Kuphunzira Kuchokera ku Banja la Yesu la Padziko Lapansi
KODI mumadziŵapo chiyani za banja la Yesu, anthu amene anali kukhala naye mpaka pamene anabatizidwa, zaka zoyambirira 30 zamoyo wake wapadziko lapansi? Kodi Mauthenga Abwino amatiuza chiyani za nkhaniyi? Nanga tingaphunzirepo chiyani pamene tikupenda mosamalitsa banja la Yesu? Mayankho a mafunso ameneŵa mungapindule nawo kwambiri.
Kodi Yesu anabadwira m’banja la mwanaalirenji? Atate ake omulera, Yosefe, anali kalipentala. Pankafunika kugwira ntchito zolimba, yomwe kaŵirikaŵiri inali yodula mitengo kuti apeze matabwa. Pafupifupi masiku 40 Yesu atabadwa, makolo ake anapita ku Yerusalemu napereka nsembe motsatira zomwe Chilamulo chinkanena. Kodi iwo anapereka nkhosa pamodzi ndi njiwa kapena nkhunda monga momwe Chilamulo chinkafunira? Ayi. Zikusonyeza kuti sakanatha kupereka zoterozo. Komabe, Chilamulo chinali ndi makonzedwe ena a zimene osauka angapereke. Mogwirizana ndi makonzedwe amenewo, Yosefe ndi Mariya anapereka “njiwa ziŵiri kapena maunda aŵiri.” Kupereka zinthu zotsika mtengo koteroko kunasonyeza kuti banja lawo linali losauka.—Luka 2:22-24; Levitiko 12:6, 8.
Chotero mungathe kuona kuti Yesu Kristu, yemwe ndi Wolamulira wam’tsogolo wa anthu onse, anabadwira ku banja la anthu osauka, amene anafunikira kugwira ntchito zolimba kuti apeze zosoŵa zawo. Yesu atakula anakhala m’misiri wa mitengo, monga mmene analili atate ake omulera. (Mateyu 13:55; Marko 6:3) “Ngakhale kuti [Yesu] anali wolemera” monga cholengedwa champhamvu chauzimu chakumwamba, Baibulo limanena kuti iye “anakhala wosauka” chifukwa cha ife. Iye analolera kukhala pamalo otsika monga munthu nakulira m’banja la anthu wamba. (2 Akorinto 8:9; Afilipi 2:5-9; Ahebri 2:9) Yesu sanabadwire ku banja lolemera, ndipo zimenezi zikanathandiza anthu kuti akhale naye momasuka kwambiri. Iwo sanatekeseke ndi malo kapena udindo wake wapamwamba. Anthuwo anayenera kumuyamikira chifukwa cha kuphunzitsa kwake, makhalidwe ake abwino, ndiponso ntchito zake zodabwitsa. (Mateyu 7:28, 29; 9:19-33; 11:28, 29) Tikutha kuona nzeru za Yehova Mulungu polola kuti Yesu adzabadwire m’banja la anthu wamba.
Tsopano tiyeni tiganizire anthu ena a m’banja la Yesu ndipo tione zimene tingaphunzire kwa iwo.
Yosefe Anali Wolungama
Pamene Yosefe anaona kuti mkazi amene anali atatomera ali ndi mimba ‘asanakumame naye,’ ayenera kuti anasokonezeka maganizo kwambiri. Iye anaganiza zoti kaya alolere zomukondabe Mariyayo kapena kudana ndi zimene anthu akanaona kuti ndi chiwerewere. Zonsezi zinkaoneka kuti zinali kum’sokonezera ufulu wake monga mwamuna wam’tsogolo wa Mariyayo. M’nthaŵi imeneyo, mkazi wotomeredwa ankaonedwa ngati mkazi amene ali pabanja. Ataganizaganiza, Yosefe anafuna kusudzula Mariya mwachinsinsi kuti iye asaponyedwe miyala monga munthu wochita chigololo.—Mateyu 1:18; Deuteronomo 22:23, 24.
Kenako mngelo anaonekera kwa Yosefe m’maloto nati: “Usaope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.” Ndipo pamene analandira malangizo a Mulungu ameneŵa, Yosefe anamvera ndipo anadzitengera Mariya.—Mateyu 1:20-24.
Chifukwa cha chosankha chimenechi, munthu wolungama ndi wokhulupirika ameneyu anakhala mmodzi wa okwaniritsa zimene Yehova ananeneratu kudzera mwa mneneri Yesaya kuti: “Taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wa mwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanueli.” (Yesaya 7:14) Yosefe analidi mwamuna wauzimu yemwe anayamikira mwayi wokhala tate wolera Mesiya, ngakhale kuti mwana woyamba wa Mariya ameneyu sanali wake.
Yosefe anapeŵa kugona ndi Mariya kufikira nthaŵi imene anabereka mwana wakeyo. (Mateyu 1:25) Kwa banja latsopanoli, kudziletsa kunali kovuta kwambiri, komabe zikuoneka kuti sanafune kuti pakhale chisokonezo chakuti kodi Tate wa mwanayo anali ndani. Chinalitu chitsanzo chapamwamba zedi cha kudziletsa! Yosefe sanalabadire zofuna mtima wake koma anaika zinthu zauzimu patsogolo.
Pamaulendo okwana anayi, Yosefe analandira malangizo ochoka kwa mngelo a mmene angalerere mwana wake wopezayo. Maulendo atatu anali a malangizo okhudza za kumene akalerere mnyamatayo. Kumvera mwamsanga kunali kofunika zedi chifukwa inali njira yopulumutsira mwanayo. M’zochitika zonsezi, Yosefe analabadira mwamsanga ndipo anatengera mwana wamng’onoyo ku Igupto kenako nabwerera naye ku Israyeli. Kuchita zimenezi kunatetezera Yesu pamene Herode anapha ana onse aamuna. Komanso, kumvera kwa Yosefe kunapangitsa kuti maulosi okhudza Mesiya akwaniritsidwe.—Mateyu 2:13-23.
Yosefe anaphunzitsa Yesu ntchito kuti athe kudzadzisamalira yekha. Choncho, Yesu sanali kudziŵika kokha kuti “mwana wa mmisiri wa mitengo” koma anali kudziŵikanso kuti “mmisiri wa mitengo.” (Mateyu 13:55; Marko 6:3) Mtumwi Paulo analemba kuti Yesu “anayesedwa m’zonse monga momwe ife.” Mwachionekere izi zinaphatikizapo kugwira ntchito zolimba kuti athandize banja lake.—Ahebri 4:15.
Pomaliza, tikuona umboni wa kudzipereka kwa Yosefe pa kulambira koona m’nkhani yomwe akutchulidwa komaliza m’Malemba Achigiriki Achikristu. Yosefe anatengera banja lake ku Yerusalemu kukachita Paskha. Amuna okhatu ndiwo analamulidwa kukakhala nawo, koma chinali chizoloŵezi cha Yosefe chotenga banja lake kupita nalo ku Yerusalemu “chaka ndi chaka.” Yosefe anali kudzimana kwambiri chifukwa ankayenda makilomita 100 kuchokera ku Nazarete mpaka ku Yerusalemu. Komabe, paulendo umene watchulidwa m’Malemba, Yesu anasiyana ndi gululo. Iye anakapezeka m’kachisi akumvetsera ndiponso kufunsa mafunso aphunzitsi a Chilamulo. Ngakhale kuti anali ndi zaka 12 zokha, Yesu anasonyeza nzeru zakuya ndiponso kuti anali kudziŵa Mawu a Mulungu. Apa, tikutha kuona kuti makolo a Yesu anaphunzitsa bwino mwana wawo, kumulera kuti akhale mwana wokonda zauzimu. (Luka 2:41-50) Mwachionekere, Yosefe anamwalira pambuyo pazochitika zimenezi chifukwa Malemba samafotokozanso za iye.
N’zoona kuti Yosefe anali munthu wolungama yemwe anasamalira bwino banja lake, mwauzimu komanso mwakuthupi. Kodi inuyo mofanana ndi Yosefe, mumaika zinthu zauzimu choyamba m’moyo wanu pozindikira zimene Mulungu akufuna kwa ife masiku ano? (1 Timoteo 2:4, 5) Kodi mumalabadira mosanyinyirika zimene Mulungu amanena m’Mawu ake, mwa kusonyeza kugonjera kofanana ndi kwa Yosefe? Kodi mumaphunzitsa ana anu moti angamalankhule zinthu zauzimu ndi anzawo?
Mariya Anali Mtumiki wa Mulungu Wopanda Dyera
Mariya, amayi ake a Yesu, anali mtumiki wabwino wa Mulungu. Pamene mngelo Gabrieli analengeza kuti Mariya adzakhala ndi mwana, Mariyayo anadabwa kwambiri. Pokhala namwali, iye anali ‘asanadziŵanepo ndi mwamuna.’ Pamene anazindikira kuti zimenezi zidzachitika ndi mphamvu ya mzimu woyera, Mariya modzichepetsa analandira uthengawo, akumati: “Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mawu anu.” (Luka 1:30-38) Iye anayamikira kwambiri mwayi wapadera umenewu wa zinthu zauzimu moti anakonzeka kuthana ndi vuto lililonse lomwe likanabwera chifukwa cha zosankha zakezo.
Ndithudi, kulolera ntchito imeneyi kunasintha moyo wake wonse monga mkazi. Ndipo panthaŵi imene anapita ku Yerusalemu kukadziyeretsa, munthu wopemphera wachikulire dzina lake Simeoni analankhula ndi Mariyayo kuti: “Lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako.” (Luka 2:25-35) Mwachionekere, iye anali kutanthauza mmene Mariya adzamvere poona anthu ambiri akum’kana Yesu ndiyeno kenako nam’khomera pamtengo wozunzirapo.
Pamene Yesu anali kukula, Mariya anakumbukirabe zinthu zimene zidzachitika pamoyo wa Yesuyo, ‘nalingalira mumtima mwake.’ (Luka 2:19, 51) Mofanana ndi Yosefe, Mariya anali munthu wokonda zauzimu ndipo ankadziŵa zochitika ndi zonenedwa zomwe zinakwaniritsa maulosi. Zomwe mngelo Gabrieli ananena kwa Mariya ziyenera kuti zinakhazikika m’maganizo ake, zakuti: “Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu; ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo ku nthaŵi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.” (Luka 1:32, 33) Mariya anaona kuti unali mwayi wapadera kwambiri kukhala mayi wa Mesiya.
Kusonyeza kuti Mariya anali wauzimu zinaonekeranso pamene anakumana ndi wachibale wake Elizabeti yemwe anakhalanso ndi pakati mozizwitsa. Atamuona, Mariya analemekeza Yehova ndipo anaonetsa chikondi chake m’Mawu a Mulungu. Iye anatchulapo za pemphero la Hana lomwe lili pa 1 Samueli chaputala 2 ndipo anaphatikizamo mfundo za m’mabuku ena a Malemba Achihebri. Kudziŵa kwambiri Malemba koteroko kunasonyeza kuti anali woyenerera kukhala mayi wodzipereka ndi woopa Mulungu. Anagwirizana ndi Yosefe kulera mwana wakeyo mwauzimu.—Genesis 30:13; 1 Samueli 2:1-10; Malaki 3:12; Luka 1:46-55.
Mariya anali ndi chikhulupiriro champhamvu mwa mwana wake monga Mesiya, ndipo sanafooke pambuyo pa imfa ya Yesuyo. Yesu atangoukitsidwa kumene kwa akufa, Mariya anali mmodzi wa ophunzira okhulupirika omwe anakumana ndi atumwi kupemphera nawo pamodzi. (Machitidwe 1:13, 14) Anapitirizabe kukhala wokhulupirika, ngakhale anakumana ndi zopsinja poona mwana wake wokondedwa akufa pamtengo wozunzirapo.
Kodi mungapindule chiyani pophunzira zochita za Mariya? Kodi mumavomereza mwayi wotumikira Mulungu ngakhale kuti pangafunikire kudzimana? Kodi mumakhudzika mtima ndi kuzindikira kufunika kwa mwayi woterewu masiku ano? Kodi mukukumbukira zimene Yesu ananeneratu ndi kuziyerekezera ndi zochitika masiku ano ‘ndi kuzilingalira mumtima mwanu’? (Mateyu, chaputala 24 ndi 25; Marko, chaputala 13; Luka, chaputala 21) Kodi mumatsanzira Mariya mwa kudziŵa bwino Mawu a Mulungu, ndi kuwagwiritsa ntchito pokambirana ndi ena? Kodi mudzapitirizabe kukhulupirira Yesu ngakhale mutakumana ndi zopinga zina zomwe zingakupangitseni kusoŵa mtendere m’maganizo chifukwa chokhala wotsatira wake?
Abale a Yesu Anatha Kusintha
Zikuoneka kuti abale a Yesu sanali kum’khulupirira kufikira imfa yake. Chiyenera kukhala chifukwa chake sanapezeke panthaŵi imene Yesu ankafa pamtengo wozunzirapo zomwe zinam’pangitsa kuikiza amayi ake m’manja mwa mtumwi Yohane. Abale ake a Yesuwo sanali kumulemekeza iye, moti panthaŵi ina anafika potchula Yesuyo kuti ‘woyaruka.’ (Marko 3:21) Popeza kuti Yesu anali ndi abale ake osakhulupirira, lerolino awo amene ali ndi abale osakhulupirira m’banja sangakayikire kuti Yesu amadziŵa mmene iwo amamvera abale awowo akamawanyodola chifukwa cha chikhulupiriro chawo.
Komabe, Yesu ataukitsidwa, abale akewo anayamba kum’khulupirira. Abale akewo anali nawo pagulu la anthu omwe anakumana ku Yerusalemu Pentekoste wa 33 C.E. asanachitike ndipo anapemphera limodzi ndi atumwi. (Machitidwe 1:14) Mwachionekere, chiukiriro cha Yesu chinasintha mitima ya abale akewo, nakhala ophunzira ake. Sitifunika kutayiratu mtima chifukwa cha achibale athu omwe sali m’choonadi.
Malemba amasonyeza kuti Yakobo, mbale wa Yesu, yemwenso Yesuyo anamuonekera anali ndi udindo waukulu mu mpingo wachikristu. Analemba kalata youziridwa ndi Mulungu kwa Akristu anzake, kuwalimbikitsa kuti apitirizebe kukhala ndi chikhulupiriro. (Machitidwe 15:6-29; 1 Akorinto 15:7; Agalatiya 1:18, 19; 2:9; Yakobo 1:1) Mbale wake winanso, Yuda, analemba kalata youziridwa yolimbikitsa Akristu anzake kumenya zolimba nkhondo ya chikhulupiriro. (Yuda 1) N’zochititsa chidwi kwambiri kuti Yakobo kapena Yuda sanakhudzepo ubale wawo wakuthupi ndi Yesu m’makalata awo kuti akope Akristu anzawo kuti akhulupirire zimene anali kunena. Ndi phunzirotu lapamwamba lodzichepetsa lomwe tingaphunzire kwa anthu ameneŵa!
Ndiyeno, ndi zinthu zina ziti zimene tingaphunzire kuchokera ku banja la Yesu? Maphunziro a kudzipereka komwe mungathe kukusonyeza m’njira izi: (1) Dziperekeni mokhulupirika ku zofuna za Mulungu ndipo khalani wokonzeka kulimbana ndi zovuta zonse zimene zingabwere chifukwa chochita zimenezo. (2) Ikani zinthu zauzimu pamalo oyamba, ngakhale kuti kungafune kudzimana. (3) Phunzitsani ana anu mogwirizana ndi Malemba. (4) Musataye mtima chifukwa cha achibale anu omwe sali m’choonadi. (5) Musadzitame chifukwa cha ubale kaya ubwenzi umene muli nawo ndi anthu ena amene ali ndi udindo waukulu mu mpingo wachikristu. Inde, kuphunzira za banja la Yesu la padziko lapansi kumatipangitsa kukhala pafupi ndi iye ndiponso kumatithandiza kuyamikira Yehova chifukwa chosankha banja wamba kuti lilere Yesu ali mwana.
[Zithunzi pamasamba 4, 5]
Yosefe anatenga Mariya monga mkazi wake ndipo anakhudzidwa ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi okhudza Mesiya
[Zithunzi patsamba 6]
Yosefe ndi Mariya anaphunzitsa ana awo zinthu zauzimu komanso ntchito
[Zithunzi patsamba 7]
Ngakhale kuti anakulira m’banja lokonda zauzimu, abale ake a Yesu sanam’khulupirire iye mpaka pambuyo pa imfa yake
[Zithunzi patsamba 8]
Abale a Yesu, Yakobo ndi Yuda analimbikitsa Akristu anzawo