Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Yesu Atsutsa Omtsutsa
YESU wapanikiza kotheratu adani ake achipembedzo kotero kuti akuwopa kumfunsa chinthu china chowonjezereka. Chotero iye ayamba kuvumbula umbuli wawo. “Muganiza bwanji za Kristu?” iye akufunsa motero. “Ali mwana wa yani?”
“Wa Davide,” Afarisiwo akuyankha.
Ngakhale kuti Yesu sakukana kuti Davide ndiye kholo lakuthupi la Kristu, kapena Mesiya, iye akufunsa kuti: “Ndipo Davide mumzimu amtchula iye bwanji ‘Ambuye’ [pa Salmo 110:], nanena, [Yehova] ananena kwa Ambuye wanga, Ukhale padzanja lamanja langa, kufikira ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako? Chifukwa chake ngati Davide amtchula iye Ambuye, ali mwana wake bwanji?”
Afarisiwo akhala chete, popeza kuti sadziŵa kudziŵika kowona kwa Kristuyo, kapena wodzozedwa. Mesiya sali kokha mbadwa yakuthupi ya Davide, monga mmene Afarisiwo mwachiwonekere akukhulupilira, koma iye adaali kumwamba ndipo adaali wamkulu kuposa Davide, kapena Ambuye.
Akumatembenukira tsopano kumakamu ndi ophunzira ake, Yesu achenjeza ponena za alembi ndi Afarisi. Popeza kuti amenewa amaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu, ‘pokhala atadzikhazika pampando wa Mose,’ Yesu akufulumiza kuti: “Chifukwa chake zinthu zirizonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge.” Koma iye akuwonjezera kuti: “Koma musatsanze ntchito zawo; pakuti iwo amalankhula, koma samachita.”
Iwo ndionyenga, ndipo Yesu akuwatsutsa m’mawu ofanana ndi amene iye adanena pamene ankadya m’nyumba ya Mfarisi wina miyezi ingapo yapitayo. “Amachita ntchito zawo zonse,” iye akutero, “kuti awonekere kwa anthu.” Ndipo akupereka zitsanzo, akumati:
“Pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zawo, nakulitsa mphonje.” Zotengera zocheperapodi zimenezi, zovalidwa pamphumi kapena pamkono, ziri ndi mbali zinayi za Chilamulo: Eksodo 13:1-10, 11-16; ndi Deuteronomo 6:4-9; 11:13-21. Koma Afarisiwo akuwonjezera mlingo wa zotengera zimenezi kupereka lingaliro lakuti iwo ndiachangu kaamba ka Chilamulo.
Yesu akupitiriza kuti iwo “akulitsa mphonje za zovala zawo.” Pa Numeri 15:38-40 Aisrayeli alamulidwa kupanga mphonje pa zovala zawo, koma Afarisi akupanga zawo kukhala zazikulu kwambiri koposa za wina aliyense. Chirichonse chikuchitidwira chiwonetsero! “Akonda malo aulemu apamwamba,” Yesu akuwatsutsa.
Mwachisoni, ophunzira ake ayambukiridwa ndi chikhumbo chimenechi cha kutchuka. Chotero iye akupereka uphungu: “Koma inu musachedwa Arabi; pakuti mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wakumwamba. Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.” Ophunzirawo ayenera kuchotsa chikhumbo cha kukhala nambala wanu! Wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu,” Yesu akulangiza motero.
Kenaka iye akulengeza mpambo wa masoka kwa alembi ndi Afarisi, akumawatcha iwo mobwerezabwereza kukhala onyenga. Iwo “atsekera anthu ufumu wakumwamba pamaso pawo,” iye akutero, ndipo “amafunkha nyumba za amasiye ndipo modziwonetsera kupanga mapemphero aatali.”
“Tsoka inu, atsogoleri akhungu,” Yesu akutero. Iye akutsutsa kusadziŵa zofunika zauzimu kwa Afarisi, monga momwe kwasonyezedwera ndi kusiyanitsa konkitsa komwe amapanga. Mwachitsanzo, amati, ‘palibe kanthu ngati aliyense alumbila kutchula kachisi, koma winawake amakhala ndi mlandu atalumbira kutchula golidi wakachisi.’ Mwa kuika kwawo chigogomezero chokulira pa golide wakachisi koposa phindu lauzimu la malo olambirawo, iwo akuvumbula kukhala kwawo akhungu kumakhalidwe abwino.
Kenaka, monga momwe anachitira poyambapo, Yesu akutsutsa Afarisi kaamba ka kunyalanyaza “zolemera Zachilamulo, ndiko kuti chiŵeruzo cholungama, ndi kuchitira chifundo, ndi kukhulupirika” pamene akupereka chisamaliro chokulirapo ku chakhumi, kapena chachikhumi, cha zomera zopanda pake.
Yesu akutcha Afarisi “atsogoleri akhungu, akukuntha udzudzu, koma ngamira mumeza.” Iwo amachotsa udzudzu m’vinyo wawo, osati kokha chifukwa chakuti ndikachilombo, koma chifukwa chakuti ndiwodetsedwa mwadzoma. Chotero, kunyalanyaza kwawo nkhani zazikulu kwambiri za Chilamulo kwayerekezeredwa ndi kumeza ngamira, imenenso iri nyama yodetsedwa mwamwambo. Mateyu 22:41–23:24; Marko 12:35-40; Luka 20:41-47; Levitiko 11:4, 21-24.
◆ Kodi nchifukwa ninji Afarisi akukhala chete pamene Yesu akuwafunsa ponena za zimene Davide adanena pa Salmo 110?
◆ Kodi nchifukwa ninji Afarisi akukulitsa zotengera zawo zokhala ndi Malemba ndi mphonje za zovala zawo?
◆ Kodi ndiuphungu wotani umene Yesu akupereka kwa ophunzira ake?
◆ Kodi ndikusiyanitsa konkitsa kotani kumene Afarisi akupanga, ndipo kodi ndimotani mmene Yesu akuwatsutsira kaamba ka kunyalanyaza nkhani zazikulu kwambiri?