Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwalingalirapo mosamala pa makope a Nsanja ya Olonda aposachedwapa? Mungakondwere kukumbukira zotsatirazi:
◻ Kodi ndi motani mmene munthu ‘amadzera kwa Yesu’ mogwirizana ndi chiitano chake pa Mateyu 11:28?
Yesu anati: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge [mtengo wake wozunzirapo, NW], nanditsate ine.” (Mateyu 16:24) Motero, kudza kwa Yesu kumatanthauza kuchita chifuniro cha Mulungu ndi cha Kristu m’malo mwa chifuniro chaumwini, tikumasenza katundu wakutiwakuti wa thayo ndi kuchita motero mopitirizabe.—8/15, tsamba 17.
◻ Kodi nchifukwa ninji ali “oŵerengeka” okha amene akupeza ‘njira yochepetsa ya kumuka nayo ku moyo’ imene Yesu anatchula pa Mateyu 7:13, 14?
Njira yopapatiza ili ndi ziletso za malamulo ndi mapulinsipulo a Mulungu. Motero, imangokopa kokha munthu amene akufunadi kugwirizanitsa moyo wake ndi miyezo ya Mulungu. Ngakhale kuti imaoneka kukhala yoletsa, ‘njira yochepetsa’ imamasula munthu pambali iliyonse yofunika. Malire ake aikidwa ndi “lamulo langwiro, ndilo laufulu.” (Yakobo 1:25)—9/1, tsamba 5.
◻ Kodi ndi motani mmene luntha lingakulitsidwire?
Luntha silimafika mofeŵa kapena mwachibadwa. Koma mwa kuleza mtima, pemphero, khama, mayanjano anzeru, kuphunzira Baibulo ndi kusinkhasinkhapo, limodzi ndi kudalira mzimu woyera wa Yehova, luntha lingakulitsidwe.—9/1, tsamba 21.
◻ Kodi ndi motani mmene nsanje ya munthu ingakhalire yothandiza?
Ingachititse wina kutetezera wokondedwa wake ku makhalidwe oipa. Ndiponso, anthu angasonyeze nsanje yoyenera pa Yehova ndi kulambiridwa kwake. (1 Mafumu 19:10)—9/15, masamba 8, 9.
◻ Kodi chimatanthauzidwa nchiyani ndi mawu a pa Genesis 50:23 onena za adzukulu a Yosefe kuti: “Anabadwa pa maondo a Yosefe”?
Zimenezi zingatanthauze kuti Yosefe anavomereza anawo kukhala mbadwa zake. Zingatanthauzenso kuti anaseŵera ndi anawo mwachikondi, akumawaseŵeretsa pa maondo ake. Lerolino atate angachite bwino kusonyeza ana awo chikondi chimodzimodzicho.—9/15, masamba 20, 21.
◻ Kodi chofunika kwambiri nchiyani kuti ukwati ndi moyo wa banja zikhale zopambana?
Kuti pakhale zotulukapo zabwino zimenezi, okwatirana ayenera kuika chifuniro cha Mulungu pa malo oyamba nthaŵi zonse. Pochita motero, okwatirana amayesayesa kumamatirana ndi kuthetsa mavuto awo mwa kugwiritsira ntchito uphungu wa Mawu a Mulungu. Motero amapeŵa kuŵaŵa mtima kwa mtundu uliwonse kumene kumakhalapo chifukwa chonyalanyaza chifuniro cha Mulungu. (Salmo 19:7-11)—10/1, tsamba 11.
◻ Kodi changu chaumulungu nchofunika motani lerolino?
Changu chaumulungu ndicho mbali yofunika kwambiri ya utumiki wa mtima wonse kwa Yehova. Chimaletsa ndipo chimathandiza kuthetsa zoyesayesa za Mdyerekezi za kuchititsa atumiki a Mulungu ‘kulema ndi kukomoka m’moyo [wawo].’ (Ahebri 12:3) Chimawatetezera pa kuyanjana kosafunikira ndi dziko ndi mzimu wake wokonda chuma, chikumachititsa maganizo awo kusumikidwa pa zinthu zakumwamba—“moyo weniweniwo.” (1 Timoteo 6:19)—10/1, tsamba 28.
◻ M’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, kodi ndi liti pamene Yesu adzakhala pa mpando wake wachifumu ndipo nchifukwa ninji? (Mateyu 25:31-33)
Fanizolo silimamusonyeza atakhala pa mpando m’lingaliro la kukhala Mfumu. M’malo mwake, iye akukhala pa mpando monga Woweruza. Kuweruzako si chinthu chochitika m’nyengo ya zaka zambiri. M’malo mwake, fanizolo likusonya kutsogolo pamene Yesu m’nthaŵi yoikika adzapereka chiweruzo ndi chilango pa mitundu.—10/15, masamba 22, 23.
◻ Kodi “mbadwo” wotchulidwa ndi Yesu kaŵirikaŵiri nchiyani?
Yesu anagwiritsira ntchito mawu akuti “mbadwo uwu” kwa makamu a anthu okhala ndi moyo panthaŵi imodzi ndi “atsogoleri [awo] akhungu” amene anapanga mtundu Wachiyuda. (Mateyu 11:16; 15:14; 24:34)—11/1, tsamba 14.
◻ Pakukwaniritsidwa komaliza kwa ulosi wa Yesu pa Mateyu 24:34-39, kodi mawu akuti “mbadwo uwu” amatanthauza chiyani?
Mwachionekere Yesu akutanthauza anthu apadziko lapansi amene amaona chizindikiro cha kukhalapo kwa Kristu koma nalephera kukonza njira zawo.—11/1, masamba 19, 31.
◻ Kodi ndi motani mmene makonzedwe a midzi yopulumukirako ndi ziletso zake zinapindulira anthu a mu Israyeli wakale?
Anasonyeza Aisrayeli kuti iwo sayenera kukhala osasamala kapena onyalanyaza moyo wa munthu. Anasonyezanso bwino lomwe kufunika kwa kusonyeza chifundo ngati kuteroko kuli koyenera. (Yakobo 2:13)—11/15, tsamba 14.
◻ Kodi mudzi wopulumukirako wophiphiritsira nchiyani?
Ndiwo makonzedwe a Mulungu otichinjiriza ku imfa chifukwa cha kuswa kwathu lamulo lake la kupatulika kwa mwazi. (Genesis 9:6)—11/15, tsamba 17.
◻ Kodi ndi motani mmene ubale Wachikristu ungatithandizire ‘kutenganso mphamvu’? (Yesaya 40:31)
Pakati pa abale ndi alongo athu Achikristu, pali ena amene akumana ndi zitsenderezo kapena mayeso amodzimodziwo ndi amene ali ndi malingaliro ofanana kwambiri ndi athu. (1 Petro 5:9) Nkotonthoza ndi kolimbitsa chikhulupiriro kudziŵa kuti zimene tikukumana nazo si zachilendo ndi kuti malingaliro athu saali achilendo.—12/1, masamba 15, 16.