Chikristu Choyambirira ndi Boma
KUTATSALA maola oŵerengeka kuti iye afe, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Simuli a dziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.” (Yohane 15:19) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti Akristu adzakhala ndi mzimu wa udani kulinga kwa olamulira a dzikoli?
Saali a Dziko Komanso Saali Adani
Mtumwi Paulo anauza Akristu okhala ku Roma kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro aakulu.” (Aroma 13:1) Momwemonso, mtumwi Petro analemba kuti: “Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse; kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino.” (1 Petro 2:13, 14) Kugonjera ku Boma ndi oimira ake oikidwa ndithudi kunali njira yovomerezedwa ndi Akristu oyambirira. Anayesayesa kukhala nzika zomvera lamulo ndi kukhala ndi mtendere ndi anthu onse.—Aroma 12:18.
Pansi pa mutu wakuti “Tchalitchi ndi Boma,” The Encyclopedia of Religion imati: “M’zaka mazana atatu zoyambirira AD tchalitchi chachikristu chinali chosiyana kwambiri ndi boma la Roma . . . Chikhalirechobe, atsogoleri achikristu . . . anaphunzitsa kumvera lamulo la Roma ndi kukhala wokhulupirika kwa mfumu, popanda kupyola malire oikidwa ndi chikhulupiriro chachikristu.”
Ulemu, Osati Kulambira
Akristu sanali ndi udani kulinga kwa mfumu ya Roma. Analemekeza ulamuliro wake ndi kuipatsa ulemu umene unayenerana ndi malo ake. Mu ulamuliro wa Mfumu Nero, mtumwi Petro analembera Akristu okhala kumadera osiyanasiyana a Ufumu wa Roma kuti: “Chitirani ulemu anthu onse. . . . Chitirani mfumu ulemu.” (1 Petro 2:17) Liwulo “mfumu” linagwiritsiridwa ntchito ndi Agiriki osati kwa mafumu akumaloko okha komanso kwa mfumu ya Roma. Mtumwi Paulo anapatsa uphungu Akristu okhala m’likulu la Ufumu wa Roma kuti: “Perekani kwa anthu onse mangawa awo; . . . ulemu kwa eni ake a ulemu.” (Aroma 13:7) Ndithudi, mfumu ya Roma inafuna ulemu. M’kupita kwa nthaŵi, inafuna ndi kulambira komwe. Koma apa, mpomwe Akristu oyambirira anaona kukhala malire.
Pozengedwa mlandu wake pamaso pa kazembe wachiroma m’zaka za zana lachiŵiri C.E., kunasimbidwa kuti Polycarp anati: “Ndine Mkristu. . . . Timaphunzitsidwa kupereka ulemu wonse woyenera . . . kwa amphamvu ndi maulamuliro oikidwa ndi Mulungu.” Komabe, Polycarp anasankha kufa m’malo mwa kulambira mfumu. Theophilus wa ku Antiokeya wochirikiza chikhulupiriro wa m’zaka za zana lachiŵiri analemba kuti: “Ndingakonde kulemekeza mfumu, osati kuilambira ayi, koma kuipempherera. Koma Mulungu, Mulungu wamoyo ndi woona ndiye amene ndimalambira.”
Mapemphero oyenera okhudza mfumu sanali ogwirizana ndi kulambira mfumu kapena utundu ayi. Mtumwi Paulo anafotokoza chifuno chake: “Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse; chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m’moyo mwathu tikakhale odikha mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu, ndi m’kulemekeza monse.”—1 Timoteo 2:1, 2.
“Osiyana ndi Chitaganya”
Khalidwe laulemu limeneli la Akristu oyambirira silinawachititse kukhala paubwenzi ndi dziko limene anali kukhalamo. Wolemba mbiri wachifalansa A. Hamman akusimba kuti Akristu oyambirira “anali osiyana ndi chitaganya.” Kwenikweni anali osiyana ndi zitaganya ziŵiri, Ayuda ndi Aroma, akumadedwa ndi kumvedwa molakwa ndi onse aŵiriwo.
Mwachitsanzo, pamene anaimbidwa mlandu wonama ndi atsogoleri achiyuda, mtumwi Paulo analankhula pamaso pa kazembe wachiroma kukana mlanduwo kuti: “Sindinachimwa kanthu kapena pachilamulo [cha Ayuda, NW], kapena pakachisi, kapena pa Kaisara. . . . Nditulukira kwa Kaisara.” (Machitidwe 25:8, 11) Podziŵa kuti Ayuda anali kufuna kumupha, Paulo anachita apilo kwa Nero, motero akumasonyeza kuti anazindikira ulamuliro wa mfumu ya Roma. Pambuyo pake, pamlandu wake woyamba ku Roma, zikuoneka kuti Paulo anamasulidwa. Koma pambuyo pake anamangidwanso, ndipo malinga ndi zimene anthu amakhulupirira, iye anaphedwa Nero atalamula zimenezo.
Ponena za mkhalidwe wovuta wa Akristu oyambirira m’chitaganya cha Roma, katswiri wa za kakhalidwe ka anthu ndi zaumulungu Ernst Troeltsch analemba kuti: “Maudindo onse ndi ntchito zimene zinakhudza kulambira mafano mwa njira iliyonse, kapena kulambira Mfumu, kapena zimene zinakhudza kukhetsa mwazi mwa njira iliyonse kapena chilango cha imfa, kapena zimene zikanachititsa Akristu kukhudzidwa ndi makhalidwe oipa akunja zinaletsedwa.” Kodi kaimidwe kameneka kanachotsapo mpata wakuti pakhale unansi wolemekezana ndi wamtendere pakati pa Akristu ndi Boma?
Kupatsa Kaisara “Mangawa” Ake
Yesu anapereka njira imene inayenera kulamulira khalidwe la Mkristu kulinga ku Boma la Roma kapena, kwenikweni, kulinga ku boma lililonse, pamene anati: “Patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” (Mateyu 22:21) Uphungu umenewu kwa otsatira a Yesu unali wosiyana kwambiri ndi maganizo a Ayuda ambiri okonda mtundu wawo amene sanafune ulamuliro wa Roma natsutsa kuti kunali kosayenera kupereka msonkho ku ulamuliro wakunja.
Pambuyo pake, Paulo anauza Akristu okhala ku Roma kuti: “Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbu mtima. Pakuti chifukwa cha ichi mupatsanso msonkho; pakuti iwo [“maulamuliro aakulu” a boma] ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi. Perekani kwa anthu onse mangawa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa.” (Aroma 13:5-7) Pamene kuli kwakuti Akristu sanali a dziko lapansi, anali ndi thayo la kukhala nzika zoona mtima, zopereka msonkho, kulipira Boma kaamba ka mautumiki ochitidwa.—Yohane 17:16.
Koma kodi mawu a Yesu anali kunena za kupereka misonkho yokha? Popeza Yesu sanazitchule za Kaisara ndi za Mulungu, pali nkhani zina zovuta kusiyanitsa zimene tiyenera kugamula malinga ndi mkhalidwe wake kapena malinga ndi chidziŵitso chathu cha Baibulo lonse. M’mawu ena, kugamula zimene Mkristu angapatse Kaisara nthaŵi zina kungaphatikizepo chikumbumtima cha Mkristuyo, chounikiridwa ndi mapulinsipulo a Baibulo.
Kulinganiza Bwino Pakati pa Zinthu Ziŵiri Zofunika
Anthu ambiri amakonda kuiŵala kuti Yesu atanena kuti zinthu za Kaisara ziyenera kupatsidwa kwa Kaisara, iye anawonjezera kuti: “[Patsani] kwa Mulungu zake za Mulungu.” Mtumwi Petro anasonyeza amene ayenera kukhala woyamba kwa Akristu. Atangomaliza kupereka uphungu wa kugonjera kwa “mfumu,” ndi “akazembe” ake, Petro analemba kuti: “Monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu. Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, chitirani mfumu ulemu.” (1 Petro 2:16, 17) Mtumwiyo anasonyeza kuti Akristu ali akapolo a Mulungu, osati a olamulira aumunthu. Pamene kuli kwakuti ayenera kuchitira ulemu woyenera aja oimira Boma, ayenera kutero m’kuwopa Mulungu, amene malamulo ake ali opambana.
Zaka zambiri zisanachitike zimenezo Petro anamveketsa bwino lomwe kupambana kwa lamulo la Mulungu pa la munthu. Sanhedrin yachiyuda inali bungwe loyang’anira limene Aroma anapatsa mphamvu yakuweruza ndi yachipembedzo yomwe. Pamene inalamula otsatira a Yesu kusiya kuphunzitsa m’dzina la Kristu, Petro ndi atumwi ena anayankha mwaulemu koma motsimikiza kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Ndithudi, Akristu oyambirira anayenera kulinganiza bwino pakati pa kumvera Mulungu ndi kugonjera koyenera ku maulamuliro aumunthu. Tertullian anati kuchiyambi cha zaka za zana lachitatu C.E.: “Ngati zonse nza Kaisara, padzatsala chiyani cha Mulungu?”
Kumvana ndi Boma
M’kupita kwa nthaŵi, kaimidwe ka Akristu a m’zaka za zana loyamba kulinga ku Boma kanafooka pang’onopang’ono. Mpatuko umene Yesu ndi atumwi ake analosera unafunga m’zaka za zana lachiŵiri ndi lachitatu C.E. (Mateyu 13:37, 38; Machitidwe 20:29, 30; 2 Atesalonika 2:3-12; 2 Petro 2:1-3) Chikristu champatuko chinamvana ndi dziko la Roma, kutengera mapwando ake akunja ndi mafilosofi ake, ndipo chinalandira ntchito zaboma ndi ntchito yausilikali.
Profesa Troeltsch analemba kuti: “Kuyambira m’zaka za zana lachitatu ndi mtsogolo mwake mkhalidwe unakhala wovuta kwambiri, pakuti Akristu anachuluka kwambiri pakati pa anthu apamwamba a Chitaganya ndi m’ntchito zapamwamba kwambiri, m’gulu la nkhondo ndi m’boma. M’ndime zingapo za zolemba zachikristu [zosachokera m’Baibulo] muli mawu aukali otsutsa kutengamo mbali kwawo m’zinthu zimenezi; komabe, timapezamonso zoyesayesa za kumvana—zigomeko zokonzedwa kutontholetsa zikumbumtima zovutika . . . Kuchokera m’nthaŵi ya Constantine zovuta zimenezi zinazimirira; kulimbana kwa Akristu ndi akunja kunatha, ndipo maudindo onse m’Boma anatseguka kwa onse.”
Chakumapeto kwa zaka za zana lachinayi C.E., Chikristu choipitsidwa ndi chogonja chimenechi chinakhala chipembedzo cha Boma la Ufumu wa Roma.
M’mbiri yake yonse, Dziko Lachikristu—loimiridwa ndi Matchalitchi a Katolika, Orthodox, ndi Protesitanti—lapitiriza kumvana ndi Boma, likumaloŵerera kwambiri m’ndale zake ndi kuchirikiza nkhondo zake. Anthu ambiri atchalitchi oona mtima amene adabwa nazo zimenezi mosakayikira angakondwe kudziŵa kuti pali Akristu lerolino amene amatsatira kaimidwe ka Akristu a m’zaka za zana loyamba pa unansi wawo ndi Boma. Nkhani ziŵiri zotsatira zidzafotokoza nkhaniyi mwatsatanetsatane.
[Chithunzi patsamba 5]
Kaisara Nero, za amene Petro analemba kuti: “Chitirani mfumu ulemu”
[Mawu a Chithunzi]
Musei Capitolini, Roma
[Chithunzi patsamba 6]
Polycarp anasankha kufa m’malo mwa kulambira mfumu
[Chithunzi patsamba 7]
Akristu oyambirira anali nzika zamtendere, zoona mtima, ndi zolipira msonkho