Musakhale Mbali ya Dzikoli
“Perekani . . . za Mulungu, kwa Mulungu.”—MAT. 22:21.
1. Kodi zingatheke bwanji kumvera Mulungu komanso olamulira?
MAWU A MULUNGU amatiuza kuti tizimvera olamulira. Koma amanenanso kuti tiyenera kumvera Mulungu osati anthu. (Mac. 5:29; Tito 3:1) Kodi mfundo zimenezi zikutsutsana? Ayi. Yesu anatchula mfundo ina imene ingatithandize kudziwa zoyenera kuchita pa nkhaniyi. Iye anati: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”[1] (Mat. 22:21) Kodi tingatsatire bwanji malangizo amenewa? Tiyenera kumvera olamulira polemekeza akuluakulu a boma, kukhoma misonkho komanso kutsatira malamulo amene anakhazikitsa. (Aroma 13:7) Koma olamulira akatiuza kuti tiphwanye malamulo a Mulungu, tiyenera kukana mwaulemu.
2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitilowerera ndale?
2 Timapereka za Mulungu kwa Mulungu tikamapewa kulowerera ndale. (Yes. 2:4) Choncho sititsutsa boma kapena kulimbikitsa anthu kuti azikonda kwambiri dziko lawo. (Aroma 13:1, 2) Sitivota, sitiima pa chisankho ndipo sitiyesa kusintha zinthu m’boma.
3. N’chifukwa chiyani sitiyenera kulowerera ndale?
3 Baibulo limatiuza zifukwa zomveka zopewera ndale. Chifukwa choyamba n’chakuti timatsanzira Yesu. Paja iye sanali “mbali ya dziko” ndipo sankalowerera ndale. (Yoh. 6:15; 17:16) Chifukwa chachiwiri n’chakuti timafuna kukhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu. Kodi zingakhale zomveka kuti tizilalikira zoti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto, uku tikuthandizira andale? Anthu a m’zipembedzo zonyenga amagawanika chifukwa cha ndale. Koma Akhristu oona amakhala ogwirizana chifukwa salola kuti ndale ziwagawanitse.—1 Pet. 2:17.
4. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti nthawi ya mapeto ino tikhoza kukumana ndi mavuto chifukwa cha ndale? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera panopa kuti tisakhale mbali ya dzikoli?
4 Mwina panopa m’dziko lathu anthu satikakamiza kuchita ndale. Koma tiyenera kudziwa kuti pamene mapeto akuyandikira, tikhoza kukumana ndi mayesero pa nkhaniyi. M’dzikoli, anthu ambiri ndi “osafuna kugwirizana ndi anzawo” komanso “osamva za ena.” Choncho m’posavuta kuti anthu akhale ogawanika. (2 Tim. 3:3, 4) M’mayiko ena, zinthu zikasintha chifukwa cha ndale, abale ndi alongo amakumana ndi mavuto osayembekezereka. Choncho tiyenera kukonzekera panopa kuti tisakhale mbali ya dzikoli. Tikutero chifukwa chakuti tikangokhala mpaka pamene mayeserowo afika, tikhoza kupezeka tagonja. Tiyeni tsopano tikambirane mfundo 4 zimene zingatithandize pokonzekera kuti tisalowerere ndale.
TIZIONA MABOMA MMENE YEHOVA AMAWAONERA
5. Kodi Yehova amaona bwanji maboma a anthu?
5 Chinthu choyamba chimene chingatithandize, ndi kuona maboma mmene Yehova amawaonera. N’zoona kuti maboma ena angaoneke kuti ndi achilungamo, koma mfundo ndi yakuti cholinga cha Yehova sichinali choti anthu azilamulirana. (Yer. 10:23) Ndale zimachititsa kuti anthu asamagwirizane komanso kuti azikonda kwambiri dziko lawo. Ngakhale wolamulira atakhala wabwino chotani, sangathetse mavuto onse. Chinanso n’chakuti kuyambira mu 1914, maboma a anthu akhala akuchita zinthu zotsutsana ndi Ufumu wa Mulungu. Koma posachedwapa Ufumuwu udzawononga maboma onse.—Werengani Salimo 2:2, 7-9.
6. Kodi tizichita bwanji zinthu ndi akuluakulu a boma?
6 Yehova walola kuti maboma akhalepo n’cholinga choti azikhazikitsa bata. Izi zimathandiza kuti tizilalikira bwinobwino uthenga wa Ufumu. (Aroma 13:3, 4) Paja Yehova amatiuzanso kuti tizipempherera olamulirawa makamaka ngati zimene angasankhe zingakhudze kulambira kwathu. (1 Tim. 2:1, 2) Mofanana ndi Paulo, timathanso kupempha thandizo la boma ngati ena sanatichitire zachilungamo. (Mac. 25:11) N’zoona kuti Baibulo limanena kuti dziko lonse lili m’manja mwa Satana. Koma silinena kuti iye amalamulira mwachindunji munthu aliyense amene ali m’boma. (Luka 4:5, 6) Choncho si bwino kunena kuti wolamulira wakutiwakuti akutsogoleredwa ndi Mdyerekezi. Tiyeneranso kupewa kunenera zoipa “maboma ndiponso olamulira.”—Tito 3:1, 2.
7. Kodi tiyenera kupewa maganizo ati?
7 Timayesetsa kumvera Mulungu popewa kukondera chipani kapena munthu wandale aliyense, kaya akutithandiza kapena akutitsutsa. Koma nthawi zina kuchita zimenezi kumakhala kovuta. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti anthu akufuna kuchotsa boma limene likuzunza anthu kuphatikizapo atumiki a Yehova. Mwina sitingachite nawo zionetsero, koma kodi mumtima mwathu timamva bwanji? (Aef. 2:2) Tizikumbukira kuti zochita komanso zoganiza zathu ziyenera kusonyeza kuti sitilowereradi ndale.
TIZIKHALA “OCHENJERA” KOMA “OONA MTIMA”
8. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife “ochenjera ngati njoka” koma “oona mtima ngati nkhunda” pa nkhani za ndale?
8 Chinthu chachiwiri chimene chingatithandize, ndi kuyesetsa kukhala “ochenjera ngati njoka koma oona mtima ngati nkhunda.” (Werengani Mateyu 10:16, 17.) Timakhala ochenjera tikamaoneratu mavuto amene angabwere, ndipo timakhala oona mtima tikamapewa kulola mavutowo kutichititsa kulowerera ndale. Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene zingatithandize pa nkhaniyi.
9. Kodi tiyenera kupewa chiyani polankhula ndi anthu?
9 Zolankhula zathu. Anthu akayamba kukambirana za ndale, tiyenera kukhala osamala kwambiri. Tikamalalikira tiyenera kupewa kuchemerera kapena kutsutsa chipani kapenanso mtsogoleri winawake. Si bwinonso kukambirana zimene andale akufuna kuchita pothetsa mavuto. M’malomwake, tiyenera kugwiritsa ntchito Baibulo powathandiza kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto onse. Tiyerekeze kuti anthu ayamba kukambirana zokhudza ukwati wa amuna kapena akazi okhaokha kapena zokhudza kuchotsa mimba. Choyenera kuchita n’kufotokoza mfundo za m’Baibulo pa nkhaniyi komanso zimene timachita potsatira mfundozo. Pochita zimenezi tisasonyeze kuti tikugwirizana ndi maganizo a anthu ena andale. Komanso anthu akamanena kuti malamulo ena ayenera kusinthidwa kapena kuchotsedwa, sitiyenera kusonyeza kuti tili mbali inayake. Tisamawakakamizenso kuti atsatire maganizo athu.
10. Kodi tingapewe bwanji kusokonezedwa ndi ofalitsa nkhani?
10 Ofalitsa nkhani. Ofalitsa nkhani ambiri amalemba nkhani mokondera mbali inayake. Ndipo mabungwe ambiri ofalitsa nkhani amakhala a boma kapena a anthu andale. Atolankhani amatha kunena zinthu zokomera boma kapena chipani chinachake. Choncho tiyenera kupewa kutengeka ndi maganizo awo. Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimakonda kumvetsera mtolankhani winawake chifukwa choti ndimagwirizana ndi zimene amanena pa nkhani za ndale?’ Ngati tikufuna kumvetsera nkhani ndi bwino kusankha kumene tingamve zoona. Komanso tizipewa kumangomvetsera nkhani zolimbikitsa ndale kapena zosagwirizana ndi “chitsanzo cha mawu olondola” opezeka m’Baibulo.—2 Tim. 1:13.
11. Kodi kukonda kwambiri chuma chathu kungatilepheretse bwanji kukhala okhulupirika?
11 Kukonda chuma. Ngati timakonda kwambiri chuma tikhoza kugonja titayesedwa pa nkhani zokhudza ndale. Mlongo wina ku Malawi, dzina lake Ruth, anaona abale ndi alongo ena akugonja m’ma 1970. Iye anati: “Anthuwa sankafuna kusiya moyo wawofuwofu. Ena anapita nafe kumsasa koma kenako anavomera kukhala mamembala achipani n’kubwerera kwawo. Ankaona kuti sangathe kukhala moyo wovutika wakumsasako.” Koma atumiki a Mulungu ambiri anakhalabe okhulupirika ndipo analolera kusiya zinthu zawo zonse n’kukhala pa mavuto azachuma.—Aheb. 10:34.
12, 13. (a) Kodi Yehova amawaona bwanji anthu? (b) Kodi tingadziwe bwanji ngati tayamba kamtima konyadira kwambiri dziko lathu?
12 Kunyada. Anthu ambiri amakonda kwambiri kwawo kumene amachokera komanso mtundu ndi chikhalidwe chawo. Koma kupanda kusamala, zimenezi zingachititse kuti tisamaone anthu komanso maboma mmene Mulungu amawaonera. N’zoona kuti Mulungu safuna kuti tizichita manyazi ndi chikhalidwe chathu. Ndipotu zimakhala zosangalatsa kwambiri anthu azikhalidwe zosiyanasiyana akakhala pamodzi. Koma tiyenera kukumbukira kuti Mulungu amaona kuti anthu onse ndi ofanana.—Aroma 10:12.
13 Choncho tisamanyadire kwambiri dziko kapena mtundu wathu mpaka kuyamba kuganiza kuti ndife apamwamba kuposa ena. Maganizo amenewa angatichititse kuti tigonje mosavuta pakabuka nkhani zokhudza ndale. Zoterezi zinachitikanso m’nthawi ya atumwi. Akhristu ena achiheberi ankachitira akazi achigiriki zinthu zopanda chilungamo. (Mac. 6:1) Ndiye kodi tingadziwe bwanji ngati tayamba kamtima konyada? Tiyerekeze kuti m’bale kapena mlongo wochokera kudziko lina wakupatsani malangizo. Kodi mungakane malangizowo n’kumaganiza kuti, ‘Munthu wobwera sangatiuze zochita’? M’malomwake tiyenera kutsatira malangizo a m’Malemba akuti: “Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.”—Afil. 2:3.
YEHOVA ANGAKUTHANDIZENI
14. (a) Kodi pemphero lingatithandize bwanji? (b) Perekani chitsanzo cha m’Baibulo chosonyeza kuti pemphero ndi lothandiza?
14 Chinthu chachitatu chimene chingatithandize kuti tizipewa kulowerera ndale, ndi kudalira Yehova. Tiyenera kupempha mzimu woyera kuti utithandize kukhala ndi makhalidwe monga kuleza mtima ndi kudziletsa. Makhalidwewa angatithandize kwambiri makamaka ngati m’dziko lathu mumachitika zachinyengo kapena zopanda chilungamo. Tingamupemphenso nzeru kuti tizitha kuzindikira zinthu zimene zingatichititse kuti tikhale osakhulupirika pa nkhani zokhudza ndale. (Yak. 1:5) Kodi muli m’ndende chifukwa chofuna kukhalabe okhulupirika? Ngati ndi choncho, mungapemphe Yehova kuti akupatseni mphamvu kuti mulimbe mtima komanso muthe kupirira mavuto alionse amene mungakumane nawo.—Werengani Machitidwe 4:27-31.
15. Kodi Mawu a Mulungu angatithandize bwanji kukhalabe okhulupirika? (Onaninso bokosi lakuti, “Mawu a Mulungu Anawathandiza Kukhalabe Okhulupirika.”)
15 Yehova angakuthandizeni pogwiritsa ntchito Mawu ake. Mungawerenge ndi kuganizira kwambiri mavesi amene angakuthandizeni kuti musalowerere ndale. Ndi bwinonso kuloweza mavesi oterewa chifukwa angadzakuthandizeni pa nthawi imene mulibe Baibulo. Mawu a Mulungu amatithandizanso kuti tizikhulupirira kwambiri madalitso amene Ufumu udzabweretse. Izi zingatithandize kuti tipirire tikamayesedwa. (Aroma 8:25) Mukhozanso kusankha malemba amene amanena za zinthu zimene inuyo mudzasangalale nazo kwambiri m’Paradaiso. Kenako muziganizira mmene mudzasangalalire malembawo akadzakwaniritsidwa.
TIZITSANZIRA ANTHU ENA OKHULUPIRIKA
16, 17. Kodi tingaphunzire chiyani kwa atumiki a Yehova okhulupirira amene sanalowerere ndale? (Onani chithunzi patsamba 27.)
16 Chinthu china chimene chingatithandize kuti tisalowerere ndale, ndi kutsanzira anthu ena okhulupirika. Nkhani zawo zingatithandize kuti tisagonje. Mwachitsanzo, Sadirake, Mesake ndi Abedinego anakana kulambira fano la ku Babulo. (Werengani Danieli 3:16-18.) Nkhani zimenezi zathandiza abale ndi alongo ambiri kuti azilimba mtima n’kukana kulambira mbendera. Nayenso Yesu sankalowerera zochitika za m’dzikoli. Iye ankadziwa kuti chitsanzo chake chingathandize otsatira ake. Choncho anati: “Limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.”—Yoh. 16:33.
17 Pali Akhristu ambiri masiku ano amene salowerera ndale. Chifukwa cha zimenezi, ena amazunzidwa, kumangidwa kapenanso kuphedwa. Kuganizira za anthu amenewa kungalimbitse chikhulupiriro chathu. Mwachitsanzo, m’bale wina wa ku Turkey anati: “M’bale Franz Reiter anali wachinyamata koma anaphedwa chifukwa chokana kulowa usilikali mu ulamuliro wa Hitler. Kalata imene analembera mayi ake usiku woti aphedwa mawa lake, inasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Ndikakumana ndi mayesero ndidzayesetsa kumutsanzira.”[2]
18, 19. (a) Kodi abale ndi alongo mumpingo wathu angatithandize bwanji kuti tisalowerere ndale? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani panopa?
18 Ngati mukukumana ndi mavuto ena chifukwa cha ndale muyenera kuuza akulu. Akuluwo angakupatseni malangizo a m’Malemba. Abale ndi alongo nawonso angakulimbikitseni ngati mutawafotokozera mavuto anuwo. Mungawapemphe kuti akupempherereni. Koma tisaiwale kuti nafenso tiyenera kupempherera abale athu komanso kuyesetsa kuwathandiza. (Mat. 7:12) Pawebusaiti yathu ya jw.org/ny pali nkhani zakuti, “Mayiko Amene a Mboni za Yehova Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira.” Nkhanizi zingakuthandizeni kudziwa anthu amene mungawapempherere. Pitani pamene alemba kuti, MALO A NKHANI, kenako pomwe alemba kuti, ZOKHUDZA MALAMULO. Pali nkhani za anthu amene amangidwa posachedwapa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ndiyeno mukhoza kusankhapo mayina a anthu ena n’kuwatchula m’mapemphero anu kuti akhalebe okhulupirika.—Aef. 6:19, 20.
19 Panopa mapeto a dzikoli ali pafupi. Choncho tisamadabwe maboma akamatikakamiza kuti tizichita nawo zandale. Chofunika ndi kulimbitsa chikhulupiriro chathu n’cholinga choti tisakhale mbali ya dzikoli.
^ [1] (ndime 1) Pamene Yesu ankanena mawuwa, Kaisara ndi amene anali wolamulira wamkulu. Choncho anagwiritsa ntchito mawuwa potanthauza boma lililonse la anthu.
^ [2] (ndime 17) Onani buku lachingelezi lakuti, Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, tsamba 662. Onaninso bokosi lakuti, “Anafa Chifukwa Chofuna Kulemekeza Mulungu” m’chaputala 14 cha buku lakuti, Ufumu wa Mulungu Ukulamulira.