-42; 9:14) Kachisi atawonongedwa mu 70 C.E, kagulu kameneka kanazimiririka.
Kufunika kwa Kukhalabe Maso
Ha, chenjezo la Yesu latsimikizirika kukhala loyenera chotani nanga! Inde, tifunikira ‘kuyang’anira chotupitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki.’ Munthu afunikira kuyang’anira zipatso zake zoipa m’Chiyuda ndi m’Dziko Lachikristu momwe lerolino.
Komabe, mosiyana kotheratu ndi zimenezo, akulu Achikristu oyeneretsedwa m’mipingo yoposa 75,500 ya Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse ‘amapenyerera iwo eni ndi chiphunzitso chawo.’ (1 Timoteo 4:16) Iwo amakhulupirira Baibulo lonse lathunthu kukhala louziridwa ndi Mulungu. (2 Timoteo 3:16) M’malo mwa kukhala osintha zinthu ndi kuchirikiza njira zawozawo zolambirira, iwo amagwira ntchito mogwirizana pansi pa chitsogozo cha gulu lozikidwa pa Baibulo limene limagwiritsira magazini ano monga chiŵiya chake chachikulu cholangizira.—Mateyu 24:45-47.
Ndi chotulukapo chotani? Mamiliyoni a anthu kuzungulira dziko lonse akukwezedwa mwauzimu pamene akumvetsetsa Baibulo, kuligwiritsira ntchito m’miyoyo yawo, ndi kuphunzitsa ena. Kuti muone mmene zimenezi zikuchitidwira, bwanji osafika pa mpingo wapafupi wa Mboni za Yehova kapena kulembera ofalitsa a magazini ano?
[Bokosi patsamba 26]
YESU ANAGANIZIRA OMVETSERA AKE
YESU KRISTU anaphunzitsa momvekera bwino, akumalingalira za omvetsera ake. Mwachitsanzo, iye anachita zimenezo pamene analankhula kwa Mfarisi Nikodemo ponena za nkhani ya “kubadwa” mwatsopano. Nikodemo anafunsa kuti: “Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kuloŵanso m’mimba ya amake ndi kubadwa?” (Yohane 3:1-5) Kodi nchifukwa ninji Nikodemo anadabwa kwambiri, popeza kuti Afarisi anakhulupirira kuti kubadwanso kunali kofunika kwa otembenuka kukhala Ayuda, ndipo mwambi wa chirabi unafanizira wotembenuka kukhala Myuda ndi “khanda lobadwa kumene”?
A Commentary on the New Testament From the Talmud and Hebraica, lolembedwa ndi John Lightfoot, imapereka chidziŵitso ichi: “Lingaliro lofala la Ayuda ponena za kuyenerera kwa Mwisrayeli . . . lidakali lozama m’maganizo a Mfarisi ameneyu” amene sakhoza “kuchotsa maganizo ake odzikweza . . . : ‘Pamene kuli kwakuti Aisrayeli . . . ali oyenera kuloŵa mu ufumu wa Mesiya, kodi mwa mawu anuŵa, mukutanthauza kuti kuli kofunika kwa aliyense kuloŵanso m’mimba mwa amake, kuti akhale Mwisrayeli watsopano?’”—Yerekezerani ndi Mateyu 3:9.
Ngakhale kuti Nikodemo anavomereza kubadwanso kwa otembenuzidwa, iye anaona kachitidwe koteroko kukhala kosatheka kwa Ayuda enieni—konga kuloŵanso m’mimba.
Panthaŵi ina, ambiri anakwiya pamene Yesu analankhula za ‘kudya thupi lake ndi kumwa mwazi wake.’ (Yohane 6:48-55) Komabe, Lightfoot akunena kuti “panalibe chinthu chofala kwambiri m’sukulu za Chiyuda mofanana ndi mawu akuti ‘kudya ndi kumwa’ m’lingaliro lokuluŵika mawu.” Iye ananenanso kuti Talmud inatchula “Kudya Mesiya.”
Chotero, zinali motero kuti malingaliro a Afarisi ndi Asaduki anayambukira kwambiri kalingaliridwe ka Ayuda m’zaka za zana loyamba. Komabe moyenerera, nthaŵi zonse Yesu analingalira za chidziŵitso ndi mikhalidwe ya omvetsera ake. Chimenechi chinali chimodzi cha zifukwa zimene zinamchititsa kukhala Mphunzitsi Wamkulu.