MUTU 10
“Malemba Amati”
1-3. Kodi Yesu ankafuna kuti anthu a ku Nazareti adziwe chiyani, ndipo anawapatsa umboni wotani?
KUMAYAMBIRIRO kwa utumiki wake, Yesu anabwerera kumzinda wakwawo ku Nazareti. Cholinga chake pa ulendowu chinali kuthandiza anthu kuti adziwe zoti iye anali Mesiya wolonjezedwa. Kodi Yesu anapereka umboni wotani wotsimikizira kuti anali Mesiya?
2 N’zosakayikitsa kuti anthu ambiri ankayembekezera kuti Yesu achita zozizwitsa chifukwa anali atamva kuti iye akuchita zozizwitsa. Komabe Yesu sanachite chozizwitsa chilichonse. M’malomwake iye anapita kusunagoge monga mwa chizolowezi chake. Kumeneko anaimirira kuti awerenge Malemba ndipo anamupatsa mpukutu wa Yesaya. Mpukutuwu unali wautali ndipo anaukulunga pandodo ziwiri. Choncho Yesu ankatambasula mbali imodzi ya mpukutuwo, kwinaku akukulunga mbali inayo mpaka anapeza ndime imene ankafuna. Kenako mokweza, anawerenga mawu amene panopa akupezeka pa Yesaya 61:1-3.—Luka 4:16-19.
3 Anthu ankadziwa kuti mawu amene akuwerengawo ndi ulosi wonena za Mesiya. Choncho onse anangokhala chete n’kumamuyang’anitsitsa. Kenako Yesu anayamba kufotokoza momveka bwino kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.” Ngakhale kuti anthuwo anadabwa ndi mawu ake ogwira mtimawo, ambiri ankafunabe kuona zozizwitsa. Molimba mtima, Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo cha m’Malemba posonyeza kuti anthuwo analibe chikhulupiriro. Pasanapite nthawi, anthu a ku Nazareti anayamba kufunafuna njira yoti amuphere.—Luka 4:20-30.
4. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani mu utumiki wake, nanga tikambirana chiyani m’mutu uno?
4 Pamenepa Yesu anasonyeza kuti ankadalira kwambiri Mawu a Mulungu omwe ndi ouziridwa ndipo anapitiriza kuchita zimenezi pa utumiki wake wonse. N’zoona kuti zozizwitsa zake zinali zofunika kwambiri chifukwa zinkasonyeza kuti mzimu wa Mulungu unali pa iye. Komabe, palibe chilichonse chimene chinali chofunika kwambiri kwa iye kuposa Malemba Opatulika. Tiyeni tione chitsanzo chimene anapereka pa nkhani imeneyi. Ambuye wathu ankagwira Malemba, ankateteza Mawu a Mulungu komanso ankafotokoza matanthauzo ake ndipo m’mutu uno tikambirana mwatsatanetsatane mmene ankachitira zimenezi.
Yesu Ankagwira Malemba
5. Kodi Yesu ankafuna kuti anthu amene ankamumvetsera adziwe chiyani, ndipo anasonyeza bwanji kuti zimene ankanenazo zinali zoona?
5 Yesu ankafuna kuti anthu adziwe kumene kunkachokera uthenga umene ankaphunzitsa. Iye anati: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga, koma ndi za amene anandituma.” (Yohane 7:16) Pa nthawi inanso, iye anati: “Sindichita chilichonse mongoganiza ndekha. Koma zimene ndimalankhula zimakhala zogwirizana ndendende ndi zimene Atate anandiphunzitsa.” (Yohane 8:28) Iye ananenanso kuti: “Zinthu zimene ndimakuuzani sindilankhula zam’maganizo mwanga, koma Atate amene ndi wogwirizana ndi ine ndi amene akuchita ntchito zake kudzera mwa ine.” (Yohane 14:10) Mobwerezabwereza, Yesu ankagwira Malemba ndipo imeneyo inali njira imodzi imene ankasonyezera kuti zimene ankanenazo zinali zoona.
6, 7. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankakonda kugwira mawu Malemba a Chiheberi, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zochititsa chidwi? (b) Kodi zimene Yesu ankaphunzitsa zinkasiyana bwanji ndi zimene alembi ankaphunzitsa?
6 Tikamaphunzira mosamala mawu a Yesu amene analembedwa, tingaone kuti iye anagwira mawu kapena anatchula mfundo zochokera m’mabuku oposa hafu ya Malemba a Chiheberi. Poyamba zimenezi sizingakhale zochititsa chidwi. Mwina mungadabwe kuti n’chifukwa chiyani Yesu sanagwire mawu mabuku onse ouziridwa amene analipo pa nthawi imene ankalalikira ndi kuphunzitsa kwa zaka zitatu ndi hafu. Komatu n’kutheka kuti iye anagwira mawu mabuku onse. Kumbukirani kuti mbali yochepa chabe ya zimene Yesu ananena ndi kuchita ndi imene inalembedwa. (Yohane 21:25) Ndipotu mawu onse a Yesu amene analembedwa mungawawerenge mokweza m’maola ochepa chabe. N’zoonekeratu kuti si zophweka kuti munthu alankhule za Mulungu ndi Ufumu wake kwa maola ochepa koma n’kumatha kugwira mawu kuchokera m’mabuku oposa hafu ya Malemba a Chiheberi. Ndipotu nthawi zambiri Yesu ankakhala alibe mipukutu polalikira. Mwachitsanzo, pa ulaliki wake wotchuka wa paphiri, Yesu anagwira mawu Malemba a Chiheberi kapena anangotchulako mfundo zake kambirimbiri kuchokera pamtima osati mochita kuwerenga.
7 Yesu ankakonda kugwira Malemba ndipo zimenezi zinasonyeza kuti ankalemekeza kwambiri Mawu a Mulungu. Anthu amene ankamumvetsera “anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake, chifukwa ankawaphunzitsa monga munthu wokhala ndi ulamuliro, osati ngati alembi.” (Maliko 1:22) Alembi akamaphunzitsa, ankakonda kutchula mfundo za m’malamulo amene arabi ophunzira kwambiri akale ankaphunzitsa. Koma Yesu sananenepo n’kamodzi komwe kuti zimene ankaphunzitsa n’zochokera m’malamulo a arabi amenewo. M’malomwake, iye ankagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pophunzitsa. Nthawi zambiri iye ankanena kuti: “Malemba amati.” Mobwerezabwereza iye ankanena mawu amenewa kapena ofanana nawo pophunzitsa otsatira ake komanso pochotsa maganizo olakwika amene anthu anali nawo.
8, 9. (a) Pamene ankayeretsa kachisi, kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ulamuliro wake unali wochokera m’Mawu a Mulungu? (b) Kodi atsogoleri a chipembedzo kukachisi anasonyeza bwanji kuti ankanyoza kwambiri Mawu a Mulungu?
8 Pamene Yesu ankayeretsa kachisi ku Yerusalemu, ananena kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo,’ koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.” (Mateyu 21:12, 13; Yesaya 56:7; Yeremiya 7:11) Chadzulo lake, Yesu anali atachita ntchito zambiri zozizwitsa kumeneko, ndipo ana anachita chidwi kwambiri n’kuyamba kumutamanda. Koma atsogoleri achipembedzo anakwiya ndipo anafunsa Yesu ngati anamva zimene anawo ankanena. Iye anawayankha kuti: “Inde. Kodi simunawerenge zimenezi kuti, ‘Mwachititsa kuti m’kamwa mwa ana ndi mwa makanda mutuluke mawu otamanda’?” (Mateyu 21:16; Salimo 8:2) Yesu ankafuna kuti anthu amenewo adziwe kuti Mawu a Mulungu akuvomereza zimene anawo ankachita.
9 Kenako atsogoleri achipembedzowo anasonkhana pamodzi ndipo anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti: “Kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi?” (Mateyu 21:23) Yesu anafotokoza momveka bwino kumene kunachokera ulamuliro wake. Iye sankaphunzitsa zinthu zatsopano, koma ankangogwiritsa ntchito zimene Mawu ouziridwa a Atate ake akunena. Choncho pofunsa funso limeneli, ansembe ndi alembiwo ankanyoza kwambiri Yehova komanso Mawu ake. M’pake kuti Yesu anawadzudzula powauza kuti zolinga zawo zinali zoipa.—Mateyu 21:23-46.
10. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu tikamagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, nanga tili ndi chiyani chimene Yesu analibe?
10 Mofanana ndi Yesu, Akhristu oona masiku ano amadalira Mawu a Mulungu mu utumiki. A Mboni za Yehova amadziwika padziko lonse lapansi chifukwa cha khama lawo pa ntchito youza ena uthenga wochokera m’Baibulo. Komanso m’mabuku athu mumakhala mawu ambiri ochokera m’Baibulo. Ifenso tikamalankhula ndi anthu mu utumiki timayesetsa kugwiritsa ntchito Malemba. (2 Timoteyo 3:16) Timasangalala kwambiri munthu akalola kuti tiwerenge naye Baibulo ndiponso kufotokoza tanthauzo la Mawu a Mulungu komanso mmene angatithandizire. N’zoona kuti ife sitidziwa zambiri ngati Yesu, koma tili ndi mabuku ambiri amene Yesu analibe. Tilinso ndi mabuku ambiri amene timagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo ndipo angatithandize kupeza lemba limene tingafune, komanso tili ndi Baibulo lonse lathunthu limene likusindikizidwabe m’zinenero zambiri. Choncho tiyeni tipitirize kutchula mawu a m’Baibulo ndiponso kuyesetsa kuliwerenga nthawi zonse tikamakambirana ndi anthu.
Yesu Ankateteza Mawu a Mulungu
11. N’chifukwa chiyani nthawi zambiri Yesu ankafunika kuteteza Mawu a Mulungu?
11 Yesu anaona kuti Mawu a Mulungu akupotozedwa, koma zimenezi sizinamudabwitse. Popemphera kwa Atate ake, Yesu anati: “Mawu anu ndi choonadi.” (Yohane 17:17) Komanso Yesu ankadziwa bwino kuti Satana, yemwe ndi “wolamulira wa dziko,” ndi “wabodza komanso tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44; 14:30) Pokana mayesero a Satana, Yesu anatchula mawu a m’Malemba katatu konse. Satana anatchula mawu a m’vesi limodzi la Masalimo ndipo mwadala, analigwiritsa ntchito molakwika, koma poyankha, Yesu anateteza Mawu a Mulungu.—Mateyu 4:6, 7.
12-14. (a) Kodi atsogoleri achipembedzo anasonyeza bwanji kuti sankalemekeza Chilamulo cha Mose? (b) Kodi Yesu anateteza bwanji Mawu a Mulungu?
12 Kawirikawiri Yesu ankateteza Malemba Opatulika kuti asagwiritsidwe ntchito kapena kutanthauziridwa molakwika. Atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake ankapotoza Mawu a Mulungu. Iwo ankalimbikitsa kwambiri anthu kuti azitsatira zinthu zing’onozing’ono za m’Chilamulo cha Mose, koma ankanyalanyaza mfundo zofunika kwambiri zimene zinali ngati phata la malamulowo. Iwo ankalimbikitsa anthu kuti azilambira mwamwambo chabe n’cholinga choti ena awaone, koma sankawalimbikitsa kuchita zinthu zofunika monga kukhala achilungamo, achifundo ndiponso okhulupirika. (Mateyu 23:23) Kodi pamenepa Yesu anateteza bwanji Chilamulo cha Mulungu?
13 Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu akafuna kunena mfundo ya m’Chilamulo cha Mose, mobwerezabwereza ankagwiritsa ntchito mawu akuti, “Inu munamva kuti anati.” Kenako iye ankanena kuti, “Koma ine ndikukuuzani kuti,” ndipo akatero ankafotokoza mfundoyo mozama osati kungowalimbikitsa kutsatira Chilamulocho mwamwambo chabe. Kodi iye ankatsutsana ndi Chilamulo? Ayi ndithu, koma ankachiteteza. Mwachitsanzo, anthu ankadziwa bwino lamulo lakuti “Musaphe munthu.” Koma Yesu anawauza kuti ngati atamvetsa mfundo ya chilamulocho, sangadane n’komwe ndi munthu, chifukwa munthu kuti aphe mnzake, amayamba wadana naye kaye. Komanso kulakalaka munthu amene sunakwatirane naye n’kosemphana ndi mfundo yaikulu ya lamulo la Mulungu loletsa kuchita chigololo.—Mateyu 5:17, 18, 21, 22, 27-39.
14 Popereka chitsanzo chomaliza, Yesu anati: “Inu munamva kuti anati: ‘Uzikonda mnzako ndipo uzidana ndi mdani wako.’ Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” (Mateyu 5:43, 44) Kodi lamulo lakuti “uzidana ndi mdani wako” linali lochokera m’Mawu a Mulungu? Ayi, atsogoleri achipembedzo anapanga okha lamuloli n’kumaphunzitsa anthu. Iwo anapangitsa Chilamulo changwiro cha Mulungu kukhala chopanda pake chifukwa chophunzitsa maganizo a anthu. Yesu anateteza mopanda mantha Mawu a Mulungu kuti asawonongedwe ndi miyambo ya anthu.—Maliko 7:9-13.
15. Kodi Yesu anateteza bwanji Chilamulo cha Mulungu kwa anthu amene ankafuna kuti chizioneka ngati chokhwimitsa zinthu kwambiri kapena cholimbikitsa nkhanza?
15 Atsogoleri achipembedzo ankapotozanso Chilamulo cha Mulungu pochipangitsa kuti chizioneka ngati chokhwimitsa zinthu kwambiri kapena cholimbikitsa nkhanza. Mwachitsanzo, pamene ophunzira a Yesu ankadutsa m’munda wa tirigu n’kumabudula ngala zake, Afarisi ena anawanena kuti akuswa Sabata. Koma Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo cha m’Malemba poteteza Mawu a Mulungu ku maganizo olakwikawo. Iye anatchula mawu a lemba limene limanena kuti Davide ndi anyamata ake atamva njala anatenga mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu m’kachisi ndi kukadyera kunja kwa kachisiyo. Yesu anasonyeza Afarisiwo kuti iwo sanamvetse mfundo yakuti Yehova ndi wachifundo komanso wokoma mtima.—Maliko 2:23-27.
16. Kodi atsogoleri achipembedzo anatani ndi lamulo la Mose lokhudza kuthetsa ukwati, nanga Yesu anathetsa bwanji vutolo?
16 Atsogoleri achipembedzo anapeza njira zachinyengo zozembera kutsatira Chilamulo cha Mulungu. Mwachitsanzo, Chilamulo chinkalola mwamuna kuthetsa ukwati ndi mkazi wake ngati wamupeza ndi “vuto linalake” lalikulu limene lingachititse manyazi banja lake. (Deuteronomo 24:1) Komabe, pamene nthawi ya Yesu inkafika, atsogoleri achipembedzo anali atapezerapo mwayi pa lamuloli ndipo ankalola amuna kusiya akazi awo pa zifukwa zing’onozing’ono monga ngati kupsereza chakudya.a Yesu anasonyeza kuti atsogoleri achipembedzowo ankapotoza kwambiri mawu ouziridwa a Mose. Kenako iye anabwezeretsa cholinga choyambirira cha Yehova pa nkhani ya ukwati chakuti mwamuna azikhala ndi mkazi mmodzi yekha, ndipo ananena kuti banja lingathe pokhapokha ngati mkazi kapena mwamuna wachita chigololo.—Mateyu 19:3-12.
17. Kodi Akhristu masiku ano angatsanzire bwanji Yesu poteteza Mawu a Mulungu?
17 Mofanana ndi Khristu, otsatira ake masiku ano amaona kuti ali ndi udindo woteteza Malemba Oyera. Atsogoleri achipembedzo akamanena kuti mfundo za makhalidwe abwino za m’Mawu a Mulungu n’zachikale, kwenikweni amakhala akutsutsa zimene Baibulo limanena. Ndipo zipembedzo zimapotoza mawu a m’Baibulo pophunzitsa zinthu zabodza n’kumanena kuti zikuchokera m’Baibulo. Koma ife timaona kuti tili ndi mwayi waukulu tikamateteza choonadi cha m’Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, timachita zimenezi tikamasonyeza kuti si zoona kuti kuli milungu itatu mwa mulungu mmodzi. (Deuteronomo 4:39) Choncho mosamala, timateteza Mawu a Mulungu mofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.—1 Petulo 3:15.
Yesu Ankatanthauzira Mawu a Mulungu Momveka Bwino
18, 19. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti Yesu ankatanthauzira Mawu a Mulungu momveka bwino?
18 Yesu analipo kumwamba pamene Malemba a Chiheberi ankalembedwa. Ndipo iye anasangalala kwambiri atamupatsa mwayi wobwera padziko lapansi kudzatanthauzira Mawu a Mulungu momveka bwino. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika pa tsiku losaiwalika Yesu ataukitsidwa, pamene anakumana ndi ophunzira ake awiri pamsewu wopita ku Emau. Ophunzirawo asanamuzindikire, anamuuza kuti anali ndi chisoni ndiponso anathedwa nzeru chifukwa cha imfa ya Mbuye wawo wokondedwa. Kodi Yesu anawayankha bwanji? Iye “anayamba kuwatanthauzira zinthu zokhudza iyeyo m’Malemba onse, kuyambira ndi Zolemba za Mose komanso zonse zimene aneneri analemba.” Kodi ophunzirawo anamva bwanji? Patapita nthawi, iwo anayamba kukambirana kuti: “Kodi si paja tinakhudzidwa kwambiri mumtima pamene amalankhula nafe mumsewu muja ndi kutifotokozera Malemba momveka bwino?”—Luka 24:15-32.
19 Pa nthawi ina tsiku lomwelo, Yesu anakumana ndi atumwi ake komanso anthu ena. Tamvani zimene anawachitira: “Anatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba.” (Luka 24:45) N’zosakayikitsa kuti zimenezo zinawakumbutsa kuti nthawi ina Yesu anachita kambirimbiri zinthu zofanana ndi zimenezi kwa iwowo komanso kwa aliyense amene ankamumvetsera. Iye nthawi zambiri ankagwira malemba odziwika bwino ndi kuwatanthauzira moti omvetserawo ankamvetsa bwino mfundo za m’Mawu a Mulungu m’njira yatsopano ndiponso mozama.
20, 21. Kodi Yesu anatanthauzira bwanji mawu amene Yehova analankhula kwa Mose pachitsamba choyaka moto?
20 Nthawi imodzi imene anachita zimenezi inali pamene ankalankhula ndi gulu la Asaduki. Anthu a m’gulu limeneli anagalukira chipembedzo cha Chiyuda koma ankagwirizana ndi ansembe. Asadukiwo sankakhulupirira kuti akufa adzauka, n’chifukwa chake Yesu anawauza kuti: “Kunena za kuuka kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti: ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’? Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa.” (Mateyu 22:31, 32) Lembali iwo ankalidziwa bwino kwambiri ndipo linalembedwa ndi Mose, munthu amene Asaduki ankamulemekeza kwambiri. Tiyeni tione mmene Yesu anatanthauzira lembali mogwira mtima.
21 Yehova analankhula ndi Mose pachitsamba choyaka moto cha m’ma 1514 B.C.E. (Ekisodo 3:2, 6) Pa nthawiyo, Abulahamu anali atamwalira ndipo panali patapita zaka 329, Isaki patapita zaka 224 ndipo Yakobo patapita zaka 197. Koma Yehova ananena kuti: “Ndine Mulungu” wawo. Asadukiwo ankadziwa kuti Yehova ndi wosiyana ndi mulungu amene anthu achikunja ankakhulupirira kuti amalamulira anthu akufa kumalo amizimu. Iye ndi Mulungu “wa anthu amoyo” monga mmene Yesu ananenera. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Yesu anamaliza ndi mawu amphamvu akuti: “Kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:38) Yehova akukumbukira atumiki ake okondedwa amene anamwalira, ndipo n’zosatheka kuti angawaiwale. Choncho Yehova ndi wotsimikiza ndi mtima wonse kuti adzawaukitsa ndipo n’chifukwa chake kwa iye onsewa ndi amoyo. (Aroma 4:16, 17) Apatu Yesu anafotokoza Mawu a Mulungu mochititsa chidwi kwambiri, ndipo n’chifukwa chake ‘gulu la anthulo linadabwa.’—Mateyu 22:33.
22, 23. (a) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pofotokoza tanthauzo la Mawu a Mulungu momveka bwino? (b) Kodi tikambirana chiyani m’mutu wotsatira?
22 Masiku ano, Akhristu ali ndi mwayi wotsanzira Yesu potanthauzira Mawu a Mulungu momveka bwino. N’zoona kuti ife si angwiro. Komabe nthawi zambiri timakambirana ndi anthu malemba amene akuwadziwa kale n’kuwafotokozera mfundo zina zimene mwina anali asanaziganizirepo. Mwachitsanzo, mwina kwa moyo wawo wonse akhala akunena mobwerezabwereza mawu akuti, “Dzina lanu liyeretsedwe” ndiponso akuti, “Ufumu wanu udze” koma sadziwa dzina la Mulungu kapenanso sadziwa kuti Ufumu wa Mulungu n’chiyani. (Mateyu 6:9, 10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Timaona kuti ndi mwayi waukulu munthu wina akavomera kuti timufotokozere mosavuta ndiponso momveka bwino choonadi cha m’Baibulo chimenechi.
23 Kuti titsanzire Yesu pouza ena choonadi, tizigwira Malemba, tiziteteza Mawu a Mulungu komanso tizifotokoza tanthauzo lake momveka bwino. M’mutu wotsatira tikambirana njira zothandiza zimene Yesu anagwiritsa ntchito kuti omvera ake amvetse bwino kwambiri choonadi cha m’Baibulo.
a Josephus, Mfarisi wolemba mbiri wa m’nthawi ya atumwi, amenenso ukwati wake unatha, ananena kuti kuthetsa ukwati kunali kololeka “pa chifukwa chilichonse (ndipo amuna ambiri amanena kuti ali ndi zifukwa zambiri zothetsera maukwati awo).”