Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
“Nsanja ya Olonda” ya August 15, 1996, inati: “M’mbali yomaliza ya chisautsocho, ‘munthu’ amene wathaŵira kumbali ya Yehova adzapulumuka.” Kodi zimenezo zikutanthauza kuti pambuyo pa mbali yoyamba ya chisautso chachikulu ambiri atsopano adzabwera kumbali ya Mulungu?
Imeneyo sindiyo inali mfundo yake.
Mawu a Yesu pa Mateyu 24:22 adzakwaniritsidwa kwenikweni mtsogolo mwa kupulumuka mbali yoyamba ya chisautso chachikulu chikudzacho, kuukira chipembedzo. Nkhaniyo inati: “Kumbukirani kuti ‘munthu,’ otsalira odzozedwa ndi a ‘khamu lalikulu’ omwe, adzakhala atapulumuka kale pamene Babulo Wamkulu awonongedwa mwamsanga ndipo kotheratu m’mbali yoyamba ya chisautsocho.”
Okhulupirika oterowo sadzakhala pangozi pamene Yesu ndi gulu lake lakumwamba aukira m’mbali yomaliza ya chisautso chachikulu. Koma nanga ndani adzapyola mbali imeneyo ya chisautsocho? Chivumbulutso 7:9, 14 chimasonyeza kuti khamu lalikulu lokhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi lidzapulumuka. Bwanji nanga za Akristu odzozedwa ndi mzimu? Nsanja ya Olonda ya August 15, 1990, pa “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” inafotokoza chifukwa chake sitiyenera kukhala oumirira kuti ndi liti pamene otsalira odzozedwa adzatengeredwa kumwamba. Choncho nkhani yaposachedwapayo (August 15, 1996) inasiya mfundoyo yosagamulidwa, ndi kungothirira ndemanga kuti: “Momwemonso m’mbali yomaliza ya chisautsocho, ‘munthu’ amene wathaŵira kumbali ya Yehova adzapulumuka.”
Kaya kuti ena atsopano adzatha kuphunzira choonadi ndi kudza kumbali ya Mulungu chisautso chachikulu chitayamba, pendani mawu a Yesu pa Mateyu 24:29-31. Chisautso chachikulu chitangoulika, chizindikiro cha Mwana wa munthu chidzaoneka. Yesu anatero kuti mitundu yonse ya dziko lapansi idzadziguguda pachifuŵa ndi kulira. Zoti anthu adzagalamuka, nkulapa, nkudza kumbali ya Mulungu ndi kukhala ophunzira oona, Yesu sananene chilichonse.
Mofananamo, m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, Mwana wa munthu adzaoneka ndipo mwachiweruzo adzalekanitsa anthu pamaziko a zimene anachita kapena sanachite kale. Yesu sananene chilichonse za anthu amene anasonyeza mikhalidwe yonga ya mbuzi ndiye mwadzidzidzi nkutembenuka ndi kukhala ngati nkhosa. Iye akudzaweruza mwa zimene anthu akhala akuchita.—Mateyu 25:31-46.
Komanso, tilibe chifukwa chokhalira oumirira pamfundoyi. Anthu a Mulungu, otsalira ndi a khamu lalikulu, akudziŵa zimene ayenera kuchita pakali pano—kulalikira ndi kuphunzitsa anthu. (Mateyu 28:19, 20; Marko 13:10) Tsopano ndi nyengo yakuti tilabadire uphungu wakuti: “Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu, (pakuti anena, M’nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m’tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza; taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso).”—2 Akorinto 6:1, 2.