Kulinganiza Tsopano Kaamba ka Zaka Chikwi Zikudzazo
“[A]dzachita ufumu pamodzi naye zaka chikwizo.”—CHIBVUMBULUTSO 20:6.
1. Kodi nchiyani chimene chidzakhala mkhalidwe wa zinthu pa dziko lapansi zaka chikwi chimodzi kuchokera pano?
NCHIYANI! Kodi tikutanthauza kuti zoposa zaka chikwi chimodzi kuchokera tsopano, mtundu wa anthu udzakhalabe pano pa dziko lapansi? Tikutanthauzadi chimenecho! Ndipo choposa apo, mtundu wonse wa anthu panthaŵiyo udzakhala wangwiro mu thupi, mtima, ndi maganizo—mofanana ndi mwamuna ndi mkazi oyamba pachiyambi pa kukhalapo kwa munthu pa chiwunda chino. Inde, zaka chikwi kuchokera pano, anthu adzakhala m’chifanizo ndi chikhalidwe cha Mulungu wawo ndi Wobwezeretsa. (Genesis 1:26-30) Iwo adzakhala akusangalala ndi moyo mokwanira mu “munda wa Edene,” paradaiso wa chisangalalo, pa dziko lapansi loyeretsedwa lomwe silidzadzazidwa mopambanitsa ndi nzika za anthu. (Genesis 2:15) Zonsezi zidzachitika m’kukwaniritsidwa kwa chifuno choyambirira cha Mlengi kulinga ku dziko lapansi ndi awo omwe anayenera kukhala pa ilo. Kukwaniritsidwa kokongola kumeneku kudzamuunikira iye kukhala wokhulupirika ku lonjezo lake lachikondi la kudalitsa mtundu wonse wa anthu mosasamala kanthu za chitsutso chonse.
2. Kodi ndimotani mmene anthu mazana 19 apitawo anadziŵira za chimene mtundu wa anthu wangwiro udzakhalira?
2 Kukwaniritsidwa kodalitsika kumeneko kudzadzaza Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Mulungu kupyolera mwa Mwana wake wolemekezedwa, yemwe anathera zaka zoposa 33 1/2 pa dziko lapansi monga munthu wangwiro zaka mazana 19 zapitazo. Ponena za mtundu wa kawonedwe kamene iye anawonekera pa nthaŵi imeneyo, timaŵerenga kuti: “Ndipo Mawu anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinawona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi chowonadi.” (Yohane 1:14) Chotero mwa Yesu Kristu, anthu a ku Israyeli nthaŵiyo anawona mmene cholengedwa chaumunthu changwiro chimawonekera. (Luka 3:23, 38) Inde, zaka mazana 19 zapitazo anthu ena anawona mmene mtundu wa anthu wangwiro udzakhalira m’Paradaiso wa pa dziko lapansi yemwe akudzayo.
3, 4. (a) Kodi ndi utali wotani umene kulamulira kwa Yehova kupyolera mwa Yesu Kristu ndi a 144,000 m’chenicheni udzatenga? (b) Kodi ndi mawu otani omwe akugwiritsiridwa ntchito kaamba ka nyengo ya nthaŵi imeneyo, ndipo kodi ndimotani mmene chimenecho chinawunikiridwa m’mitu ya mabukhu ena a Watch Tower?
3 Utali wa Ufumu wa Yehova kupyolera mwa Yesu Kristu ndi ophunzira ake olemekezeka a 144,000 unanenedweratu kukhala wa zaka chikwi. Ponena za Kulamulira kwa Zaka Chikwi kumeneko, mtumwi Yohane wokalamba analemba kuti: “Ndipo ndinawona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinawona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mawu a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira chirombo, kapena fano lake, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lawo; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka chikwi. Otsala a akufa sanakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka chikwi. Ndiko kuuka kwa akufa koyamba. Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nawo pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiŵiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi naye zaka chikwizo.”—Chibvumbulutso 20:4-6.
4 Popeza kuti zaka chikwi ziri chikwi cha zaka (m’Chingelezi millennium), nyengo imeneyo ikutchedwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu. Awo omwe amalandira ndi kuphunzitsa chiphunzitso cha Baibulo chimenechi nthaŵi zina amatchedwa achilikizi a zaka chikwi kapena okhulupirira m’zaka chikwi, mogwirizana ndi liwu la Chigriki kaamba ka “chikwi.” Mosangalatsa, mavolyumu a Studies in the Scriptures (ofalitsidwa papitapo ndi Watch Tower Bible and Tract Society) poyambapo anatchedwa Millennial Dawn. Ndipo bukhu la nyimbo logwiritsiridwa ntchito pa nthaŵi ina ndi International Bible Students linali ndi mutu wakuti Hymns of the Millennial Dawn.
5. Kodi ndi uti umene udzakhala mkhalidwe wa Satana ndi ziwanda mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu?
5 Mawu akuti “zaka chikwi” pa Chibvumbulutso 20:4 sali ophiphiritsira koma amalozera ku zaka chikwi za kalenda. Mkati mwa Zaka Chikwi zimenezo, Satana Mdyerekezi ndi makamu ake a ziwanda adzakhala m’phompho, popeza kuti asananene za Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu, mtumwi Yohane ananena kuti: “Ndipo ndinawona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdyerekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthaŵi.”—Chibvumbulutso 20:1-3.
6. (a) Kodi ndi deti liti limene Aroma Katolika ena apereka kaamba ka mapeto a Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu? (b) Ngati kudzinenera kwa Akatolika kunali kowona, kodi ndi utali wotani umene kanthaŵi ka kumasulidwa kwa Satana kuchoka mu dzenje lakuya kwatenga kale?
6 Aroma Katolika ena adzinenera kuti Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu kunatha mu 1799 pamene magulu ankhondo a Chifrench analanda Roma ndi kutsitsa papa monga wolamulira wake, kotero kuti iye anapitikitsidwa monga wandende kunka ku France, kumene anamwalira. Mtsogoleri wachipembedzo Wachikatolika wanena kuti Satana ndi ziwanda zake kenaka anamasulidwa kuchoka ku “dzenje lakuya,” kapena “phompho,” kuti akonzenso chatsopano ntchito yawo yonyenga “kwa kanthaŵi.” (Chibvumbulutso 20:1-3, Douay Version Yachikatolika) Ngati chimenecho chinali chowona, icho chikatanthauza kuti “kanthaŵi[ko]” kapitiriza kale kwa zaka 190, popanda malekezero oyembekezeredwa.
7. Kodi nchiyani chimene Baibulo limasonyeza ponena za nthaŵi ndi mkhalidwe wa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu?
7 Ngakhale kuli tero, mogwirizana ndi Malemba, Kulamulira kowona kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu kudakali kutsogolo. Kukwaniritsidwa kwamakono kwa ulosi wa Baibulo kukusonyeza kuti iko kuli pafupi kwenikweni. Mkati mwa Zaka Chikwi zenizenizo, Satana ndi ziwanda zake adzaikidwadi m’phompho, ndipo Yesu Kristu ndi oloŵa m’nyumba anzake a 144,000 adzalamulira mtundu wonse wa anthu popanda kuloŵereramo kwa gulu la Mdyerekezi. Dalitso losatha la mtundu wonse wa anthu wowomboledwa, m’kukwaniritsidwa kwa pangano la Yehova ndi “bwenzi” lake Abrahamu, lidzayamba ndi “khamu lalikulu,” omwe adzapulumuka “chisautso” chosayerekezedwako chimene dongosolo la zinthu loipa iri lidzatha nacho. Lidzafutukukira kwa anthu akufa mabiliyoni angapo owomboledwa ndi “mwazi wa Mwanawankhosa,” Yesu Kristu. (Yakobo 2:21-23; Chibvumbulutso 7:1-17; Genesis 12:3; 22:15-18; Mateyu 24:21, 22) Kufika pa nthaŵiyo, awa adzawukitsidwa kuchokera ku tulo tawo ta imfa m’manda a chikumbukiro kupita ku moyo pa dziko lapansi.—Yohane 5:28, 29.
Gulu Lachikristu
8. Kodi ndi gulu lotani limene bukhu lakuti The New Creation linalongosola, koma kodi ndi ntchito yolinganiza yotani imene ilo silinawoneretu?
8 M’kugwira ntchito kwa chifuno chaumulungu, gulu latsopano lasangalala ndi madalitso amenewo kwa zaka mazana angapo. Ponena za gulu limenelo, timaŵerenga kuti: “Ngati munthu aliyense ali mwa Kristu, ali wolengedwa watsopano.” “M’dulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano [cholengedwa chatsopano, King James Version].” (2 Akorinto 5:17; Agalatiya 6:15) Kumbuyoko mu 1904, bukhu lakuti The New Creation linakokera chisamaliro ku gulu latsopano limeneli lomwe linakhalako m’zana loyamba C.E. (Studies in the Scriptures, Mpambo wa VI, Phunziro V, lokhala ndi mutu wakuti “The Organization of the New Creation” [Gulu la Chilengedwe Chatsopano]) Ponena za kawonedwe kake ka chimene mapeto a Nthaŵi za Akunja mu 1914 akatanthauza, bukhu limenelo silinawone ntchito ya gulu yozizwitsa yomwe ikachitika pambuyo pa ziyambukiro zopondereza za nkhondo ya dziko yoyamba ya mbiri ya munthu.—Luka 21:24, KJ.
9. Kodi ndi ku ntchito yotani kumene otsalira a chilengedwe chatsopano anagalamukira?
9 Kusungiriridwa kwa otsalira a chilengedwe chatsopano chauzimu kufika kumapeto kwa Nkhondo ya Dziko ya I mu 1918 ndi kusungidwa kwawo amoyo m’thupi kuloŵa m’chaka cha pambuyo pa nkhondo cha 1919 kunadza monga chinthu chozizwitsa. Koma mkhalidwe wa zaka chikwi unali usanabwerebe. Mwachiwonekere, kenaka, panali ntchito yambiri kaamba ka otsalira a chilengedwe chatsopano yofunikira kuichita pa dziko lapansi asanazindikire chiyembekezo chawo cha kumwamba cha kugawana ndi Yesu Kristu m’ntchito ya zaka chikwi. Chotero, chifuno chokulira chinali cha kuchiritsa ndi kulinganizanso otsalira. Chotero, ndi chikhulupiriro chosagwedezeka ndi kufunitsitsa kaamba ka ntchito yosangalatsa yomwe inali kutsogolo, iwo anagalamukira ku ntchito.
10. Kodi ndi mafunso otani amene anabuka m’chigwirizano ndi mamiliyoni oyembekezeredwa kupulumuka kuloŵa m’dongosolo latsopano la zinthu?
10 Kupulumuka pa dziko lapansi kochitidwa ndi ena a mtundu wa anthu kupyola mapeto a tsoka la dongosolo loipa iri ndi kupitirizabe kuloŵa m’Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu kunayembekezeredwa ndi otsalira odzozedwa. Ichi chinali tero makamaka pambuyo pa kuperekedwa kwa nkhani yapoyera yakuti “Mamiliyoni Omwe Ali ndi Moyo Tsopano Sadzafa Konse” pa Los Angeles, California, m’chaka cha nkhondo cha 1918. Kodi mamiliyoni amenewa odzapulumuka Harmagedo kutsogolo anafunikira kulinganizidwa? (Chibvumbulutso 16:14-16) Asanaloŵetsedwe mu Zaka Chikwi kudzakhala mbali ya “dziko latsopano,” kodi iwo akafunikira kudziloŵetsa mu ntchito yolalikira Ufumu limodzi ndi otsalira? (2 Petro 3:13) Mafunso amenewa akayankhidwa ndi zochitika za pambuyo pa nkhondo.
11. (a) Kodi nchiyani chimene chinafunikira kuchitidwa ndi nkhosa zina zomwe zinafunikira kukhala gulu limodzi ndi otsalira? (b) Kodi nchifukwa ninji kusiyana m’ziyembekezo sikuli chifukwa cha kugawanika pakati pa otsalira ndi nkhosa zina?
11 Mawu otsatirawa a Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, anazindikiridwa pa nthaŵi yabwino:“Ndipo nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola iri, izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.” (Yohane 10:16) Ngati otsalira odzozedwa anafunikira kulinganizidwa kaamba ka ntchito ya pambuyo pa nkhondo kuchokera mu 1919 kupita mtsogolo ndipo ngati pambuyo pake nkhosa zina zinafunikira kukhala gulu limodzi ndi otsalira m’khola limeneli, kenaka chiyani? Nkulekeranji, popeza kuti nkhosa zina zimenezo zikafunikiranso kulinganizidwa m’chigwirizano ndi otsalira amenewo! Chenicheni chakuti nkhosa zina zinali ndi chiyembekezo chosiyana—chija cha moyo m’paradaiso wa padziko lapansi wosangalatsa—sichinali chochititsa kugawana pakati pa iwo ndi otsalira. Onsewo anali kutsatira kokha Mbusa mmodzi, ndipo sipakakhala kusiyana pakati pa magulu aŵiriwo kufikira kulemekezedwa kwa otsalira odzozedwa mu Ufumu.
12. (a) Kodi nchiyani chimene chiri chofunika koposa kuposa chipulumuko cha mtundu wa anthu? (b) Kodi ndi liti ndipo nchifukwa ninji chimene kulengeza Ufumu kunakhalira chifuno choyambirira?
12 Chipulumuko cha anthu kuchokera ku uchimo ndi imfa, ndi mapeto a kulamulidwa ndi dziko la Satana, ndi kubwezeretsedwa kwa mtundu wa anthu omvera ku dziko lonse lapansi la Paradaiso wokhazikitsidwanso ziri mbali zapadera za chifuno chachikondi cha Yehova. Ngakhale kuli tero, pali chinachake chofunika koposa m’chilengedwe chonse chaponseponse. Kodi icho nchiyani? Chiri kuyeretsedwa kwa ulamuliro wa chilengedwe chaponseponse wa Yehova Mulungu limodzi ndi kuyeretsedwa kwa dzina lake loyera. Nthaŵi ya kulengeza Ufumu wa Yehova kochitidwa ndi Mfumu yolamulira, Yesu Kristu, inagogomezeredwa mu 1922 pa msonkhano wachiŵiri wa International Bible Students pa Cedar Point, Ohio. Popeza kuti Nthaŵi za Akunja zinali zitatha mu 1914, inali nthaŵi yake kulabadira mawu aulosi a Yesu akuti: “Ndipo uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale umboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Ufumu womwe ukayeretsa ulamuliro wa chilengedwe chaponseponse wa Yehova ndi kuyeretsa dzina lake loyera unali utakhazikitsidwa m’mwamba mu 1914, ndipo Yesu Kristu anali kulamulira pakati pa adani ake. Iyi inali mbiri yabwino yaikulu yofunikira kulalikidwa ndi zochititsa zonse zomwe zinalipo kaamba ka kulengezera Mfumu ndi Ufumu wake!
13. Kaamba ka ntchito ya kulengeza Ufumu, kodi nchiyani chimene Mulungu anapereka, ndipo kodi nchifukwa ninji?
13 Yehova ali wolinganiza pa mlingo wa chilengedwe chaponseponse, popeza kuti iye ali Wam’mwambamwamba, Wamkulukulu. Iye tsopano anazindikira za kulinganiza kotheratu, pano pa dziko lapansi, kwa ntchito ya kulengeza Ufumu wake ku mitundu yonse mapeto a dongosolo lazinthu iri asanadze. Ziŵalo za otsalira a odzozedwa opulumuka zinalimbikitsidwa, mwakutero, kukhala gulu la mitunduyonse lokwaniritsa chifuniro chake. Awa afunikira kulengeza ku dziko kuti chifukwa cha kutokosa kwa Satana ulamuliro wa chilengedwe chaponseponse wa Yehova, ponse paŵiri zenizeni ndi kuwona kwa ulamuliro umenewo ziyenera kuyeretsedwa, kulungamitsidwa, kwa nthaŵi zonse.
Gulu la Zaka Chikwi Zisadakhale
14. (a) Nyengo yathu Yachisawawa isadakhale, kodi ndi gulu liti limene linakhala mbali ya padziko lapansi ya gulu la chilengedwe chaponseponse la Yehova? (b) Kodi ndimotani mmene Davide anatsimikizira kukhala wolinganiza wapadera?
14 Kwa zaka mazana 15 Nyengo yathu Yachisawawa isadakhale, Yehova Mulungu anali ndi gulu lowoneka ndi maso pa dziko lapansi. Iye anagwiritsira ntchito mneneri Mose monga nkhoswe Yake m’kulinganiza mtundu wa Israyeli pambuyo pa kupulumutsidwa kwake kuchoka mu Igupto, ulamuliro woyamba wa dziko wa mbiri ya Baibulo. Pansi pa Chilamulo cha Mose, Israyeli anakhala mbali yowoneka ndi maso ya gulu la chilengedwe chaponseponse la Yehova. Wolinganiza wowonekera pakati pa anthu osankhidwa amenewa a Mulungu anali mbusa ndi mfumu Davide, za amene timaŵerenga kuti: “Davide anawalinganiza iwo [Alevi omwe anatumikira pa kachisi ya Yehova] m’magulu, otchedwa ndi dzina la Gerisomu, Kohati, ndi Merari, ana aamuna a Levi.” “Iye anawalinganiza iwo [ansembe] mwa kuchita maere pa iwo, popeza kuti panali nduna zopatulika ndi nduna za Mulungu mumzera wa Eleazara ndi uja wa Itamara.”—1 Mbiri 23:3, 6; 24:1, 5, The New English Bible.
15. (a) Kodi ndi mumkhalidwe wotani mmene Aisrayeli anatulukira kuchoka mu Igupto? (b) Kodi ndaninso omwe anasankha kuchoka mu Igupto, ndipo kodi iwo anakhala ndi Aisrayeli?
15 Mazanamazana a zaka nthaŵi ya Davide isadakhale, pamene Aisrayeli anachoka mu Igupto, iwo sanatuluke mu mkhalidwe wa piringupiringu koma anatuluka m’njira ya dongosolo. Ichi chinasonyeza ntchito yabwino ya gulu ku mbali ya nkhoswe yawo, Mose. Khamu lalikulu la osakhala Aisrayeli linatuluka nawo, likumasankha kugwirizana ndi anthu a Mulungu wochita zozizwitsa, Yehova, yemwe anali wamphamvu koposa kuposa milungu yonse ya mu Igupto. Mosasamala kanthu za zovuta zambiri, nthaŵi zina pambuyo pake “khamu losakanizikana” limeneli lokhala ndi ubwino kulinga kwa anthu osankhika a Yehova linali lidakali ndi iwo m’chipululu chowopsya cha Sinai. (Eksodo 12:37-51; Numeri 11:4) Limodzi ndi Aisrayeli, khamu losakanizikana limenelo mwachiwonekere linaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa pansi pa utsogoleri wa mloŵa m’malo wa Mose, Yoswa, popeza kuti Mulungu analamulira kuti mphatso ipangidwe kumeneko kaamba ka nzika zogonera zoterozo.
16. (a) Kodi ndani omwe khamu losakanizikana linachitira chithunzi? (b) Kodi nchiyani chimene awa ayenera kuchita kuti apulumuke mapeto a dongosolo lino?
16 Khamu losakanizikana limenelo lochokera mu Igupto wa Farao linachitira chithunzi khamu lalikulu la zana la 20. Iwo sali Aisrayeli auzimu koma ali nkhosa zina za Mbusa Wabwino, Yesu Kristu. Limodzi ndi otsalira odzozedwa, iwo amayang’ana kutsogolo ku kupulumuka kotheratu kuchoka ku mnzake wa Igupto, dongosolo la zinthu la dziko limene Farao Wamkulu, Satana Mdyerekezi, ali mulungu. (Yohane 10:16; 2 Akorinto 4:4; Chibvumbulutso 7:9) Koma kodi nchiyani chimene afunikira kuchita kuti apulumuke chiwonongeko chachiwawa cha dziko lakale la Satana ndi kuloŵa m’dziko latsopano lolonjezedwa pansi pa Yoswa Wamkulu, Yesu Kristu? (2 Petro 3:13) Iwo afunikira kukhala ogwirizana ndi makonzedwe olinganiza a maziko a gulu lowoneka ndi maso la Yehova, otsalira odzozedwa.
17. M’dziko losalinganizidwa iri, kodi ndimotani mmene awo a khamu lalikulu amachitira, ndipo kodi iwo amayang’ana kutsogolo ku chiyani?
17 Makamaka chiyambire pakati pa zaka makumi anayi za zana la 20 ndi pamene khamu lalikulu la nkhosa zina labweretsedwa m’gulu limodzi lolinganizidwa pansi pa Mbusa mmodzi wolemekezedwa, Mfumu yolamulira, Yesu Kristu. M’dziko limene likupitiriza kukhala losagwirizana mowonjezereka chotero mosasamala kanthu za kukhalapo kwa gulu la Mitundu Yogwirizana, awo a khamu lalikulu limeneli amachirikiza ndi mtima wonse otsalira odzozedwa ndipo chotero amapereka umboni wa mphamvu yogwirizanitsa ya mzimu woyera wa Yehova. Mogamulapo, iwo amapitirizabe kukhala olinganizidwa ndi otsalira pamene akuyang’ana kutsogolo ku utumiki wapadera pa dziko lapansi mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu.
Kodi Ndi Ati Omwe Ali Malingaliro Anu?
◻ Kodi nchiyani chimene Malemba amasonyeza ponena za nthaŵi ndi mkhalidwe wa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu?
◻ Kodi nchiyani chimene chiri chofunika koposa kuposa chipulumuko cha mtundu wa anthu?
◻ Nyengo yathu Yachisawawa isadakhale, kodi ndi gulu liti limene linakhala mbali ya padziko lapansi ya gulu la chilengedwe chaponseponse la Yehova?
◻ Kodi ndimotani mmene awo ochitiridwa chithunzi ndi khamu losakanizikana akupulumukira kuloŵa m’Kulamulira kwa Zaka Chikwi?