Phunzitsani Mwanzeru Ndi Mosonkhezera
“Mtima wa wanzeru upangitsa pakamwa pake kusonyeza nzeru, ndipo uwonjezera chisonkhezero pa milomo yake.”—MIYAMBO 16:23, NW.
1. Kodi n’chifukwa chiyani kuphunzitsa Mawu a Mulungu si kungofotokoza mfundo chabe?
CHOLINGA chathu monga aphunzitsi a Mawu a Mulungu ndicho kuunikira maganizo a ophunzira athu ndiponso mitima yawo. (Aefeso 1:18) Chotero kuphunzitsa si kungofotokoza mfundo. Miyambo 16:23 (NW) imati: “Mtima wa wanzeru upangitsa pakamwa pake kusonyeza nzeru, ndipo uwonjezera chisonkhezero pa milomo yake.”
2. (a) Kodi kukopa kumatanthauzanji? (b) Kodi n’zotheka motani kuti Akristu onse akhale aphunzitsi osonkhezera?
2 Mtumwi Paulo anagwiritsadi ntchito pulinsipulo limeneli pochita ntchito yake yophunzitsa. Pamene anali ku Korinto, “anafotokozera m’sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Ahelene.” (Machitidwe 18:4) Malinga ndi umboni wina, liwu lachigiriki lotembenuzidwa panopo kuti “kopa” limatanthauza “kusintha malingaliro a munthu mwa kumusonkhezera ndi mfundo zomveka kapena khalidwe.” Pogwiritsa ntchito mfundo zokhutiritsa, Paulo ankatha kusonkhezera anthu kuti asinthe malingaliro awo. Luso lake la kukopa linali labwino kwambiri moti adani ake anali kumuopa. (Machitidwe 19:24-27) Ngakhale zinali motero, Paulo pophunzitsa sanasonyeze kuti limenelo linali luso laumunthu. Iye anauza Akorinto kuti: “Mawu anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mawu okopa a nzeru, koma m’chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu; kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m’nzeru ya anthu, koma mumphamvu ya Mulungu.” (1 Akorinto 2:4, 5) Popeza kuti Akristu onse amathandizidwa ndi mzimu wa Yehova Mulungu, onse angakhale aphunzitsi osonkhezera. Koma motani? Tiyeni tione zina mwa njira zophunzitsira mogwira mtima.
Mvetserani Bwino
3. Kodi n’chifukwa chiyani nzeru n’zofunika pophunzitsa ena, ndipo wophunzira Baibulo tingamufike motani pamtima?
3 Njira yoyamba yophunzitsira bwino ndiyo kumvetsera, osati kuyankhula. Monga momwe taonera pa Miyambo 16:23, kuti tikhale osonkhezera tiyenera kukhala anzeru. Ndithudi Yesu ankawadziŵa bwino anthu amene anali kuwaphunzitsa. Yohane 2:25 amati: “Anadziŵa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.” Koma kodi tingadziŵe bwanji zimene zili m’mitima ya anthu amene tikuphunzitsa? Njira imodzi ndiyo mwa kukhala womvetsera bwino. Yakobo 1:19 amati: “Munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula.” N’zoona kuti si anthu onse amene amafotokoza zakukhosi kamodzi n’kamodzi. Pamene ophunzira athu a Baibulo afika potsimikizira kuti timawaderadi nkhaŵa, angafotokoze zakukhosi mosavuta. Nthaŵi zambiri, mafunso okoma mtima komanso anzeru angatithandize kufika pamtima ndi ‘kutunga’ mawu awo amenewo.—Miyambo 20:5.
4. Kodi n’chifukwa chiyani akulu achikristu ayenera kumvetsera bwino?
4 Makamaka akulu achikristu ayenera kumvetsera kwambiri. M’pokhapo pamene ‘angadziŵedi mayankhidwe awo a kwa yense akatani.’ (Akolose 4:6) Miyambo 18:13 imachenjeza kuti: “Wobwezera mawu asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi.” Abale ena aŵiri n’cholinga chabwino anapatsa mlongo wina uphungu wonena za kutsatira za dziko chifukwa chakuti mlongoyo sanapezeke pamisonkhano ina. Mlongoyo anakhumudwa kwambiri kuti akuluwo sanamufunse chifukwa chimene sanapezekerepo. Iye anali atangochitidwa kumene opaleshoni. Ndiye n’kofunika chotani nanga kumvetsera tisanapereke uphungu!
5. Kodi akulu angathetse motani mikangano imene imabuka pakati pa abale?
5 Kwa akulu, nthaŵi zambiri kuphunzitsa kumaphatikizapo kupatsa ena uphungu. Kumvetsera n’kofunika kwambiri pamenepanso. Kumvetsera n’kofunika makamaka pakakhala kusamvana pakati pa Akristu. Akulu angatsanzire ‘Atate amene aweruza mopanda tsankhu’ pokhapokha atamvetsera. (1 Petro 1:17) Pankhani ngati zimenezi, nthaŵi zambiri pamakhala kupsetsana mtima, ndipo ndi bwino kuti mkulu azikumbukira uphungu wa pa Miyambo 18:17 umene umati: “Woyamba kudzinenera ayang’anika wolungama; koma mnzake afika namuululitsa zake zonse.” Mphunzitsi wabwino adzamvetsera kwa abale onse aŵiri. Mwa kupereka pemphero, amathandiza kuti pakhale mtendere. (Yakobo 3:18) Pakakhala kupsetsana mtima, anganene kuti mbale aliyense amufotokozere zakukhosi mwachindunji, m’malo moti aŵiriwo azikangana. Mwa kufunsa mafunso oyenera, mkuluyo angadziŵe bwino mmene nkhaniyo ilili. Nthaŵi zambiri amapeza kuti kusafotokozerana bwino zinthu, osati kuipa mtima, n’kumene kumachititsa mikanganoyo. Koma ngati pali mapulinsipulo a Baibulo amene aswedwa, mphunzitsi wachikondi tsopano angalangize mwanzeru, atamva zonena za anthu onse aŵiri.
Kufunika kwa Kufeŵetsa Zinthu
6. Kodi Paulo ndi Yesu anapereka chitsanzo chotani cha kufeŵetsa zinthu pophunzitsa?
6 Kufeŵetsa zinthu ndilo luso linanso lofunika pophunzitsa. Inde, timafuna kuti ophunzira Baibulo ‘azindikire pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama [kwa choonadi] n’chiyani.’ (Aefeso 3:18, 19) Pali mbali zina za chiphunzitso cha m’Baibulo zimene zili zosangalatsa komanso zovuta nthaŵi zambiri. (Aroma 11:33) Ngakhale zili motero, pamene Paulo analalikira kwa Agiriki, iye anagogomezera uthenga wosavuta kumva wa ‘Kristu wopachikidwa.’ (1 Akorinto 2:1, 2) Yesunso ankalalikira m’njira yosavuta kumva ndi yokopa. Pa Ulaliki wake wa pa Phiri, iye sanagwiritse ntchito mawu apatali. Komabe, ulalikiwo uli ndi zina mwa mfundo zazikulu kwambiri za choonadi zimene zinanenedwapo.—Mateyu, machaputala 5-7.
7. Kodi zinthu tingazifeŵetse motani pochititsa maphunziro a Baibulo?
7 Ifenso tikhoza kufeŵetsa zinthu pophunzitsa maphunziro a Baibulo. Motani? Mwa kusumika maganizo pa “zinthu zofunika kwambiri.” (Afilipi 1:10, NW) Pofotokoza nkhani zikuluzikulu, tiyenera kuyesa kuzifotokoza m’mawu osavuta. Tiyenera kusumika maganizo pa malemba aakulu m’malo moyesa kuŵerenga ndi kukambirana lemba lililonse la m’Baibulo limene lasonyezedwa m’chofalitsa. Zimenezi zimafuna kuti ifeyo tikhale okonzekera bwino. Tiyenera kupeŵa kutchulira wophunzira mfundo zambirimbiri, tikumapeŵa kupambutsidwa ndi nkhani zosafunika kwenikweni. Ngati wophunzira ali ndi funso lomwe silikukhudzana mwachindunji ndi nkhani yomwe tikuphunzira, mwanzeru tinganene kuti tidzakambirana funsolo titamaliza phunzirolo.
Kugwiritsa Ntchito Bwino Mafunso
8. Kodi ndi motani mmene Yesu anagwiritsira ntchito bwino mafunso?
8 Luso lina la kuphunzitsa ndilo kufunsa mafunso othandiza. Yesu Kristu anagwiritsa ntchito kwambiri mafunso pophunzitsa. Mwachitsanzo, Yesu anafunsa Petro kuti: “Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana awo kodi, kapena kwa akunja? Ndipo mmene iye anati, Kwa akunja, Yesu ananena kwa iye, Chifukwa chake anawo ali aufulu.” (Mateyu 17:24-26) Pokhala Mwana wobadwa yekha wa Iye amene amalambiridwa pakachisi, ndithudi Yesu sanakhudzidwe ndi lamulo lokhoma msonkho wa pakachisi. Koma Yesu anaphunzitsa choonadi chimenechi mwa kugwiritsa ntchito bwino mafunso. Chotero Yesu anathandiza Petro kufika pa lingaliro lolondola malinga ndi chidziŵitso chimene Petroyo anali nacho kale.
9. Kodi mafunso tingawagwiritse ntchito motani pa maphunziro a Baibulo?
9 Tingagwiritse ntchito bwino mafunso pa maphunziro a Baibulo. Wophunzira akaphonya yankho, pangakhale chilakolako chofuna kumuuza lolondola, koma kodi lidzakhazikikadi m’maganizo mwake? Nthaŵi zambiri kumakhala bwino kutsogolera wophunzirayo ku mfundo yolondola mwa kumufunsa mafunso. Mwachitsanzo, ngati akuvutika kumvetsa chifukwa chimene Mulungu ayenera kumutchulira dzina, tingamufunse kuti, ‘Kodi dzina lanu ndi lofunika kwa inuyo? . . . Chifukwa chiyani? . . . Mungamve bwanji ngati wina akukana kukuitanani ndi dzina lanu? . . . Kodi si zomveka kuti Mulungu amafuna kuti tidzimutchula dzina lake?’
10. Kodi akulu angagwiritse ntchito motani mafunso pothandiza anthu amene ali ndi chisoni mumtima?
10 Akulunso angagwiritse ntchito bwino mafunso pobusa gulu. Ambiri mumpingo akumana ndi masautso ambirimbiri m’dziko la Satanali ndipo angamadzimve kuti ndi odetsedwa ndi osakondedwa. Mkulu angakambirane ndi munthu wotero mwa kunena kuti: ‘Ngakhale mukunena kuti mukudzimva kukhala wodetsedwa, kodi Yehova amakuonani motani? Ngati Atate wathu wachikondi wakumwamba analola Mwana wake kufa ndi kukuperekerani dipo, kodi zimenezo sizikutanthauza kuti Mulungu amakukondani?’—Yohane 3:16.
11. Kodi mafunso osayembekeza yankho ndi antchito yanji, ndipo tingawagwiritse ntchito motani pokamba nkhani poyera?
11 Mafunso osayembekezera yankho ndi njira inanso yophunzitsira bwino. Omvetsera sapereka mayankho, koma mafunsowo amawathandiza kusinkhasinkha. Nthaŵi zambiri aneneri akale anali kufunsa mafunso otero pofuna kusonkhezera omvetsera awo kuganizapo kwambiri. (Yeremiya 18:14, 15) Yesu anagwiritsa ntchito bwino mafunso osayembekezera yankho amenewo. (Mateyu 11:7-11) Mafunso otero amakhala ogwira mtima kwambiri makamaka pokamba nkhani poyera. M’malo mongouza omvera kuti ayenera kuchita zinthu ndi mtima wonse kuti akondweretse Yehova, kungakhale kogwira mtima kwambiri kufunsa kuti, ‘Ngatidi sitichita utumiki wathu ndi mtima wonse, kodi Yehova adzakondwera?’
12. Kodi kufunsa mafunso ofuna kudziŵa lingaliro la munthu n’kofunika motani?
12 Mafunso ofuna kudziŵa lingaliro la wina n’ngothandiza pofuna kuona ngati wophunzira Baibulo akukhulupiriradi zimene akuphunzira. (Mateyu 16:13-16) Wophunzira angayankhe molondola kuti chisembwere n’choipa. Koma bwanji osafufuzabe ndi mafunso monga akuti, Inuyo mumauona bwanji muyezo wa Mulungu wa makhalidwe? Kodi mumaganiza kuti n’ngwokhwimitsa zinthu momkitsa? Kodi munganene kuti kutsatira kapena kusatsatira miyezo ya Mulungu ndi nkhanidi yaikulu?
Mafanizo Ofika Pamtima
13, 14. (a) Kodi kufanizira chinthu kumatanthauzanji? (b) Kodi n’chifukwa chiyani mafanizo abwino amagwira mtima?
13 Njira inanso yofikira omvera ndi ophunzira Baibulo pamtima ndiyo mwa kugwiritsa ntchito mafanizo ogwira mtima. Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “fanizo” kwenikweni amatanthauza “kuika pambali pa, kapena pamodzi.” Pamene mufanizira, mufotokoza chinachake mwa ‘kuchiika pambali pa’ chinachake chofanana nacho. Mwachitsanzo, Yesu anafunsa kuti: “Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? Kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani?” Poyankha, Yesu anatchula mbewu ya mpiru yodziŵikayo.—Marko 4:30-32.
14 Aneneri a Mulungu anagwiritsa ntchito mafanizo amphamvu ambiri. Pamene Asuri, amene anali atatumikira monga chiŵiya cha Mulungu cholangira Aisrayeli, anayamba kuchita nkhanza popanda chifukwa, Yesaya anavumbula kudzikuza kwawo mwa fanizo ili: “Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza.” (Yesaya 10:15) Pophunzitsa ena, Yesu nayenso anagwiritsa ntchito kwambiri mafanizo. Akuti “sanalankhula nawo wopanda fanizo.” (Marko 4:34) Mafanizo abwino n’ngothandiza kwambiri chifukwa chakuti amaloŵa m’maganizo ndi mumtima momwe. Amalola omvetsera kuloŵetsa chidziŵitso chatsopano mosavuta mwa kuchiyerekezera ndi chinachake chimene amachidziŵa.
15, 16. Kodi n’chiyani chidzapangitsa mafanizo kukhala ogwira mtima kwambiri? Tchulani zitsanzo.
15 Kodi mafanizo ofikadi pamtima tingawagwiritse ntchito motani? Choyamba, fanizo liyenera kufanana ndi chinthu chimene chikufotokozedwa. Ngati zinthu zoyerekezeredwazo si zikufanana kwenikweni, fanizo lidzasokoneza omvetsera m’malo mowaunikira. N’cholinga chabwino, wokamba nkhani wina anayesa kufotokoza kugonjera kwa otsalira odzozedwa kwa Yesu Kristu mwa kuwayerekezera ndi galu wokhulupirika wa panyumba. Koma kodi kufanizira konyazitsa ngati kumeneku kungakhaledi kwabwino? Baibulo limafotokoza lingaliro lofananalo m’njira yosangalatsa kwambiri ndiponso yolemekezeka. Limayerekezera otsatira odzozedwa 144,000 a Yesu ndi “mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.”—Chivumbulutso 21:2.
16 Mafanizo amakhala ogwira mtima kwambiri pamene akhudzana ndi zochitika m’miyoyo ya anthu. Fanizo la Natani la mwana wa nkhosa yemwe anaphedwa linam’gwira mtima Mfumu Davide chifukwa chakuti anali kukonda nkhosa, pokhala anali mbusa wa nkhosa adakali mnyamata. (1 Samueli 16:11-13; 2 Samueli 12:1-7) Fanizolo likadanena za ng’ombe yaimuna, mwina silikadam’gwira mtima chotero. Mofananamo, mafanizo ozikidwa pa zinthu zakuya za sayansi kapena pa mbiri yakale yosadziŵika bwino sangakhale othandiza kwenikweni kwa omvetsera athu. Yesu anazika mafanizo ake pa zochitika zatsiku ndi tsiku. Anakamba za zinthu zodziŵika monga nyali, mbalame za kumwamba, ndi maluŵa akuthengo. (Mateyu 5:15, 16; 6:26, 28) Omvetsera a Yesu anali kuzigwirizanitsa mosavuta zinthu zimenezi.
17. (a) Kodi mafanizo athu tingawazike pachiyani? (b) Kodi mafanizo amene ali mu zofalitsa zathu tingawagwirizanitse motani ndi mikhalidwe ya ophunzira athu?
17 Mu utumiki wathu timakhala ndi mipata yambiri yogwiritsa ntchito mafanizo osavuta kumva komanso ogwira mtima. Khalani maso. (Machitidwe 17:22, 23) Mwina fanizo lingazikidwe pa ana a womvetserayo, nyumba yake, ntchito yake, kapena zimene amakonda kuchita. Kapena malinga ndi mmene timamudziŵira wophunzira Baibuloyo, tingafutukule mafanizo operekedwa m’buku limene tikuphunziralo. Mwachitsanzo, tiyeni titenge fanizo logwira mtima limene lili mu ndime 14 ya mutu 8 m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Limanena za kholo lachikondi limene lanenezedwa ndi mnansi wake. Tingaganizire mmene tingagwirizanitsire fanizolo ndi mikhalidwe ya wophunzira Baibulo amene ali kholo.
Kuŵerenga Malemba Mwaluso
18. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kumaŵerenga mosaphonyaphonya?
18 Paulo analangiza Timoteo kuti: “Usamalire kuŵerenga, kuchenjeza, kulangiza.” (1 Timoteo 4:13) Popeza kuti Baibulo ndilo maziko a kuphunzitsa kwathu, kuliŵerenga mosaphonyaphonya n’kopindulitsa. Alevi anali ndi mwayi woŵerengera anthu a Mulungu Chilamulo cha Mose. Kodi anali kuphonyaphonya pochiŵerenga kapena kuchiŵerenga ndi liwu limodzi losasintha? Ayi, pa Nehemiya 8:8, Baibulo limati: “Naŵerenga iwo m’buku m’chilamulo cha Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa choŵerengedwacho.”
19. Kodi tingawongolere motani kaŵerengedwe kathu ka Malemba?
19 Amuna ena achikristu amene amakamba bwino nkhani amalephera kuŵerenga bwino. Kodi angawongolere motani? Mwa kukonzekera. Inde, mwa kuŵerenga mokweza mobwerezabwereza mpaka atayamba kuŵerenga mosaphonyaphonya. Ngati pali makaseti a m’chinenero chanu a Baibulo, n’kwanzeru kumamvetsera mmene woŵerengayo akugogomezerera ganizo ndi kusinthasintha mawu ndi kumvetsera mmene mayina ndi mawu achilendo amatchulidwira. Mwa kukonzekera, ngakhale mayina monga Kangazakufunkhafulumirakusakaza angaŵerengedwe mosavuta ndithu.—Yesaya 8:1.
20. Kodi ‘tingadzipenyerere tokha ndi chiphunzitsocho’ motani?
20 Monga anthu a Yehova, tili ndi mwayi waukulu chotani nanga pogwiritsidwa ntchito monga aphunzitsi! Chotero, aliyense wa ife asauone mopepuka udindo umenewo. Tiyeni ‘tidzipenyerere tokha ndi chiphunzitsocho.’ (1 Timoteo 4:16) Tingakhale aphunzitsi abwino mwa kumvetsera bwino, mwa kufeŵetsa zinthu, mwa kufunsa mafunso othandiza, mwa kugwiritsa ntchito mafanizo ogwira mtima, ndiponso mwa kuŵerenga malemba mwaluso. Tonsefe tipinduletu ndi maphunziro amene Yehova akupereka kudzera mwa gulu lake, popeza kuti zimenezo zingatithandize kukhala ndi “lilime la ophunzira.” (Yesaya 50:4) Mwa kugwiritsa ntchito bwino ziwiya zonse zoperekedwa kuti tizigwiritse ntchito mu utumiki, kuphatikizapo mabolosha, makaseti, ndi makaseti a vidiyo, tingaphunzire kuphunzitsa mwanzeru ndi mosonkhezera.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi kumvetsera bwino kungatithandize motani pophunzitsa?
◻ Kodi Paulo ndi Yesu tingawatsanzire motani pa kufeŵetsa zinthu pophunzitsa?
◻ Kodi ndi mafunso otani amene tingagwiritse ntchito pophunzitsa ena?
◻ Kodi ndi mafanizo otani amene amagwira mtima kwambiri?
◻ Kodi luso lathu monga oŵerenga poyera tingaliwongolere motani?
[Chithunzi patsamba 16]
Mphunzitsi wabwino amamvetsera kuti apeze nzeru
[Zithunzi patsamba 18]
Yesu anazika mafanizo ake pazinthu zatsiku ndi tsiku