Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Uphungu Wowongolera Wowonjezereka
PAMENE adakali m’nyumba ku Kapernao, chinachake pambali pa kutsutsana kwa atumwiwo konena za amene ali wamkulu koposa chikukambitsiridwa. Chochitika ichinso chingakhale chinawoneka pa kubwerera kwawo ku Kapernao, pamene Yesu sanalipo mwaumwini. Mtumwi Yohane akusimba kuti: “Tinawona wina ali kutulutsa ziwanda m’dzina lanu ndipo tinamletsa, chifukwa satsatana nafe.”
Mwachiwonekere Yohane akuwona atumwiwo monga gulu lapadera, lokhala ndi dzina la ochiritsa. Chotero iye akudzimva kuti munthuyo anali kuchita ntchito zamphamvuzo mosayenera chifukwa iye sanali mbali ya gulu lawo.
Komabe, Yesu akumpatsa uphungu kuti: “Musamamletsa iye pakuti palibe munthu adzachita champhamvu m’dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera ine zoipa; pakuti iye wosatsutsana ndi ife athandizana nafe. Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m’dzina langa chifukwa muli ake a Kristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphoto yake.”
Sichinali choyenera kwa munthu ameneyu kumtsatira Yesu mwa kuthupi kuti akhale kumbali yake. Mpingo Wachikristu unali usanakhazikitsidwe, chotero kusakhala kwake mbali ya gulu lawo sikunatanthauze kuti iye anali wa mpingo wina. Munthuyo ndithudi anali ndi chikhulupiriro m’dzina la Yesu ndipo chotero anapambana m’kutulutsa ziwanda. Iye anali kuchita chinachake choyerekezedwa moyanjidwa ndi chimene Yesu ananena kuti chikafunikira mphotho. Kaamba ka kuchita ichi, Yesu akusonyeza kuti, iye sadzataya mphoto yake.
Koma bwanji ngati mwamunayo anakhumudwitsidwa ndi mawu ndi kachitidwe ka atumwiwo? Ichi chikakhala chowopsya kwambiri! Yesu akuwona kuti: “Ndipo yense amene adzalakwitsa kamodzi ka tiana timeneto takukhulupirira ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wamphero ukolowekedwe m’khosi mwake naponyedwe iye m’nyanja.”
Yesu akunena kuti otsatira ake ayenera kuchotsa m’miyoyo yawo chirichonse chomwe chiri chokondedwa kwa iwo monga dzanja, phazi, kapena diso chomwe chingawapangitse iwo kukhumudwa. Chiri chabwino kukhala wopanda chinthu chokondedwa kwambiri chimenechi ndi kulowa mu Ufumu wa Mulungu koposa kusungilira icho ndi kuponyedwa mu Gehena (dzenje la zinyalala loyaka moto pafupi ndi Yerusalemu) yemwe amaphiphiritsira chiwonongeko chosatha.
Yesu akuchenjezanso kuti: “Yang’anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang’ono awa; pakuti ndinena kwa inu kuti angelo awo apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wakumwamba.” Iye kenaka akuchitira chitsanzo kufunika koposa kwa “ang’ono awa” mwa kuwauza ponena za munthu yemwe anali ndi nkhosa 100 koma ataya imodzi. Munthuyo amasiya 99 kukafunafuna yotaikayo, Yesu akulongosola tero, ndipo pa kuipeza iyo amasangalala kwambiri pa iyo koposa 99 zimene ali nazo. “Chomwecho,” Yesu kenaka akumaliza “sichiri chifuniro cha Atate wanga wa kumwamba kuti mmodzi wa ang’ono awa ataike.”
Mwinamwake akumasunga m’maganizo kutsutsana kwa atumwi ake pakati pawo, Yesu akusonkhezera kuti: “Khalani nawo mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake.” Chakudya chosakolera chimakoleretsedwa ndi mchere. Chotero, mchere wophiphiritsira umapangitsa chimene wina achiwona kukhala chopepuka kuchilandira. Kukhala ndi mchere woterowo kudzathandiza kusunga mtendere.
Koma chifukwa chakupanda ungwiro kwa munthu, panthaŵi zina kukangana kowopsya kumabuka. Yesu anaperekanso zitsogozo za kusamalira izo. “Ngati mbale wako akuchimwira iwe,” Yesu akunena kuti, “pita numlangize pa nokha iwe ndi iye. Ngati akumvera iwe, wabweza mbale wako.” Ngati iye samvera, Yesu akulangiza, “onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena aŵiri, kuti atsimikizidwe mawu onse pakamwa pa mboni ziŵiri kapena zitatu.”
Kokha monga chochita chomalizira, Yesu akunena kuti, tengani nkhaniyo “ku mpingo,” kunena kuti kwa oyang’anira athayo mu mpingo omwe angapereke chigamulo cha chiweruzo. Ngati wochimwayo sadzagwirizana ndi chigamulo chawo, Yesu akumaliza kuti, “akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.”
M’kupanga chosankha choterocho, oyang’anira afunikira kumamatira mwathithithi ku malangizo a Mawu a Yehova. Chotero, pamene iwo apeza munthu wolakwa ndipo afunikira chilango, chiweruzo ‘chidzakhala chomangidwa kale kumwamba.’ Ndipo ngati “mudzimasula pa dziko lapansi,” kunena kuti, apeza wina wopanda liwongo, chidzakhala “chitamasulidwa kale kumwamba.” M’kulingalira kwa chiweruzo kumeneku, Yesu akunena kuti, “kuli aŵiri kapena atatu osonkhanira m’dzina langa, ndiri komweko pakati pawo.” Mateyu 18:6-20; Marko 9:38-50; Luka 9:49, 50.
◆ Nchifukwa ninji chinali chosayenera m’tsiku la Yesu kutsagana naye?
◆ Ndi mowopsya chotani mmene iliri nkhani ya kukhumudwitsa a ang’ono, ndipo ndimotani mmene Yesu anachitira chitsanzo kufunika kwa ang’ono oterowo?
◆ Nchiyani chimene mwinamwake chinasonkhezera chilimbikitso cha Yesu kaamba ka atumwi ake kukhala ndi mchere mwa iwo eni?
◆ Ndi kufunika kotani kumene kulipo pa ‘kumanga’ ndi ‘kumasula’?