Khalani Ogalamuka mu “Nthaŵi ya Mapeto”
‘Yang’anirani, [khalani ogalamuka, “NW”] . . . : pakuti simudzi ŵa nthaŵi yake.’—MARKO 13:33.
1. Kodi tiyenera kuchita motani pamene zochitika zochititsa chidwi zikufunyululuka mu “nthaŵi ya mapeto” ino?
PAMENE zochitika zochititsa chidwi zikufunyululuka mu “nthaŵi ya mapeto” ino, kodi Akristu ayenera kuchita motani? (Danieli 12:4, NW) Iwo sanasiidwe m’malere. Yesu Kristu anapereka ulosi wa chizindikiro chokhalamo zambiri umene wakhala ukukwaniritsidwa m’zaka za zana lino la 20. Ananeneratu mbali zambiri zimene zasonyeza nyengo ino chiyambire 1914 kukhala yapadera. Pokhala wozoloŵerana ndi ulosi wa Danieli wonena za “nthaŵi ya mapeto,” Yesu anamaliza ulosi wake waukulu mwakusonkhezera ophunzira ake ‘kukhala ogalamuka.’—Luka 21:36, NW.
2. Kodi nchifukwa ninji pali kufunika kwakukulu kwakukhala ogalamuka kuuzimu?
2 Kodi nkukhaliranji ogalamuka? Chifukwa chakuti ino ndiyo nthaŵi yovuta kopambana m’mbiri ya anthu. Kugonjera kukuwodzera kwauzimu panthaŵi ino kukakhala kwatsoka kwa Akristu. Ngati tikhala odzidalira kapena kulola mitima yathu kulemetsedwa ndi nkhaŵa za moyo, tidzakhala paupandu. Pa Luka 21:34, 35, Yesu Kristu anatichenjeza kuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi.”
3, 4. (a) Kodi Yesu anatanthauzanji mwakunena kuti tsiku la mkwiyo wa Mulungu lidzawagwera anthu modzidzimutsa “ngati msampha”? (b) Popeza kuti Mulungu sindiye amatchera msampha, kodi nchifukwa ninji tsikulo lidzafikira anthu onse modzidzimutsa?
3 Yesu anali ndi chifukwa chabwino pamene anati tsiku la Yehova ‘likatifikira modzidzimutsa ngati msampha.’ Msampha umakhala ndi khwekwe, ndipo umagwiritsiridwa ntchito kugwirira mbalame ndi zinyama. Msampha umakhala ndi chilimba, ndipo aliyense amene aloŵa mumsamphawo amafwamphula chilimbacho. Ndiyeno msamphawo umatsekeka, nugwira mkoleyo. Zonsezi zimachitika modzidzimutsa kwambiri. Mofananamo, Yesu anati, ofooka kuuzimu adzadzidzimuka ndi kuwonongedwa pa “tsiku la mkwiyo” la Mulungu.—Miyambo 11:4.
4 Kodi Yehova Mulungu ndiye amatchera anthu msampha? Ayi, samadikirira kugwira anthu modzidzimutsa ndi kuwawononga. Koma tsikulo lidzafikira anthu onse modzidzimutsa chifukwa chakuti iwo sakulingalira mwamphamvu Ufumu wa Mulungu. Amatsatira njira yawo ya zolondola za moyo, akumanyalanyaza tanthauzo la zochitika zowazinga. Komabe, zimenezi sizimasintha programu ya Mulungu. Iye ali ndi nthaŵi yake yoikidwiratu yothetsera mlandu. Ndipo, mwachifundo, samasiya anthu muumbuli wa kusadziŵa chiweruzo chake chirinkudza.—Marko 13:10.
5, 6. (a) Chifukwa cha chiweruzo chirinkudza, kodi ndikakonzedwe kachikondi kotani kamene Mlengi wapangira zolengedwa zaumunthu, koma kodi anthu ambiri akulabadira motani? (b) Kodi nziti zomwe tidzakambitsirana zotithandiza kukhala ogalamuka?
5 Chenjezo lapasadakhale limeneli liri kakonzedwe kachikondi ka Mlengi wamkulu, yemwe amafuna kuti zolengedwa zake zaumunthu zikhale ndi moyo wabwino pano pachoikapo mapazi ake chophiphiritsira. (Yesaya 66:1) Amakonda nzika za malo amene akunenedwa kukhala wapondapo mapazi ake. Chotero kupyolera mwa oimira ake apadziko lapansi ndi nthumwi, amazichenjeza za zochitika zomwe zili kutsogolo. (2 Akorinto 5:20) Komabe, mosasamala kanthu ndi chenjezo loperekedwa, zochitika zimenezo zidzafikira banja laumunthu modzidzimutsa ngati kuti ilo laloŵa mumsampha. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anthu ochuluka ali mtulo tauzimu. (1 Atesalonika 5:6) Kokha anthu ochepa ndamene alabadira chenjezolo ndipo ndiwo adzapulumuka kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu.—Mateyu 7:13, 14.
6 Pamenepa, kodi ndimotani mmene ife tingakhalire ogalamuka m’nthaŵi ino ya mapeto kuti tiŵerengeredwe pakati pa anthu amene adzapulumutsidwa? Yehova amapereka chithandizo chofunika. Tiyeni tikambitsirane zinthu zisanu ndi ziŵiri zimene tingachite.
Limbanani ndi Zocheukitsa
7. Kodi ndichenjezo lotani lonena za zocheukitsa limene Yesu anapereka?
7 Choyamba, tiyenera kulimbana ndi zocheukitsa. Pa Mateyu 24:42, 44, Yesu anati: ‘Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu. Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthaŵi m’mene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.’ Kanenedwe ka Yesu panopa kamasonyeza kuti panthaŵi ino yovuta, pakakhala zocheukitsa zambiri, ndipo zocheukitsa zimatsogolera ku chiwonongeko. M’tsiku la Nowa zinthu zambiri zinatanganitsa anthu. Chotero, anthu ocheukitsidwawo ‘sanadziŵa’ za zimene zinali kuchitika, ndipo Chigumula chinawapululutsa onse. Mofananamo, Yesu anachenjeza nati: ‘Kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.’—Mateyu 24:37-39.
8, 9. (a) Kodi ndimotani mmene zolondola zozoloŵereka za moyo zingaticheukitsire mwaupandu? (b) Kodi ndimachenjezo otani amene Paulo ndi Yesu anatipatsa?
8 Ndiponso, kumbukirani kuti m’chenjezo lake pa Luka 21:34, 35, Yesu anali kufotokoza mbali za moyo zozoloŵereka, monga ngati kudya, kumwa, ndi kudera nkhaŵa kupeza zokhalira moyo. Zinthuzi nzodziŵika kwa anthu onse, kuphatikizapo ophunzira a Ambuye Yesu. (Yerekezerani ndi Marko 6:31.) Zinthu zimenezi zingakhale zopanda upandu mwa izo zokha, komabe ngati zaloledwa, zingaticheukitsedi, kutitanganitsa, ndipo motero kuloŵetsa kuwodzera kwauzimu kwaupandu mwa ife.
9 Motero, tisanyalanyaze konse chinthu chofunika koposa—kupeza chivomerezo cha Mulungu. Mmalo momwerekera ndi kulondola zinthu zozoloŵereka za moyo, tiyeni tizigwiritsire ntchito kokha kumlingo wochepa wofunika kutichirikiza. (Afilipi 3:8) Siziyenera kuphimba zabwino Zaufumu. Monga momwe Aroma 14:17 amanenera, ‘ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa mzimu woyera.’ Kumbukirani mawu a Yesu pamene anati: ‘Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.’ (Mateyu 6:33) Ndiponso, pa Luka 9:62, Yesu analengeza kuti: ‘Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang’ana za kumbuyo, ayenera ufumu wa Mulungu.’
10. Kodi pamakhala upandu wotani ngati sitisumikabe maso athu kutsogolo kuchonulirapo?
10 Pamene tayamba kulima, titero kunena kwake, tiyenera kukhala mumzera wowongoka. Munthu wolima amene amayang’ana kumbuyo sadzalima mzera wowongoka. Amacheukitsidwa ndipo angapatutsidwe mosavuta kapena kuimitsidwa mwa kuloŵa m’chopinga chinachake. Tisakhale monga mkazi wa Loti, amene anayang’ana kumbuyo ndipo analephera kupulumuka. Tifunikira kusumikabe maso athu kutsogolo kuchonulirapo. Kuti tichite zimenezo tiyenera kulimbana ndi zocheukitsa.—Genesis 19:17, 26; Luka 17:32.
Pempherani ndi Khama Lonse
11. Kodi nchiyani chimene Yesu anagogomezera atatichenjeza za upandu wa kucheutsidwa?
11 Komabe, pali zina zowonjezereka zimene tingachite kuti tikhale ogalamuka. Chinthu chachiŵiri chofunika ndicho: Kupemphera ndi khama lonse. Atatichenjeza za upandu wakukhala ocheukitsidwa ndi zolondola zozoloŵereka za moyo, Yesu anapereka uphungu uwu: ‘Dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.’—Luka 21:36.
12. Kodi ndipemphero lotani limene lifunika, ndipo nchiyani chimakhala chotulukapo?
12 Motero, tiyenera kupembedzera mosalekeza za kuwopsa kwa mkhalidwe wathu ndi kufunikira kwathu kukhala amaso. Tiyeni timfikire Mulungu mwapemphero ndi kuchonderera kwakhama. Pa Aroma 12:12, Paulo anati: ‘Limbikani chilimbikire m’kupemphera.’ Ndipo pa Aefeso 6:18, timaŵerenga kuti: ‘Mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthaŵi yonse mwa mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere.’ Iyi siiri nkhani chabe ya kupereka pemphero monga ngati kuti inali nkhani wamba yosanunkha kanthu. Kukhalapo kwathu kwenikweniko kuli paupandu. Nchifukwa chake tifunikira kupempha chithandizo cha Mulungu ndi khama lonse. (Yerekezerani ndi Ahebri 5:7.) Mwanjira imeneyo tidzakhalabe kumbali ya Yehova. Palibe chirichonse chimene chidzatithandiza kwambiri kuchita zimenezi koposa ‘kudikira nyengo zonse, ndi kupemphera.’ Pamenepo Yehova adzatisunga mumkhalidwe wa kukhala maso. Pamenepo, nkofunika chotani nanga kulimbikira kupemphera!
Mamatirani ku Gulu la Yehova ndi Ntchito Zake
13. Kodi tifunikira kugwirizana ndi ayani kuti tikhalebe ogalamuka?
13 Timafuna kupulumuka zinthu zonsezi zimene zidzadzera dzikoli. Timafuna kuima pamaso pa Mwana wa munthu, tiri ndi chivomerezo chake. Chifukwa chake pali chinthu chachitatu chimene tingachite: Kumamatira zolimba ku gulu la Yehova lateokratiki. Tifunikira kugwirizana kotheratu ndi gulu limenelo ndi kuchita ntchito zake. Mwanjira imeneyi tidzadzisonyeza mosakaikiridwa monga Akristu ogalamuka.
14, 15. (a) Kodi ndikuchita ntchito yotani kumene kudzatithandiza kukhala ogalamuka? (b) Kodi ndani anganene pamene ntchitoyo idzatha, ndipo kodi ife tiyenera kuiwona motani ntchitoyo? (c) Chisautso chachikulu chitapita, kodi nchiyani chomwe tidzazindikira titayang’ana m’mbuyo kupenda ulaliki wa Ufumu umene tinauchita?
14 Chogwirizana kwambiri ndi zimenezo ndichinthu chachinayi chimene chingatithandize kukhala ogalamuka. Tiyenera kukhala pakati pa amene akuchenjeza anthu za kudza kwa mapeto a dongosolo lino la zinthu. Mapeto otheratu a dongosolo lino la zinthu lakale sadzachitika kufikira “uthenga uwu wabwino wa ufumu” utalalikidwa kumlingo umene Mulungu Wamphamvuyonse walinganiza. (Mateyu 24:14) Mboni za Yehova sindizo zimene ziyenera kusankha pamene ntchito ya kulalikira idzathera. Yehova yekha ndiye ali ndi mphamvu yakutero. (Marko 13:32, 33) Ngakhale nditero, ndife otsimikiza mtima kugwira ntchito zolimba monga momwe tingathere malinga ngati kulalikira za Ufumu wa Mulungu, boma labwino koposa limene anthu angakhale nalo, kudakali kofunika. Kuulika kwa ‘chisautso chachikulu’ kudzachitika pamene tidakali kuchita ntchito imeneyi. (Mateyu 24:21) M’nthaŵi yonse ya mtsogolo, opulumuka adzayang’ana kumbuyo ndi kuvomereza kuti Yesu Kristu sanali mneneri wonyenga. (Chivumbulutso 19:11) Ntchito ya kulalikira idzakhala itachitidwa kumlingo waukulu woposa zimene otengamo mbali m’ntchitoyo adayembekezera.
15 Moyenerera, panthaŵi yosaiŵalika pamene ntchitoyo idzakhala itamalizidwa mokhutiritsa Mulungu mwiniyo, anthu ambiri adzakhala atatengamo mbali koposa nyengo ina iriyonse yapita. Tidzakhala oyamikira chotani nanga kuti tinakhalamo ndi phande m’ntchito yaikulu imeneyi! Mtumwi Petro akutitsimikizira kuti Yehova ‘safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’ (2 Petro 3:9) Chifukwa chake, mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu Wamphamvuyonse ikugwira ntchito kwambiri lerolino kuposa ndi kalelonse, ndipo Mboni za Yehova zikukhumba kupitirizabe muntchito yosonkhezeredwa ndi mzimu imeneyi. Chotero mamatirani zolimba ku gulu la Yehova, ndipo khalani otanganitsidwa muuminisitala wake wapoyera. Zimenezi zidzakuthandizani kukhala ogalamuka.
Dzipendeni Nokha
16. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupenda mkhalidwe wathu wauzimu watsopano lino?
16 Pali chinthu chachisanu chimene tingachite kotero kuti tikhale ogalamuka. Aliyense payekha, ayenera kupenda mkhalidwe wake watsopano lino. Zimenezi nzoyenerera tsopano koposa ndi kalelonse. Tifunikira kupereka umboni wosonyeza mbali imene tikuimako motsimikiza. Pa Agalatiya 6:4, Paulo anati: ‘Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha.’ Dzipendeni mogwirizana ndi mawu a Paulo pa 1 Atesalonika 5:6-8: ‘Chifukwa chake tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere. Pakuti iwo akugona agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku. Koma ife popeza tiri a usana tisaledzere, titavala chapachifuŵa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chiri chiyembekezo cha chipulumutso.’
17. Pamene tikudzipenda, kodi tiyenera kudzifunsa mafunso otani?
17 Bwanji za ife? Pamene tidzipenda tokha mogwirizana ndi Malemba, kodi timadziwona kukhalabe ogalamuka, tikumapanga chiyembekezo cha chipulumutso monga chisoti? Kodi ndife anthu amene tadzilekanitsa motsimikizirika kudongosolo lakale la zinthu ndi kusachirikizanso malingaliro ake? Kodi tiridi ndi mzimu wa dziko latsopano la Mulungu? Kodi ndife amaso ponena za kumene dongosolo lino likupita? Ngati tiridi tero, tsiku la Yehova silidzatidzidzimutsa ngati mbala.—1 Atesalonika 5:4.
18. Kodi ndimafunso enanso ati amene tiyenera kudzifunsa, ndipo nchiyani chidzatulukapo?
18 Komabe, bwanji ngati kudzipenda kwathu kuvumbula kuti tikukalimira kukhazikitsa njira ya moyo wabwino, wosavuta, wosangalatsa, ndi womasuka? Bwanji ngati tapeza kuti maso athu auzimu akhala olema ndi kuwodzera ndi tulo? Kodi tiri mumkhalidwe wonga wamaloto, tikumalondola maloto akudziko? Ngati zimenezi ziri choncho, tiyeni tigalamuke!—1 Akorinto 15:34.
Sinkhasinkhani pa Maulosi Okwaniritsidwa
19. Kodi ndimaulosi ati amene tawona kukwaniritsidwa kwake?
19 Tsopano tafika pa chinthu chachisanu ndi chimodzi chimene chidzatithandiza kukhala ogalamuka: Kusinkhasinkha pa maulosi ambiri omwe akwaniritsidwa m’nthaŵi ino ya mapeto. Tapyola kale chaka cha 77 kuyambira pamene nthaŵi zoikidwiratu za amitundu zinatha mu 1914. Pamene tiyang’ana m’mbuyo zaka zoposa makumi asanu ndi aŵiri mphambu zisanu, timawona mmene ulosi umodzi wotsatizana ndi unzake wakwaniritsidwira—kubwezeretsedwa kwa kulambira kowona; kulanditsidwa kwa otsalira odzozedwa, pamodzi ndi atsamwali awo, kuloŵa m’paradaiso wauzimu; kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu padziko lonse; ndi kuwonekera kwa khamu lalikulu. (Yesaya 2:2, 3; mutu 35; Zekariya 8:23; Mateyu 24:14; Chivumbulutso 7:9) Pakhala kulemekezedwa kwa dzina lalikulu la Yehova ndi ulamuliro wa m’chilengedwe chonse, limodzinso ndi kuwonjezereka kwa wamng’ono kukhala chikwi ndi wochepa kukhala mtundu wamphamvu, Yehova akumafulumizitsa zimenezi m’nthaŵi yake. (Yesaya 60:22; Ezekieli 38:23) Ndipo masomphenya a mtumwi Yohane olembedwa m’Chivumbulutso tsopano akufika pachimake.
20. Kodi Mboni za Yehova ziri ndi chikhutiro chotani, ndipo kodi zatsimikizira kukhala chiyani?
20 Chifukwa chake, koposa ndi kalelonse, Mboni za Yehova ziri zokhutiritsidwa kwambiri ndi kulondola kwa kuzindikira kwawo tanthauzo la zochitika za dziko chiyambire 1914. Pokhala ndi chikhutiro chotero, zatsimikizira kukhala zipangizo zogwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu Wam’mwambamwamba. Ndizo zimene zapatsidwa thayo lakulengeza uthenga wa Mulungu panthaŵi ino yosaiŵalika. (Aroma 10:15, 18) Inde, mawu a Yehova onena za nthaŵi ya mapeto akhaladi owona. (Yesaya 55:11) Chifukwa chake, zimenezi ziyenera kutisonkhezera kuchirimika kufikira tiwona kukwaniritsidwa kotsirizira kwa malonjezo onse a Mulungu operekedwa ndi Yesu Kristu.
Chipulumutso Chiri Pafupi Koposa Pamene Tinakhala Okhulupirira
21. Kodi tiri ndi chithandizo chachisanu ndi chiŵiri chotani cha kukhalabe ogalamuka kuuzimu?
21 Potsirizira, nachi chithandizo chachisanu ndi chiŵiri cha kukhalabe ogalamuka: Nthaŵi zonse kumbukirani kuti chipulumutso chathu chiri pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira. Chofunika koposa nchakuti, kulemekezedwa kwa ulamuliro wa chilengedwe chonse wa Yehova ndi kuyeretsedwa kwa dzina lake ziri pafupi kwambiri. Choncho kufunika kwa kukhala ogalamuka nkofulumira koposa ndi kalelonse. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Chitani ichi, podziŵa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthaŵi yabwino ya kuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chiri pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupira. Usiku wapita, ndi dzuŵa layandikira.’—Aroma 13:11, 12.
22. Kodi tiyenera kuyambukiridwa motani ndi kuyandikira kwa chipulumutso chathu?
22 Popeza kuti chipulumutso chathu chiri pafupi kwambiri chotero, tifunikira kukhalabe ogalamuka! Sitiyenera kulola zikondwerero zaumwini kapena zakudziko zirizonse kutsamwitsa chiyamikiro chathu cha zimene Yehova akuchitira anthu ake m’nthaŵi ino ya mapeto. (Danieli 12:3) Tifunikira kusonyeza khama lalikulu koposa ndi kalelonse kotero kuti tisapatutsidwe panjira imene Mawu a Mulungu amatisonyeza momvekera bwino. (Mateyu 13:22) Umboni umasonyeza bwino lomwe kuti dziko lino liri m’masiku ake otsiriza. Posachedwapa lidzachotsedwapo kotheratu ndi kuloŵedwa mmalo ndi dziko latsopano lolungama.—2 Petro 3:13.
23. Kodi Yehova adzatithandiza mwanjira yotani, ndipo kudzadzetsa madalitso otani?
23 Pamenepo, zivute zitani, tiyeni tikhale ogalamuka. Koposa ndi kalelonse, khalani amaso kuzindikira nthaŵi imene tirimo. Kumbukirani, Yehova sadzagona tulo m’zimenezi. Mmalomwake, adzatithandiza nthaŵi zonse kukhala amaso m’nthaŵi ino ya mapeto. Usiku wapita. Dzuŵa layandikira. Chotero galamukani! Posachedwapa tidzawona tsiku lokongola koposa masiku onse, pamene Ufumu Waumesiya udzakwaniritsa chifuno cha Yehova kaamba ka dziko lapansi!—Chivumbulutso 21:4, 5.
Kodi Mayankho Anu Ngotani?
◻ Kodi Yesu anatanthauzanji pamene ananena kuti tsiku la mkwiyo wa Mulungu likawagwera anthu “ngati msampha”?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulimbana ndi zocheukitsa, ndipo tingachite motani zimenezo?
◻ Kodi ndipemphero lotani lomwe lifunikira kuti tikhalebe ogalamuka?
◻ Kodi ndikugwirizana ndi ayani kumene kuli kofunika?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupenda mkhalidwe wathu wauzimu?
◻ Kodi ulosi umatithandiza motani m’kukhala kwathu ogalamuka?