Labadirani Mawu Aulosi a Mulungu
“Tili nawo mawu a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira.”—2 PETRO 1:19.
1, 2. Kodi mungasimbe chitsanzo chiti cha mesiya wonyenga?
KWA zaka mazana ambiri, amesiya onyenga akhala akuyesa kulosera za m’tsogolo. M’zaka za zana lachisanu C.E., mwamuna wina amene anadzitcha kuti Mose ananyenga Ayuda pachilumba cha Krete kuti iyeyo ndiye mesiya ndi kuti adzawalanditsa ku kuponderezedwa kwawo. Patsiku lachipulumutso lomwe anasankha, anam’tsatira kupita pansonga inayake pomwe Nyanja ya Mediterranean amaionera m’musi kwambiri. Iye ananena kuti iwo anangofunikira kudziponya m’nyanjamo, ndipo nyanjayo idzagaŵikana akuona. Ambiri amene anadziponya m’madzimo anamira, ndipo mesiya wonyenga ameneyo anathaŵa.
2 M’zaka za zana la 12, kunaonekanso “mesiya” wina ku dziko la Yemen. Mloŵam’malo wa Muhammad, kapena kuti mtsogoleri, anam’pempha kuti apereke chizindikiro cha umesiya wake. “Mesiyayu” ananena kuti adulidwe mutu ndi mtsogoleriyo. Analosera kuti adzaukitsidwa mwamsanga ndipo chimenecho chidzakhala chizindikirocho. Mtsogoleriyo anavomereza zimenezo—ndipo kutha kwa “mesiya” ameneyo kunali komweko.
3. Kodi Mesiya woona ndani, ndipo utumiki wake unasonyeza chiyani?
3 Amesiya onyenga ndi maulosi awo amalephera kotheratu, koma kulabadira mawu aulosi a Mulungu sikogwiritsa mwala konse. Mesiya woonayo, Yesu Kristu, ndiye anali kukwaniritsidwa kwenikweni kwa maulosi ambiri a m’Baibulo. Mwachitsanzo, pogwira mawu ulosi wa Yesaya, wolemba Uthenga Wabwino Mateyu analemba kuti: “Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali, njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordano, Galileya la anthu akunja, anthu akukhala mumdima adaona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo okhala m’malo a mthunzi wa imfa, kuwala kunatulukira iwo. Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:15-17; Yesaya 9:1, 2) Yesu ndiye anali “kuwala kwakukulu” kumeneko ndipo utumiki wake unasonyeza kuti ndiye anali Mneneri woloseredwa ndi Mose. Awo amene anakana kumvera Yesu anali kudzawonongedwa.—Deuteronomo 18:18, 19; Acts 3:22, 23.
4. Kodi Yesu anakwaniritsa motani Yesaya 53:12?
4 Yesu anakwaniritsanso mawu aulosi a Yesaya 53:12 akuti: “Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anaŵerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.” Podziŵa kuti posachedwa adzapereka moyo wake waumunthu kukhala dipo, Yesu analimbitsa chikhulupiriro cha ophunzira ake. (Marko 10:45) Zimenezi anazichita mwapadera kwambiri mwa kusandulika.
Kusandulika Kumangirira Chikhulupiriro
5. Kodi kusandulika kwa Yesu mungakulongosole motani m’mawu anuanu?
5 Kusandulika kwa Yesu kunali chochitika chaulosi. Yesu anati: “Mwana wa munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake . . . Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalaŵa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa munthu atadza mu ufumu wake.” (Mateyu 16:27, 28) Kodi ena mwa atumwi anamuonadi Yesu akudza mu Ufumu wake? Mateyu 17:1-7 amati: “Atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake, napita nawo paokha paphiri lalitali; ndipo iye anasandulika pamaso pawo.” Chinalitu chochitika chochititsa chidwi kwabasi! “Nkhope yake inawala monga dzuŵa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbu monga kuwala. Ndipo onani, Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo, alinkulankhula ndi iye.” Ndiponso, “mtambo wowala unawaphimba iwo,” ndipo anamva mawu enieni a Mulungu akunena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye. Ndipo pamene ophunzira anamva, anagwa nkhope zawo pansi, naopa kwakukulu. Ndipo Yesu anadza, nawakhudza nati, Ukani, musaopa.”
6. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anatcha kusandulikako kuti masomphenya? (b) Kodi kusandulika kunali chitsanzo cha chiyani?
6 Chochitika chochititsa mantha chimenechi chiyenera kuti chinachitikira pa chimodzi mwa zitunda za Phiri la Herimoni, kumene Yesu ndi atumwi atatuwo anagona. Mwachionekere kusandulika kumeneko kunachitika usiku, zimene zinakupangitsa kukhala kooneka kwambiri. Chifukwa chimodzi chimene Yesu anatchera kusandulikako kuti chooneka (kapena, masomphenya) chinali chakuti Mose ndi Eliya amene anaonekawo sanali enieniwo chifukwa anamwalira kalekale. Kristu yekha ndi amene analidi pamenepo kwenikweni. (Mateyu 17:8, 9) Masomphenya ozunguza mutu amenewo anapatsa Petro, Yakobo, ndi Yohane chitsanzo chosaiwalika cha kukhalapo kwa Yesu kwaulemerero m’mphamvu ya Ufumu. Mose ndi Eliya akukwaniritsidwa ndi oloŵa nyumba anzake a Yesu, ndipo masomphenyawo analimbitsa kwambiri umboni wake wonena za Ufumu ndi zakuti adzakhala mfumu m’tsogolo.
7. Tikudziŵa bwanji kuti Petro anali kukumbukira bwino lomwe za kusandulika?
7 Kusandulika kumeneko kunathandiza kulimbitsa chikhulupiriro cha atumwi atatuwo amene anali kudzakhala otsogolera mumpingo wachikristu. Nkhope ya Yesu itawala kwambiri, zovala zake zikunyezimira ndi kuyera, ndiponso mawu a Mulungu iyemwini akunena kuti Yesu ndi Mwana Wake wokondedwa amene ayenera kumumvera—zonsezi zinakwaniritsa chifuno chake bwino lomwe. Koma atumwiwo sanayenere kuuza aliyense za choonekacho mpaka Yesu ataukitsidwa. Patapita zaka 32, Petro anali kukumbukira bwino kwambiri masomphenya a kusandulika. Ponena za masomphenyawo ndi tanthauzo lake, analemba kuti: “Pakuti sitinatsata miyambi yachabe, pamene tinakudziŵitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m’maso ukulu wake. Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumudzera Iye mawu otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye; ndipo mawu aŵa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m’phiri lopatulika lija.”—2 Petro 1: 16-18.
8. (a) Chilengezo cha Mulungu chonena za Mwana wake chikusonyeza chiyani? (b) Kodi mtambo womwe unaonekera pakusandulika unasonyeza chiyani?
8 Chofunika kwambiri chinali chilengezo cha Mulungucho chakuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye.” Mawu ameneŵa akunena za Yesu monga Mfumu yoikidwa ya Mulungu, imene zolengedwa zonse ziyenera kumvera. Mtambo womwe unawaphimba unasonyeza kuti kukwaniritsidwa kwa masomphenya ameneŵa kudzakhala kosaoneka. Kudzaonedwa kokha ndi maso a kuzindikira a awo amene akuzindikira “chizindikiro” cha kukhalapo kosaoneka kwa Yesu m’mphamvu za Ufumu. (Mateyu 24:3) Kwenikweni, malangizo a Yesu akuti asauze munthu za masomphenyawo mpaka ataukitsidwa kwa akufa akusonyeza kuti kukwezedwa kwake ndi kulandira kwake ulemerero zidzachitika ataukitsidwa.
9. N’chifukwa chiyani kusandulika kuyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu?
9 Atanena za kusandulika, Petro anati: “Ndipo tili nawo mawu a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa m[i]tima yanu; ndi kudziŵa ichi poyamba, kuti palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pachokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.” (2 Petro 1:19-21) Kusandulika kukutsimikizira kudalirika kwa mawu aulosi a Mulungu. Tiyenera kulabadira mawu amenewo ndipo osati “miyambi yachabe” imene Mulungu saichirikiza kapena kuiloleza. Chikhulupiriro chathu m’mawu aulosi chiyenera kulimbitsidwa ndi kusandulikako chifukwa chakuti zenizeni za m’chitsanzo cha masomphenya a ulemerero wa Yesu ndi mphamvu za Ufumu zikuchitikadi tsopano. Inde, tili ndi umboni wosatsutsika wakuti Kristu alipo lerolino monga Mfumu yamphamvu yakumwamba.
Mmene Nthanda Ikutulukira
10. Kodi “nthanda” imene Petro anatchula ndiye ndani kapena ndiye chiyani, nanga mwayankhiranji motero?
10 Petro analemba kuti: “Muchita bwino powasamalira [mawu aulosiwo], monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda [“mpaka kutacha ndipo nthanda n’kutuluka, m’mitima mwanu,” NW].” Kodi “nthanda” imeneyo ndiye ndani kapena ndiye chiyani? Chivumbulutso 22:16 chimatcha Yesu Kristu kuti “nyenyezi yonyezimira ya nthanda.” Mu nyengo zina pachaka, nyenyezi zimenezi ndizo zimamalizira kutuluka kum’maŵa. Zimaonekera dzuŵa litangotsala pang’ono kutuluka, motero zimalengeza kuyamba kwa tsiku latsopano. Petro anagwiritsa ntchito mawu akuti “nthanda” kunena Yesu pambuyo pakuti Iye walandira mphamvu ya Ufumu. Panthaŵiyo, Yesu anatulukira m’chilengedwe chonse, kuphatikizapo dziko lathu lapansili! Pokhala Nthanda yaumesiya, akulengeza tsiku latsopano, kapena kuti nyengo, imene ikuyamba kwa anthu onse omvera.
11. (a) N’chifukwa chiyani 2 Petro 1:19 sakutanthauza kuti “nthanda” ikutuluka m’mitima yakuthupi ya anthu? (b) Kodi 2 Petro 1:19 mungam’longosole motani?
11 Mabaibulo ambiri amalimbikitsa mfundo yakuti mawu a mtumwi Petro olembedwa pa 2 Petro 1:19 amanena za mtima weniweni wa munthu. Mtima wa munthu wamkulu umalemera kokha magilamu pakati pa 250 ndi 300. Kodi Yesu Kristu, amene tsopano ndi cholengedwa chaulemerero chauzimu kumwamba, angatuluke motani m’ziŵalo zazing’onozi za anthu? (1 Timoteo 6:16) Zoonadi, mitima yathu yophiphiritsa ikukhudzidwa m’nkhaniyi, popeza kuti ndi imene timalabadira nayo mawu aulosi a Mulungu. Koma yang’anitsitsani pa 2 Petro 1:19, ndipo mudzaona kuti Baibulo la New World Translation limagwiritsa ntchito mipatuliro pofuna kusiyanitsa mawu ofotokozerawo akuti “mpaka kutacha ndipo nthanda n’kutuluka” ndi mawu oyambirira m’vesilo komanso ndi mawu akuti “m’mitima mwanu.” Vesi limeneli lingalembedwenso motere: ‘Tili nawo mawu a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira monga nyali younikira m’malo a mdima, ndiko kuti m’mitima mwanu, kufikira kukacha, nikauka nthanda.’
12. Kodi mitima ya anthu ili mumkhalidwe wotani, koma zinthu zili motani ndi Akristu enieni?
12 Kodi mitima yophiphiritsa ya mtundu wa anthu ochimwa ili mumkhalidwe wotani? Ayi ndithu, mitima yawo ili mumdima wauzimu! Komabe, ngati ndife Akristu oona, zili ngati kuti tili ndi nyali imene ikuwala m’mitima mwathu, imene popanda nyaliyo mitimayo ikanakhala mumdima. Monga momwe mawu a Petro akusonyezera, kulabadira mawu aulosi ounikira a Mulungu n’kumene kudzapangitsa Akristu enieni kukhala ogalamuka ndi ozindikira mpaka m’bandakucha wa tsiku latsopano. Adzakhala akudziŵa kuti Nthanda yatuluka, osati m’mitima yawo yakuthupi, koma m’chilengedwe chonse.
13. (a) N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikizira kuti Nthanda yatuluka kale? (b) N’chifukwa chiyani Akristu angathe kupirira zovuta za m’tsiku lathu zimene Yesu analosera?
13 Nthandayo yatuluka kale! Tingakhale otsimikizira ponena za zimenezo mwa kulabadira ulosi waukulu wa Yesu wonena za kukhalapo kwake. Lerolino, tikuona kukwaniritsidwa kwake m’zochitika monga nkhondo zamtundu wachilendo, njala, zivomezi, ndi kulalikira uthenga wabwino kwa padziko lonse. (Mateyu 24:3-14) Ngakhale kuti mikhalidwe yovuta yomwe Yesu analosera imatikhudzanso ifeyo monga Akristu, timatha kupirira tili ndi mtendere ndi chimwemwe cha mumtima. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti timalabadira mawu aulosi a Mulungu ndipo tili ndi chikhulupiriro m’zinthu zam’tsogolo zimene akulonjeza. Tikudziŵa kuti tatsala pang’ono penipeni kuloŵa m’nthaŵi zabwino koposa chifukwa chakuti tili m’kati mwenimweni mwa “nthaŵi ya chimaliziro”! (Danieli 12:4) Dziko lili pamavuto oloseredwa pa Yesaya 60:2 kuti: “Taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu.” Kodi munthu angaione bwanji njira yake mumdima umenewu? Iye ayenera kulabadira mawu aulosi a Mulungu modzichepetsa tsopano lino, nthaŵi isanathe. Anthu a mtima woona afunikira kutembenukira kwa Yehova Mulungu, Gwero la moyo ndi kuunika. (Salmo 36:9; Machitidwe 17:28) Pokhapokha ngati munthu akuchita zimenezi m’pamene angakhale ndi kuunikiridwa koona komanso chiyembekezo chodzakhala ndi tsogolo losangalatsa zedi limene Mulungu wakonzera anthu omvera.—Chivumbulutso 21:1-5.
“Kuunika Kunadza ku Dziko Lapansi”
14. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tidzaone kukwaniritsidwa kwa maulosi ogwira mtima a m’Baibulo?
14 Malemba amasonyeza bwino lomwe kuti Yesu Kristu akulamulira monga Mfumu tsopano. Popeza kuti anayamba kulamulirako mu 1914, maulosi ogwira mtima adzakwaniritsidwabe. Kuti tidzaone kukwaniritsidwa kwake, tiyenera kukhala anthu ofatsa osonyeza chikhulupiriro mwa Yesu Kristu, kulapa ntchito zauchimo ndi machimo ochitidwa mosadziŵa. Inde, awo amene amakonda mdima sadzalandira moyo wosatha. Yesu anati: “Chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zawo zinali zoipa. Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake. Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.”—Yohane 3:19-21.
15. Kodi chidzachitika n’chiyani ngati sitisamala chipulumutso chimene Mulungu watikonzera kudzera mwa Mwana wake?
15 Kuunika kwauzimu kunadza m’dziko kudzera mwa Yesu, ndipo kum’mvetsera n’kofunika kwambiri. Paulo analemba kuti: “Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m’manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana, koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika woloŵa nyumba wa zonse.” (Ahebri 1:1, 2) Kodi chidzachitika n’chiyani ngati tikana chipulumutso chimene Mulungu watikonzera kudzera mwa Mwana wake? Paulo anapitiriza kuti: “Ngati mawu adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, ndipo cholakwira chilichonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama, tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife; pochita umboni pamodzi nawo Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogaŵira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.” (Ahebri 2:2-4) Inde, Yesu ndi wofunika kwambiri pa kulengezedwa kwa mawu aulosi.—Chivumbulutso 19:10.
16. N’chifukwa chiyani tingakhalire ndi chikhulupiriro chonse m’maulosi onse a Yehova Mulungu?
16 Monga momwe taonera, Petro anati: “Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pachokha.” Anthu paokha sangapereke ulosi woona, koma tingakhale ndi chikhulupiriro chonse m’maulosi onse a Mulungu. Ameneŵa amachokera kwa Yehova Mulungu iyemwini. Mwa mzimu woyera, iye wapangitsa atumiki ake kumvetsa mmene maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwira. Ndithudi, ndife othokoza kwambiri Yehova kuti taona kukwaniritsidwa kwa ochuluka mwa maulosi otereŵa chiyambire m’chaka cha 1914. Ndipo ndife otsimikiza zedi kuti maulosi otsalawo okhudza kutha kwa dongosolo loipali la zinthu adzakwaniritsidwa. N’kofunika kuti tizilabadirabe maulosi a Mulungu pamenenso tikuwalitsa kuunika kwathu. (Mateyu 5:16) Tikuthokozatu kwambiri kuti Yehova akuchititsa ‘kuunika kuti kutiwalire mumdima wa ndiweyani’ womwe ukukuta dziko lapansi lerolino!—Yesaya 58:10.
17. N’chifukwa chiyani tikufunikira kuunika kwauzimu kochokera kwa Mulungu?
17 Kuunika kwa dzuŵa kumapangitsa kuti tithe kuona. Kumapangitsanso kuti zomera zimene zimatipatsa chakudya chochuluka zikule bwino. Palibe chimene tingachite popanda kuunika kwa dzuŵaku. Nanga bwanji za kuunika kwauzimu? Kumatipatsa chitsogozo ndi kutisonyeza za m’tsogolo monga momwe kunaloseledwera m’Mawu a Mulungu, Baibulo. (Salmo 119:105) Mwachikondi, Yehova Mulungu ‘amatumiza kuunika kwake ndi choonadi.’ (Salmo 43:3) Ndithudi tiyenera kuthokoza kwambiri kaamba ka zogaŵira zimenezi. Chotero tiyeni tichite zonse zomwe tingathe kuti kuunika kwa “chidziŵitso cha ulemerero wa Mulungu” kuloŵe mwa ife kotero kuti kuwalire mumtima wathu wophiphiritsa.—2 Akorinto 4:6; Aefeso 1:18.
18. Kodi Nthanda ya Yehova ndi yokonzeka kuchitanji tsopano?
18 Ha! Ndifetu odala kwabasi kudziŵa kuti mu 1914, Yesu Kristu, Nthandayo, anatulukira m’chilengedwe chonse nayamba kukwaniritsa masomphenya a kusandulika! Nthanda ya Yehova ilipo tsopano, yokonzeka kuchita chifuno cha Mulungu pokwaniritsa kusandulika kuja mowonjezeka, mwa “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Dongosolo lakale lino litachotsedwapo, Yehova adzakwaniritsa lonjezo lake la “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” mmene tidzam’tamanda kosatha monga Ambuye Mfumu yachilengedwe chonse ndi Mulungu wa ulosi woona. (2 Petro 3:13) Mpaka pamene tsiku lalikululo lidzafika, tiyeni tipitirizebe kuyenda m’kuunika kwaumulungu mwa kulabadira mawu aulosi a Mulungu.
Kodi Mungayankhe Motani?
• Kodi kusandulika kwa Yesu mungakulongosole motani?
• Kodi kusandulika kukumangirira motani chikhulupiriro?
• Kodi Nthanda ya Yehova ndiye ndani kapena n’chiyani, ndipo inatuluka liti?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kulabadira mawu aulosi a Mulungu?
[Chithunzi patsamba 13]
Kodi mungalongosole tanthauzo la kusandulika?
[Chithunzi patsamba 15]
Nthanda yatuluka kale. Kodi mukudziŵa kuti yatuluka motani komanso liti?