Anachita Chifuniro cha Yehova
Amtama Yesu Kuti Ndiye Mesiya ndi Mfumu!
KHAMU lophokosera lomaloŵa m’Yerusalemu pa Nisani 9, 33 C.E., linadabwitsa Ayudeya ambiri. Ngakhale sikunali kwachilendo kuona anthu ochuluka akuloŵa mumzinda Paskha asanayambe, alendo ameneŵa anali osiyana. Ngwazi yawo inali mwamuna wokwera mwana wa bulu. Mwamunayo anali Yesu Kristu, ndipo anthu anali kuyala zovala ndi makhwatha a kanjedza patsogolo pake namafuula kuti: “Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m’dzina la Ambuye! Hosana m’Kumwambamwamba!” Poona khamulo, ambiri omwe anali kale m’Yerusalemu anadziphatika ku khamulo.—Mateyu 21:7-9; Yohane 12:12, 13.
Ngakhale kuti iwo anali kumtama Yesu tsopano, iye anadziŵa kuti ziyeso zikumyembekeza. Potitu nanga m’masiku asanu okha adzaphedwa mumzinda womwewunso! Inde, Yesu anadziŵa kuti Yerusalemu ndi chigawo choipa, ndipo anaonetsera poyera kuloŵa kwake m’Yerusalemu lingaliro limenelo ali nalo m’maganizo.
Ulosi Wakale Ukwaniritsidwa
Mu 518 B.C.E., Zekariya ananeneratu kuti Yesu adzaloŵa ndi chikondwerero chachikulu m’Yerusalemu. Analemba kuti: “Fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pa bulu, ndi mwana wamphongo wa bulu. . . . Ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.”—Zekariya 9:9, 10.
Chotero, kuloŵa kwa Yesu m’Yerusalemu pa Nisani 9 kunakwaniritsa ulosi wa Baibulo. Sichinali chochitika wamba koma chinali cholinganizidwa bwino. Zisanachitike, adakali kunja kwa Yerusalemu, Yesu analangiza ophunzira ake aŵiri kuti: “Mukani kumudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nawo kwa Ine. Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asoŵa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza.” (Mateyu 21:1-3) Koma kodi nchifukwa ninji Yesu anafuna kuloŵa m’Yerusalemu atakwera bulu, ndipo zimene khamulo linachita zinatanthauzanji?
Nkhani ya Chifumu
Kaŵirikaŵiri chinthu choona ndi maso chimakumbukika kuposa mawu olankhulidwa. Chotero, nthaŵi zina Yehova anafuna kuti aneneri ake achitire chithunzi uthenga wawo waulosi kuti ugogomezereke. (1 Mafumu 11:29-32; Yeremiya 27:1-6; Ezekieli 4:1-17) Njira yopambana imeneyi yoperekera uthenga woona ndi maso inaika chithunzi chosazimiririka m’maganizo ngakhale a nkhutu kumve weniweni. Mofananamonso, Yesu anachitira chithunzi uthenga wamphamvu mwa kuloŵa m’Yerusalemu atakwera bulu. Motani?
M’nthaŵi za Baibulo bulu anali kugwiritsiridwa ntchito pazochitika zachifumu. Mwachitsanzo, Solomo pokadzozedwa kuti akhale mfumu, anakwera “nyulu,” mbewu ya bulu ndi kavalo. (1 Mafumu 1:33-40) Choncho kuloŵa kwa Yesu m’Yerusalemu atakwera bulu kunatanthauza kuti anali kudzisonyeza yekha kuti ndi mfumu.a Zimene khamulo linachita zinagogomezera uthenga umenewu. Gululo, limene mosakayika linali la Agalileya, linayala zovala zawo patsogolo pa Yesu—chizindikiro chokumbutsa chilengezo chapoyera cha ufumu wa Yehu. (2 Mafumu 9:13) Pom’tchula Yesu kuti “mwana wa Davide” anamchirikiza kuti ngwoyenera kulamulira. (Luka 1:31-33) Ndipo pogwiritsira ntchito makhwatha a kanjedza mwachionekere anasonyeza kugonjera kwawo ulamuliro wake wachifumu.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 7:9, 10.
Chotero, khamu limene linaloŵa m’Yerusalemu pa Nisani 9 linalengeza uthenga womveka wakuti Yesu anali Mesiya ndi Mfumu yoikidwa ndi Mulungu. Ndithudi, sikuti onse anakondwa kuona Yesu akudziŵikitsidwa mwanjira imeneyi. Makamaka Afarisi anaganiza kuti kunali kosayenera konse kuti Yesu alemekezedwe ndi ulemu wachifumu woterewo. “Mphunzitsi,” anatero, mosakayika atakwiya, “dzudzulani ophunzira anu.” Yesu anawayankha kuti: “Ndinena ndi inu, ngati awa akhala chete miyala idzafuula.” (Luka 19:39, 40) Inde, Ufumu wa Mulungu ndiwo unali mutu wa ulaliki wa Yesu. Anaulengeza uthenga umenewu molimba mtima kaya anthu anaulandira kapena sanaulandire.
Zimene Tiphunzirapo
Yesu anafunikira kulimba mtima kwambiri kuti aloŵe m’Yerusalemu mwanjira imene mneneri Zekariya ananeneratu. Anadziŵa kuti mwakutero anali kunyanyula mkwiyo wa adani ake. Asanakwere kumwamba, Yesu analamula otsatira ake kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kuichita ntchito imeneyi kumafunanso kulimba mtima. Si onse amene amakondwa pakumva uthenga umenewu. Ena amachita nawo mphwayi, ena amautsutsa. Maboma ena aikira malire ntchito yolalikira kapena angoiletseratu.
Komabe, Mboni za Yehova zimazindikira kuti uthenga wabwino wa Ufumu wokhazikitsidwa ndi Mulungu uyenera kulalikidwa, kaya anthu amvetsera kapena kukana. (Ezekieli 2:7) Pamene akupitiriza kuchita ntchito yopulumutsa moyo imeneyi, amalimbikitsidwa ndi lonjezo la Yesu lakuti: “Onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.”—Mateyu 28:20.
[Mawu a M’munsi]
a Nkhani ya Marko yawonjezera kuti mwana wa buluyo anali “amene palibe munthu anakhalapo kale lonse.” (Marko 11:2) Mwachionekere, nyama yomwe sinagwiritsiridwepo ntchito inali yoyenerera zochitika zopatulika.—Yerekezerani ndi Numeri 19:2; Deuteronomo 21:3; 1 Samueli 6:7.