Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwasangalala ndi kuŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati mwatero, mudzachita chidwi pokumbukira zinthu zotsatirazi:
◻ Kodi tanthauzo la liwu lachigiriki lakuti pa.rou.si’a logwiritsiridwa ntchito pa Mateyu 24:3, 27, 37, 39 nchiyani?
Expository Dictionary of New Testament Words ya Vine imati: “PAROUSIA . . . amatanthauza zonse ziŵiri kufika ndi kukhalapo limodzi.” Chifukwa chake, siili chabe nyengo ya kufika, koma kukhalapo koyambira pa nthaŵi yakufika kumka mtsogolo.—8/15, tsamba 11.
◻ Kodi ndi motani mmene ‘masiku awo anafupikitsidwira’ kotero kuti “munthu” apulumuke m’zaka za zana loyamba, ndipo kodi zidzachitika motani pamlingo waukulu? (Mateyu 24:22)
Mu 66 C.E., Aroma mosayembekezera anafupikitsa kuzinga kwawo Yerusalemu, akumalola “munthu” wachikristu kuthaŵa. Mofananamo, tili ndi chiyembekezo chakuti kuukira Babulo Wamkulu kukudzako kudzafupikitsidwa m’njira ina yake. Chotero Akristu odzozedwa ndi atsamwali awo adzapulumuka chiwonongeko chothekera.—8/15, masamba 18-20.
◻ Kodi tiyenera kuchitanji ngati munthu ayamba kudya zizindikiro za pa Chikumbutso kapena aleka kutero?
Palibe chifukwa chimene Akristu alionse ayenera kudera nkhaŵa. Yesu anati: “Ine ndine Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira [nkhosa, NW] zanga.” Ndi chitsimikizo chofananacho, Yehova amawadziŵa awo amene wasankhadi monga ana auzimu. (Yohane 10:14; Aroma 8:16, 17)—8/15, tsamba 31.
◻ Kodi chifuno chachikulu cha Chilamulo cha Mose chinali chiyani?
Makamaka, chinaphunzitsa Aisrayeli za kufunikira kwawo Mesiya, amene akanawawombola ku mkhalidwe wawo wauchimo. (Agalatiya 3:24) Chilamulo chinawaphunzitsanso mantha aumulungu ndi kumvera, ndipo chinathandiza Israyeli kukhalabe wopatuka pa machitachita oipa a mitundu yomzinga. (Levitiko 18:24, 25)—9/1, tsamba 9.
◻ Kodi chifuno cha pangano latsopano nchiyani? (Yeremiya 31:31-34)
Ndicho kutulutsa mtundu wa mafumu ndi ansembe odalitsa anthu onse. (Eksodo 19:6; 1 Petro 2:9; Chivumbulutso 5:10)—9/1, masamba 14, 15.
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ndi luso la kupepesa?
Kupepesa kungathandize kuthetsa kupweteka kumene kupanda ungwiro kumachititsa, ndipo kungachiritse maunansi osokonezeka. Kupepesa kulikonse kumene timachita kuli phunziro la kudzichepetsa ndipo kumatiphunzitsa kusamala kwambiri za malingaliro a ena.—9/15, tsamba 24.
◻ Kodi Chigumula cha dziko lonse cha m’tsiku la Nowa chinachitikadi kalelo?
Inde. Nthano zakale zosimba za chigumula cha dziko lonse zimapezeka kuzungulira dziko lonse, kuchokera ku maiko a ku America kufika ku Australia. Kufala kwa nkhani imeneyi kumachirikiza mfundo yakuti chigumula cha dziko lonse chinachitikadi, monga momwe Baibulo limasimbira. (Genesis 7:11-20)—9/15, tsamba 25.
◻ Kodi kukhala wochereza alendo kumaphatikizaponji? (Aroma 12:13)
Mawuwo kuchereza alendo atembenuzidwa kuchokera ku liwu lachigiriki lopangidwa ndi mawu aŵiri otanthauza “chikondi” ndi “mlendo.” Chotero, kuchereza alendo kumangotanthauza “kukonda alendo.” Koma kumaposa chikondi chozikidwa pa lamulo, chosonyezedwa chifukwa cha thayo. Nkozikidwa pa chikondi ndi ubwenzi weniweni.—10/1, tsamba 9.
◻ Kodi Paulo akunenanji ponena za ukwati ndi umbeta m’kalata yake yoyamba kwa Akorinto, chaputala 7?
Ukwati ngwololedwa ndipo, m’mikhalidwe ina, ngwoyenera kwa ena. Komabe umbeta ulidi wabwino kwa mwamuna kapena mkazi wachikristu amene akufuna kutumikira Yehova ndi zocheukitsa zochepa.—10/15, tsamba 13.
◻ Kodi ndi motani mmene mkulu ‘amadzisungira mbumba yake ya iye yekha’? (1 Timoteo 5:8)
Mkulu ayenera ‘kudzisungira mbumba yake’—mkazi wake limodzinso ndi ana ake—mwakuthupi, mwauzimu, ndi mwamaganizo.—10/15, tsamba 22.
◻ Kodi ndi motani mmene Yehova amaperekera chitonthozo kwa atumiki ake?
Mzimu woyera wa Mulungu umagwira ntchito monga “wotonthoza.” (Yohane 14:16, NW, mawu amtsinde) Njira inanso imene Mulungu amaperekera chitonthozo ndiyo kudzera m’Baibulo. (Aroma 15:4) Mulungu amadziŵa zosoŵa za mmodzi ndi mmodzi ndipo akhoza kutigwiritsira ntchito kutonthozana wina ndi mnzake, monga momwe Paulo anapezera chitonthozo m’lipoti la Tito lonena za Akorinto. (2 Akorinto 7:11-13)—11/1, masamba 10, 12.
◻ Kodi mafotokozedwe a Paulo akuti Yehova ali “Atate wa zifundo [zachisoni, NW],” opezeka pa 2 Akorinto 1:3 amatanthauzanji?
Nauni yachigiriki yotembenuzidwa kuti “zifundo zachisoni” imachokera ku liwu logwiritsiridwa ntchito kusonyeza chisoni pa kuvutika kwa wina. Motero Paulo akulongosola chisoni cha Mulungu kwa atumiki Ake onse okhulupirika amene akuvutika m’nsautso.—11/1, tsamba 13.
◻ Kodi kusala kudya kwa Aisrayeli pa Tsiku Lotetezera kunali kukwaniritsanji? (Levitiko 16:29-31; 23:27)
Kusunga kusala kudya kunasonkhezera anthu a Israyeli pa kuzindikira kwambiri za mkhalidwe wawo wauchimo ndi kufunikira kwa chiombolo. Mwa kusala kudya anasonyeza chisoni chifukwa cha machimo awo ndi kulapa pamaso pa Mulungu.—11/15, tsamba 5.
◻ Kodi lamulo loperekedwa kwa achichepere lakuti, “Kumbukira, tsopano lino, Mlengi wako Wamkulu” limatanthauzanji? (Mlaliki 12:1, NW)
Umboni wina umanena kuti liwu lachihebri lotembenuzidwa kuti “kumbukira” kaŵirikaŵiri limapereka lingaliro la “kukonda kwa maganizo ndi mchitidwe zimene zimatsagana ndi chikumbukiro.” Choncho kumvera lamuloli kumatanthauza zambiri kuposa kungoganiza za Yehova. Kumaloŵetsamo ntchito, kuchita zimene zimamkondweretsa.—12/1, tsamba 16.