“Ngati Mulungu Ali ndi Ife, Adzatikaniza Ndani?”
“Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?”—AROMA 8:31.
1. Kodi ndani omwe anatsagana ndi Aisrayeli pochoka ku Igupto, nanga n’chiyani chinawachititsa zimenezo?
PA ULENDO wa Aisrayeli wochoka ku Igupto komwe anakhalako zaka 215, zochuluka mwa zaka zimenezi ali muukapolo, “anthu ambiri [osakanizika] anakwera nawo.” (Eksodo 12:38) Omwe sanali Aisrayeli anakumana ndi miliri khumi yochititsa mantha yomwe inawononga kwambiri mu Igupto ndi kuchititsa manyazi milungu yonyenga ya kumeneko. Panthaŵi imodzimodziyo, anaona—makamaka kuyambira pa mliri wachinayi—kuti Yehova amateteza anthu ake. (Eksodo 8:23, 24) Ngakhale kuti ankadziŵa zochepa zokhudza chifuno cha Yehova, iwo anali otsimikizira chinthu chimodzi: Milungu ya Igupto inalephera kuteteza Aiguptowo, pamene Yehova anasonyeza mphamvu zake mwa kumenyera nkhondo Aisrayeli.
2. N’chifukwa chiyani Rahabi anathandiza ozonda dziko achiisrayeli, ndipo n’chifukwa chiyani chikhulupiriro chake pa Mulungu wawo sichinagwe padera?
2 Zaka makumi anayi zitadutsa, Aisrayeli atatsala pang’ono kukaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Yoswa, woloŵa mmalo mwa Mose, anatuma amuna aŵiri kuti akazonde dzikolo. Kumeneko iwo anakumana ndi Rahabi, nzika ya mu Yeriko. Kuchokera pa zimene anamva zokhudza zodabwitsa zomwe Yehova anachita poteteza anthu ake m’zaka 40 kuchokera pamene anatuluka mu Igupto, anadziŵa kuti ngati akufuna kulandira madalitso a Mulungu, ayenera kuthandiza anthu ake. Chifukwa choti anasankha mwanzeru, iye ndi am’banja lake sanawonongedwe pamene Aisrayeli amalanda mzindawo. Kupulumuka kwawo mozizwitsa unali umboni woonekeratu wakuti Mulungu anali nawo. Chotero, chikhulupiriro chomwe Rahabi anali nacho pa Mulungu wa Aisrayeli sichinagwe padera.—Yoswa 2:1, 9-13; 6:15-17, 25.
3. (a) Kodi Yesu anachita chozizwitsa chotani pafupi ndi mzinda womangidwanso wa Yeriko, nanga kodi atsogoleri achipembedzo achiyuda anachitanji? (b) Kodi Ayuda, komanso pambuyo pake ambiri omwe sanali Ayuda, anazindikira chiyani?
3 Patapita zaka 1500, Yesu Kristu anachiritsa wopemphetsa wosaona pafupi ndi mzinda womangidwanso wa Yeriko. (Marko 10:46-52; Luka 18:35-43) Mwamuna ameneyu anapempha Yesu kuti am’chitire chifundo, kusonyeza kuti ankadziŵa kuti Mulungu anali kuchirikiza Yesu. Komabe, atsogoleri achipembedzo achiyuda ndi otsatira awo, ankakana kuvomereza kuti zozizwitsa zomwe Yesu anali kuchita zinali umboni wakuti anali kuchita ntchito ya Mulungu. Mmalo mwake, ankayesa kum’tola zifukwa. (Marko 2:15, 16; 3:1-6; Luka 7:31-35) Ngakhale panali umboni wodziŵikiratu wakuti Yesu amene anamupha anauka, sanafune n’komwe kuvomereza kuti zimenezo zinachitika chifukwa cha mphamvu ya Mulungu. Mmalo mwake, anatsogolera kuzunza otsatira a Yesu, kuyesa kuwalepheretsa ntchito yawo ‘yolalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.’ Koma Ayuda ena, ndiponso patapita nthaŵi ambiri osakhala Ayuda, analingalira zinthu zimenezi mozama ndi kuona kufunika kwake. Kwa iwo zinali zodziŵikiratu kuti Mulungu anakana atsogoleri achiyuda odzilungamitsawo ndipo anali kumbali ya otsatira a Yesu Kristu odzichepetsawo.—Machitidwe 11:19-21.
Kodi Mulungu Ali Kumbali ya Yani Lerolino?
4, 5. (a) Kodi anthu ena amalingalira motani pankhani yosankha chipembedzo? (b) Kodi ndi funso lofunika liti lothandiza kudziŵa chipembedzo choona?
4 Poyankha mafunso pa TV posachedwapa okhudza chipembedzo choona, mtsogoleri wina wachipembedzo anati: “Ndingavomereze kuti chipembedzo ichi n’choona ngati chimasintha mikhalidwe ya munthu pamene akutsatira ziphunzitso zake.” Kunena zoona, chipembedzo choona chimasinthadi munthu. Koma kodi zikutanthauza kuti ngati chipembedzo chikusintha mikhalidwe ya anthu kukhala yabwino ndiye kuti Mulungu akuchichirikiza? Kodi imeneyi ndi njira yokhayo yodziŵira ngati chipembedzo chili choona?
5 Aliyense amaona kufunika kodzisankhira, kuphatikizapo kusankha chipembedzo chimene wakonda. Koma kukhala ndi ufulu wosankha sikutanthauza kuti munthu adzasankha moyenera. Mwachitsanzo, anthu ena amasankha chipembedzo poona kuchuluka kwa anthu ake, chuma chake, miyambo yake yokopa, kapena chifukwa chakuti abale awo ali m’chipembedzo chimenecho. Palibe n’chimodzi chomwe mwa zinthu zimenezi chomwe chingathandize munthu kudziŵa ngati chipembedzocho chili choona kapena ayi. Funso lofunika kwambiri pankhaniyi ndi lakuti: N’chipembedzo chiti chomwe chimalimbikitsa otsatira ake kuchita chifuno cha Mulungu ndi kupereka umboni wogwira mtima wakuti Mulungu ali kumbali yake, mwakuti otsatira ake n’kufikira ponena molimba mtima kuti, “Mulungu ali ndi ife”?
6. Ndi mawu ati a Yesu othandiza kuzindikira chipembedzo choona ndi chonyenga?
6 Yesu anakhazikitsa lamulo lothandiza kusiyanitsa kulambira koona ndi kulambira konyenga pamene anati: “Yang’anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m’kati mwawo ali afisi olusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.” (Mateyu 7:15, 16; Malaki 3:18) Tiyeni tipende zina mwa “zipatso,” kapena kuti zizindikiro za chipembedzo choona kuti titsimikize kuti ndani amene Mulungu akuwachirikiza lerolino.
Mmene Tingadziŵire Ovomerezedwa ndi Mulungu
7. Kodi tikati kuphunzitsa zokhazo zochokera m’Baibulo tikutanthauzanji?
7 Ziphunzitso zawo n’zochokera m’Baibulo. Yesu anati: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine. Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro Chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.” Ndipo anatinso: “Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu.” (Yohane 7:16, 17; 8:47) Kunena mosapita m’mbali, kuti munthu akhale wovomerezeka ndi Mulungu, ayenera kuphunzitsa zokhazo zimene Mulungu wavumbula m’Mawu ake ndi kukana ziphunzitso zochokera m’nzeru kapena miyambo ya anthu.—Yesaya 29:13; Mateyu 15:3-9; Akolose 2:8.
8. N’chifukwa chiyani kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu polambira kuli kofunika?
8 Amagwiritsa ntchito ndi kulengeza dzina la Mulungu, lakuti Yehova. Yesaya ananeneratu kuti: “Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa. Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziŵike ichi m’dziko lonse.” (Yesaya 12:4, 5) Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Choncho kaya anali achiyuda kapena ayi, Akristu anayenera kukhala “anthu a dzina lake.” (Machitidwe 15:14) N’zodziŵikiratu kuti Mulungu amakondwera kugwirizana ndi omwe akunyadira kwambiri kukhala “anthu a dzina lake.”
9. (a) N’chifukwa chiyani anthu am’chipembedzo choona amadziŵika ndi chimwemwe? (b) Kodi Yesaya anasiyanitsa motani chipembedzo choona ndi chonyenga?
9 Amasonyeza umunthu wa Mulungu wa chimwemwe. Monga wolemba “uthenga wabwino,” Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Chotero zingatheke bwanji kuti olambira ake akhale opanda chimwemwe kapena amsunamo nthaŵi zonse? Ngakhale pali kuvuta kwa zinthu m’dziko ndi mavuto aumwini, Akristu enieni amakhalabe achimwemwe chifukwa chakuti amadya chakudya chonona chauzimu nthaŵi zonse. Yesaya anawasiyanitsa ndi achipembedzo chonyenga kuti: “Atero Ambuye Yehova, taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi. Taonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wachisoni; ndipo mudzafuula chifukwa cha kusweka mzimu.”—Yesaya 65:13, 14.
10. Kodi amene ali m’chipembedzo choona amapeŵa motani kuphunzira kuchita chabwino mwa kuyamba achita kaye choipa?
10 Mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo ndizo maziko a makhalidwe ndi zosankha zawo. Wolemba Miyambo akutilangiza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umulemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:5, 6) Mulungu amayanja omwe amadalira malangizo ochokera kwa iye osati amene amadalira ziphunzitso zotsutsana za anthu onyalanyaza nzeru yaumulungu. Mulimonse mmene munthu amayesera kuchita zinthu m’moyo wake mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, momwemonso adzapeŵa kuphunzira chabwino mwa kuyamba wachita kaye choipa.—Salmo 119:33; 1 Akorinto 1:19-21.
11. (a) N’chifukwa chiyani otsata chipembedzo choona sagaŵikana ena kukhala atsogoleri achipembedzo ndipo ena anthu wamba? (b) Kodi amene akutsogolera pakati pa anthu a Mulungu ayenera kupereka chitsanzo chotani ku gulu?
11 Amachita zinthu monga momwe mpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba unkachitira. Yesu anapereka mfundo yachikhalidwe yakuti: “Inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa kumwamba. Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu. Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu.” (Mateyu 23:8-11) Mpingo wa abale sukhala ndi gulu la atsogoleri achipembedzo odzikweza omwe amadzipatsa mayina aulemu ndi kudziona ngati apamwamba kuposa ena onse mumpingo. (Yobu 32:21, 22) Amene akuŵeta nkhosa za Mulungu akuuzidwa kuchita zimenezo “osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.” (1 Petro 5:2, 3) Abusa enieni achikristu amapeŵa kuyesa kuchita ufumu pa chikhulupiriro cha ena. Monga antchito anzawo muutumiki wa Mulungu, iwo amayesetsa kusonyeza chitsanzo chabwino.—2 Akorinto 1:24.
12. Kodi Mulungu amafuna kuti omwe akufuna kuvomerezedwa ndi iye aziwaona motani maboma a anthu?
12 Amamvera maboma a anthu koma saloŵerera m’zandale. Wolephera ‘kumvera maulamuliro a akulu’ sangayembekezere kuvomerezedwa ndi Mulungu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti “iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu. Kotero kuti iye amene atsutsana nawo ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu.” (Aroma 13:1, 2) Komabe, Yesu anazindikira kuti pangabuke zina zosokoneza pamene anati: “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” (Marko 12:17) Amene akufuna kuvomerezedwa ndi Mulungu ayenera ‘kufunafuna Ufumu [wa Mulungu] ndi chilungamo chake choyamba,’ panthaŵi imodzimodziyo kumvera malamulo a m’dziko omwe akugwirizana ndi maudindo awo apamwamba kwa Mulungu. (Mateyu 6:33; Machitidwe 5:29) Yesu anagogomeza za kusaloŵerera m’ndale pamene ankanena za ophunzira ake kuti: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” Pambuyo pake anawonjezera kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.”—Yohane 17:16; 18:36.
13. Kodi chikondi chimachita mbali yotani podziŵikitsa anthu a Mulungu?
13 Alibe tsankho pochitira “onse chokoma.” (Agalatiya 6:10) Chikondi cha Mkristu chilibe tsankho, amalandira anthu onse mosalingalira za mtundu wa khungu lawo, mmene alili pankhani ya zachuma kapena maphunziro, dziko lawo, kapena chinenero chawo. Anthu ovomerezedwa ndi Mulungu amadziŵika chifukwa chochitira onse zabwino makamaka okhulupirira anzawo. Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—Yohane 13:35; Machitidwe 10:34, 35.
14. Kodi anthu oyanjidwa ndi Mulungu amakondedwa ndi wina aliyense? Fotokozani.
14 Amalolera kuzunzidwa chifukwa chochita chifuno cha Mulungu. Yesu anachenjezeratu otsatira ake kuti: “Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mawu anga, adzasunga anunso.” (Yohane 15:20; Mateyu 5:11, 12; 2 Timoteo 3:12) Omwe amavomerezedwa ndi Mulungu amanyozedwa nthaŵi zonse, monga momwe zinalili kwa Nowa, amene anatsutsa dziko lapansi ndi chikhulupiriro chake. (Ahebri 11:7) Lerolino, amene akufuna kuvomerezedwa ndi Mulungu sayenera kuchepetsa mphamvu ya Mawu a Mulungu kapena kunyalanyaza mfundo zachikhalidwe zaumulungu pofuna kupeŵa chizunzo. Pamene akutumikira Mulungu mokhulupirika, amadziŵa kuti anthu ‘adzayesa n’chachilendo nawachitira mwano.’—1 Petro 2:12; 3:16; 4:4.
Nthaŵi Yodziŵa Zoona Zake
15, 16. (a) Ndi mafunso ati amene angatithandize kuzindikira chipembedzo chovomerezeka ndi Mulungu? (b) Kodi anthu mamiliyoni ambiri atsimikizira kuti chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
15 Dzifunseni kuti, ‘Ndi gulu liti lachipembedzo lomwe n’lodziŵika bwino chifukwa chotsatira kwambiri Mawu a Mulungu ngakhale kuti ziphunzitso zake zisiyane ndi zikhulupiriro za anthu ambiri? Ndani amagogomeza kufunika kwa dzina lenileni la Mulungu, ngakhale kuligwiritsa ntchito kumene podzidziŵikitsa okha? Ndani amene amanena mosakayika kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetsa mavuto omwe anthu akukumana nawo? Ndani amene amatsatira miyezo yamakhalidwe ya m’Baibulo, ngakhale kuti ena awanene kuti ndi otsalira? Ndi gulu liti limene limadziŵika kuti lilibe atsogoleri achipembedzo olipidwa, ndi kuti onse m’gululi ndi alaliki? Ndani omwe amayamikiridwa kuti ndi nzika zotsata malamulo, ngakhale kuti amakana kuloŵerera m’zandale. Ndani amene mwachikondi amathera nthaŵi ndi ndalama kuthandiza ena kuphunzira za Mulungu ndi chifuno chake? Ndipo ngakhale amachita zinthu zotamandika zonsezi, ndani amene akunyozedwa, kunyodoledwa, ndi kuzunzidwa?’
16 Anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi adziŵa zoona zake ndipo atsimikizira kuti Mboni za Yehova zokha n’zomwe zili m’chipembedzo choona. Atsimikizira zimenezi kuchokera pa zimene Mboni za Yehova zimaphunzitsa, ndiponso khalidwe lawo, komanso chifukwa cha mapindu omwe chipembedzo chawo chadzetsa. (Yesaya 48:17) Pa chifukwa chimenechi, anthu miyandamiyanda akunena, monga momwe Zekariya 8:23 analoserera kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”
17. N’chifukwa chiyani si kudzitukumula Mboni za Yehova zitati chipembedzo chawo ndiye choona?
17 Kodi tingati n’kudzitukumula ngati Mboni za Yehova zitati izo zokha ndiye zovomerezeka ndi Mulungu? Zikungofanana ndi Aisrayeli omwe ananena ali ku Igupto, kuti iwo okha ndi amene akuyanjidwa ndi Mulungu ngakhale Aigupto analinso ndi zikhulupiriro zawo. Kapenanso zikungofanana ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba omwe anati iwo ndiwo akuyanjidwa ndi Mulungu osati achipembedzo chachiyuda. Sitingachite kufunsa ngati zimenezi zili zoona. M’mayiko 235, Mboni za Yehova zikugwira ntchito yomwe Yesu ananeneratu kuti otsatira ake enieni adzaichita m’nthaŵi yachimaliziro. Iye anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14.
18, 19. (a) N’chifukwa chiyani palibe chifukwa chakuti Mboni za Yehova zibwerere mmbuyo pantchito yawo yolalikira, ngakhale zikutsutsidwa? (b) Kodi Salmo 41:11 akuchitira motani umboni wakuti Mulungu akuimira kumbuyo Mboni?
18 Mboni za Yehova zidzapitirizabe kugwira ntchito imeneyi, sizidzalola chizunzo kapena chitsutso kulepheretsa ntchito yawo. Ntchito ya Yehova iyenera ndipo idzachitika. Zomwe ena ayesa kuchita m’zaka 100 zapitazo pofuna kulepheretsa Mboni kukwaniritsa ntchito ya Mulungu zalephereratu, chifukwa Yehova analonjeza kuti: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m’chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi choloŵa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chawo chimene chifuma kwa Ine.”—Yesaya 54:17.
19 Mfundo yakuti Mboni za Yehova n’zolimba ndi zokangalika tsopano lino kuposa kale—ngakhale kuti zikutsutsidwa padziko lonse—ndi umboni wakuti Yehova amakondwera ndi zochita zawo. Mfumu Davide inati: “Umo ndidziŵa kuti mukondwera ndi ine, popeza mdani wanga sandiseka.” (Salmo 41:11; 56:9, 11) Sizidzatheka mpang’ono pomwe adani a Mulungu kufuula monga opambana polimbana ndi anthu a Yehova, chifukwa chakuti Mtsogoleri wawo, Yesu Kristu, akupita patsogolo kukagonjetsa komaliza!
Kodi Mungayankhe?
• N’zitsanzo zakale ziti za anthu omwe anavomerezedwa ndi Mulungu?
• Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingatithandize kudziŵa chipembedzo choona?
• Kodi n’chifukwa chiyani inuyo panokha muli wotsimikiza kuti Mulungu akuvomereza Mboni za Yehova?
[Chithunzi patsamba 13]
Amene akufuna kuvomerezedwa ndi Mulungu, ziphunzitso zawo ziyenera kuchokera m’Mawu ake basi
[Chithunzi patsamba 15]
Akulu achikristu amapereka zitsanzo zabwino ku gulu