Chiyembekezo Chotsimikizika
PAFUPIFUPI zaka 2,000 zapitazo, Yesu, amene nthaŵi zambiri amatchedwa kuti munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako, anapatsidwa chilango cha kuphedwa popanda chifukwa. Atapachikidwa pamtengo wozunzira, munthu wochita zoipa amene anapachikidwa pambali pake ananena mwamwano kuti: “Kodi suli Kristu Iwe? Udzipulumutse wekha ndi ife.”
Atanena zimenezo wochita zoipa wina amenenso anali kuphedwa anam’dzudzula munthuyo ponena kuti: “Kodi suwopa Mulungu, poona uli m’kulangika komweku? Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tilikulandira zoyenera zimene tinazichita: koma munthu uyu sanachita kanthu kolakwa.” Kenaka anatembenukira kwa Yesu ndi kupempha kuti: “Ndikumbukireni mmene muloŵa Ufumu wanu.”
Yesu anayankha kuti: ‘Indetu, ndinena ndi iwe lerolino, udzakhala ndine m’Paradaiso.’—Luka 23:39-43.
Yesu anali ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri m’tsogolo mwake. Paulo anatchulapo mmene chiyembekezochi chinam’khudzira Yesu, ponena kuti: “Chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzira, NW], nanyoza manyazi.”—Ahebri 12:2.
“Chimwemwe” chimene chinaikidwa pamaso pa Yesu chikuphatikizapo kukakhalanso ndi Atate wake kumwamba ndipo kenaka n’kudzakhala Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu. Kuphatikizanso apo, iye adzakhala ndi chimwemwe cholandilira atsatiri ake oyesedwa ndi okhulupirika amene adzalamulire naye monga mafumu padziko lapansi. (Yohane 14:2, 3; Afilipi 2:7-11; Chivumbulutso 20:5, 6) Choncho, kodi Yesu anali kutanthauzanji polonjeza munthu wochita zoipa uja kuti adzakhala m’Paradaiso?
Kodi Pali Chiyembekezo Chotani kwa Wochita Zoipayo?
Munthu uja sanayenerere kukalamulira ndi Yesu kumwamba. Iye sali m’gulu la anthu amene Yesu ankatchula ponena kuti: “Inu ndinu amene munakhala ndi ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira ine.” (Luka 22:28, 29) Komabe, Yesu analonjeza munthu wochita zoipayo kuti adzakhala m’Paradaiso pamodzi ndi iye. Kodi lonjezo limenelo lidzakwaniritsidwa bwanji?
Mwamuna ndi mkazi woyamba, Adamu ndi Hava, anaikidwa ndi Yehova Mulungu, m’paradaiso, munda wosangalatsa wochedwa Edene. (Genesis 2:8, 15) Edene anali padziko lapansi, ndipo Mulungu anafuna kuti dziko lonse lapansi likhale paradaiso. Komabe, Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu ndipo anatulutsidwa m’mudzi wawo wokongolawo. (Genesis 3:23, 24) Koma Yesu anavumbula kuti Paradaiso adzabwezeretsedwa ndipo kuti adzakhala padziko lonse.
Pamene mtumwi Petro anafunsa Yesu mphotho imene iye pamodzi ndi atumwi anzake adzalandire chifukwa chomutsata, Yesu analonjeza kuti: ‘Inu amene munanditsata ine, m’kubadwanso, pamene Mwana wa munthu adzakhala pachimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pamipando khumi ndi iŵiri.’ (Mateyu 19:27, 28) Mfundo yofunika n’njakuti, m’nkhani yolongosola macheza omwewa yolembedwa ndi Luka, m’malo monena kuti “m’kubadwanso,” iye akulemba zoti Yesu ananena kuti “m’nthaŵi ilinkudza.”—Luka 18:28-30.
Motero, Yesu Kristu akadzakhala pansi, pampando wake waulemelerero kumwamba, iye pamodzi ndi omwe adzalamulire naye adzakhazikitsa dongosolo latsopano lazinthu lolungama. (2 Timoteo 2:11, 12; Chivumbulutso 5:10; 14:1, 3) Kudzera mwaulamuliro wa Yesu wakumwamba, cholinga cha Mulungu choyambirira chofuna kuti dziko lonse lapansi likhale paradaiso chidzakwaniritsidwa!
Panthaŵi ya ulamuliro Waufumu umenewu, Yesu adzakwaniritsa lonjezo lake kwa wambanda amene anafa naye pamodzi. Iye adzamuukitsa ndipo munthu amene uja adzakhala nzika ya padziko lapansi yolamulidwa ndi Yesu. Ndiyeno munthu wochita zoipayo adzapatsidwa mwayi wakuti akwaniritse zimene Mulungu amafuna ndi kukhala kosatha molamulidwa ndi Ufumuwo. N’zoona kuti tingakhale osangalala ndi chiyembekezo cha m’Baibulo chakuti tingakhale kosatha m’Paradaiso padziko lapansi!
Moyo Ungakhale Wofunikadi
Tangoganizirani chabe mmene chiyembekezo chachikulu chimenechi chingakhudzire moyo wathu. Chingathe kuteteza maganizo athu kuti tisavulale chifukwa choganiza moipa. Mtumwi Paulo anayerekezera chiyembekezo chimenechi ndi mbali yofunika kwambiri ya zovala zankhondo yauzimu. Iye ananena kuti tiyenera kuvala “chiyembekezo cha chipulumutso” ‘monga chisoti.’—1 Atesalonika 5:8; Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4.
Chiyembekezo chimenecho n’chopatsa moyo. M’paradaiso amene akubwerayo, kusungulumwa kudzaloŵedwa m’malo ndi misozi ya chimwemwe pamene “Mulungu wakuukitsa akufa,” adzakhala akubwezeretsa kumoyo okondedwa athu apamtima. (2 Akorinto 1:9) Panthaŵiyo kukhumudwa kodza chifukwa cha kufooka kwathupi, zoŵaŵa, ndiponso kulephera kuyenda, zidzaiwalika, chifukwa chakuti “wopunduka adzadumpha ngati nswala.” Thupi la munthu ‘lidzakhala loti see ngati la mwana,’ ndipo munthu “adzabwerera ku masiku a ubwana wake.”—Yesaya 35:6; Yobu 33:25.
Panthaŵiyo, m’pamene “wokhalamo sadzanena, ine ndidwala,” kuthedwa nzeru chifukwa cha matenda aakulu kudzaiwalika. (Yesaya 33:24) Kusoŵa chochita chifukwa cha kuvutika maganizo kwa nthaŵi yaitali kudzasanduka “kukondwa kosatha.” (Yesaya 35:10) Kutaya chiyembekezo chifukwa chokhala ndi matenda akupha kudzatheratu pamodzinso ndi imfa, imene ili mdani wa mtundu wa anthu.—1 Akorinto 15:26.
[Zithunzi patsamba 18]
Kumbukirani za chiyembekezo chosangalatsa cha dziko latsopano la Mulungu nthaŵi zonse