Masoka Achilengedwe—Kodi Ali Chizindikiro cha Nthaŵi?
“MTUNDU umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.” Ndi mawu ameneŵa Yesu Kristu anafotokoza kwa ophunzira ake zaka mazana 19 zapitazo kuti zochitika zatsoka zotero, limodzi ndi kuwonjezereka kwa kusayeruzika ndi kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kwa padziko lonse, zikadziŵikitsa chizindikiro cha chiungwe chosonyeza “mapeto a dongosolo la zinthu.” (NW)—Mateyu 24:3-14.
Polingalira zimenezo, tiyenera kufunsa kuti, Kodi ife tikuona zivomezi, mikuntho, kusefukira kwa madzi, zilala, ndi njala zowopsa kwambiri kuposa mibadwo yapitayo? Ndipo mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwa sayansi ndi maluso azopangapanga, kodi anthu ambiri kuposa kale akuvutika monga chotulukapo chake?
Kwa ambiri yankho nlakuti inde. Mwachitsanzo, magazini otchedwa kuti New Scientist akuchenjeza kuti “dziko liyenera kuyembekezera masoka owonjezereka m’ma 1990 kuposa zaka makumi zapitazo.” Mofananamo, mu UN Chronicle ya June 1991, mkulu wa World Meteorological Organization anati: “Mkhalidwewo uli woonekera bwino kwambiri. Kuyambira m’ma 1960 kudzafika m’ma 1980 . . . , pakhala kuŵirikiza kusanu m’kuchitika kwa masoka aakulu achilengedwe, ndi kuŵirikiza kutatu kwa kutayikiridwa chuma kowonkhetsedwa pamodzi.” Poyesa kuona zamtsogolo pankhaniyi, World Health, magazini a UN World Health Organization, anati: “Zitsanzo za masoka achilengedwe ndi ziyambukiro za kuwononga kwake zingathe kupezedwa m’mbiri yonse. Komabe, pamene zaka za zana la 21 zikuyandikira, tikuyang’anizana ndi kusintha m’kuwonjezereka kwa chiŵerengero cha anthu, mikhalidwe ya chilengedwe ndi luso lazopangapanga zimene zimachititsa ziŵerengero zambiri za anthu kukhala kwambiri pangozi yoyambukiridwa ndi masoka achilengedwe ndi ochititsidwa ndi anthu omwe.”
Aliyense amene amayang’ana mosamalitsa zinthu zimene zikuchitika sali wodabwa ndi ndemanga zotero. Nkhani zofalitsidwa sizimakhala zopanda nkhani zochititsa nthumanzi, kaya zikhale za kuphulika kwa phiri ku Philippines, chivomezi ku California, kusefukira kwa madzi ku Bangladesh, njala ku Somalia, mkuntho ku Hawaii, kapena mafunde a m’nyanja ku Nicaragua. Mwezi uliwonse sumatha popanda nkhani yosimba za tsoka lochitika kumbali ina yadziko.
Anthu ena amangonyalanyaza zimenezi. Iwo amanena kuti kuwonjezereka kwa masoka kumene kukuonekeraku munthaŵi yathu kuli chabe chifukwa cha kufalitsidwa bwino kwa nkhani kapena kusungidwa bwino kwa zolembedwa. Iwo amanenanso kuti anthu ambiri akuvutika ndi masoka kokha chifukwa chakuti lerolino pali anthu ambiri. Kodi mawu ameneŵa ngokwanira?
Taonani zimene zikunenedwa munkhani ya New Scientist yogwidwa mawu pamwambapa. “Panali masoka 523 ochitiridwa lipoti m’ma 1960 ndipo 767 m’ma 1970. Podzafika m’ma 1980, chiŵerengerocho chinali chitafika pa 1387.” Ikupitirizanso kunena kuti “mbali ina yochititsa kukwerako mkati mwa zaka khumi zapitazo ingakhale chifukwa cha kuwonjezereka kwa kuchitira lipoti masoka mowona mtima mu China ndi Soviet Union.” Ndiyeno ikuwonjezera kuti: “Ngakhale zili choncho, chiŵerengerocho chikukula.” Kuwonjezereka kowopsa kumeneku kwa chiŵerengero cha masoka sikunganenedwe kuti nchifukwa cha kuchitiridwa lipoti kwabwinopo kapena kusungidwa bwino kwa zolembedwa kokha.
Ndiponso, UN Chronicle ya March 1992 imasimba kuti: “Mkati mwa zaka makumi aŵiri zapitazo, pafupifupi anthu mamiliyoni [atatu] ataya miyoyo yawo ndipo 800 miliyoni ayambukiridwa ndi ‘kusokonezeka kwa zinthu, umphaŵi ndi mavuto’ zochititsidwa ndi masoka achilengedwe.” Zimenezi zikutanthauza kuti pafupifupi munthu mmodzi mwa asanu ndi aŵiri alionse okhala padziko lapansi wayambukiridwa ndi mtundu wina wa tsoka kapena ngozi. Zimenezo nzochititsadi kakasi ndipo zimachititsa munthu kusakayikira kuti nyengo yathu ino ndiyo ya kusintha kwa zinthu ndi kusakhazikika.
Popeza kuti Baibulo limaneneratu za nthaŵi yotero ya nsautso yaikulu, kodi zimenezi zimatanthauza kuti Mulungu ndiye amene amachititsa masoka ndi mavuto amene amatsatirapo? Anthu ambiri amaganiza choncho. Koma kodi maumboni amasonyezanji? Ndipo chinthu chofunika kwambiri nchakuti, kodi Baibulo limasonyezanji?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Chikuto: W. Faidley/Weatherstock
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Chithunzithunzi chapakati: Mark Peters/Sipa Press
WHO/League of Red Cross