Mutu 7
Kodi Baibulo Limadzitsutsa?
Chinenezo chimene kaŵirikaŵiri chimapangidwa motsutsana ndi Baibulo nchakuti limadzitsutsa. Kaŵirikaŵiri, anthu amene amapanga chinenezo chimenechi iwo eniwo sanaŵerenge Baibulo; iwo amangobwereza zimene iwo amva. Komabe, ena, apeza chimene chimawonekera kukhala kudzitsutsa kwenikweni ndipo amavutika nazo.
1, 2. (Phatikizamoni mawu oyamba.) (a) Kodi ndichitsutso chotani chimene kaŵirikaŵiri chimapangidwa motsutsana ndi Baibulo? (b) Poyerekezera ndime zosiyanasiyana za Baibulo, kodi nchiyani chimene tiyenera kukumbukira? (c) Kodi ndiziti zimene ziri zina za zifukwa chifukwa chake pali kusiyana nthaŵi zina kwa mmene olemba Baibulo aŵiri amasimbira chochitika chimodzimodzicho?
NGATI liridi Mawu a Mulungu, Baibulo liyenera kukhala logwirizana, osati lodzitsutsa. Nangano, nchifukwa ninji, ndime zina zimawonekera kukhala zikutsutsana ndi zina? Kuti tiyankhe, tifunikira kukumbukira kuti, pamene kuli kwakuti Baibulo liri Mawu a Mulungu, linalembedwa ndi anthu angapo mkati mwa nyengo ya zaka mazana angapo. Olemba ameneŵa anali ndi ziyambi zosiyanasiyana, njira za kalembedwe, ndi mphatso, ndipo zosiyana zonsezi zimasonyezedwa m’zolemba zawo.
2 Ndiponso, ngati olemba aŵiri kapena oposa afotokoza chochitika chimodzimodzi, wina angaphatikizemo mfundo zimene wina angazisiye. Ndiponso, olemba osiyana amalemba nkhani m’njira zosiyanasiyana. Mmodzi angazilembe motsatira tsatanetsatane wa nthaŵi, pamene wina angatsatire kakonzedwe kosiyana. M’mutu uno, tidzafotokoza zina zonenedwa kukhala kudzitsutsa m’Baibulo ndi kulingalira mmene zingagwirizanitsidwire, tikumalingalira zimene tazitchula pamwambapazi.
Mboni Zodziimira
3, 4. Ponena za mkulu wankhondo amene kapolo wake anadwala, kodi nkusiyana kowonekera kotani kumene kulipo pakati pa cholembedwa cha Mateyu ndi chija cha Luka, ndipo kodi zolembedwa zimenezi zingagwirizanitsidwe motani?
3 “Zodzitsutsa,” zina zimabuka pamene tiri ndi zolembedwa ziŵiri kapena zoposa za chochitika chimodzimodzi. Mwachitsanzo, pa Mateyu 8:5 timaŵerenga kuti pamene Yesu anadza ku Kapernao, “anadza kwa Iye kenturiyo, nampempha Iye,” akumapempha Yesu kuti achiritse mtumiki wake. Koma pa Luka 7:3, timaŵerenga za mkulu wankhondo ameneyu kuti “anatuma kwa iye akulu a Ayuda, namfunsa Iye [Yesu] kuti adze kupulumutsa kapolo wake.” Kodi mkulu wankhondoyo analankhula ndi Yesu, kapena kodi iye anatumiza akulu?
4 Yankho liri lomvekera bwino, kuti mwamunayo anatuma akulu a Ayuda. Nangano, nchifukwa ninji, Mateyu amanena kuti mwamuna uyu iye mwini anadandaulira Yesu? Chifukwa chakuti, kwenikweni, mwamunayo anapempha Yesu kupyolera mwa akulu a Ayuda. Akuluwo anatumikira monga omnenera.
5. Kodi nchifukwa ninji Baibulo limanena kuti Solomo anamanga kachisi, pamene ntchito yeniyeniyo mwachiwonekere inachitidwa ndi ena?
5 Kufotokoza zimenezi mwafanizo, pa 2 Mbiri 3:1, timaŵerenga kuti: “Pamenepo Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu.” Pambuyo pake, timaŵerenga kuti: “Momwemo Solomo anatsiriza nyumba ya Yehova.” (2 Mbiri 7:11) Kodi Solomo iye mwiniyo anamanga kachisi kuyambira pachiyambi mpaka kumaliza? Ndithudi ayi. Ntchito yeniyeni ya kumangayo inachitidwa ndi unyinji wa amisiri ndi antchito. Koma Solomo anali wolinganiza ntchitoyo, wokhala ndi thayo. Chotero, Baibulo limanena kuti iye anamanga nyumbayo. M’njira yofananayo, Uthenga Wabwino wa Mateyu ukutiuza kuti mkulu wankhondoyo anafikira Yesu. Koma Luka amapereka tsatanetsatane wowonjezereka wakuti iye anamfikira kupyolera mwa akulu a Ayuda.
6, 7. Kodi tingagwirizanitse motani zolembedwa za Uthenga Wabwino ziŵiri zosiyana zonena za pempho la ana a Zebedayo?
6 Nachi chitsanzo chofanana nacho. Pa Mateyu 20:20, 21, timaŵerenga kuti: “Anadza kwa Iye [Yesu] amake a ana a Zebedayo ndi ana ake omwe, namgwadira, ndi kumpempha kanthu.” Chimene iye anapempha nchakuti ana ake aamuna ayenera kukhala ndi udindo woyanjidwa kopambana pamene Yesu aloŵa mu Ufumu wake. M’cholembedwa cha Marko cha chochitika chimodzimodzichi, timaŵerenga kuti: “Anadza kwa iye [Yesu] Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, nanena naye, Mphunzitsi, tifuna kuti mudzatichitire chimene chirichonse tidzapempha kwa inu.” (Marko 10:35-37) Kodi anali ana aŵiri a Zebedayo, kapena kodi anali mayi wawo, amene anapereka pempholo kwa Yesu?
7 Mwachiwonekere, anali ana aŵiri a Zebedayo amene anapempha, monga momwe Marko akufotokozera. Koma iwo anakuchita kupyolera mwa amayi ŵawo. Mayiwo anali owalankhulira. Zimenezi zikuchirikizidwa ndi lipoti la Mateyu lakuti pamene atumwi enawo anamva zimene amayi ŵa ana a Zebedayo anachita, iwo anapsa mtima osati ndi amayiwo, koma “ndi abale aŵiriwo.”—Mateyu 20:24.
8. Kodi kuli kothekera motani kuti zolembedwa ziŵiri za chochitika chimodzimodzicho zimasiyana china ndi chinzake ndipo zonse ziŵirizo ziikhala chowonadi?
8 Kodi munayamba mwamvapo anthu aŵiri akulongosola chochitika chimene iwo onse aŵiri anachiwona? Ngati kuli choncho, kodi munawona kuti munthu aliyense amagogomezera mfundo zimene zinamgwira mtima? Wina angasiye zinthu zimene winayo anaphatikizamo. Komabe, iwo onse aŵiri anali kusimba chowonadi. Ziri chimodzimodzi ndi zolembedwa zonena za Mauthenga Abwino anayiwo a utumiki wa Yesu, chimodzimodzinso ndi zochitika zina za m’mbiri zosimbidwa ndi olemba Baibulo oposa mmodzi. Wolemba aliyense analemba chidziŵitso cholondola ngakhale pamene winayo anabwezeretsa mfundo zimene winayo anazilumpha. Mwakulingalira zolembedwa zonsezo, kumvetsetsa kokwanira kwa zimene zinachitika kungathe kupezedwa. Kusiyanako kumatsimikizira kuti zolembedwa za Baibulo ziri zodziimira. Ndipo kugwirizana kwake kofunikako kumatsimikizira kuti ziri zowona.
Ŵerengani Mawu Apatsogolo ndi Apambuyo
9, 10. Kodi mawu apatsogolo ndi apambuyo amatithandiza motani kuwona kumene Kaini anapeza mkazi wake?
9 Kaŵirikaŵiri, zosagwirizana zowonekerazo zingathe kuthetsedwa ngati ife tingoyang’ana pamawu apatsogolo ndi apambuyo. Mwachitsanzo, lingalirani, vuto lodzutsidwa kaŵirikaŵiri lonena za mkazi wa Kaini. Pa Genesis 4:1, 2 timaŵerenga kuti: “M’kupita kwanthaŵi [Hava] anabala Kaini ndipo anati: ‘Ndabala munthu mwachithandizo cha Yehova.’ Pambuyo pake iye anabala, mbale wake Abele.” Monga momwe kuli kodziŵikiratu, Kaini anapha Abele; koma pambuyo pake, timaŵerenga kuti Kaini anakhala ndi mkazi ndi ana. (Genesis 4:17) Ngati Adamu ndi Hava anali ndi ana aamuna aŵiri okha, kodi Kaini anampeza kuti mkazi wake?
10 Chothetsera vutolo chiri m’chenicheni chakuti Adamu ndi Hava anali ndi ana oposa aŵiri. Malinga ndi mawu apatsogolo ndi apambuyo iwo anali ndi banja lalikulu. Pa Genesis 5:3 timaŵerenga kuti Adamu anabala mwana wina wamwamuna wotchedwa Seti ndiyeno, m’vesi lotsatirapo, timaŵerenga kuti: “Iye anabala ana aamuna ndi aakazi.” (Genesis 5:4) Chotero Kaini, ayenera akukhala atakwatira mmodzi wa alongo ake kapena mmodzi wa adzukulu ake. Kuchiyambiyambi kumeneko kwa mbiri ya anthu, pamene mtundu wa anthu unali pafupi kwambiri ndi ungwiro, ukwati woterowo mwachiwonekere sunapange maupandu alionse kaamba ka ana a chigwirizanocho amene akakhalapo lerolino.
11. Kodi ndikunenedwa kukhala kosagwirizana kotani pakati pa Yakobo ndi mtumwi Paulo kumene ena amakusonya?
11 Kulingalira kwathu mawu apatsogolo ndi apambuyo kumatithandizanso kumvetsetsa zimene ena amazinena kukhala kusagwirizana pakati pa mtumwi Paulo ndi Yakobo. Pa Aefeso 2:8, 9, Paulo akunena kuti Akristu amapulumutsidwa mwachikhulupiriro, osati mwa ntchito. Iye akunena kuti: “Mwapulumutsidwa mwa chikhulupiriro . . . osati mwa ntchito.” Komabe, Yakobo, akuumirira pa kufunika kwa ntchito. Iye akulemba kuti: “Monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, momwenso chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.” (Yakobo 2:26) Kodi ndimotani mmene mawu aŵiriŵa angagwirizanitsidwire?
12, 13. Kodi ndimotani mmene mawu a Yakobo amathandizirira koposa kutsutsa awo a mtumwi Paulo?
12 Polingalira mawu apatsogolo ndi apambuyo a Paulowo, timapeza kuti mawu a mmodzi amathandizira enawo. Mtumwi Paulo akusonyeza za zoyesayesa za Ayuda za kusunga Chilamulo cha Mose. Iwo amakhulupirira kuti ngati iwo asunga Chilamulo m’mfundo zake zonse, iwo akakhala olungama. Paulo anasonyeza kuti zimenezi zinali zosatheka. Sitingathe konse kukhala olungama—ndipo motero kuyenerera chipulumutso—mwa ntchito zathu za ife eni, pakuti mwa choloŵa ndife ochimwa. Tingathe kupulumutsidwa kokha mwachikhulupiriro m’nsembe ya dipo ya Yesu.—Aroma 5:18.
13 Komabe, Yakobo, akuwonjezera mfundo yofunika kwambiri yakuti chikhulupiriro mwa icho chokha chiri chopanda phindu ngati sichichirikizidwa ndi ntchito. Munthu amene adzinenera kukhala ndi chikhulupiriro mwa Yesu ayenera kuchitsimikizira mwa zimene iye amachita. Chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chikhulupiriro chakufa ndipo sichidzatsogolera kuchipulumutso.
14. Kodi ndindime zotani zimene Paulo akusonyeza kuti iye ali wogwirizana kotheratu ndi lamulo la makhalidwe abwino lakuti chikhulupiriro cha moyo chiyenera kusonyezedwa ndi ntchito?
14 Mtumwi Paulo anali wogwirizana kotheratu ndi zimenezi, ndipo iye kaŵirikaŵiri amatchula mitundu yantchito zimene Akristu ayenera kukhala akuchita kusonyeza chikhulupiriro chawo. Mwachitsanzo, kwa Aroma iye analemba kuti: “Ndi mtima munthu amasonyeza chikhulupiriro kaamba ka chilungamo, koma ndi pakamwa munthu amapanga chilengezo chapoyera kaamba ka chipulumutso.” Kupanga “chilengezo chapoyera”—kugaŵana chikhulupiriro chathu ndi ena—nkofunika kaamba ka chipulumutso. (Aroma 10:10; wonaninso 1 Akorinto 15:58; Afeso 5:15, 21-33; 6:15; 1 Timoteo 4:16; 2 Timoteo 4:5; Ahebri 10:23-25.) Komabe, palibe ntchito, imene Mkristu angachite, ndipo ndithudi palibe kuyesayesa kwa kukwaniritsa Chilamulo cha Mose, kumene kudzampezetsa kuyenera kwa moyo wosatha. Iyitu ndiyo “mphatso imene Mulungu amapereka” kwa awo amene amasonyeza chikhulupiriro.—Aroma 6:23; Yohane 3:16, NW.
Malingaliro Osiyana
15, 16. Kodi ndimotani mmene onse aŵiri Mose ndi Yoswa angakhalire olondola pamene mmodzi ananena kuti kummaŵa kwa Yordano kunali “tsidya lino” lamtsinje pamene winayo ananena kuti linali “tsidya lija”?
15 Nthaŵi zina olemba Baibulo analemba za chochitika chimodzimodzi mwa malingaliro osiyana, kapena iwo anapereka zolembedwa zawo m’njira zosiyana. Pamene kusiyanasiyana kumeneku kulingaliridwa, kowonekera kudzitsutsa kwina kowonjezereka nkosavuta kukuthetsa. Chitsanzo cha chimenechi chiri m’Numeri 35:14, kumene Mose akulankhula za chigawo chakummaŵa kwa Yordano kukhala “tsidya lino la Yordano.” Komabe, Yoswa, ponena za malo akummaŵa kwa Yordano, anawatcha “tsidya lija la Yordano.” (Yoswa 22:4) Kodi nziti zimene ziri zolondola?
16 Kunena zowona, zonse nzolondola. Malinga ndi kunena kwa cholembedwacho m’Numeri, Aisrayeli anali asanawoloke Mtsinje wa Yordano kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, chotero kwa iwo kummaŵa kwa Yordano kunali “tsidya lino.” Komatu Yoswa anali atawoloka kale Yordano. Iye tsopano, mwakuthupi, anali kumadzulo kwa mtsinjewo, m’dziko la Kanani. Chotero kwa iye, kummaŵa kwa Yordano kunali, “tsidya lija.”
17. (a) Kodi ndikunenedwa kukhala kusagwirizana kotani kumene ena amakusonya m’mitu iŵiri yoyambirira ya Genesis? (b) Kodi nchiyani chimene chiri chifukwa chachikulu cha kuwonera kukhala kusiyanako?
17 Mowonjezerapo, mmene kufotokoza kwaumbidwira kungathe kutsogolera kukudzitsutsa kowonekera. Pa Genesis 1:24-26, Baibulo limasonyeza kuti zinyama zinalengedwa munthu asanalengedwe. Koma pa Genesis 2:7, 19, 20, likuwonekera kukhala likunena kuti munthu analengedwa zinyama zisanalengedwe. Kodi nchifukwa ninji pali kusiyanako? Chifukwa chakuti zolembedwa ziŵirizo zonena za chilengedwe zikuchifotokoza m’malingaliro aŵiri osiyana. Choyambacho chikufotokoza chilengedwe chakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zirimo. (Genesis 1:1–2:4) Chachiŵiricho chikusumika maganizo pakulengedwa kwa anthu ndi kugwera kwawo muuchimo.—Genesis 2:5–4:26.
18. Kodi tingagwirizanitse motani kuwonekera kukhala kusiyana pakati pa zolembedwa zachilengedwe ziŵiri m’mitu yoyambirira ya Genesis?
18 Cholembedwa choyambiriracho chalembedwa motsatira ndandanda ya nthaŵi, chogaŵidwa m’zigawo zotsatanatsatana zisanu ndi chimodzi za “masiku.” Chachiŵiricho chalembedwa m’ndandanda ya kufunika kwa mitu ya nkhani. Pambuyo pa mawu oyamba aafupi, icho moyenerera chikumka mwachindunji kukulengedwa kwa Adamu, popeza kuti iye ndi banja lake ndiwo nkhani yaikuli imene ikutsatirapo. (Genesis 2:7) Pamenepo chidziŵitso china chikuloŵetsedwamo pamene chikufunika. Tikumva kuti pambuyo pa kulengedwa kwake Adamu anali kudzakhala m’munda wa Edene. Chotero kubzalidwa kwa munda wa Edene tsopano kukutchulidwa. (Genesis 2:8, 9, 15) Yehova akuuza Adamu kutcha dzina “chinyama chirichonse chakuthengo ndi mbalame iriyonse youluka m’mlengalenga.” Tsopano, kenako, iri nthaŵi ya kutchula kuti “Yehova Mulungu anali kupanga kuchokera m’nthaka” zolengedwa zonsezi, ngakhale kuli kwakuti kulengedwa kwawo kunayamba kalekale Adamu asanawonekere padziko.—Genesis 2:19; 1:20, 24, 26.
Kuŵerenga Cholembedwacho Mosamalitsa
19. Kodi ndichisokonezo chowonekera chotani chimene chiripo m’cholembedwa cha Baibulo cha kugonjetsedwa kwa Yerusalemu?
19 Nthaŵi zina, chokha chimene chimafunika kuthetsa chowonekera ngati kudzitsutsa ndicho kuŵerenga cholembedwacho mosamalitsa ndi kusinkhasinkha ponena za chidziŵitso choperekedwacho. Ziri choncho pamene tikulingalira kugonjetsedwa kwa Yerusalemu ndi Aisrayeli. Yerusalemu anandandalikidwa kukhala mbali ya choloŵa cha Benjamini, koma timaŵerenga kuti fuko la Benjamini linali losakhoza kuwugonjetsa. (Yoswa 18:28; Oweruza 1:21) Timaŵerenganso kuti Yuda anali wosakhoza kugonjetsa Yerusalemu—monga ngati kuti anali mbali ya choloŵa cha fuko limenelo. Potsirizira pake, Yuda anagonjetsa Yerusalemu, akumautentha ndi moto. (Yoswa 15:63; Oweruza 1:8) Komabe, zaka mazana ambiri pambuyo pake, Davide nayenso akusimbidwa kukhala akugonjetsa Yerusalemu.—2 Samueli 5:5-9.
20, 21. Mwa kupenda mosamalitsa mfundo zonse zoyenerera, kodi nchiyani chimene chikutuluka m’mbiri ya kulanda kwa Ahebri m’zinda wa Yerusalemu?
20 Mongowonera patali choyamba, zonsezi zingawonekere kukhala zosokoneza maganizo, koma kwenikweni palibe kuwombana. Kunena zowona, malire pakati pa choloŵa cha Benjamini ndi Yuda anali kuyenda modutsa Chigwa cha Hinomu, kudutsa mzinda wamakedzana wa Yerusalemu. Pambuyo pake chimene chinafikira kutchedwa Mzinda wa Davide kwenikweni chiri m’chigawo cha Benjamini, monga momwedi Yoswa 18:28 amanenera. Koma kuli kowonekera bwino kuti mzinda wa Ayebusi wa Yerusalemu unadutsa Chigwa cha Hinomu ndipo motero kukaloŵerera m’chigawo cha Yuda, kotero kuti Yuda, nayenso, anayenera kumenyana nkhondo ndi nzika zake za Kanani.
21 Benjamini anali wosakhoza kugonjetsa mzindawo. Pachochitika china, Yuda anagonjetsa Yerusalemu ndi kuutentha. (Oweruza 1:8, 9) Koma mwachiwonekere magulu ankhondo a Yuda anayendabe, ndipo zina za nzika zoyambirira zinalandanso mzindawo. Pambuyo pake, iwo anapanga mgwirizano wa kulimbalimba kumene Yuda kapenanso Benjamini sakanatha kuuchotsa. Motero, Ayebusi anapitirizabe m’Yerusalemu kufikira Davide atagonjetsa mzindawo zaka mazana ambiri pambuyo pake.
22, 23. Kodi ndani amene ananyamula mtengo wozunzirapo wa Yesu kumka nawo kumalo ophera?
22 Tikufika pachitsanzo chathu chachiŵiri m’Mauthenga Abwino. Ponena za kutengedwa kwa Yesu kumka naye kukaphedwa, mu Uthenga Wabwino wa Yohane timaŵerenga kuti: “Anasenza [mtengo wozunzirapo] yekha, natuluka.” (Yohane 19:17) Komabe, m’Luka timaŵerenga kuti: “Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kurene, ali kuchokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pa Yesu.” (Luka 23:26) Kodi Yesu ananyamula mtengo wa imfa yake, kapena kodi Simoni anamnyamulira iye?
23 Choyamba, Yesu mwachiwonekere anadzinyamulira mtengo wozunzirapo, monga momwe Yohane akusonyezera. Koma pambuyo pake, monga momwe Mateyu, Marko, ndi Luka akuchitira umboni, Simoni wa ku Kurene anakakamizidwa kuloŵa m’ntchito ya kumnyamulira mbali yonse yotsalira ya ulendowo kukafika pamalo ophedwerawo.
Umboni wa Kudziimira
24. Kodi nchifukwa ninji sitikudabwa kupeza zosiyana zowonekera bwino m’Baibulo, koma kodi sitiyenera kufika pakunenanji kuchokera m’zimenezi?
24 Zowona, pali kusagwirizana kwina kowonekera bwino m’Baibulo kumene kuli kovuta kukugwirizanitsa. Koma sitiyenera kulingalira kuti iko kuli kudzitsutsa kotsimikizirika. Kaŵirikaŵiri iri chabe nkhani ya kupanda chidziŵitso chokwanira. Baibulo limapereka chidziŵitso cholinganira kukhutiritsa kusoŵa kwathu kwauzimu. Koma likadatipatsa tsatanetsatane aliyense ponena za chinthu chirichonse chotchulidwa, likanakhala nkhokwe yaikulu kopambana ya mabukhu ndi yosanyamulika, koposa ndi kukhala bukhu lopepuka, ndi losavuta kunyamula limene tiri nalo lerolino.
25. Kodi Yohane akunenanji ponena za cholembedwa cha utumiki wa Yesu, ndipo kodi ndimotani mmene zimenezi zikutithandizira kumvetsetsa chifukwa chake Baibulo silimatipatsa mfundo iriyonse yonena za chochitika chirichonse?
25 Ponena za utumiki wa Yesu, mtumwi Yohane analemba limodzi ndi kukukumaza koyenerera kuti: “Kunena zowona, pali zinthu zina zambiri zimenenso Yesu anachita, zimene, ngati zikadalembedwa zonse mwatsatanetsatane, ndiganiza kuti, dziko lonse lenilenilo silikanakhala ndi malo osunga mipukutu yolembedwayo.” (Yohane 21:25, NW) Kukanakhala pafupifupi kosatheka kulemba mfundo zonse zonena za mbiri yaitali ya anthu a Mulungu kuchokera kwa makolo akale kudzafika kumpingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba!
26. Kodi Baibulo liri ndi chidziŵitso chokwanira chakuti ife tikhale otsimikizira za chenicheni chotani chofunika kwambiri?
26 Kwenikweni, Baibulo liri chozizwitsa cha kufupikitsa. Liri ndi chidziŵitso chokwanira kutitheketsa kulizindikira kukhala loposa bukhu la anthu chabe. Kusiyanasiyana kulikonse kumene iro liri nako kumatsimikizira kuti olembawo analidi mboni aliyense payekha. Kumbali ina, kugwirizana kwapaderako kwa Baibulo—kumene tidzakufotokoza mwatsatanetsatane m’mutu wamtsogolo—kumasonyeza mosakaikitsa kukhala kwake loyambidwa ndi Mulungu. Ndiro mawu a Mulungu, osati a munthu.
[Mawu Otsindika patsamba 89]
Kulingalira mawu apatsogolo ndi apambuyo kaŵirikaŵiri kumathandiza kuthetsa zonenedwa kukhala kudzitsutsa
[Mawu Otsindika patsamba 91]
Kowonekera kukhala kusagwirizana m’Baibulo kumatsimikizira kuti olembawo analidi mboni aliyense payekha
[Bokosi patsamba 93]
“Zosiyana” Siziyenera Kukhala Kudzitsutsa
Kenneth S. Kantzer, katswiri wa zaumulungu, panthaŵi ina anafotokoza mwafanizo mmene malipoti aŵiri osimba chochitika chimodzimodzicho angawonekerere kukhala otsutsana ndipo komabe onse aŵiri kukhala owona. Analemba kuti: “Papitapo mayi wa bwenzi lathu lokondedwa anaphedwa. Choyamba tinamva za imfayo kupyolera mwa bwenzi lathu lodalirika lokondana nalo limene linasimba kuti mayi wa bwenzi lathulo anali ataima pangodya yakhwalala akudikira basi, anagundidwa ndi basi lina limene linali kudutsa, anavulazidwa kowopsa, ndipo anafa patapita mphindi zoŵerengeka.”
Mwamsanga pambuyo pake, anamva lipoti losiyana kwambiri. Iye akuti: “Tinamva kwa mdzukulu wamkazi womwalirayo kuti iye anali atagundana, anaponyeredwa kunja kwa galimoto limene anakwera, ndipo anafera pomwepo. Mnyamatayo anali wotsimikizira ponena za maumboni akewo.
“Pambuyo pake . . . tinafufuzafufuza kuti tiwone kugwirizana kwake. Tidamva kuti gogoyo anali kuyembekezera basi, iye anagundidwa ndi basi lina, ndipo anavulazidwa kowopsa. Ananyamulidwa ndi galimoto limene linali kudutsa ndi kuthamangira naye kuchipatala, koma m’kufulumirako galimoto limene linawanyamulalo kumka kuchipatala linagundana ndi galimoto lina. Gogoyo anaponyeredwa kunja kwa galimotolo ndi kufera pomwepo.”
Inde, zolembedwa ziŵiri zonena za chochitika chimodzimodzicho zingathe kukhala zowona ngakhale kuli kwakuti zingawonekere kukhala zikusiyana china ndi chinzake. Nthaŵi zina ziri choncho ponena za Baibulo. Mboni zosiyana zingafotokoze mfundo zosiyanasiyana ponena za chochitika chimodzimodzicho. Komabe, mmalo mwa kukhala zotsutsana, zimene iwo akulemba ndizothandizana, ndipo ngati tilingalira zolembedwa zonsezo, timapeza kumvetsetsa kwabwinopo kwa chimene chinachitika.