Kukumbukira Masiku Omaliza a Yesu Padziko
NDI tsiku lachisanu ndi chiŵiri m’mwezi wachiyuda wa Nisani m’chaka cha 33 C.E. Tayerekezerani kuti mukuona zimene zikuchitika m’dera lachiroma la Yudeya. Atachoka m’Yeriko wokhala ndi mitengo yokongola, Yesu Kristu ndi ophunzira ake akukwera chitunda mwachangu mumsewu wafumbi wokhotakhota. Enanso ambiri ali paulendo wawo wopita ku Yerusalemu kukachita nawo phwando la pachaka la Paskha. Komabe, ophunzira a Kristu akuganizira chinachake choposa kukwera chitunda chotopetsa chimenechi.
Ayuda akhala akulakalaka Mesiya woti awamasule m’goli lachiroma. Ambiri akukhulupirira kuti Yesu wa ku Nazarete ndiye Mpulumutsi woyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali ameneyo. Kwa zaka zitatu ndi theka, iye wakhala akulankhula za Ufumu wa Mulungu. Wachiritsa odwala ndi kudyetsa anjala. Inde, watonthoza anthu. Koma atsogoleri achipembedzo ngokwiya chifukwa chakuti Yesu wakhala akuwatsutsa koŵaŵa ndipo iwo akungofuna kumupha basi. Koma, si uyo, patsogolo pa ophunzira ake akukwera chitunda molimba mtima mumsewu woumawo.—Marko 10:32.
Pamene dzuŵa likuzimiririka kuseri kwa Phiri la Azitona chapatsogolo pawo, Yesu ndi anzake akufika pamudzi wa Betaniya, pamene adzagona masiku akudzawo asanu ndi limodzi. Pamudzipo akulandiridwa ndi mabwenzi awo apamtima Lazaro, Mariya, ndi Marita. Iwo akutsitsimulidwa madzulowo ndi mphepo yozizirira atayenda m’dzuŵa lotentha ndipo ndicho chiyambi cha Sabata la Nisani 8.—Yohane 12:1, 2.
Nisani 9
Sabatalo litatha, anthu ali piringupiringu m’Yerusalemu. Alendo zikwizikwi afika kale mumzindawo kudzachita Paskha. Koma phokoso limene tikumvali nlachilendo panthaŵi ino yachaka. Makamu ofunitsitsa kuona zimene zikuchitika akuthamangira kuzipata za mzinda m’misewu yaing’ono. Pamene atuluka mopapatiza pazipata zothina ndi anthu, taonani zimene akuona! Anthu ambiri osangalala akutsika Phiri la Azitona mumsewu wochokera ku Betefage. (Luka 19:37) Kodi zonsezi zikutanthauzanji?
Taonani! Yesu wa ku Nazarete akubwera atakwera pa mwana wa bulu. Anthu akuyala zovala mumsewu patsogolo pake. Ena akukupiza makhwatha a kanjedza othyoledwa kumene ndipo akufuula kuti: “Wolemekezeka Iye wakudza m’dzina la Ambuye, ndiye Mfumu ya Israyeli”!—Yohane 12:12-15.
Pamene khamulo liyandikira Yerusalemu, Yesu akuyang’ana mzindawo ndipo akumva chisoni chachikulu. Ayamba kulira, ndipo tikumumva akuneneratu kuti mzindawu udzawonongedwa. Pasanapite nthaŵi, Yesu afika pakachisi ndipo aphunzitsa makamuwo nachiritsa anthu akhungu ndi opunduka amene adza kwa iye.—Mateyu 21:14; Luka 19:41-44, 47.
Akulu ansembe ndi alembi adziŵa zimenezi. Iwo akukwiya chotani nanga ndi zinthu zodabwitsa zimene Yesu akuchita ndiponso ndi kukondwera kwa makamuwo! Polephera kubisa mkwiyo wawo, Afarisi akuti: “Mphunzitsi, dzudzulani ophunzira anu.” “Ndinena ndi inu,” akuyankha motero Yesu, “ngati awa akhala chete miyala idzafuula.” Asanachoke, Yesu aona kuti m’kachisi akuchitiramo malonda.—Luka 19:39, 40; Mateyu 21:15, 16; Marko 11:11.
Nisani 10
Yesu akufika msanga pakachisi. Dzulo lake, iye anakwiya kwambiri chifukwa chakuti ena akuchita malonda adzaoneni ndi kulambira kwa Atate wake, Yehova Mulungu. Choncho, mwachangu choyaka moto, ayamba kuthamangitsira kunja awo amene akugula ndi kugulitsa m’kachisi. Kenako agubuduza mathebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. “Chalembedwa,” Yesu akukalipa motero, “Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.”—Mateyu 21:12, 13.
Ansembe aakulu, alembi, ndi akuluakulu ena akunyansidwa kwambiri ndi zochita za Yesu ndi kuphunzitsa kwake poyera. Iwo akufunitsitsa zedi kuti amuphe! Koma akulephera kuchita zimenezo chifukwa cha khamulo popeza kuti anthu akuchita chidwi ndi chiphunzitso cha Yesu ndipo ‘akumlendeŵera Iye kuti amve.’ (Luka 19:47, 48) Pamene kuyamba kuda, Yesu ndi atsamwali ake akubwerera ku Betaniya mosangalala kukagona.
Nisani 11
Ndi mmaŵa kwambiri, ndipo Yesu ndi ophunzira ake ali kale paulendo wopita ku Yerusalemu kudutsa Phiri la Azitona. Atafika pakachisi, ansembe aakulu akumfikira Yesu mosataya nthaŵi. Iwo akukumbukira kwambiri zimene iye anachita kwa osintha ndalama ndi amalonda a m’kachisi. Adani akewa akufunsa moipidwa kuti: “Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?” “Inenso ndikufunsani mawu amodzi,” Yesu akutero. “Ngati mundiuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi: Ubatizo wa Yohane, uchokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu?” Ataunjikizana, otsutsawo akambitsirana kuti: “Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye? Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.” Posoŵa chonena, ayankha mofooka nati: “Sitidziŵa ife.” Yesu awayankha modekha nati: “Inenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi.”—Mateyu 21:23-27.
Adani a Yesu tsopano afuna kumkola mwa kuyesa kumchititsa kunena chinthu chimene angamgwirirepo. Iwo akufunsa kuti: “Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iyayi?” “Tandionetsani Ine ndalama yamsonkho,” Yesu akuyankha. Nafunsa kuti: “Nchayani chithunzithunzi ichi, ndi kulemba kwake?” “Cha Kaisara,” iwo akutero. Mowazizwitsa, Yesu akunena mokweza kuti onse amve nati: “Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”—Mateyu 22:15-22.
Atatsutsa adani ake kotheratu moti iwo asoŵa chonena, Yesu tsopano awadzudzula pamaso pa makamu a anthu ndi ophunzira ake. Tamverani pamene adzudzula alembi ndi Afarisi mopanda mantha. Iye akuti: “Musatsanza ntchito zawo; pakuti iwo amalankhula, koma samachita.” Molimba mtima, atchula masoka ambiri amene adzawagwera, awatcha atsogoleri akhungu ndiponso onyenga. “Njoka inu, obadwa inu a mamba,” Yesu akutero, “mudzatha bwanji kuthaŵa kulanga kwake kwa gehena?”—Mateyu 23:1-33.
Chidzudzulo choŵaŵa chimenechi sichikutanthauza kuti Yesu sakuona ubwino wa anthu ena. Pambuyo pake, iye akuona anthu akuika ndalama m’zosungiramo ndalama za m’kachisi. Iye akukhudzika mtima chotani nanga ataona mkazi wamasiye waumphaŵi akuikamo ndalama zake zonse—timakobiri tiŵiri tochepa mphamvu! Pomuyamikira mochokera pansi pa mtima, Yesu akunena kuti, kwenikweni, iye waikamo kuposa onse amene anaikamo ndalama zambiri “mwa unyinji wawo.” Mwachikondi chake chachikulu, Yesu amayamikira kwambiri zonse zimene munthu angathe kuchita.—Luka 21:1-4.
Yesu tsopano akuchoka pakachisi kwa nthaŵi yomaliza. Ophunzira ake ena akunena za kukongola kwa kachisiyo, nati “anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka.” Mowadabwitsa, Yesu akuyankha kuti: “Adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala unzake, umene sudzagwetsedwa.” (Luka 21:5, 6) Pamene atumwi atsatira Yesu potuluka mumzinda wapiringupiringu umenewo, iwo sakudziŵa bwino chimene akutanthauza.
Eya, posapita nthaŵi Yesu ndi atumwi ake akukhala pansi nasangalala ndi mtendere ndi bata m’Phiri la Azitona. Pamene akuyang’ana kukongola kwa Yerusalemu ndi kwa kachisi, Petro, Yakobo, Yohane, ndi Andreya akupempha Yesu kuti amasulire ulosi wake wodabwitsawo. “Mutiuze ife,” iwo akutero, “zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika [“kukhalapo,” NW] kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?”—Mateyu 24:3; Marko 13:3, 4.
Poyankha, Mphunzitsi Wamkuluyo akupereka ulosi wapaderadi. Akuneneratu za nkhondo zazikulu, zivomezi, njala, ndi miliri. Yesu akuloseranso kuti uthenga wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi. “Pomwepo,” iye akuchenjeza motero, “padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.”—Mateyu 24:7, 14, 21; Luka 21:10, 11.
Atumwi anayiwo akumvetsera mosamalitsa pamene Yesu akufotokoza mbali zina za ‘chizindikiro cha kukhalapo kwake.’ Iye akugogomezera kuti iwo afunikira ‘kudikira.’ Chifukwa ninji? “Pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu,” iye akuyankha motero.—Mateyu 24:42; Marko 13:33, 35, 37.
Limeneli lakhala tsiku losaiŵalika kwa Yesu ndi atumwi ake. Kwenikweni, ndilo tsiku lomaliza la utumiki wapoyera wa Yesu asanammange, kumzenga mlandu, ndi kumupha. Popeza kuti kwayamba kuda, iwo akuyamba kuyenda ulendo wobwerera ku Betaniya, mtunda waufupi kuseri kwa phirilo.
Nisani 12 ndi 13
Pa Nisani 12, Yesu akukhala phee ndi ophunzira ake. Iye akudziŵa kuti atsogoleri achipembedzo akufunitsitsa kumupha, ndipo sakufuna kuti iwo asokoneze phwando lake la Paskha tsiku lotsatira madzulo. (Marko 14:1, 2) Tsiku lotsatiralo, Nisani 13, anthu ngotanganidwa ndi kupanga makonzedwe omaliza a Paskha. Mwamsanga masana, Yesu atumiza Petro ndi Yohane kuti akawakonzere Paskha m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu. (Marko 14:12-16; Luka 22:8) Kutangotsala pang’ono kuti dzuŵa liloŵe, Yesu ndi atumwi ake ena khumi akuwapeza kumeneko kuti achite phwando lomaliza la Paskha.
Nisani 14, Dzuŵa Litaloŵa
Yerusalemu ali ngwee ndi mwezi wokhwima umene ukutuluka kuseri kwa Phiri la Azitona. M’chipinda chachikulu chokonzedwa bwino, Yesu ndi 12 enawo ali pagome lachakudya. “Ndinalakalaka ndithu kudya Paskha uwu pamodzi ndi inu, ndisanayambe kusautsidwa,” iye akutero. (Luka 22:14, 15) Patapita nthaŵi atumwiwo akudabwa kuona Yesu akunyamuka ndi kuvula malaya ake akunja. Atatenga chopukutira ndi mkhate wa madzi, akuyamba kusambitsa mapazi awo. Ndi phunziro losaiŵalika chotani nanga la kutumikira modzichepetsa!—Yohane 13:2-15.
Komabe, Yesu akudziŵa kuti mmodzi mwa amuna ameneŵa—Yudasi Isikariote—ali wokonzekera kumpereka kwa atsogoleri achipembedzo. Chifukwa cha zimenezo, iye akuvutika maganizo kwambiri. “Mmodzi wa inu adzandipereka Ine,” akuwauza motero. Atumwiwo akugwidwa chisoni chachikulu ndi zimenezi. (Mateyu 26:21, 22) Atachita Paskha, Yesu akuuza Yudasi kuti: “Chimene uchita, chita msanga.”—Yohane 13:27.
Yudasi atachoka, Yesu akuyambitsa madyerero okumbukira imfa yake imene yayandikira. Akutenga mtanda wa mkate wopanda chotupitsa, ayamika m’pemphero, aunyema, nalangiza atumwi 11 amenewo kuti adye. “Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa,” akuwauza motero. Kenaka akutenga chikho cha vinyo wofiira. Atamdalitsa vinyowo, akuwapatsira chikhocho, nawauza kuti amwe. Yesu akuwonjezera kuti: “Ichi ndicho mwazi wanga wa pangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.”—Luka 22:19, 20; Mateyu 26:26-28.
Madzulo osaiŵalika amenewo, Yesu akuphunzitsa atumwi ake okhulupirika zinthu zambiri zothandiza, kuphatikizapo kufunika kwa kukondana monga abale. (Yohane 13:34, 35) Iye akuwatsimikizira kuti adzalandira “nkhoswe,” mzimu woyera. Udzawakumbutsa zinthu zonse zimene iye anawauza. (Yohane 14:26) Pambuyo pake madzulowo, ayenera kuti akulimbikitsidwa kwambiri kumva Yesu akuwapempherera mokhudzika mtima. (Yohane, chaputala 17) Ataimba nyimbo zachitamando, iwo akutuluka m’chipinda chapamwambacho ndi kutsatira Yesu kunja kozizira bwino usiku.
Atadutsa Chigwa cha Kedroni, Yesu ndi atumwi ake akupita ku amodzi mwa malo awo apamtima, munda wa Getsemane. (Yohane 18:1, 2) Pamene atumwi ake adikira, Yesu apita payekha kukapemphera. Iye akupsinjika maganizo kwadzaoneni pamene akupempha Mulungu mochokera mumtima kuti amthandize. (Luka 22:44) Kungolingalira za chitonzo chimene angadzetse pa dzina la Atate wake wakumwamba ngati atalephera, kukumvutisa maganizo koopsa.
Yesu wangomaliza kumene kupemphera, Yudasi Isikariote akufika ndi khamu la anthu amene anyamula malupanga, mikunkhu, ndi miuni. “Tikuoneni, Rabi,” akutero Yudasi, ndipo apsompsona Yesu. Chimenechi nchizindikiro chakuti amunawo amgwire Yesu. Mwadzidzidzi, Petro mwamsanga akukantha kapolo wa mkulu wa ansembe ndi kumdula khutu. “Tabweza lupanga lako m’chimakemo,” Yesu akutero pamene akuchiritsa khutu la munthuyo. “Onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.”—Mateyu 26:47-52.
Zonsezi zikuchitika pakanthaŵi kochepa! Yesu akugwidwa ndi kumangidwa. Chifukwa cha mantha ndiponso atasoŵa chochita, atumwiwo akumsiya Mbuyawo nathaŵa. Yesu akutengeredwa kwa Anasi, mkulu wa ansembe wakale. Kenako akutengeredwa kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kukazengedwa mlandu. Mmamaŵa, bwalo la Sanhedrin monyenga liimba Yesu mlandu wa mwano. Kenako, Kayafa akumtumiza kwa bwanamkubwa wa Roma, Pontiyo Pilato. Iyeyu akutumiza Yesu kwa Herode Antipa, wolamulira wa Galileya. Herode ndi asilikali ake anyodola Yesu. Kenako amtumizanso kwa Pilato. Pilato akusonyeza kuti Yesu alidi wosachimwa. Koma atsogoleri achipembedzo achiyuda amkakamiza kugamula kuti Yesu aphedwe. Atamnyoza ndi kumzunza ndithu, Yesu akutulutsidwa ndipo akupita naye ku Golgota kumene akumkhomera pamtengo wozunzirapo mopanda chifundo ndipo akufa imfa yopweteka koopsa.—Marko 14:50–15:39; Luka 23:4-25.
Likanakhala tsoka lalikulu koposa m’mbiri yonse ngati imfa ya Yesu ikadakhala mapeto a moyo wake wonse. Komatu si mmene zinalili. Pa Nisani 16, 33 C.E., ophunzira ake anadabwa kupeza kuti waukitsidwa kwa akufa. M’kupita kwa nthaŵi, anthu oposa 500 anadzionera ndi maso kuti Yesu anakhalanso ndi moyo. Ndipo patapita masiku 40 ataukitsidwa, gulu la otsatira ake okhulupirika linamuona akukwera kumwamba.—Machitidwe 1:9-11; 1 Akorinto 15:3-8.
Moyo wa Yesu ndi Inu
Kodi zimenezi zikukukhudzani motani inuyo—tingoti tonsefe? Ndithudi, utumiki wa Yesu, imfa yake ndi kuukitsidwa kwake zimalemekeza Yehova Mulungu ndipo nzofunika kwambiri kuti chifuno Chake chachikulu chikwaniritsidwe. (Akolose 1:18-20) Nzofunika kwambiri kwa ife chifukwa chakuti machimo athu amakhululukidwa pamaziko a nsembe ya Yesu, chotero timakhala paunansi wathithithi ndi Yehova Mulungu.—Yohane 14:6; 1 Yohane 2:1, 2.
Ngakhale anthu akufa akukhudzidwa. Kuukitsidwa kwa Yesu kumapereka mwaŵi wakuti iwo akakhalenso ndi moyo m’dziko lapansi la Paradaiso limene Mulungu analonjeza. (Luka 23:39-43; 1 Akorinto 15:20-22) Ngati mukufuna kudziŵa zambiri zokhudzana ndi nkhanizi, tikukupemphani kuti mudzakhale nawo pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu pa April 11, 1998, pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kwanuko.
[Bokosi patsamba 6]
“Phanga la Achifwamba”
YESU anali ndi chifukwa chabwino chonenera kuti eni malonda aumbombo anasandutsa kachisi wa Mulungu kukhala “phanga la achifwamba.” (Mateyu 21:12, 13) Kuti alipire msonkho wa pakachisi, Ayuda ndi otembenukira kuchiyuda ochokera kumaiko ena anayenera kusinthanitsa ndalama zakwawo ndi ndalama zololedwa. M’buku lake lakuti The Life and Times of Jesus the Messiah (Moyo ndi Nthaŵi za Yesu Mesiya), Alfred Edersheim anafotokoza kuti osintha ndalama anali kuyamba malonda awo m’madera osiyanasiyana pa Adara 15, patatsala mwezi umodzi kuti Paskha ichitike. Kuyambira pa Adara 25, iwo anali kuloŵa m’mabwalo a kachisi m’Yerusalemu kuti akapezerepo phindu pa Ayuda ndi otembenukira kuchiyuda amene anali kusonkhana miyandamiyanda. Eni malondawo anali kupeza phindu lalikulu, popeza anali kufuna malipiro pachidutswa chilichonse cha ndalama chimene asintha. Popeza Yesu anawatcha achifwamba zikusonyeza kuti malipiro amenewo anali aakulu kwambiri moti, kwenikweni, anali kubera ndalama anthu osauka.
Ena sanali kubwera ndi nyama zawo zodzapereka nsembe. Aliyense amene anabweretsa nyama yake anayenera kuipimitsa kwa wopima wa pakachisi—ndipo anayenera kulipira. Pofuna kupeŵa tsoka lakuti nyama yawo nkukanidwa atayenda nayo ulendo wautali, ambiri anali kugula nyama “yovomerezedwa” ndi Alevi kwa amalonda adyera a pakachisi. “Anthu ambiri aumphaŵi anali kuwalipiritsa ndalama zambiri pamenepo,” anatero katswiri wina wamaphunziro.
Pali umboni wakuti mkulu wa ansembe wakale Anasi ndi banja lake anali kuchirikiza kwambiri amalonda a pakachisiwo. Zolemba za Arabi zimasimba za “Misika [ya pakachisi] ya ana a Anasi.” Iwo anali kupeza ndalama zambiri pamsonkho wa osintha ndalama ndiponso mwa kugulitsa nyama pamabwalo a kachisi. Katswiri wina wamaphunziro anati zimene Yesu anachita mwa kutulutsira kunja amalondawo “anazichita osati chabe chifukwa chofuna kuthetsa khalidwe la ansembe komanso pofuna kuwathetsera njira yawo yopezera ndalama.” Kaya chinali chifukwa chotani, adani ake anali ofunitsitsadi kumupha!—Luka 19:45-48.
[Tchati patsamba 4]
Masiku Omaliza a Moyo wa Yesu Monga Munthu
Nisani 33 C.E. Zochitika Munthu Wamkulua
7 Lachisanu Yesu ndi ophunzira ake ayenda 101, ndime 1
kuchokera ku Yeriko kupita ku
Yerusalemu (Nisani 7 ndilo
Lamlungu, April 5, 1998,
ngakhale kuti masiku achihebri
anali kuyamba madzulo ndi kutha
madzulo tsiku lotsatira)
8 Lachisanu madzulo Yesu ndi ophunzira ake afika ku 101,
Betaniya; Sabata liyamba ndime 2-4
Loŵeruka Sabata (Lolemba, April 6, 1998) 101, ndime 4
9 Loŵeruka madzulo Akudya ndi Simoni wakhate; Mariya 101,
adzoza Yesu ndi mafuta a nardo; ndime 5-9
ambiri abwera kuchokera ku
Yerusalemu kudzaona ndi
kumvetsera Yesu
Lamlungu Kuloŵa m’Yerusalemu mwachipambano;
aphunzitsa m’kachisi 102
10 Lolemba Ulendo wokaloŵa m’Yerusalemu mmaŵa; 103, 104
ayeretsa kachisi; Yehova alankhula
ali kumwamba
11 Lachiŵiri Ku Yerusalemu, aphunzitsa pakachisi 105 mpaka 112,
mwa kugwiritsira ntchito mafanizo; ndime 1
atsutsa Afarisi; aona chopereka
cha mkazi wamasiye; apereka
chizindikiro cha kukhalapo kwake
kwamtsogolo
12 Lachitatu Tsiku la phee ndi ophunzira ake 112,
ku Betaniya; Yudasi alinganiza ndime 2-4
zompereka
13 Lachinayi Petro ndi Yohane akonzekera Paskha 112,
ku Yerusalemu; Yesu ndi atumwi ndime 5 mpaka
khumi enawo awatsatira madzulo 113, ndime 1
kwambiri (Loweruka April 11, 1998)
14 Lachinayi madzulo Phwando la Paskha; Yesu asambitsa 113,
mapazi a atumwi; Yudasi atuluka ndime 2
kuti adzapereke Yesu; Kristu mpaka 117
ayambitsa Chikumbutso cha imfa
yake (Dzuŵa litaloŵa, Loŵeruka,
April 11, 1998)
Nthaŵi itapyola Aperekedwa ndi kugwidwa m’munda wa 118 mpaka 120
pakati pa usiku Getsemane; atumwi athaŵa; azengedwa
mlandu pamaso pa ansembe aakulu
ndi Sanhedrin; Petro akana Yesu
Lachisanu kuyambira Alinso pamaso pa Sanhedrin; 121 mpaka 127,
pa kuloŵa kwa dzuŵa kwa Pilato, kenako kwa Herode, ndime 7 kubwereranso kwa Pilato;
aweruzidwa kuti aphedwe;
apachikidwa; aikidwa m’manda
15 Loŵeruka Sabata; Pilato alola alonda 127, ndime 8-10
kukalonda manda a Yesu
16 Lamlungu Yesu aukitsidwa 128
[Mawu a M’munsi]
a Amene andandalitsidwa pano ndiwo manambala a mitu m’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mukufuna tchati chosonyeza malifalensi atsatanetsatane a utumiki womalizira wa Yesu, onani buku lakuti “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” patsamba 290. Mabuku ameneŵa anafalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.