Khalani Olama M’maganizo—Mapeto Ali Pafupi
“Mapeto a zinthu zonse asendera pafupi. Chifukwa chake, khalani olama m’maganizo, ndipo khalani maso kulinga kumapemphero.”—1 PETRO 4:7, NW.
1. (a) Kodi mtsogoleri wachipembedzo wina ndi otsatira ake anagwiritsidwa mwala motani? (b) Popeza kuti ziyembekezo zina sizinakwaniritsidwe, kodi ndimafunso otani amene angafunsidwe?
“NDINAITANIDWA ndi Mulungu mkati mwa pemphero langa lomalizira la usiku wa lero. Iye wandiuza kuti anthu 116,000 adzakwera kumwamba ndipo manda a akufa okhulupirira okwanira 3.7 miliyoni adzatseguka.” Anatero mtsogoleri wa Mishoni ya Coming Days usiku wotsatiridwa ndi October 28, 1992, tsiku lawo loloseredwa la chiweruzo. Komabe, pamene October 29 inafika, panalibe ngakhale munthu mmodzi amene anakwera kumwamba, ndipo panalibe manda a akufa amene anatseguka. Mmalo mokwatulidwira kumwamba, okhulupirira tsiku lachiweruzo a m’Korea amenewo anawona kuti tsikulo linangokhala tsiku wamba. Masiku achiweruzo afika ndi kupita, koma onenera za chiweruzowo samasintha konse. Kodi Akristu ayenera kuchitanji? Kodi ayenera kuleka kukhulupirira kuti mapeto akuyandikira mofulumira?
2. Kodi ndani anauza atumwiwo za tsiku lamtsogolo la chiweruzo, ndipo kodi iwo anaphunzira zimenezi ali m’mikhalidwe yotani?
2 Kuti tiyankhe, tiyeni tikumbukire chochitika pamene Yesu anali kukambirana m’tseri ndi ophunzira ake. Kumeneko, m’chigawo cha Kaisareya wa Filipi, kumpoto koma chakummaŵa kwa Nyanja ya Galileya, kumbuyo kwawo kukuwoneka phiri lokongola la Hermoni lalikululo, iwo anamumva akunena mosabisa kuti akaphedwa. (Mateyu 16:21) Panali kudzanso mawu ena otonthoza. Atawafotokozera kuti kukhala wophunzira wake kumatanthauza kukhala ndi moyo wodzimana mosalekeza, Yesu anachenjeza kuti: “Mwana wa munthu adzabwera muulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe awo.” (Mateyu 16:27) Yesu ananena za kubwera kwake kwa mtsogolo. Komabe, pachochitikachi, iye akakhala Woweruza. Panthaŵiyo chilichonse chikadalira pakuti kaya akapeza munthu akumtsatira mokhulupirika kapena ayi. Chiweruzo cha Yesu chikadalira pamkhalidwe wa munthu, zilibe kanthu kuti munthuyo ali ndi chuma cha kudziko chochuluka kapena chochepa motani. Ophunzira ake anayenera kukumbukira kwambiri mfundo imeneyi. (Mateyu 16:25, 26) Motero, ali Yesu Kristu iyemwiniyo amene akuuza otsatira ake kuyembekezera kufika kwake kwaulemerero, ndi chiweruzo chake.
3. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kutsimikizirika kwa kubwera kwake kwamtsogolo?
3 Zimene Yesu akunena kenako zimasonyeza kutsimikizirika kwa kubwera kwake kwamtsogolo. Motsimikiza mtima iye akuti: “Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalaŵa ndithu imfa, kufikira adzawona Mwana wa munthu atadza mu ufumu wake.” (Mateyu 16:28) Mawuŵa akukwaniritsidwa pambuyo pa masiku asanu ndi limodzi. Masomphenya oŵala a kusandulika kwa Yesu akuchititsa chidwi ophunzira ake okondedwawo. Iwo akuwonadi nkhope ya Yesu ikunyezimira ngati dzuŵa ndi malaya ake akuŵala. Kusandulikako kunali chithunzi cha ulemerero wa Kristu ndi Ufumu wake. Ha, nchitsimikiziro champhamvu chotani nanga cha maulosi a Ufumuwo! Nchisonkhezero chotani nanga kwa ophunzira ake chokhalira olama m’maganizo!—2 Petro 1:16-19.
Chifukwa Chake Kukhala Wolama m’Maganizo Kuli Kofunika Mwamsanga
4. Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kukhala maso mwauzimu ponena za kubwera kwake?
4 Chaka chisanathe, tikupeza Yesu atakhala pa Phiri la Azitona, akukambirananso m’tseri ndi ophunzira ake. Pamene iwo ayang’ana pamzinda wa Yerusalemu, iye alongosola chimene chidzakhala chizindikiro cha kukhalapo kwake kwamtsogolo nachenjeza kuti: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.” Otsatira ake ayenera kukhala maso mosalekeza chifukwa chakuti nthaŵi ya kufika kwake sidziŵika. Nthaŵi zonse ayenera kukhala oikonzekera.—Mateyu 24:42.
5. Kodi kufunika kwa kukhala maso kungachitiridwe fanizo motani?
5 Kabweredwe ka Ambuye, kadzafanana ndi ka mbala. Iye akupitiriza kuti: “Koma dziŵani ichi, kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe.” (Mateyu 24:43) Mbala simapereka chilengezo kudziŵitsa mwininyumba pamene ikafika; chida chake chachikulu ndicho kudzidzimutsa. Motero, mwininyumbayo ayenera kukhala maso nthaŵi zonse. Komabe, kwa Mkristu wokhulupirika, kukhala maso kosagona tulo sikumachititsidwa ndi kuwopa kudzidzimutsidwa kulikonse. Mmalomwake, kumasonkhezeredwa ndi chiyembekezo chachidwi cha kudza kwa Kristu muulemerero wake kudzayambitsa Zaka Chikwi za mtendere.
6. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala olama m’maganizo?
6 Mosasamala kanthu ndi kukhala maso konseko, palibe ndi mmodzi yemwe amene adzadziŵa pasadakhale tsiku lenileni la kufika kwake. Yesu akuti: “Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa m’nthaŵi imene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.” (Mateyu 24:44) Nchifukwa chake pali kufunika kwa kukhala olama m’maganizo. Ngati Mkristu akanalingalira kuti tsiku lakutilakuti, Kristu sakabwera, mwinamwake ndilo likakhala tsiku lenileni limene akafika! Ndithudi, pokhala ndi cholinga chabwino, Akristu okhulupirika kalelo anayesa mowona mtima kuneneratu pamene mapeto akafika. Komabe, chenjezo la Yesu latsimikiziridwa kukhala lowona panthaŵi zambiri: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.”—Mateyu 24:36.
7. Kuti tikhale otsatira a Kristu, kodi tiyenera kukhala ndi moyo wotani?
7 Motero, kodi tiyenera kutengapo lingaliro lotani? Lakuti, kuti tikhale otsatira a Kristu, tiyenera nthaŵi zonse kukhala okhulupirira kuti mapeto a dongosolo ili la zinthu ayandikira.
8. Kodi nchiyani chakhala chizindikiro cha Akristu chiyambire m’masiku oyambirira a Chikristu?
8 Mkhalidwe wa maganizo woterowo wakhala nthaŵi zonse chizindikiro cha Akristu, monga momwe olemba mbiri ndi asikolala a Baibulo amavomerezera. Mwachitsanzo, akonzi a The Translator’s New Testament, pa liwu lakuti “Tsiku” pampambo wawo womasulira mawu, amanena kuti: “Akristu a m’nthaŵi za NT[Chipangano Chatsopano] anakhala ndi moyo akumayembekezera Tsikulo (ndiko kuti nthaŵi) pamene dziko lilipoli limodzi ndi zoipa zake zonse likawonongedwa ndipo Yesu akabwerera padziko lapansi kudzaweruza anthu onse, akumayambitsa nyengo yatsopano ya mtendere ndi kuyamba Umbuye wake padziko lonse.” Buku la Encyclopædia Britannica limati: “Kukula kwapadera kwapadziko lonse kwa Chikristu kumasonyeza mwachindunji chiyembekezo cha Akristu cha nthaŵi yamapeto, mwanjira ya chiyembekezo choyandikiracho cha kubweranso kwa Kristu. Chiyembekezo cha Akristu cha nthaŵi ya mapeto sichinali chikhumbo wamba chofuna kudza kwa Ufumu wa Mulungu.”
Chimene Kukhala Wolama m’Maganizo Kumatanthauza
9. Ngakhale kuti zina za ziyembekezo za Petro za Mesiya zinali zosalondola, kodi nchifukwa ninji iye anakhalabe wachidaliro?
9 Patapita zaka pafupifupi 30 pambuyo pa makambitsirano achikondi amenewo amene Yesu anachita ndi ophunzira ake okondedwa kwambiri, Petro sanatope ndi kudikira kufika kwa mapeto. Ngakhale kuti ziyembekezo zake ndi za ophunzira anzake zoyambirira zonena za Mesiya zinali zosalondola, iye anakhalabe wachidaliro kuti chikondi cha Yehova ndi mphamvu yake zinatsimikiziritsa kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chawo. (Luka 19:11; 24:21; Machitidwe 1:6; 2 Petro 3:9, 10) Iye akutchula nsonga yomvedwa mosalekeza m’Malemba Achigiriki onse pamene akuti: “Mapeto a zinthu zonse asendera pafupi.” Ndiyeno akufulumiza Akristu anzake kuti: “Chifukwa chake, khalani olama m’maganizo, ndipo khalani maso kulinga kumapemphero.”—1 Petro 4:7.
10. (a) Kodi kukhala wolama m’maganizo kumatanthauzanji? (b) Kodi kuwona zinthu zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kumaloŵetsamonji?
10 Kukhala “olama m’maganizo” sikutanthauza kukhala wochenjera mwalingaliro lakudziko. Yehova amati: “Ndidzawononga nzeru za anzeru, ndi kuchenjera kwa ochenjera ndidzakutha.” (1 Akorinto 1:19) Liwulo limene Petro akugwiritsira ntchito lingatanthauze “kukhala wabata m’maganizo.” Bata lauzimu limeneli limachita ndi kulambira kwathu. Chifukwa chake, pokhala okhazikika m’maganizo, timawona zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova; timazindikira zinthu zofunika kwambiri ndi zosafunika. (Mateyu 6:33, 34) Poyang’anizana ndi mapeto oyandikirawo, sitimatengeka ndi moyo womwerekera; ndipo sitimakhala osasamala za nyengo imene tikukhalamo. (Yerekezerani ndi Mateyu 24:37-39.) Mmalomwake, timalamuliridwa ndi kudekha ndi uchikatikati wa malingaliro, maganizo, ndi mayendedwe, zosonyezedwa choyamba kwa Mulungu (‘kukhala maso kulinga kumapemphero’) ndiyeno kwa mnansi wathu (‘kukhala ndi chikodi chachikulu kwa wina ndi mnzake’).—1 Petro 4:7, 8, NW.
11. (a) Kodi “kupangidwa atsopano m’mphamvu yosonkhezera maganizo” athu kumatanthauzanji? (b) Kodi mphamvu yatsopano yamaganizo imatithandiza motani kupanga zosankha zabwino?
11 Kukhala wolama m’maganizo kumaloŵetsamo “kupangidwa [kwathu] atsopano m’mphamvu yosonkhezera maganizo” athu. (Aefeso 4:23, NW) Kodi nchifukwa ninji kupangidwa atsopano? Popeza kuti tili ndi choloŵa cha kupanda ungwiro ndipo tikukhala m’mikhalidwe yauchimo, maganizo athu akulamuliridwa ndi chikhoterero chotsutsa mkhalidwe wauzimu. Mphamvu imeneyo nthaŵi zonse imatsogolera malingaliro ndi mtima m’njira yokondetsa zinthu zakuthupi ndi yadyera. Motero, pamene munthu akhala Mkristu, amafunikira mphamvu yatsopano, kapena mkhalidwe wolamulira maganizo ake, umene udzatsogolera malingaliro ake kunjira yolungama, njira yauzimu, yakukhala wofuna kudzimana. Mwachitsanzo, pamene ayang’anizana ndi chosankha m’maphunziro, ntchito, zokondweretsa, maseŵera, mavalidwe, kapena chilichonse, chikhoterero chake choyamba chidzakhala kupenda nkhaniyo ndi lingaliro lauzimu mmalo mwa lakuthupi ladyera. Mkhalidwe wamaganizo watsopano umenewu umakupangitsa kukhala kosavuta kugamula nkhani ndi maganizo olama akuzindikira kuti mapeto ali pafupi.
12. Kodi ndimotani mmene tingakhalirebe “athanzi m’chikhulupiriro”?
12 Kukhala olama m’maganizo kumatanthauza kuti tili ndi thanzi labwino lauzimu. Kodi ndimotani mmene tingakhalire “athanzi m’chikhulupiriro”? (Tito 2:2, NW) Tiyenera kudyetsa maganizo athu ndi mtundu woyenera wa chakudya. (Yeremiya 3:15) Kudya mosalekeza Mawu a Mulungu a chowonadi kochilikizidwa ndi kugwira ntchito kwa mzimu woyera kudzatithandiza kusunga kukhazikika kwathu kwauzimu. Chifukwa chake, kukhazikika m’kuphunzira kwathu, limodzi ndi utumiki wakumunda, m’pemphero, ndi m’mayanjano Achikristu, nkofunika kwambiri.
Mmene Kulama m’Maganizo Kumatichinjirizira
13. Kodi kulama maganizo kumatichinjizira motani kuti tisachite zolakwa zopusa?
13 Kulama m’maganizo kungatichinjirize kuti tisachite cholakwa chopusa chimene chingatitayitse moyo wathu wosatha. Kodi zimenezi nzotheka motani? Mtumwi Paulo akulankhula za “lamulo la maganizo.” Kwa munthu wathanzi m’chikhulupiriro, lamulo la maganizo limenelo limalamuliridwa ndi chinthu chimene amakonda, ndicho “lamulo la Mulungu.” Zowona, “lamulo la uchimo” limalimbana ndi lamulo la maganizo. Komabe, Mkristu angakhale wolakika ndi chithandizo cha Yehova.—Aroma 7:21-25, NW.
14, 15. (a) Kodi ndimphamvu ziŵiri ziti zimene zimalimbirana kulamulira maganizo? (b) Kodi ndimotani mmene tingagonjetsere nkhondo ya maganizo?
14 Paulo akupitiriza mwakusonyeza kusiyana kwakukulu pakati pa maganizo olamuliridwa ndi thupi lauchimo, amene amasumika pamoyo wodzifunira maubwino adyera, ndi maganizo olamuliridwa ndi mzimu wa Mulungu, amene amasumika pa moyo wodzimana muutumiki wa Yehova. Paulo akulemba motere pa Aroma 8:5-7: “Iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere. Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja kuchilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.”
15 Ndiyeno m’ vesi 11, Paulo akufotokoza mmene maganizo amene amagwirizana ndi mzimu woyera amapambanira nkhondoyo kuti: ‘Koma ngati mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa ukhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa mzimu wake wakukhala mwa inu.’
16. Kodi kulama m’maganizo kumatitetezera ku zonyengerera zotani?
16 Chotero, mwakukhala olama m’maganizo, sitidzanyengedwa ndi zonyengerera zokhalapo nthaŵi zonse za dziko lino, lodzaza ndi kudzimwerekeretsa m’mitundu yonse yosaneneka ya zosangulutsa, zinthu zakuthupi, ndi makhalidwe achisembwere. Maganizo athu olama adzatiuza ‘kuthaŵa dama’ ndi kupeŵa zotulukapo zake zatsoka. (1 Akorinto 6:18) Mkhalidwe wathu wa maganizo olama udzatisonkhezera kuika zabwino za Ufumu patsogolo ndipo udzatetezera kulingalira kwathu pamene tiyesedwa ndi mwaŵi wa ntchito yakudziko imene ingafooketse unansi wathu ndi Yehova.
17. Kodi ndimotani mmene mlongo mpainiya anasonyezera kulama maganizo poyang’anizana ndi mathayo a zandalama?
17 Mwachitsanzo, m’dziko lotentha la ku Southeast Asia, pali mlongo wachichepere amene anaika zabwino za Ufumu patsogolo m’maganizo. Iye anali atakulitsa chikondi cha utumiki wanthaŵi yonse. M’dzikolo ntchito zambiri nzamasiku asanu ndi limodzi kapena ndi aŵiri akugwira ntchito tsiku lonse. Pamene anamaliza maphunziro payunivesite, atate wake, amene sanali Mboni ya Yehova, anamuyembekezera kupezera banja ndalama zambiri. Koma pakuti iye anali ndi chikhumbo champhamvu cha upainiya, anapeza ntchito ya theka la tsiku nayamba utumiki waupainiya. Zimenezi zinakwiyitsa atate wake, amene anawopseza kutayira katundu wake m’khwalala. Chifukwa cha kutchova juga, iwo anali ndi ngongole zambiri, ndipo anayembekezera mwana wawoyo kulipirira ngongole zawo. Mchimwene wake wamng’ono anali kuphunzira payunivesite, ndipo chifukwa cha ngongole, panalibe ndalama zolipirira maphunziro ake. Mchimwene wakeyo analonjeza kuti ngati mlongo wake akamthandiza, iye akasamalira banja akadzaloŵa ntchito. Mtima wa mlongoyo unagaŵanika paŵiri, kukonda mlongo wakeyo ndi kukonda utumiki waupainiya. Atapenda nkhaniyo mosamalitsa, anasankha kupitiriza upainiya ndi kufunafuna ntchito ina. Monga yankho la mapemphero ake, anapeza ntchito yabwino kumene anali wokhoza kuthandiza ndalama banja lonse ndi mlongo wakeyo limodzinso ndi kupitiriza ndi chikondi chake choyamba, utumiki waupainiya.
Funafunani Chithandizo cha Yehova Posunga Kulama Maganizo
18. (a) Kodi nchifukwa ninji anthu ena amamva kukhala olefuka? (b) Kodi ndimalemba ati amene angatonthoze awo amene amamva kukhala olefuka?
18 Otsatira a Kristu ena angakupeze kukhala kovuta kusunga kulama kwawo maganizo. Kuleza mtima kwawo kungakhale kukuzilala powona kuti dongosolo la zinthu lilipoli likupitirizabe kukhalapo kwanthaŵi yoposa imene anailingalira. Zimenezi zingawalefule. Komabe, mapeto adzafika. Yehova walonjeza zimenezo. (Tito 1:2) Ndipo adzateronso Paradaiso wa padziko lapansi. Yehova watsimikizira zimenezo. (Chivumbulutso 21:1-5) Pamene dziko latsopano lifika, padzakhala “mtengo wa moyo” kwa onse amene anasunga kulama m’maganizo kwawo.—Miyambo 13:12.
19. Kodi kulama maganizo kungasungidwe motani?
19 Kodi ndimotani mmene tingasungire kulama maganizo? Funafunani chithandizo cha Yehova. (Salmo 54:4) Yandikirani kwa iye. Timasangalala chotani nanga kuti Yehova amakhumba kuti tiyandikane naye! “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu,” amatero wophunzira Yakobo. (Yakobo 4:8) Paulo akuti: “Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani. Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi. Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:4-7) Ndipo pamene zothodwetsa za dongosolo la zinthu lomafali zikuwonekera kukhala zolemera mosakhoza kuzisenza, zitulireni Yehova, ndipo iye adzakuchilikizani.—Salmo 55:22.
20. Kodi tiyenera kupitiriza kuchitanji, malinga ndi 1 Timoteo 4:10?
20 Inde, mapeto ali pafupi, chotero khalanitu olama m’maganizo! Unali uphungu wabwino zaka 1,900 zapitazo; uli uphungu wofunikanso kwambiri lerolino. Tipitirizetu kugwiritsira ntchito mphamvu zathu zamaganizo olama kutamanda Yehova pamene akupitiriza kutitsogolera motetezereka kuloŵa m’dziko lake latsopano.—1 Timoteo 4:10.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi kulama m’maganizo nchiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji kukhala wolama m’maganizo kuli kofunika mwamsanga kwambiri?
◻ Kodi tingapangidwe atsopano motani m’mphamvu yosonkhezera maganizo athu?
◻ Kodi ndinkhondo yosalekeza yotani imene tiyenera kumenya m’maganizo athu?
◻ Kodi tingasunge motani kulama kwathu m’maganizo?
[Chithunzi patsamba 15]
Kuyandikira kwa Mulungu m’pemphero kumatithandiza kusunga kulama maganizo
[Chithunzi patsamba 17]
Pokhala olama m’maganizo, sitidzakopedwa ndi zonyengerera za dziko lino