“Iye Amene Aŵerenga M’kalata Azindikire”
“Mmene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, . . . chitaima m’malo oyera . . . pomwepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri.”—MATEYU 24:15, 16.
1. Kodi chenjezo limene Yesu anapereka lopezeka pa Luka 19:43, 44 linali ndi chotsatirapo chotani?
TIKACHENJEZEDWA za tsoka limene lili pafupi kuchitika titha kulipeŵa. (Miyambo 22:3) Choncho lingalirani mmene zinalili kwa Akristu m’Yerusalemu Aroma ataukira mzindawo mu 66 C.E. Yesu anali atachenjeza kuti mzindawo udzazingidwa ndi kuwonongedwa. (Luka 19:43, 44) Ayuda ambiri ananyalanyaza mawu ake. Koma ophunzira ake anamvera chenjezo lake. Chotero, anapulumuka tsoka la mu 70 C.E.
2, 3. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi ndi ulosi wa Yesu wolembedwa pa Mateyu 24:15-21?
2 Mu ulosi wokhudzanso ife lerolino, Yesu anafotokoza chizindikiro chachiungwe chophatikizapo nkhondo, njala, zivomezi, miliri, ndi kuzunzidwa kwa Akristu olalikira za Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:4-14; Luka 21:10-19) Yesu anatchulanso mfundo imene inali kudzathandiza ophunzira ake kudziŵa kuti chimaliziro chili pafupi—‘chonyansa cha kupululutsa chitaima m’malo oyera.’ (Mateyu 24:15) Tiyeni tiwapendenso mawu ofunika amenewo kuti tione mmene angakhudzire miyoyo yathu tsopano ndi m’tsogolo.
3 Atafotokoza chizindikirocho, Yesu anati: “Mmene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Danieli mneneri, chitaima m’malo oyera (iye amene aŵerenga m’kalata azindikire) pomwepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri: iye ali pamwamba pa chindwi, asatsikire kunyamula za m’nyumba mwake; ndi iye wa m’munda asabwere kutenga chofunda chake. Koma tsoka ali nalo iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana m’masiku awo! Ndipo pempherani kuti kuthaŵa kwanu kusakhale pa nyengo yachisanu, kapena pa Sabata; pakuti pomwepo padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko.”—Mateyu 24:15-21.
4. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Mateyu 24:15 anakwaniritsidwa m’zaka za zana loyamba?
4 Nkhani zosimbidwa ndi Marko ndi Luka zikutchula mfundo zowonjezeka. Pamene Mateyu akuti “chitaima m’malo oyera,” Marko 13:14 akuti “chilikuima pomwe sichiyenera.” Luka 21:20 akuwonjezapo mawu a Yesu akuti: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira.” Zimenezi zikutithandiza kuona kuti kukwaniritsidwa koyamba kunakhudza nkhondo ya Aroma pa Yerusalemu ndi kachisi wake—malo oyera kwa Ayuda koma amene sanalinso oyera kwa Yehova—imene inayamba mu 66 C.E. Chipululutso chotheratu chinachitika pamene Aroma anawononga mzindawo ndi kachisi wake mu 70 C.E. Kodi “chonyansa” chinali chiyani panthaŵiyo? Ndipo ndi motani mmene ‘chinaimira m’malo oyera’? Mayankho a mafunso ameneŵa adzatithandiza kumvetsa bwino kukwaniritsidwa kwamakono.
5, 6. (a) N’chifukwa chiyani oŵerenga Danieli chaputala 9 anafunikira kuzindikira? (b) Kodi ulosi wa Yesu wonena za “chonyansa” unakwaniritsidwa motani?
5 Yesu analimbikitsa oŵerenga kugwiritsa ntchito kuzindikira. Oŵerenga chiyani? Mwachionekere, oŵerenga Danieli chaputala 9. Pamenepo tikupezapo ulosi wosonyeza nthaŵi imene Mesiya adzaonekera ndipo ukuneneratu kuti “adzalikhidwa” patapita zaka zitatu ndi theka. Ulosiwo umati: ‘Pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.’—Danieli 9:26, 27; onaninso Danieli 11:31; 12:11.
6 Ayuda anali kuganiza kuti zimenezi zikukhudza kuipitsa kachisi kumene Antiochus IV anachita zaka pafupifupi 200 zapitazo. Komano Yesu anasonyeza kuti sizinali zimenezo, nawalimbikitsa kuzindikira popeza “chonyansa” chimenecho chinali kudzaonekanso ndi ‘kuima m’malo oyera.’ Mwachionekere, Yesu anali kunena za gulu lankhondo la Aroma limene linali kudzabwera mu 66 C.E. ndi zizindikiro zachilendo. Zizindikiro zimenezo, zimene anali nazo kuyambira kalekale, kwenikweni zinali mafano ndipo zinali zonyansa kwa Ayuda.a Komano, kodi ndi liti pamene asilikaliwo anali ‘kudzaima m’malo oyera’? Zimenezo zinachitika pamene gulu lankhondo la Aroma, ndi mbendera zawozo, anaukira Yerusalemu ndi kachisi wake, amene Ayuda anali kumuona ngati woyera. Aroma anayamba kugwetsa ngakhale linga la kachisi. Ndithudi, chimene chinali chonyansa kwa nthaŵi yaitali chinali chitaima pamalo oyera tsopano!—Yesaya 52:1; Mateyu 4:5; 27:53; Machitidwe 6:13.
“Chonyansa” Chamakono
7. Ndi ulosi uti wa Yesu umene ukukwaniritsidwa m’nthaŵi yathu?
7 Kuyambira nthaŵi ya Nkhondo Yadziko I, taona kukwaniritsidwa kwakukulu kwa chizindikiro cha Yesu cholembedwa pa Mateyu chaputala 24. Koma kumbukirani mawu ake akuti: “Mmene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa . . . chitaima m’malo oyera . . . pomwepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri.” (Mateyu 24:15, 16) Mbali imeneyi ya ulosiwo iyeneranso kukwaniritsidwa m’nthaŵi yathu.
8. Kwa zaka zambiri, kodi Mboni za Yehova zakhala zikunena kuti “chonyansa” m’nthaŵi ya makono ndi chiyani?
8 Posonyeza chidaliro cha atumiki a Yehova chakuti ulosi umenewu udzakwaniritsidwa, Nsanja ya Olonda yachingelezi ya January 1, 1921, inafotokoza ulosiwo mougwirizanitsa ndi zimene zinali kuchitika ku Middle East. Pambuyo pake, m’kope lachingelezi la December 15, 1929, patsamba 374, Nsanja ya Olonda motsimikiza inati: “Cholinga chonse cha bungwe la League of Nations ndicho kutembenuza anthu kuchoka kwa Mulungu ndi kwa Kristu, choncho ndicho chopululutsa, ntchito ya Satana, ndiponso chonyansa pamaso pa Mulungu.” Choncho mu 1919 “chonyansa” chinaonekera. M’kupita kwa nthaŵi, bungwe la League linaloŵedwa m’malo ndi bungwe la United Nations. Mboni za Yehova kwa nthaŵi yaitali zasonyeza kuti mabungwe a anthu ofuna kudzetsa mtendere ameneŵa ndi onyansa pamaso pa Mulungu.
9, 10. Kodi kamvedwe koyamba ka chisautso chachikulu kanakhudza motani kamvedwe kathu ka nthaŵi imene “chonyansa” chidzaima m’malo oyera?
9 Nkhani yoyambayo yafotokoza mwachidule kamvedwe katsopano ka mbali yaikulu ya Mateyu chaputala 24 ndi 25. Kodi kuwongolera n’kofunika ponena za ‘chonyansa choima m’malo oyera’? Zikusonyeza choncho. Ulosi wa Yesu ukugwirizanitsa kwambiri ‘kuima m’malo oyera’ kumeneku ndi kuyambika kwa ‘chisautso’ chimene analoseracho. Choncho ngakhale kuti “chonyansa” chakhala chilipo kwa nthaŵi yaitali, kugwirizana kwa ‘kuima [kwake] m’malo oyera’ ndi chisautso chachikulu kuyenera kukhudza kamvedwe kathu. Motani?
10 Anthu a Mulungu poyamba ankaganiza kuti mbali yoyamba ya chisautso chachikulu inayambika mu 1914 ndi kuti mbali yomalizira idzadza pankhondo ya Armagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16; yerekezani ndi Nsanja ya Olonda yachingelezi ya April 1, 1939, tsamba 110.) Choncho titha kuona chifukwa chake panthaŵi ina tinkaona ngati kuti “chonyansa” chamakono chiyenera kuti chinaima m’malo oyera Nkhondo Yadziko I itangotha.
11, 12. Mu 1969, kodi ndi kamvedwe katsopano kotani kamene kanafotokozedwa ponena za chisautso chachikulu?
11 Komabe, m’zaka zaposachedwapa tayamba kuona zinthu mosiyanako. Lachinayi pa July 10, 1969, pa Msonkhano Wamitundu Yonse wa “Peace on Earth” (Mtendere Padziko Lapansi) ku New York City, F. W. Franz, amene panthaŵiyo anali wachiŵiri kwa pulezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society, anapereka nkhani yogwira mtima. Pofotokoza kamvedwe koyamba ka ulosi wa Yesu, Mbale Franz anati: “Panali mafotokozedwe akuti ‘chisautso chachikulu’ chinayamba mu 1914 C.E. ndi kuti sichinachitike chonse panthaŵiyo koma Mulungu anaimitsa Nkhondo Yadziko I m’November 1918. Kuyambira pamenepo Mulungu analola kuti pakhale nthaŵi yoti otsalira ake odzozedwa mwa Akristu osankhidwa agwire ntchito asanalole mbali yomalizira ya ‘chisautso chachikulu’ kuyamba pankhondo ya Armagedo.”
12 Kenako anapereka mafotokozedwe ena atsopano akuti: “Kuti zigwirizane ndi zochitika za m’zaka za zana loyamba, . . . ‘chisautso chachikulu’ chamakono sichinayambe mu 1914 C.E. M’malo mwake, zimene zinachitikira Yerusalemu wophiphiritsira wamakono mu 1914-1918 zinali chabe ‘zoŵaŵa zoyamba’ . . . ‘Chisautso chachikulu’ chonga chomwe sichidzakhalaponso chidakali m’tsogolo, popeza chimenecho chidzakhala kuwonongedwa kwa ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga (kuphatikizapo Dziko Lachikristu) kenako ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse’ pa Armagedo.” Zimenezi zinatanthauza kuti chisautso chachikulu chonsecho chinali chidakali m’tsogolo.
13. Kodi n’chifukwa chiyani kuli kwanzeru kunena kuti m’tsogolo “chonyansa” ‘chidzaima m’malo oyera’?
13 Zimenezi zikukhudzana kwambiri ndi kuzindikira nthaŵi imene “chonyansa” chidzaima m’malo oyera. Kumbukirani zimene zinachitika m’zaka za zana loyamba. Aroma anaukira Yerusalemu mu 66 C.E., koma anabwerera mosayembekezereka, zimene zinalola ‘anthu’ achikristu kupulumuka. (Mateyu 24:22) Chotero, tikuyembekeza kuti chisautso chachikulu chidzayamba posachedwapa, koma chidzafupikitsidwa chifukwa cha osankhidwa a Mulungu. Mfundo yaikulu ndi iyi: Kalelo, ‘chonyansa choima m’malo oyera’ chinakhudzana ndi kuukira kwa Aroma kotsogozedwa ndi Kazembe Gallus mu 66 C.E. Kuukira kwamakono kofanana ndi kwakaleko—kuyambika kwa chisautso chachikulu—kudakali m’tsogolo. Choncho malinga ndi umboni umene ulipo, “chonyansa cha kupululutsa,” chimene chakhalapo kuyambira 1919, chidzaima m’malo oyera m’tsogolo.b Kodi zimenezi zidzachitika motani? Ndipo kodi zingatikhudze motani?
Kuukira Kwam’tsogolo
14, 15. Kodi Chivumbulutso chaputala 17 chikutithandiza motani kumvetsa zimene zidzachitika Armagedo itatsala pang’ono kuchitika?
14 Buku la Chivumbulutso limafotokoza kuukiridwa ndi kuwonongedwa kwa chipembedzo chonyenga kwam’tsogolo. Chaputala 17 chimafotokoza chiweruzo cha Mulungu pa ‘Babulo Wamkulu, Amayi wa Achigololo’—ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Dziko Lachikristu ndiyo mbali yaikulu ndipo limati lili paunansi wa pangano ndi Mulungu. (Yerekezani ndi Yeremiya 7:4.) Zipembedzo zonyenga, kuphatikizapo Dziko Lachikristu, kwa nthaŵi yaitali zakhala zikuchita chigololo ndi “mafumu a dziko,” koma zimenezi zidzatha zipembedzo zimenezo zitapululutsidwa. (Chivumbulutso 17:2, 5) Kodi ndani adzazipululutsa?
15 Buku la Chivumbulutso limanena za “chilombo chofiiritsa” chimene chikukhalapo kwa kanthaŵi, n’kusoŵa, kenako n’kubweranso. (Chivumbulutso 17:3, 8) Chilombo chimenechi chikuchirikizidwa ndi olamulira a dziko. Mfundo zotchulidwa mu ulosiwo zikutithandiza kuzindikira kuti chilombo chophiphiritsira chimenechi ndi bungwe lofuna kudzetsa mtendere limene linapangidwa mu 1919 monga League of Nations (“chonyansa”) limene tsopano lili United Nations. Chivumbulutso 17:16, 17 chikusonyeza kuti m’tsogolomu Mulungu adzapangitsa olamulira ena aumunthu amene ali amphamvu mu “chilombo” chimenechi kupululutsa ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Kuukira kumeneko ndiko kudzakhala chiyambi cha chisautso chachikulu.
16. Kodi ndi zinthu zoonekeratu zotani zokhudza chipembedzo zimene zikuchitika?
16 Popeza kuti chiyambi cha chisautso chachikulu chidakali m’tsogolo, kodi ‘kuima m’malo oyera’ kudakali m’tsogolo? Umboni ukusonyeza zimenezo. Pamene kuli kwakuti “chonyansa” chinaonekera kumayambiriro kwa zaka za zana lino ndipo chakhalapo kwa zaka zambirimbiri, patsogolopa chidzaima “m’malo oyera” m’njira inayake. Monga momwe otsatira Kristu a m’zaka za zana loyamba analili ndi chidwi choona mmene ‘kuima m’malo oyera’ kudzachitikira, Akristu amakono alinso ndi chidwi chomwecho. Zoonadi, kuti tidziŵe zonse tiyenera kudikira kukwaniritsidwa kwenikweniko. Koma n’zoonekeratu kuti m’mayiko ena anthu owonjezereka ayamba kale kunyansidwa ndi chipembedzo. Anthu ena andale, mogwirizana ndi Akristu akale amene anasiya chikhulupiriro choona, akusonkhezera anthu kudana ndi zipembedzo, makamaka kudana ndi Akristu oona. (Salmo 94:20, 21; 1 Timoteo 6:20, 21) Chotero, maulamuliro andale ngakhale tsopano lino ‘akuchita nkhondo pa Mwanawankhosa,’ ndipo monga momwe Chivumbulutso 17:14 chikusonyezera, nkhondo imeneyi idzakula. Pamene kuli kwakuti sangamenyane maso ndi maso ndi Mwanawankhosa wa Mulungu—Yesu Kristu pamalo ake okwezeka, aulemerero—iwo adzakulitsa chitsutso chawo pa olambira oona a Mulungu, makamaka “opatulika” ake. (Danieli 7:25; yerekezani ndi Aroma 8:27; Akolose 1:2; Chivumbulutso 12:17.) Mulungu watitsimikizira kuti Mwanawankhosa limodzi ndi amene ali kumbali yake adzapambana.—Chivumbulutso 19:11-21.
17. Mosaumirira mfundo yopanda umboni, kodi tinganenenji za mmene “chonyansa” chidzaimira m’malo oyera?
17 Tikudziŵa kuti chipembedzo chonyenga chidzapululutsidwa. Babulo Wamkulu ‘waledzera ndi mwazi wa oyera mtima’ ndipo wakhala monga mfumu, koma iye adzawonongedwabe. Chisonkhezero chonyansa chimene wachita pa mafumu a dziko lapansi chidzasintha mwadzidzidzi pamene ‘nyanga khumi za chilombo’ zidzadana naye ndi kum’chita chiwawa. (Chivumbulutso 17:6, 16; 18:7, 8) “Chilombo chofiiritsa” chikadzaukira mkazi wachipembedzo wachigololoyo, “chonyansa” chidzakhala chitaima m’njira yoopsa m’malo amene Dziko Lachikristu limati oyera.c Choncho kupululutsa kudzayamba ndi Dziko Lachikristu lopanda chikhulupiriro limenelo, limene limadzinenera kukhala loyera.
‘Kuthaŵa’—Motani?
18, 19. Kodi paperekedwa zifukwa zotani zosonyeza kuti ‘kuthaŵira kumapiri’ sikudzatanthauza kusintha chipembedzo?
18 Atalosera za ‘kuima m’malo oyera kwa chonyansa,’ Yesu anachenjeza ozindikira kuti ayenera kuchitapo kanthu. Kodi anatanthauza kuti nthaŵi itatha kale—“chonyansa” ‘chitaima m’malo oyera’—anthu ambiri adzathaŵa kuchoka m’zipembedzo zonyenga n’kuyamba kulambira koona? Kutalitali. Talingalirani za kukwaniritsidwa koyamba. Yesu anati: ‘A m’Yudeya athaŵire kumapiri: ndi iye amene ali pamwamba pa chindwi asatsike, kapena asaloŵe kukatulutsa kanthu m’nyumba mwake; ndi iye amene ali kumunda asabwere kudzatenga malaya ake. Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana masiku awo! Ndipo pempherani kuti kusakhale m’nyengo yachisanu.’—Marko 13:14-18.
19 Yesu sananene kuti a m’Yerusalemu okha ndiwo ayenera kuthaŵa, ngati kuti mfundo yake inali yakuti anayenera kuchoka m’likulu la kulambira kwachiyuda; komanso chenjezo lake silinatchule kusintha chipembedzo—kuthaŵa m’chonyenga ndi kuloŵa m’choona. Ndithudi ophunzira a Yesu sanafunikire chenjezo kuti athaŵe m’chipembedzo chawo kukaloŵa m’china; iwo anali atakhala kale Akristu oona. Ndipo chiukiro cha mu 66 C.E. sichinasonkhezere otsatira Chiyuda m’Yerusalemu ndi m’Yudeya yense kusiya chipembedzo chimenecho ndi kuyamba Chikristu. Polofesa Heinrich Graetz ananena kuti awo amene anathamangitsa Aroma anabwereranso mumzindawo: “Azelote, akuimba nyimbo zachilakiko zankhondo, anabwerera ku Yerusalemu (pa October 8), mitima yawo ikugunda ndi chiyembekezo chosangalatsa chakuti adzakhala omasuka ndi aufulu. . . . Kodi Mulungu sanali atawathandiza mwachifundo monga momwe Anathandizira makolo awo akale? Mitima ya Azelote sinaope kalikonse ka m’tsogolo.”
20. Kodi ophunzira oyambirira anamvera motani chenjezo la Yesu lakuti athaŵire kumapiri?
20 Choncho, kodi osankhidwa ochepawo kalelo anautsatira motani uphungu wa Yesu? Mwa kuchoka m’Yudeya ndi kuthaŵira kumapiri kutsidya kwa Yordano, anasonyeza kuti sali mbali ya dongosolo lachiyuda, m’zandale kapena m’zachipembedzo. Iwo anasiya minda, nyumba, osatenga ngakhale katundu wawo m’nyumba zawo. Pokhala ndi chidaliro chakuti Yehova adzawachirikiza ndi kuwathandiza, anaika kum’lambira patsogolo pa china chilichonse chooneka ngati chofunika.—Marko 10:29, 30; Luka 9:57-62.
21. Kodi sitiyenera kuyembekeza chiyani “chonyansa” chikadzaukira?
21 Tsopano, talingalirani za kukwaniritsidwa kwakukulu. Kwa zaka zambiri takhala tikulimbikitsa anthu kutuluka m’chipembedzo chonyenga ndi kuyamba kulambira koona. (Chivumbulutso 18:4, 5) Anthu miyandamiyanda atero. Ulosi wa Yesu susonyeza kuti chisautso chachikulu chikadzayamba, miyandamiyanda ya anthu adzatembenukira ku kulambira koyera; ndithudi, panalibe kutembenuka kwa Ayuda ochuluka mu 66 C.E. Komabe, Akristu oona adzalimbikitsidwa kwambiri kumvera chenjezo la Yesu ndipo adzathaŵa.
22. Kulabadira kwathu uphungu wa Yesu wonena za kuthaŵira kumapiri kungaphatikizepo chiyani?
22 Panopo sitingadziŵe tsatanetsatane yense wa chisautso chachikulu, koma titha kuona kuti kwa ifeyo, kuthaŵa kumene Yesu ananena sikudzakhala kuthaŵira kumalo ena. Anthu a Mulungu ali kale padziko lonse lapansi, pafupifupi m’ngondya zonse. Koma tingakhale otsimikiza kuti nthaŵi yothaŵa ikadzakwana, Akristu adzayenera kupitirizabe kudzipatula ku magulu a zipembedzo zonyenga. Chochititsanso chidwi n’chakuti Yesu anachenjeza za kusabwerera kunyumba kwako kukatenga zovala kapena katundu wina. (Mateyu 24:17, 18) Choncho m’tsogolomu tingadzakhale ndi mayesero okhudzana ndi mmene timaonera zinthu zakuthupi; kodi ndizo zofunika kwambiri, kapena kodi chipulumutso chimene chidzadza kwa onse a kumbali ya Mulungu ndicho chofunika koposa? Inde, kuthaŵa kwathu kungaphatikizepo mavuto ena ndi usiŵa. Tidzayenera kukhala okonzeka kuchita zonse zofunikira, monga momwe anachitira anzathu a m’zaka za zana loyamba amene anathaŵa m’Yudeya kumka ku Pereya, kutsidya kwa Yordano.
23, 24. (a) Kodi ndi kuti kokha kumene tidzapeza chitetezo? (b) Kodi chenjezo la Yesu lonena za ‘chonyansa chitaima m’malo oyera’ liyenera kutikhudza motani?
23 Tiyenera kutsimikizira kuti Yehova ndi gulu lake longa phiri akhalebe pothaŵira pathu. (2 Samueli 22:2, 3; Salmo 18:2; Danieli 2:35, 44) Kumeneko n’kumene tidzapeza chitetezo! Sitidzatsatira miyandamiyanda ya anthu amene adzathaŵira “kumapanga,” ndi kubisala mu “matanthwe a mapiri”—magulu ndi mabungwe a anthu amene adzakhalapo kwa kanthaŵi kochepa kwambiri Babulo Wamkulu atapululutsidwa. (Chivumbulutso 6:15; 18:9-11) Zoonadi, nthaŵi zingadzayambe kukhala zovuta kwambiri—monga momwe ziyenera kuti zinalili mu 66 C.E. kwa akazi oyembekezera amene athaŵa kuchoka m’Yerusalemu kapena mmene zinalili kwa aliyense amene anali paulendo m’nyengo yozizira ndiponso yamvula. Koma tingakhale otsimikizira kuti Mulungu adzapereka chipulumutso. Tiyeni tsopano lino tikulitse chidaliro chathu pa Yehova ndi Mwana wake, amene tsopano akulamulira monga Mfumu ya Ufumuwo.
24 Palibe chifukwa choti tidzichitira mantha ndi zimene zidzachitika. Kalelo Yesu sanafune ophunzira ake kuchita mantha, ndipo sakufuna kuti tikhale amantha kaya lerolino kapena masiku akudzawo. Anatichenjeza kotero kuti tizikonzekera m’mitima ndi m’maganizo mwathu. Ndi iko komwe, Akristu omvera sadzalangidwa pamene chiwonongeko chibwera pachipembedzo chonyenga ndi dongosolo lonse loipali. Adzazindikira ndi kumvera chenjezo la ‘chonyansa chitaima m’malo oyera.’ Ndiponso iwo adzachitapo kanthu motsimikiza mogwirizana ndi chikhulupiriro chawo chosagwedera. Tisaiŵaletu zimene Yesu analonjeza kuti: “Iye wakupirira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa.”—Marko 13:13.
[Mawu a M’munsi]
a “Zizindikiro za Aroma zinali kusungidwa monga milungu mu akachisi a ku Roma; ndipo anthu ameneŵa akamagonjetsa mitundu ina ulemu wawo pa zizindikirozo unali kuwonjezeka . . . [Kwa asilikali] mwina ndizo zinali chinthu chopatulika koposa padziko lapansi. Msilikali wachiroma anali kulumbira pa chizindikiro chake.”—The Encyclopædia Britannica, 11th Edition.
b Tiyenera kukumbukira kuti pamene kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesu mu 66-70 C.E. kungatithandize kumvetsa mmene adzakwaniritsidwira pachisautso chachikulu, kukwaniritsidwa kuŵiri kumeneku sikungafanane ndendende chifukwa chakuti kukuchitika m’mikhalidwe yosiyana.
c Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya December 15, 1975, masamba 741-4.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi “chonyansa cha kupululutsa” chinadzionetsera motani m’zaka za zana loyamba?
◻ N’chifukwa chiyani kuli kwanzeru kulingalira kuti “chonyansa” chamakono chidzaima m’malo oyera panthaŵi ina m’tsogolo?
◻ Kodi ndi kuukira kotani kwa “chonyansa” kumene kwaloseredwa m’Chivumbulutso?
◻ Kodi ndi ‘kuthaŵa’ kotani kumene tingafunikire kuchita?
[Chithunzi patsamba 16]
Babulo Wamkulu akutchedwa “Amayi wa Achigololo”
[Chithunzi patsamba 17]
Chilombo chofiiritsa cha m’Chivumbulutso chaputala 17 ndicho “chonyansa” chimene Yesu anali kunena
[Chithunzi patsamba 18]
Chilombo chofiiritsa chidzatsogolera kuukira ndi kuwononga chipembedzo