Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Phunziro m’Kukhululukira
YESU mwachiwonekere adakali m’nyumba mu Kapernao ndi ophunzira ake. Iye wakhala akukambitsirana ndi iwo mmene angasamalire mavuto pakati pa abale, chotero Petro akufunsa kuti: “Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzakhululukira iye kangati?” Popeza aphunzitsi Achiyuda anavomereza kukhulukira kufika ku nthaŵi zitatu, Petro mwinamwake analingalira icho kukhala kuolowa manja kulingalira kuti: “Kufikira kasanu ndi kaŵiri kodi?”
Koma lingaliro lonse la kusunga cholembera chimenecho liri lolakwa. Yesu akuwongolera Petro: “Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kaŵiri, koma kufikira [nthaŵi makumi asanu ndi aŵiri mphambu zisanu ndi ziŵiri, NW].” Iye akusonyeza kuti sipayenera kukhala malire ku nthaŵi zimene Petro adzakhululukira mbale wake.
Kuti asindikize pa ophunzira ake thayo lawo la kukhululukira, Yesu akuwauza fanizo. Ilo liri ponena za mfumu yomwe ikufuna kukhazikitsa ngongole ndi akopolo ake. Kapolo mmodzi wabweretsedwa kwa iye yemwe ali ndi ngongole yaikulu ya unyinji wa 60,000,000 denarii (chifupifupi ZK400,000,000). Palibe njira iriyonse imene iye angalipire iyo. Chotero, monga mmene Yesu akulongosolera, mfumuyo ikumlamula iye ndi mkazi wake ndi ana ake kugulitsidwa ndipo kuti alipire.
Pa chimenecho kapoloyo agwa pansi pamapazi a mbuye wake napempha kuti: “bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu.”
Atasonkhezeredwa ndi chifundo, mbuyeyo mwachifundo akhululukira ngongole yaikulu ya kapoloyo. Koma mwamsanga pambuyo pa chimenecho, Yesu akupitiriza, kapolo ameneyu apita ndi kupeza kapolo mnzake yemwe anamkongoletsa kokha 100 denarii (chifupifupi ZK720.00). Mwamunayo amgwira kapolo mnzake pakhosi ndi kuyamba kumkanyanga iye, nanena: “Bwezera chija unachikongola.”
Koma kapolo mnzakeyo alibe ndalama. Chotero akugwada pansi pa mapazi a kapolo amene ali mngongole kwa iye, napembedzera: “Bakandiyembekeza ine, ndipo ndidzakubwezera.” Mosiyana ndi mbuye wake, kapoloyu ali wopanda chifundo, ndipo iye apangitsa kapolo mnzake kuponyedwa m’ndende.
Chabwino, Yesu akupitiriza, akapolo ena omwe anawona chomwe chinachitika anapita ndikuuza mbuyeyo. Iye, kenaka, mopsya mtima anaitanitsa kapoloyo. “Kapolo woipa iwe,” iye akutero, “Ndinakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja unandipempha ine. Kodi iwenso sukadamchitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni?” Ataputidwa kufikira mkwiyo, mbuyeyo apereka kapolo wopanda chifundoyu kwa andende kufikira iye atalipira zonse zimene anamkongola.
Kenaka Yesu akumaliza: “Chomwechonso Atate wanga adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.”
Ndi phunziro labwino chotani nanga m’kukhululukira! Kuyerekezedwa ndi ngongole yaikulu ya chimo imene Mulungu watikhululukira ife, cholakwa chirichonse chimene chingachitidwe kwa ife ndi mbale Wachikristu chingakhaledi chaching’ono. M’kuwonjezerapo, Yehova Mulungu watikhululukira ife nthaŵi zikwi zambiri. Kaŵirikaŵiri, sitimadziŵa nkomwe ponena za machimo athu motsutsana ndi iye. Chotero, kodi sitingakhululukire mbale wanthu nthaŵi zochepa, ngakhale ngati ife tiri ndi chifukwa choyenera cha kudandaulira? Kumbukirani, monga mmene Yesu anaphunzitsira mu Ulaliki wa pa Phiri, Mulungu “adzakhululukira mangawa athu, monga ifenso tikhululukira amangawa athu.” Mateyu 18:21-35; 6:12; Akolose 3:13.
◆ Nchiyani chimene chikudzutsa funso la Petro ponena za kukhululukira mbale wake, ndipo nchifukwa ninji iye angalingalire lingaliro lake la nthaŵi zisanu ndi ziŵiri kukhala kuolowa manja?
◆ Ndimotani mmene yankho la mfumu ku kudandaula kwa kapolo wake linasiirana ndi yankho ladandaulo la kapolo ku kapolo mnzake?
◆ Nchiyani chimene tikuphunzira kuchokera ku fanizo la Yesu?