Chizindikiro—Kodi Mukuchilabadira Icho?
“TIKUFUNA anthu a dziko lirilonse kusangalala ndi kutukuka, mkhalidwe wabwino ndi chimwemwe. Msewu ku ichi umakhala kupyolera m’kupita ku dziko lopanda nyukliya, lopanda upandu.”—Perestroika, lolembedwa ndi mtsogoleri wa Soviet Mikhail Gorabachev.
Molungamitsika, ambiri amakaikira kuti munthu ndithudi ali wokhoza kutulutsa mikhalidwe yotereyi ya dziko. Mtsogoleri wina, Yesu Kristu, analonjeza chinachake chokulira—dziko lapansi la paradaiso pamene ngakhale dongosolo la imfa lidzabwezedwa. (Mateyu 5:5; Luka 23:43; Yohane 5:28, 29) Ndithudi, njira yokwanitiritsira chimenechi iri kulowerera kwaumulungu. M’kuyankha ku funso lakuti “ndi liti” pamene kulowerera koteroko kukadza, Yesu ananena kuti: “Ufumu wa Mulungu sukudza ndi mawonekedwe.” Poyamba, kokha oyanganira achidwi okhala ndi diso lophiphiritsira la chowombankhanga angazindikire iwo. (Luka 17:20, 37) Nchifukwa ninji tero?
Chifukwa Chimene Timafunikira Chizindikiro
Chiyambire kukwera kwake kumwamba, Yesu Kristu “wakhala m’kuwunika kosakhozeka kufikako amene munthu sanamuwona, kapena sakhoza kumuwona.” (1 Timoteo 6: 16) Chotero, maso aumunthu enieni sadzamuwonanso iye kachiŵiri. Monga mmene Yesu ananenera pa tsiku lomalizira la moyo wake wa padziko lapansi: “Kwa kanthaŵi kochepa dziko silidzandiwonanso ine.” (Yohane 14:19) Iye angawonedwe kokha mwa njira yophiphiritsira.—Aefeso 1:18; Chivumbulutso 1:7.
Komabe, Yesu ananena kuti chikakhala chotheka kaamba ka ophunzira ake kuzindikira pamene Ufumu wa Mulungu ukayamba kulamulira. Motani? Mwanjira ya chizindikiro. M’kuyankha ku funso lakuti, “Nchiyani chimene chidzakhala chizindikiro cha kufika kwanu?” Yesu anandandalitsa chitsimikiziro chowoneka ndi maso cha kulamulira kwake kosawoneka kwa mtsogolo.—Mateyu 24:3.
Lophatikizidwa mu chizindikirocho linali fanizo losonyeza mtundu wa anthu omwe akakhoza kupindula kuchokera ku ilo. “kumene kuli konse uli mtembo,” Yesu anatero, “[ziwombankhanga, NW] Onse amene afuna kupulumuka chimaliziro cha dongosolo liripoli kulowa m’dziko latsopano la Mulungu ayenera ‘kusonkhana pamodzi’ ndi kusangalala ndi chakudya chauzimu limodzi ndi “osankhidwa” a Kristu onga chiwombankhanga.—Mateyu 24:31, 45-47.
Kudzichinjiriza Molimbana ndi Kusaleza Mtima
Palibe munthu amene angadziŵe tsiku la kutha kwa dongosolo loipa liripoli. “Ponena za tsikulo ndi ora,” Yesu anati, “palibe aliyense adziŵa, ngakhale angelo m’mwamba kapena Mwana, koma Atate ndiwo.”—Marko 13:32, 33.
Kodi chingakhale kuti, ngakhale ndi tero, chizindikiro chikachitika kupyolera mu utali wa mibadwo yambiri ya anthu? Ayi. Chizindikiro chiyenera kuchitika mkati mwa mbadwo wachindunji umodzi. Mbadwo wofananawo womwe unachitira umboni chiyambi cha chizindikiro udzachitiranso umboni kaindeinde wake “m’chisautso chachikulu chomwe sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko.” Akatswiri a mbiri yakale atatu, Mateyu, Marko, ndi Luka, analemba chitsimikiziro cha Yesu cha ichi.—Marko 13;19, 30; Mateyu 24:13, 21, 22, 34; Luka 21:28, 32.
Pali, ngakhale kuli tero, ngozi ya kukhala wosaleza mtima. Zaka makumi asanu ndi aŵiri mphambu zinayi zapita chiayambire kuwulika kwa Nkhondo ya Dziko ya I mu 1914. Kuchokera ku kawonedwe kaumunthu, ichi chingawoneke kukhala nthaŵi yaitali kwambiri. Koma Akristu ena okhala ndi maso onga a chowombankhanga omwe anawona Nkhondo ya Dziko ya I akalipobe amoyo kwenikweni. Mbadwo wawo sunapitebe.
Pamene iye anapereka chizindikirocho, Yesu anachenjeza ponena za ngozi ya kukhala wosaleza mtima. Iye analankhula za anthu omwe akanena m’mitima yawo: “Mbuye wanga wachedwa.” Yesu anasonyeza kuti kudzimva koteroko, ngati sikunawongoleredwe, kungatsogolere ku kachitidwe kopusa. (Mateyu 24:38-51) Atumwi a Kristu ali ndi zambiri zonena ponena za ichi.
“Oseka”
Mogwirizana ndi wolemba Baibulo Yuda, atumwi a Kristu anafuula chenjezo lotsatirali: “M’nthaŵi yotsiriza padzakhala oseka, akuyenda monga mwa zilakolako [zawo za zinthu zosakhala zaumulungu, NW].”—Yuda 17, 18.
Chilakolako kaamba ka moyo m’dziko latsopano loyera chingalowedwe m’malo mopepuka ndi “zilakolako [za zinthu zosakhala zaumulungu, NW].” Ichi chiri makamaka changozi lerolino chifukwa cha njira zadziko za kalongosoledwe ndi kumabitsirana. Kulibe ndi kalelonse m’mbiri ya munthu pamene chiwawa, kukhulupirira mizimu, ndi chisembwere cha kugonana zakhala zolandirika kumlingo wotere. Izo zakhala kaŵirikaŵiri mitu ya pa wailesi ndi kuwonetsera kwa nyimbo, ndipo zikuwoneka m’maprogramu osiyanasiyana a pa TV, mavideo, kusatsa malonda, mabukhu, ndi magazini.
Chizindikiro chimaloza ku mapeto a zopanda umulungu zoterozo. Mwachibadwa, kenaka, anthu ena omwe ali ndi chilakolako kaamba ka zinthu zopanda umulungu amaseka chizindikirocho. Monga momwe kunanenedweratu, iwo amatsutsa kuti “zinthu zonse zikupitirizabe ndendende monga pa chilengedwe.”—2 Petro 3:3, 4.
‘Chikondi Chizirara’
Posachedwapa, mkonzi wa zaka 75 zakubadwa wa ku America, Paul Bowles, anafunsidwa ndi magazini ya Newsweek. Akumayankha funso lakuti, “Kodi ndi kati komwe kali kawonedwe kako ka dziko?” Bowles ananena kuti: “Dziko lapita ku zidutswa m’makhalidwe abwino. Palibe aliyense amene ali wowona mtima mpang’ono pomwe monga mmene analiri zaka 60 zapitazo. Panali nsonga ya chimene chiri mwamuna; unali mkhalidwe wa mtengo woposa wa mwambo wathu wa Kumadzulo. Tsopano palibe aliyense yemwe [amasamala]. Palinso kugogomezera kokulira pa ndalama.”
Mkhalidwe umenewu uli kokha monga mmene Baibulo linaneneratu. Yesu ananeneratu kuti: “chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusayeruzika chikondi cha unyinji chidzazirara.” (Mateyu 24:12; 2 Timoteo 3:1-5) Pamene dyera ndi umbombo ziwonjezeka, chikondi kaamba ka Mulungu chimatsika. Anthu owonjezerekawonjezeraka amasonyeza kuti amaika zikhumbo zawo patsogolo pa malamulo a Mulungu mwa kudzilowetsa m’machitidwe aupandu, uchigaŵenga, kachitidwe ka malonda kosawona mtima, chisembwere cha kugonana, ndi kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka.
Ena amazindikira kukwaniritsidwa kwa chizindikiro koma amalephera kuchita pa icho chifukwa cha kukutidwa mokulira m’kudzikondweretsa iwo eni. Ku mbali ina, kulabadira chizindikiro kumafunikira chipiriro m’kusonyeza chikondi chopanda dyera kaamba ka Mulungu ndi mnansi.—Mateyu 24:13, 14.
“Zodera Nkhaŵa za Moyo”
Yesu anachenjezanso kuti, pambali pa zosangalatsa zadyera, zofunika zaumoyo za lamulo zikakhoza kumwereketsa ena kotero kuti akakhoza kunyalanyaza chizindikiro. Iye analimbikitsa kuti: “Mudziyang’anire nokha kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha. Pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi.”—Luka 21: 34, 35.
Baibulo, ndithudi, limalimbikitsa moyo wachimwemwe wa banja. (Aefeso 5:24–6:4) Kaŵirikaŵiri ichi chimafunikira kuti mutu wa banja ukhale wolowetsedwamo mu mkhalidwe wina wa ntchito kapena malonda kupanga mphatso kaamba ka mkazi wake ndi ana. (1 Timoteo 5:8) Komabe, chikakhala kupanda kuyang’ana bwino kulola moyo wa wina kuzungulira mokulira pa banja, malonda, ndi zinthu za kuthupi. Chifukwa cha ngoziyi, Yesu anachenjeza kuti: “Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu: anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m’chingalawa, ndipo chinadza chigumula nichowononga onsewo . . . Momwemo kudzakhala tsiku la kuvumbuluka Mwana wa munthu.”—Luka 17:26-30; Mateyu 24:36-39.
“Kutengedwa” kapena “Kusiidwa”?
Ora latha kale. Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu udzalowerera kudzalungamitsa zinthu. Kenaka munthu aliyense adzayambukiridwa mu imodzi ya njira ziŵiri. Monga mmene Yesu analongosolera: “Pomwepo adzakhala aŵiri m’munda: mmodzi adzatengedwa ndi wina adzasiidwa; aŵiri adzakhala opera pamphero: mmodzi adzatengedwa ndi wina adzasiidwa.”—Mateyu 24: 40, 41.
Pamene nthaŵi yovuta imeneyo ifika, kodi malo anu adzakhala otani? Kodi mudzasiidwa ku chiwonongeko, kapena kodi mudzatengedwa kaamba ka kupulumuka? Kukutsogozani inu m’njira yolondola, lingalirani kachiŵirinso fanizo limene Yesu anapereka: “Pamene pali mtembo, pomweponso [ziwombankhanga, NW] zidzasonkhanidwa konko.”—Luka 17:34-37; Mateyu 24:28.
Yesu chotero anali kugogomezera kufunika kwa kukhala ndi kachitidwe kowona patali, kogwirizana. Awo otengedwa kaamba ka chipulumutso ali amene amasonkhana pamodzi mokhazikika ndi kupindula kuchokera ku kuleredwa kwauzimu kumene Mulungu amapereka. Mamiliyoni angapo apeza kuti kudya kwauzimu koteroko kumachokera ku kuyanjana kwathithithi ndi umodzi wa mipingo yoposa 55,000 ya Mboni za Yehova ndi kupyolera m’kuphunzira zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo zonga ngati chimene mukuŵerengachi.
Oposa mamiliiyoni atatu a Mboni za Yehova amasonyeza chikhulupiriro mu chizindikirocho mwa kugawana “mbiri yabwino ya ufumu” ndi anansi awo. (Mateyu 24:14) Kodi mukuyankha motsimikizirika ku mbiri yabwinoyo? Ngati ndi tero, mungaike ku mtima lonjezo la kupulumuka kulowa m’dziko la paradaiso.
[Chithunzi patsamba 5]
Ambiri ali olowetsedwa kwenikweni m’zosangalatsa kotero kuti amanyalanyaza chizindikiro
[Chithunzi patsamba 6]
Kulabadira chizindikiro kumaphatikizapo kusonkhana pamodzi kudya pa Mawu a Mulungu