Khalani Odzichepetsadi
“Mudzapulumutsa anthu osautsidwa [“odzichepetsa,” NW].”—2 SAMUELI 22:28.
1, 2. Kodi olamulira ambiri a dzikoli akhala ofanana m’njira yotani?
ZILIZA zazikulu ngati mapiri za pa manda a mafumu a ku Aigupto zimaikira umboni woti olamulira akalekale adzikoli analidi anthu odziwika. Anthu enanso amene anali odziwika m’mbiri ya anthu ndi Sanakeribu wa ku Asuri, Alesandro Wamkulu wa ku Girisi, ndiponso Juliasi Kaisara wa ku Roma. Atsogoleri onsewa anali ofanana m’njira imodzi. Mbiri yawo sisonyeza kuti anali anthu odzichepetsadi.—Mateyu 20:25, 26.
2 Kodi pa olamulira tatchulawa mungaganize kuti analipo wina amene ankakonda kufunafuna anthu wamba ovutika a mu ufumu wake kuti awalimbikitse? Ayi simunganize choncho. Ndipo palibe amene angaganize kuti winawake mwa olamulirawa ankapita ku nyumba zonyozeka za amphawi oponderezedwa kuti akawalimbikitse. Olamulira amenewa n’ngosiyana kwambiri ndi Yehova Mulungu, yemwe ali Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse.
Chitsanzo Choposa Zonse cha Kudzichepetsa
3. Kodi Wolamulira Wamkulu amawachitira zotani anthu amene amawalamulira?
3 Ngakhale kuti Yehova n’ngwamkulu kwambiri moti anthufe sitingathe n’komwe kumvetsa, ‘maso ake ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.’ (2 Mbiri 16:9) Nanga Yehova amatani akaona olambira ake odzichepetsa amene akusautsidwa ndi ziyeso zosiyanasiyana? Tinganene kuti iye ‘amakhala’ ndi anthu otere mwa mzimu wake woyera pofuna “kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.” (Yesaya 57:15) Motero anthuwo akatsitsimulidwa amayambiranso kumutumikira mosangalala. Apatu Mulungu amasonyeza kudzichepetsa kwakukulu.
4, 5. (a) Kodi wamasalmo ankaona motani kalamuliridwe ka Mulungu? (b) Kodi mawu akuti Mulungu ‘amadzichepetsa’ kuti athandize “wosauka” amatanthauza chiyani?
4 Palibe munthu wina aliyense m’chilengedwe chonse amene anadzichepetsapo ngati mmene wadzichepetsera Ambuye Mfumu pofuna kuthandiza anthu ochimwafe. M’pake wamasalmo kulemba kuti: “Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse, ulemerero wake pamwambamwamba. Akunga Yehova Mulungu wathu ndani? Amene akhala pamwamba patali, nadzichepetsa apenye zam’mwamba ndi za pa dziko lapansi. Amene autsa wosauka kum’chotsa kufumbi, nakweza waumphawi kum’chotsa kudzala.”—Salmo 113:4-7.
5 Yehova ndi wolungama ndiponso woyera motero alibe maganizo alionse ‘odzikuza.’ (Marko 7:22, 23) Koma mawu oti “kudzichepetsa” a pa lemba la Salmo 113:6 amatanthauzanso kudzitsitsa n’kufika pa mlingo wa munthu amene ali wapansi, pamene ukuchita zinthu ndi munthuyo. Mmenemutu ndi mmene Mulungu wathu alili. Iye amasamalira mwachikondi anthu amene amamulambira ngakhale kuti anthuwo ndi opanda ungwiro.—2 Samueli 22:36.
Chifukwa Chomwe Yesu Analili Wodzichepetsa
6. Kodi chinthu chachikulu kwambiri chosonyeza kudzichepetsa chimene Yehova anachita n’chiyani?
6 Chinthu chachikulu kwambiri chimene Mulungu anachita chosonyeza kudzichepetsa ndiponso chikondi ndicho kutumiza Mwana wake woyamba wokondedwa kuti adzabadwe padziko lapansi n’kuleredwa ngati munthu pofuna kutipulumutsa. (Yohane 3:16) Yesu anatiphunzitsa choonadi chokhudza Atate wake wakumwamba ndipo kenaka anapereka moyo wake wangwiro kuti ‘achotse tchimo la dziko lapansi.’ (Yohane 1:29; 18:37) Yesu anatsanzira ndendende makhalidwe a Atate wake, kuphatikizapo khalidwe la Yehova la kudzichepetsa, motero anachita mofunitsitsa zonse zimene Mulungu anam’tuma. Palibe mngelo kapena munthu winanso amene anasonyeza chitsanzo chabwino zedi cha kudzichepetsa kuposa Yesu. Komabe si onse amene anayamikira kudzichepetsa kwa Yesuku, ndipo adani ake ankamuona ngati “munthu wachabechabe pakati pa anzake.” (Danieli 4:17, [4:14, Malembo Oyera]) Komabe, mtumwi Paulo anazindikira kuti Akristu anzake ayenera kutsanzira Yesu motero ayenera kudzichepetsa akamachita zinthu ndi Akristu anzawo.—1 Akorinto 11:1; Afilipi 2:3, 4.
7, 8. (a) Kodi Yesu anaphunzira bwanji kudzichepetsa? (b) Kodi Yesu ananena mawu oti chiyani kwa anthu ofuna kuyamba kumutsatira?
7 Paulo anatchulapo za chitsanzo chapamwamba cha Yesuchi polemba kuti: “Mukhale nawo mtima m’kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, ameneyo, pokhala nawo maonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa.”—Afilipi 2:5-8.
8 Ena angafunse kuti ‘Kodi Yesu anaphunzira bwanji kudzichepetsa?’ Anatero pokhala kwa zaka zosawerengeka ndi Atate wake wakumwamba, ndipo panthawiyi iye anali “mmisiri” wamkulu polenga zinthu zonse. (Miyambo 8:30) Adamu ndi Hava atapandukira Mulungu m’munda wa Edene, Mwana Woyamba Kubadwa wa Mulungu anaona kudzichepetsa kwa Atate wake poona zimene anachita nawo anthu ochimwawo. Motero, Yesu atabwera padziko lapansi anasonyeza kudzichepetsa kwa Atate wake n’kunena mawu otilimbikitsa akuti: “Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.”—Mateyu 11:29; Yohane 14:9.
9. (a) Kodi Yesu ankawakondera chiyani ana? (b) Kodi Yesu anaphunzitsa phunziro lotani pogwiritsira ntchito kamwana?
9 Popeza kuti Yesu anali wodzichepetsadi, tiana sitimachita naye mantha, koma timam’konda. Nayenso anasonyeza kuti ankakonda ana ndipo ankacheza nawo. (Marko 10:13-16) Kodi Yesu ankawakondera chiyani ana? Anawotu anali ndi makhalidwe abwino omwe ena mwa ophunzira a Yesu achikulire ankavutika kukhala nawo nthawi zonse. Aliyense amadziwa kuti ana aang’ono amaona anthu aakulu kuti n’ngowaposa. N’chifukwa chaketu ana amakonda kufunsa mafunso ambirimbiri. Inde, poyerekezera ndi anthu aakulu ambiri, ana amamvera pophunzitsidwa ndipo kawirikawiri sakhala odzikuza. Panthawi ina, Yesu anatenga mwana n’kuuza ophunzira ake kuti: “Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.” Ndiye anapitiriza kunena kuti: “Yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 18:3, 4) Yesu ananena lamulo lakuti: “Aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.”—Luka 14:11; 18:14; Mateyu 23:12.
10. Kodi ndi mafunso otani amene tikambirane?
10 Mawu amenewa amabukitsa mafunso ofunika. Kukhala wodzichepetsadi ndi mbali ya makhalidwe ofunika kukhala nawo kuti tidzakhale ndi moyo wosatha, koma kodi n’chifukwa chiyani nthawi zina Akristu zimawavuta kukhala odzichepetsa? N’chifukwa chiyani zimativuta kusiya mtima wodzitukumula, n’kuchita zinthu modzichepetsa tikakumana ndi mayesero? Ndipo kodi n’chiyani chingatithandize kukhala odzichepetsadi?—Yakobo 4:6, 10.
Chifukwa Chimene Kudzichepetsa Kumakhalira Kovuta
11. N’chifukwa chiyani zili zosadabwitsa kuti kukhala odzichepetsa kumativuta?
11 Ngati mumavutika kukhala munthu wodzichepetsa, dziwani kuti si inu nokha amene muli ndi vuto limeneli. Kale mu 1920, magazini ino inalongosola malangizo a m’Baibulo onena za kufunika kokhala wodzichepetsa, ndipo inati: “Podziwa kuti Ambuye amaona kuti kudzichepetsa n’kofunika kwambiri, zimenezi ziyenera kulimbikitsa ophunzira onse oona kukhala ndi khalidwe limeneli tsiku lililonse.” Kenaka magaziniyi inavomereza kuti: “Ngakhale kuti Malemba amatilimbikitsa m’njira zosiyanasiyana pankhaniyi, kupanda ungwiro kwa anthufe kumachititsa anthu otsatira njira ya Ambuye kuvutika kwambiri kusonyeza khalidwe limeneli, mwina kuposa makhalidwe ena onse.” Mawu amenewa akusonyeza chifukwa chimodzi chimene chimachititsa Akristu kuvutika kuti akhale odzichepetsa. Chifukwa chake n’chakuti kupanda ungwiro kwa anthufe kumatichititsa kufuna kutamidwa. Ichi n’chifukwa choti tinachokera kwa makolo ochimwa, Adamu ndi Hava, amene anatengeka ndi zinthu zongokomera iwowo.—Aroma 5:12.
12, 13. (a) Kodi n’chiyani m’dzikoli chimachititsa kuti Akristu azivutika kukhala odzichepetsa? (b) Ngakhale kuti kukhala odzichepetsa n’kovuta pakokha koma kodi ndani amachititsa kuti kuzitivuta kwambiri?
12 Chifukwa china chimene zingativutire kukhala odzichepetsa n’chakuti dziko tikukhalamoli limalimbikitsa anthu kuti aziyesetsa kukhala oposa ena. Chimodzi mwa zolinga zazikulu zimene dzikoli limalimbikitsa anthu kukhala nazo ndicho “chilakolako cha thupi [lauchimo] ndi chilakolako cha maso, [ndiponso] matamandidwe a moyo.” (1 Yohane 2:16) Anthu otsatira Yesu sayenera kulola kuti zilakolako zadzikozi ziwalowerere, koma ayenera kukhala a diso lakumodzi ndi kumangoganizira zochita chifuniro cha Mulungu basi.—Mateyu 6:22-24, 31-33; 1 Yohane 2:17.
13 Chifukwa chachitatu chimene kudzichepetsa kulili kovuta n’chakuti amene anayambitsa kudzikuza, yemwe ali Satana Mdyerekezi, ndiye akulamulira dzikoli. (2 Akorinto 4:4; 1 Timoteo 3:6) Satana amalimbikitsa makhalidwe ake oipa. Mwachitsanzo, Satanayu anafuna kuti Yesu alambire iyeyo kuti amupatse “mayiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo.” Pakuti Yesu anali wodzichepetsa nthawi zonse, iye anakaniratu zimene Mdyerekezi ankam’patsazi. (Mateyu 4:8, 10) Masiku anonso Satana amayesa Akristu powachititsa kufuna kukhala aulemerero. Komatu Akristu odzichepetsa amayesetsa kutsatira chitsanzo cha Yesu, popereka chitamando ndiponso ulemu kwa Mulungu.—Marko 10:17, 18.
Kukhala Wodzichepetsadi
14. Kodi kudzichepetsa kwachinyengo n’kutani?
14 M’kalata yake yopita kwa Akolose, mtumwi Paulo anachenjeza kuti si bwino kudzichepetsa mongofuna kudzionetsera pamaso pa anthu. Paulo ananena kuti uku n’kudzichepetsa kwachinyengo. Anthu amene amadzichepetsa mongodzionetsera si anthu amakhalidwe auzimu. Koma amasonyeza kuti kwenikweni iwo ndi anthu ‘odzitukumula.’ (Akolose 2:18, 23) Yesu anapereka zitsanzo za anthu odzichepetsa mwachinyengowa. Iye anadzudzula Afarisi chifukwa choti ankapemphera modzionetsera ndipo akamasala kudya ankakhala ndwii pofuna kuti anthu adziwe kuti akusala kudya. Mosiyana ndi Afarisiwa, ngati tikufuna kuti mapemphero athu a patokha azimvedwa ndi Mulungu, tiyenera kuwanena modzichepetsa.—Mateyu 6:5, 6, 16.
15. (a) Kodi tingatani kuti tikhalebe odzichepetsa? (b) Kodi ena mwa anthu amene ali zitsanzo zabwino za kudzichepetsa ndani?
15 Akristu amathandizidwa kupitiriza kukhala odzichepetsadi poganizira kwambiri za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, omwe ali zitsanzo zabwino koposa za kudzichepetsa. Kuti atero amafunika kuti nthawi zonse aziphunzira Baibulo ndiponso mabuku ofotokoza za m’Baibulo omwe amaperekedwa kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Oyang’anira m’mipingo amafunika kwambiri kumaphunzira Baibulo ndi mabuku olifotokoza ‘kuti mtima wawo usadzikuze pa abale awo.’ (Deuteronomo 17:19, 20; 1 Petro 5:1-3) Taganizirani za zitsanzo zambirimbiri za anthu amene anadalitsidwa chifukwa cha khalidwe lawo lodzichepetsa, monga Rute, Hana, Elisabeti, ndi anthu ena ambiri. (Rute 1:16, 17; 1 Samueli 1:11, 20; Luka 1:41-43) Taganiziraninso zitsanzo za anthu ambiri otchuka amene anakhalabe odzichepetsa potumikira Yehova, monga Davide, Yosiya, Yohane Mbatizi, ndi mtumwi Paulo. (2 Mbiri 34:1, 2, 19, 26-28; Salmo 131:1; Yohane 1:26, 27; 3:26-30; Machitidwe 21:20-26; 1 Akorinto 15:9) Nanga bwanji za zitsanzo zambiri zamakono za anthu odzichepetsa amene tili nawo m’mipingo yathu? Poganizira za zitsanzo zimenezi, Akristu oona amathandizidwa kukhala ‘odzichepetsa’ pochita zinthu ndi ena.—1 Petro 5:5.
16. Kodi utumiki wachikristu umatithandiza bwanji kukhala odzichepetsa?
16 Kuchita utumiki wachikristu nthawi zonse kungatithandizenso kukhala odzichepetsa. Kudzichepetsa kungatithandize kulankhula zogwira mtima tikakumana ndi anthu osawadziwa amene timawapeza polalikira nyumba ndi nyumba ndiponso m’malo ena. Zimakhala choncho makamaka ngati poyambirira eninyumba sanasonyeze chidwi ndi uthenga wa Ufumu kapena ngati anachita chipongwe. Nthawi zambiri anthu amatsutsa zikhulupiriro zathu, ndipo kudzichepetsa kungathandize Mkristu kuyankha mafunso “ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Atumiki ena odzichepetsa a Mulungu asamukira m’madera atsopano ndipo athandiza anthu a zikhalidwe zosiyanasiyana komanso opeza mosiyanasiyana. Atumiki oterewa nthawi zina amafunika kudzichepetsa kuti achite ntchito yovuta yophunzira chinenero chatsopano kuti athandize bwino anthu amene akufuna kuwauza uthenga wabwino. Izitu n’zoyamikika kwambiri.—Mateyu 28:19, 20.
17. Kodi ndi maudindo achikristu otani amene munthu amafunika kukhala wodzichepetsa kuti awakwaniritse?
17 Chifukwa chodzichepetsa, anthu ambiri achita ntchito zawo zachikristu potsogoza kaye zofuna za ena osati zawo. Mwachitsanzo, bambo amene ali Mkristu amafunika kudzichepetsa kuti azitha kukonzekera ndiponso kuchititsa phunziro la Baibulo lopindulitsa ndi ana ake. Kudzichepetsa kumathandizanso ana kulemekeza ndiponso kumvera makolo awo, amene ali opanda ungwiro. (Aefeso 6:1-4) Akazi amene amuna awo ali osakhulupirira nthawi zambiri amayenera kuchita zinthu modzichepetsa kuti athe kukopa amuna awo kuyamba choonadi chifukwa choona ‘mayendedwe awo oyera ndi kuopa kwawo,’ kapena kuti ulemu wawo waukulu. (1 Petro 3:1, 2) Kudzichepetsa ndi chikondi chololera kuvutikira ena zimafunikanso kwambiri kuti tisamalire makolo odwala ndiponso okalamba.—1 Timoteo 5:4.
Kudzichepetsa Kumathetsa Mavuto
18. Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji kuthetsa mavuto?
18 Anthu onse otumikira Mulungu ndi opanda ungwiro. (Yakobo 3:2) Nthawi zina, Mkristu angasiyane maganizo ndi Mkristu mnzake. Winayo angakhale ndi chifukwa chomveka choipidwa ndi zochita za mnzakeyo. Nthawi zambiri, nkhani zotere zingathe kuthetsedwa potsatira malangizo akuti Akristu ayenera “kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso.” (Akolose 3:13) Inde, kutsatira malangizo amenewa sikophweka, koma kudzichepetsa kungam’thandize munthu kuti akwanitse kutero.
19. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikamalankhula ndi munthu amene watikhumudwitsa?
19 Nthawi zina Mkristu angaone kuti zimene mnzake anamulakwira n’zazikulu kwambiri moti sangathe kungozinyalanyaza. Zikatero, ndiye kuti kudzichepetsa kungam’thandize kupita kwa mnzakeyo n’cholinga choti akakhazikitse mtendere. (Mateyu 18:15) Chifukwa chimodzi chimene chimachititsa kuti nkhani zizipitirirabe pakati pa Akristu awiri amene ayambana n’chakuti mwina mmodzi wa iwo kapena awiri onsewo n’ngodzitukumula kwambiri moti satha kuvomereza kulakwa kwawo. Mwinanso Mkristu amene anayamba kufuna kuthetsa nkhaniyo, analoza chala mnzakeyo ngati kuti iyemwini n’ngosalakwa. Mosiyana ndi zimenezi kukhala ndi mtima wodzichepetsadi kungathandize kuthetsa nkhani zambiri zotere.
20, 21. Kodi chinthu chimodzi chothandiza kwambiri kuti tikhale odzichepetsa n’chiyani?
20 Chinthu chofunika kwambiri kuti tikhale odzichepetsa ndicho kupemphera kuti Mulungu atithandize ndiponso kuti atipatse mzimu wake. Koma kumbukirani kuti ‘Mulungu . . . amapatsa chisomo [komanso mzimu wake woyera] kwa odzichepetsa.’ (Yakobo 4:6) Motero ngati mwasemphana maganizo ndi Mkristu mnzanu, pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni kuvomereza modzichepetsa mbali imene inuyo mwalakwa, kaya ndi yaing’ono kapena yaikulu. Ngati winawake wakukhumudwitsani koma kenaka n’kukupepesani moona mtima, inuyo muyenera kudzichepetsa n’kumukhululukira. Ngati zikukuvutani kukhululuka, pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni kuthetsa kamzimu kalikonse kodzikuza kamene katsala mumtima mwanumo.
21 Kumvetsa mfundo yoti kudzichepetsa kumatipindulitsa m’njira zambiri kuyenera kutilimbikitsa kuyamba ndiponso kupitiriza kukhala ndi khalidwe lamtengo wapatali limeneli. Kuti tikwanitse kuchita zimenezi Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu ndiwo ali zitsanzo zathu zabwino kwambiri. Tisaiwale mawu olimbikitsa awa amene Mulungu ananena: “Mphotho ya chifatso [“kudzichepetsa,” NW] ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.”—Miyambo 22:4.
Mfundo Zofunika Kuzisinkhasinkha
• Ndani amene ali zitsanzo zabwino kwambiri za kudzichepetsa?
• N’chifukwa chiyani kudzichepetsa kuli kovuta?
• N’chiyani chingatithandize kukhala odzichepetsa?
• N’chifukwa chiyani kupitiriza kukhala odzichepetsa kuli kofunika kwambiri?
[Chithunzi patsamba 26]
Yesu anali wodzichepetsadi
[Chithunzi patsamba 28]
Dzikoli limalimbikitsa anthu kufuna kukhala apamwamba kuposa ena
[Mawu a Chithunzi]
WHO photo by L. Almasi/K. Hemzǒ
[Chithunzi patsamba 29]
Kudzichepetsa kumatithandiza kulankhula ndi anthu osawadziwa tikamachita utumiki
[Zithunzi patsamba 30]
Nthawi zambiri n’zotheka kuthetsa kusagwirizana maganizo podzichepetsa n’kukwirira nkhaniyo ndi chikondi
[Zithunzi patsamba 31]
Pali njira zambiri zimene Akristu amasonyezera kudzichepetsa