Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Chizindikiro cha Masiku Otsiriza
TSOPANO ndi Lachiŵiri masana. Pamene Yesu ali khale pa Phiri la Azitona, akumayang’ana chapansi ku kachisi, Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane adza kwa iye mwamseri. Iwo ali odera nkhaŵa za kachisi, popeza kuti Yesu wangotha kuneneratu kuti ‘palibe mwala udzasiyidwa pa unzake m’katimo.’
Koma mwachiwonekere iwo ali ndi zambiri m’maganizo awo pamene akubwera kwa Yesu. Milungu ingapo pasadakhale, iye analankhula za “kukhalapo,” (NW) kwake, nthaŵi ya “kuvumbuluka Mwana wa munthu.” Ndipo pa chochitika cha poyambirira, iye anali atawawuza ponena za “mathedwe a [dongosolo la zinthu, NW].” Chotero atumwiwo ali ofunitsitsa kudziŵa.
“Mutiwuze ife,” iwo akutero, “zija zidzaoneka liti [zothera m’chiwonongeko cha Yerusalemu ndi kachisi wake]? ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a [dongosolo la zinthu, NW]?” M’chenicheni, funso lawo nlambali zitatu. Choyamba, iwo afuna kudziŵa ponena za chimaliziro cha Yerusalemu ndi kachisi wake, kenaka ponena za kukhalapo kwa Yesu m’ulamuliro wa Ufumu, ndiyeno ponena za chimaliziro cha dongosolo lonse la zinthu.
M’yankho lake lalitali, Yesu akuyankha mbali zonse zitatu za funsolo. Iye akupereka chizindikiro chimene chikuzindikiritsa pamene dongosolo la zinthu Lachiyuda lidzatha; komanso akupereka zowonjezereka. Iye akuperekanso chizindikiro chimene chidzadziŵitsa ophunzira ake akutsogolo kuti akukhala m’nthaŵi yakukhalapo kwake ndipo kufupi ndi chimaliziro cha dongosolo lonse la zinthu.
Pamene zaka zikupita, atumwiwo akuyamba kuwona kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu. Inde, zinthu zenizenizo zimene ananeneratu ziyamba kuchitika m’tsiku lawo. Chotero, Akristu amene adakali moyo zaka 37 pambuyo pake, mu 70 C.E., sakugwidwa mwadzidzidzi ndi chiwonongeko cha dongosolo Lachiyuda ndi kachisi wake.
Komabe, kukhalapo kwa Kristu ndi chimaliziro cha dongosolo la zinthu sizikuchitika mu 70 C.E. Kukhalapo kwake mu ulamuliro wa Ufumu kukuchitika mtsogolo kwambiri. Koma liti? Kulingalira kwa ulosi wa Yesu kukuvumbula chimenechi.
Yesu akuneneratu kuti padzakhala “nkhondo ndi mbiri za nkhondo.” “Mtundu umodzi wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina,” ndipo kudzakhala njala, zivomezi, ndi miliri. Ophunzira ake adzadedwa ndi kuphedwa. Aneneri onyenga adzauka ndi kusokeretsa ambiri. Kusayeruzika kudzawonjezeka, ndipo chikondi cha ambirimbiri chidzazilala. Panthaŵi imodzimodziyo, mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu idzalalikidwa padziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kukhala mboni ku mitundu yonse.
Ngakhale kuti ulosi wa Yesu unali ndi kukwaniritsidwa kochepera chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. chisanafike, kukwaniritsidwa kwake kokulira kukuchitika m’nthaŵi ya kukhalapo kwake ndi ya chimaliziro cha dongosolo la zinthu. Kubwereramo kosamalitsa m’zochitika za padziko chiyambire 1914 kumavumbula kuti ulosi wamphamvu wa Yesu wakhala ukukwaniritsidwa mwambali yake yokulira chiyambire chaka chimenecho.
Mbali ina yachizindikiro imene Yesu akupereka ndiyo kuwonekera kwa “chonyansa cha kupululutsa.” Mu 66 C.E. chonyansa chimenechi chinawonekera mumkhalidwe wa “magulu a ankhondo” a Roma amene anazinga Yerusalemu ndi kuderera linga la kachisi. “Chonyansa cha kupululutsa” chinaima m’malo amene sichinayenera.
M’kukwaniritsidwa kokulira kwa chizindikirocho, chonyansa cha kupululutsacho ndicho Chigwirizano cha Amitundu ndi wochiloŵa m’malo wake, Mitundu Yogwirizana. Gulu la mtendere wa dziko limeneli likuwonedwa ndi Dziko Lachikristu kukhala liri m’malo a Ufumu wa Mulungu. Nkunyansa kotani nanga! Chotero, m’kupita kwa nthaŵi, maufumu a ndale zadziko ogwirizana ndi UN adzatembenukira Dziko Lachikristu (Yerusalemu wophiphiritsira) nadzamuwononga.
Chotero Yesu ananeneratu kuti: “Padzakhala masauko akulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.” Pamene kuli kwakuti chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. chinalidi chisautso chachikulu, chokhala ndi osimbidwa kuphedwa oposa pa miliyoni imodzi, sichinali chisautso chachikulu kuposa Chigumula cha dziko lonse cha m’tsiku la Nowa. Chotero kukwaniritsidwa kokulira kwa mbali imeneyi ya ulosi wa Yesu sikunachitikebe. Mateyu 24:2-22; 13:40, 49; Marko 13:3-20; Luka 21:7-24; 19:43, 44; 17:20-30; 2 Timoteo 3:1-5.
◆ Kodi nchiyani chikudzutsa funso la atumwi, komabe nchiyani chimene ali nacho m’maganizo awo?
◆ Kodi ndi mbali iti ya ulosi wa Yesu imene inakwaniritsidwa mu 70 C.E., koma kodi nchiyani chimene sichinachitike panthaŵiyo?
◆ Kodi nliti pamene ulosi wa Yesu unakhala ndi kukwaniritsidwa kwake koyamba, komabe nliti pamene ukhala ndi kukwaniritsidwa kokulira?
◆ Kodi chonyansacho nchiyani m’kukwaniritsidwa kwake koyamba ndi kothera?
◆ Kodi nchifukwa ninji chisautso chachikulu sichinakhale ndi kukwaniritsidwa kwake komalizira pa kuwonongedwa kwa Yerusalemu?