Kodi Mungalolere Kudzimana Chiyani Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha?
“Munthu angapereke chiyani chosinthanitsa ndi moyo wake?”—MAT. 16:26.
1. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anamuyankha mwamphamvu Petulo?
MTUMWI Petulo anadabwa kwambiri ndi zimene anamva. Mtsogoleri wake amene anali kumukonda, Yesu Khristu, analankhula “molimba mtima” kuti anali pafupi kuzunzidwa ndi kufa. Petulo, mosakayikira anali ndi zolinga zabwino, podzudzula Yesu kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye; musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.” Yesu anatembenuka ndi kuyang’ana ophunzira ake ena. Mwina iwonso anali ndi maganizo olakwika ngati amenewa. Ndiyeno anati kwa Petulo: “Ndichokere, Satana! Ndiwe chopunthwitsa kwa ine, chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”—Maliko 8:32, 33; Mat. 16:21-23.
2. Kodi Yesu anafotokoza kuti chofunika n’chiyani kuti munthu akhale wophunzira wake weniweni?
2 Zimene Yesu ananena kenako, zinamuthandiza Petulo kuona chifukwa chake Yesu anamuyankha mwamphamvu choncho. Yesu “anaitana khamu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake” ndipo anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo, ndi kunditsatira mosalekeza. Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya; koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine, ndi uthenga wabwino, adzaupulumutsa.” (Maliko 8:34, 35) Ndithudi, Yesu anali atatsala pang’ono kupereka moyo wake ndipo ankayembekezeranso kuti anthu omutsatira akhale okonzeka kudzimana chifukwa chotumikira Mulungu. Iwo akachita zimenezi, adzalandira mphoto yaikulu.—Werengani Mateyo 16:27.
3. (a) Kodi Yesu anafunsa omvera ake mafunso otani? (b) Kodi funso lachiwiri la Yesu linawakumbutsa chiyani omvera ake?
3 Panthawi yomweyi Yesu anafunsanso mafunso awiri ofunika kwambiri. Loyamba n’lakuti: “Pali phindu lanji ngati munthu apata dziko lonse koma n’kutaya moyo wake?” Ndipo lachiwiri n’lakuti: “N’chiyani kwenikweni chimene munthu angapereke chosinthanitsa ndi moyo wake?” (Maliko 8:36, 37) Kwa anthu, yankho la funso loyambalo n’lodziwikiratu. N’zopandadi phindu ngati munthu atapata dziko lonse koma n’kutaya moyo wake. Katundu amakhala waphindu ngati munthu ali ndi moyo chifukwa m’pamene angathe kum’gwiritsa ntchito. Funso la Yesu lachiwiri lakuti: “N’chiyani kwenikweni chimene munthu angapereke chosinthanitsa ndi moyo wake?” liyenera kuti linawakumbutsa omvera ake zimene Satana ananena m’masiku a Yobu kuti: “Munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.” (Yobu 2:4) Kwa anthu amene salambira Yehova, zimene Satana ananena zingakhale zoona. Anthu ambiri angachite chilichonse, ngakhale kusamvera mfundo za makhalidwe abwino, n’cholinga chakuti akhale ndi moyo. Koma mmenemu si mmene Akhristu amaonera zinthu.
4. Kodi n’chifukwa chiyani mafunso a Yesu amatanthauza zambiri kwa Akhristu?
4 Tikudziwa kuti Yesu sanabwere kudzatipatsa moyo wathanzi, chuma, komanso moyo wautali m’dziko lino. Iye anabwera kudzapereka mwayi wakuti tidzakhale ndi moyo wosatha m’dziko latsopano, ndipo moyo umenewu ndi umene uli wofunika kwambiri kwa ife. (Yoh. 3:16) Mkhristu angaone kuti funso loyamba la Yesu limatanthauza kuti, “Pali phindu lanji ngati munthu atapata dziko lonse koma n’kutaya chiyembekezo chake cha moyo wosatha?” Yankho n’lakuti, zilibe phindu m’pang’ono pomwe. (1 Yoh. 2:15-17) Kuti tithe kuyankha funso lachiwiri la Yesu lija, tifunika kudzifunsa kuti, ‘Kodi panopo ndingalolere kudzimana chiyani kuti ndidzakhale ndi moyo wosatha m’dziko latsopano?’ Yankho lathu la funso limeneli, malinga ndi zimene tikuchita pamoyo wathu, limasonyeza kulimba kwa chiyembekezo chathu.—Yerekezerani ndi Yohane 12:25.
5. Kodi tingatani kuti tilandire mphatso ya moyo wosatha?
5 Komabe, Yesu sananene kuti tingagule moyo wosatha. Moyo wathu, ngakhale wanthawi yochepa umene timakhala nawo m’dongosolo lino, ndi mphatso. Sitingaugule komanso sitingachite zinthu zotiyeneretsa kupatsidwa moyo. Njira yokha imene tingalandirire mphatso ya moyo wosatha ndiyo “kukhulupirira Khristu Yesu” ndi Yehova, “wopereka mphoto kwa anthu om’funafuna ndi mtima wonse.” (Agal. 2:16; Aheb. 11:6) Komabe, tifunika kusonyeza chikhulupiriro mwa zochita zathu, popeza “chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.” (Yak. 2:26) Choncho, tikamaganizira za funso la Yesu limeneli, tingachite bwino kuganizira mofatsa zimene tingalolere kudzimana m’dongosolo lino la zinthu ndiponso zimene tingalolere kuchita potumikira Yehova kuti tisonyeze kuti chikhulupiro chathu chilidi cha moyo.
“Khristu Sanadzikondweretse Yekha”
6. Kodi n’chiyani chinali chofunika kwambiri kwa Yesu?
6 Mtima wa Yesu sunali pa zinthu zimene akanatha kupeza m’dzikoli koma unali pa zinthu zofunika kwambiri ndipo anapewa mtima wofuna chuma. Iye anali wodzimana ndiponso womvera Mulungu. Iye sanadzikondweretse yekha, ndipo anati: “Ndimachita zinthu zom’kondweretsa [Mulungu] nthawi zonse.” (Yoh. 8:29) Kodi Yesu anali wofunitsitsa kuchita chiyani kuti asangalatse Mulungu?
7, 8. (a) Kodi Yesu anapereka chiyani, nanga anadalitsidwa bwanji? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa chiyani?
7 Nthawi ina Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mat. 20:28) M’mbuyomo, Yesu atauza otsatira ake kuti watsala pang’ono ‘kupereka moyo wake,’ Petulo anamuuza kuti adzikomere mtima. Komabe, Yesu sanatsatire zimenezi. Iye anapereka moyo wake wangwiro, chifukwa cha anthu. Chifukwa chakuti Yesu sanadzikonde, tsogolo lake linali labwino. Iye anaukitsidwa ndipo “anakwezedwa kudzanja lamanja la Mulungu.” (Mac. 2:32, 33) Choncho, Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife.
8 Mtumwi Paulo analangiza Akhristu a ku Roma kuti ‘asamadzikondweretse’ okha ndipo anawakumbutsa kuti “ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha.” (Aroma 15:1-3) Choncho, kodi tingagwiritse ntchito motani malangizo amenewa ndipo tidzalolera kudzimana chiyani potsanzira Khristu?
Yehova Amafuna Kuti Tim’patse Zabwino Kwambiri
9. Kodi Mkhristu amachita chiyani kwenikweni akadzipereka kwa Mulungu?
9 M’nthawi ya Aisiraeli, Chilamulo cha Mose chinanena kuti akapolo achiheberi azimasulidwa m’chaka cha 7 cha ukapolo wawo kapena m’chaka Choliza Lipenga. Komabe, panali chinthu china chimene akanachita. Ngati kapolo anali kuwakonda Ambuye ake, amatha kusankha kukhalabe kapolo pakhomopo kwa moyo wake wonse. (Werengani Deuteronomo 15:12, 16, 17.) Ifenso timachita zofanana ndi zimenezi tikadzipereka kwa Mulungu. Timavomereza mwa kufuna kwathu kuti tizichita zimene Mulungu akufuna, osati zofuna zathu. Tikamachita zimenezi, timasonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova ndiponso kuti timafuna kumutumikira kosatha.
10. Kodi n’chifukwa chiyani ndife chuma cha Mulungu, ndipo zimenezi ziyenera kukhudza bwanji maganizo ndi zochita zathu?
10 Ngati panopo mukuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, mukulalikira uthenga wabwino, ndipo mumapezeka pamisonkhano yachikhristu, ndiye kuti mukuchita bwino kwambiri. Tikukhulupirira kuti posachedwapa mudzafuna kudzipereka kwa Yehova ndipo mudzafunsa ngati zimene Mwaitiopiya anafunsa Filipo kuti: “Chindiletsa kubatizidwa n’chiyani?” (Mac. 8:35, 36) Ndiyeno ubwenzi wanu ndi Mulungu udzakhala ngati wa Akhristu amene Paulo anawalembera kuti: “Simuli a inu nokha, pakuti munagulidwa ndi mtengo wake.” (1 Akor. 6:19, 20) Kaya tikuyembekezera kukakhala ndi moyo kumwamba kapena padziko lino lapansi, ngati tinadzipereka kwa Yehova, ndiye kuti ndife Ake. Choncho, n’kofunika kwambiri kupewa zilakolako zadyera ndiponso ‘tileke kukhala akapolo a anthu.’ (1 Akor. 7:23) Ndi mwayi waukulu kukhala mtumiki wokhulupirika amene Yehova angamugwiritse ntchito mmene akufunira.
11. Kodi Akhristu ayenera kupereka chiyani nsembe, ndipo zimenezi zikutanthauza chiyani kwenikweni malinga ndi nsembe zimene zinkaperekedwa m’Chilamulo cha Mose?
11 Paulo analangiza okhulupirira anzake kuti: “Mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kulingalira.” (Aroma 12:1) Mawu amenewa ayenera kuti anakumbutsa Akhristu achiyuda za nsembe zimene ankapereka polambira asanayambe kutsatira Yesu. Iwo ayenera kuti ankadziwa kuti m’Chilamulo cha Mose, nyama zoperekedwa pa guwa la Yehova zinayenera kukhala zabwino kwambiri. Iye sankalandira nyama iliyonse yolumala kapena yodwala. (Mal. 1:8, 13) N’chimodzimodzi ndi ifeyo tikamapereka matupi athu “nsembe yamoyo.” Timapereka kwa Yehova zinthu zabwino kwambiri, osati zotsala tikachita zofuna zathu. Tikadzipereka kwa Mulungu, timamupatsa moyo wathu wonse, kuphatikizapo mphamvu zathu, chuma chathu ndi luso lathu. (Akol. 3:23) Kodi tingapereke bwanji zinthu zabwino kwambiri kwa Yehova?
Gwiritsani Ntchito Nthawi Yanu Mwanzeru
12, 13. Kodi njira imodzi imene tingam’patsire zabwino kwambiri Yehova ndi iti?
12 Njira imodzi imene tingam’patsire Yehova zinthu zabwino kwambiri ndiyo yogwiritsa ntchito nthawi yathu mwanzeru. (Werengani Aefeso 5:15, 16.) Kuti zimenezi zitheke, tifunika kudziletsa. Zinthu za m’dzikoli komanso kupanda kwathu ungwiro kumatipangitsa kuti tizingothera nthawi yathu pa zinthu zosangalatsa kapena pa zimene tikufuna. N’zoona kuti “kanthu kali konse kali ndi nthawi yake,” pali nthawi yosangalala, yopuma ndiponso yogwira ntchito kuti tithe kusamalira maudindo athu achikhristu. (Mlal. 3:1) Komabe, Mkhristu wodzipereka safunika kuchita zimenezi monyanyira koma afunika kugwiritsa ntchito nthawi yake mwanzeru.
13 Paulo atapita ku Atene, anaona kuti “nzika zonse za mu Atene ndi alendo ogonera kumeneko, anali kuthera nthawi yawo yonse yopuma akufotokoza kapena kumvetsera nkhani yatsopano.” (Mac. 17:21) Masiku anonso, anthu ambiri amawononga nthawi yawo mwanjira imeneyi. Pali zinthu zambiri zimene zingatidyere nthawi monga kuonera TV, kuchita masewera a pa kompyuta, ndi kuona zinthu zina n’zina pa Intaneti. Kulekerera zinthu zimenezi, kungatipangitse kunyalanyaza moyo wathu wauzimu. Tingafike poona kuti ndife otanganidwa kwambiri moti tilibe nthawi yochitira “zinthu zofunika kwambiri,” zokhudza utumiki wathu kwa Yehova.—Afil. 1:9, 10.
14. Kodi ndi mafunso ati amene tifunika kuwaganizira mofatsa?
14 Choncho, monga atumiki a Yehova odzipereka, tidzifunse kuti, ‘Kodi pa zimene ndimachita tsiku lililonse, ndimakhala ndi nthawi yowerenga Baibulo, yosinkhasinkha ndi yopemphera?’ (Sal. 77:12; 119:97; 1 Ates. 5:17) ‘Kodi ndimakhala ndi nthawi yokonzekera misonkhano yachikhristu? Kodi ndimalimbikitsa ena mwa kuyankha pamisonkhano?’ (Sal. 122:1; Aheb. 2:12) Mawu a Mulungu amatiuza kuti Paulo ndi Baranaba anakhala “nthawi yaitali, . . . akulankhula molimba mtima mwa mphamvu ya Yehova.” (Mac. 14:3) Kodi mungasinthe zinthu zina pamoyo wanu kuti muzikhala ndi “nthawi yaitali” mu ntchito yolalikira, mwinanso kuti muchite upainiya?—Werengani Aheberi 13:15.
15. Kodi akulu amagwiritsa ntchito bwanji nthawi yawo mwanzeru?
15 Mtumwi Paulo ndi Baranaba atapita ku mpingo wachikristu wa ku Antiokeya, “anakhala ndi ophunzirawo nthawi yaitali” akuwalimbikitsa. (Mac. 14:28) Nawonso akulu achikondi masiku ano amagwiritsa ntchito nthawi yawo yambiri akulimbikitsa ena. Kuwonjezera pa utumiki wakumunda, akulu amayesetsa kuweta nkhosa, kufufuza nkhosa zotayika, kuthandiza odwala, ndiponso kusamalira maudindo ena mumpingo. Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, kodi moyo wanu ungakuloleni kuyesetsa kuti muyenerere kulandira maudindo amenewa mumpingo?
16. Kodi ndi njira zina ziti zimene ‘tingachitire zabwino achibale athu m’chikhulupiriro’?
16 Anthu ambiri amasangalala kuthandiza anthu amene ataya zinthu zawo chifukwa cha masoka achilengedwe kapena masoka amene amayambika chifukwa cha zochita za anthu. Mwachitsanzo, mlongo wina wa zaka za m’ma 60 amene amatumikira pa Beteli, anayenda kangapo maulendo ataliatali kukathandiza anthu amene anagweredwa masoka. Kodi n’chifukwa chiyani anagwiritsa ntchito masiku ake atchuthi m’njira imeneyi? Iye anati: “Ngakhale kuti ndilibe maluso enaake apadera, unali mwayi wanga kugwira ntchito iliyonse imene inkafunika. Ndinalimbikitsidwa kwambiri kuona chikhulupiriro cholimba cha abale ndi alongo amene anataya katundu wawo wambiri.” Komanso, anthu ambiri padziko lonse amathandiza kumanga Nyumba za Ufumu ndi Nyumba za Msonkhano. Tikamathandiza pa zinthu ngati zimenezi, ‘timachitira zabwino achibale athu m’chikhulupiriro.’—Agal. 6:10.
“Ine Ndili Nanu Pamodzi Masiku Onse”
17. Kodi inuyo mungalolere kuchita chiyani kuti mudzapeze moyo wosatha?
17 Anthu osakonda Mulungu atsala pang’ono kuwonongedwa. Sitikudziwa kuti zimenezi zichitika liti. Komabe, tikudziwa kuti “nthawi yotsalayi yafupika” ndipo “zochitika za padzikoli zikusintha.” (Werengani 1 Akorinto 7:29-31.) Zimenezi zikusonyeza kufunika kwa funso la Yesu lakuti: “N’chiyani kwenikweni chimene munthu angapereke chosinthanitsa ndi moyo wake?” Ndithudi, tidzachita zilizonse zimene Yehova angatipemphe n’cholinga chakuti tikapeze “moyo weniweniwo.” (1 Tim. 6:19) Tifunikadi kumvera malangizo a Yesu akuti ‘tim’tsatire mosalekeza’ ndiponso “kufuna ufumu choyamba.”—Mat. 6:31-33; 24:13.
18. Kodi tingakhale ndi chikhulupiriro chotani, ndipo n’chifukwa chiyani?
18 N’zoona kuti kutsatira Yesu n’kovuta nthawi zina, ndipo mogwirizana ndi mawu a Yesu, ena ataya miyoyo yawo m’dongosolo lino la zinthu. Komabe, mofanana ndi Yesu, timapewa ‘kudzikomera mtima.’ Timakhulupirira mawu olimbikitsa amene anauza otsatira ake odzozedwa akuti: “Ine ndili nanu pamodzi masiku onse mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mat. 28:20) Choncho, tiyeni tiyesetse mmene tingathere kugwiritsa ntchito nthawi yathu ndi luso lathu mu utumiki wopatulika. Tikamachita zimenezi, timasonyeza kuti timakhulupirira kuti Yehova adzatipulumutsa pa chisautso chachikulu kapena adzatiukitsa m’dziko latsopano. (Aheb. 6:10) Tikatero, tidzasonyeza kuti timaona mphatso ya moyo kukhala yamtengo wapatali.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wofunitsitsa kutumikira Mulungu ndiponso anthu ena?
• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kudzikana tokha, ndipo tingachite bwanji zimenezi?
• M’nthawi ya Aisiraeli, kodi Yehova ankalandira nsembe zotani, ndipo zimenezi zikutithandiza bwanji masiku ano?
• Kodi nthawi yathu tingaigwiritse ntchito bwanji mwanzeru?
[Zithunzi patsamba 26]
Nthawi zonse Yesu ankachita zinthu zokondweretsa Mulungu
[Chithunzi patsamba 28]
Aisiraeli oyamikira ankapereka zinthu zabwino kwambiri zothandizira kulambira koona
[Zithunzi patsamba 29]
Timasangalatsa Mulungu mwa kugwiritsa ntchito nthawi yathu mwanzeru