Chaputala 5
Kuunika Kaamba ka “Mapeto a Dongosolo la Zinthu”
1. Kodi ndi ukwati waukulu wotani wa ‘m’mapeto a dongosolo lino la zinthu,’ umene “Kalonga wa Mtendere” ananeneratu, ndipo m’fanizo lotani?
PONENA za “mapeto a dongosolo la zinthu,” “Kalonga wa Mtendere” ananena pa Mateyu 24:38 kuti “pakakhala kukwatira ndi kukwatiŵa.” Koma mkati mwa nyengo imodzimodziyo, kumwamba kukayambika ukwati waukulu koposa onse. Ndiwo ukwati wotchulidwa m’fanizo la Yesu la onyamula nyali khumi, anamwali khumi.—Mateyu 24:3; 25:1-12.
2. (a) Kodi ukwati wa m’fanizo umenewu ukuchitika panthaŵi iti ya tsiku? (b) Kodi nchiyani chimene chimatsatira ukwatiwo, ndipo kodi kuunika kumaperekedwa motani?
2 Ukwati umenewu ukuchitikira ku Middle East. Ukuchitika usiku kwambiri, pafupi ndi pakati pausiku. Choyamba pakhala ukwati wa mkwati ndi mkwatibwi ndipo pambuyo pake pali dzoma lomka kunyumba yamadyerero. Njirayo njosaunikiridwa ndi magetsi a m’khwalala. Kuunika kukuchokera kwa okhala m’dzoma la ukwatiwo, ndipo openyerera angathe kuwona ukwatiwo ukupita, akumafunira okwatirana chatsopanowo chimwemwe.
3, 4. (a) Kodi ndani amene ali ndi chikondwerero mwa akudza akutsatirawo, ndipo anachita makonzedwe otani? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwa fanizo limeneli kumawonjezera umboni wa chowonadi chotani? (c) Kodi tingakhale achimwemwe ngati tichita chiyani?
3 Chifukwa cha chikhoterero chawo chachibadwa chaukazi, anamwali amakondwera ndi ukwati. Motero, anamwali khumi akuyembekezera pambali pa njira kufikira ukwatiwo ufika pamene iwo ali. Ali ndi chikhumbo cha kuunikira chochitika chimenechi ndipo chifukwa cha zimenezo iwo onse akufika atanyamula nyali zoyaka, koma ali asanu okha amene ali ndi mafuta ounikira ngati pali kufunika kofulumira. Asanu ameneŵa ndiwo anamwali ochenjera. Tiyenera kukondwera ndi kukwaniritsidwa kwa fanizo limeneli lerolino, chifukwa chakuti mogwirizana ndi kunena kwa Yesu Kristu, kumatsimikizira mowonjezereka kuti tiri kumapeto kwa dongosolo lakale la zinthu.—Mateyu 25:13.
4 Tingakondwere ngati tiri anzeru ndipo tiwona kukwaniritsidwa kwa ukwati umenewu woposa maukwati onse limodzi ndi ophatikizidwamo! Kodi ndani lerolino amene ali oyanjidwa mwa kuloŵetsedwa m’phwandoli? Kodi alipo mwa ife? Tiyeni tiwone!
5. Kodi nchiyani chimene chinapanga kusiyana pakati pa anamwali khumi, ndipo kodi kunachitikanji mkwati atachedwa?
5 Fanizo limene Yesu anapereka la anamwali khumi limaphatikizapo “ufumu wakumwamba,” boma la dziko lodalitsira anthu onse. Motero Yesu Kristu anapitirizabe kunena kuti: “Ufumu wakumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zawo, natuluka kukakomana ndi mkwati. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. Pakuti opusawo, mmene anatenga nyali zawo, sanadzitengeranso mafuta; koma anzeruwo anatenga mafuta m’nsupa zawo, pamodzi ndi nyali zawo. Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anawodzera, nagona tulo.”—Mateyu 25:1-5.
6. (a) Kodi anamwali khumi anaphiphiritsira yani? (b) Kodi nchifukwa ninji mkwatibwi sakutchulidwa m’fanizo?
6 Chotero kodi anamwali khumi anaphiphiritsira ayani? Iwo anaphiphiritsira mamembala oyembekezeredwa a mkwatibwi wa Mkwati wauzimu, Yesu Kristu. Mosakaikira kaamba ka chifukwa chimenechi mkwatibwi sakutchulidwa dzina m’fanizo la Yesu; mkwati yekha akuwonekera. Motero, palibe chisokonezo ponena za kutanthauzira, monga ngati kuti anamwaliwo anaphiphiritsira kagulu kenanso.
7. Kodi ndimkati mwa nyengo yotani mmene kunawonekera kuti Mkwati anachedwetsa ulendo wake wodzatenga mkwatibwi, ndipo chifukwa ninji?
7 Kugwirizanitsidwa kwa mamembala amtsogolo a kagulu ka mkwatibwi kwa Mkwati wawo wakumwamba mu ukwati sikunachitike, monga momwe kudayembekezeredwa, pamapeto a “nthaŵi zoikidwiratu za amitundu,” mu 1914. (Luka 21:24) Mwachiwonekere, kwa iwo kunawonekera ngati kuti Mkwati anachedwa m’kudza kwake, ngakhale kuti kukhala pafupi kwake mu Ufumu wake wakumwamba kunachitika mu 1914. Zaka zomvetsa chisoni zimenezo za Nkhondo Yadziko I zinatsimikizira kukhala usiku wa mdima wa ndiwe yani m’zochitika za kagulu ka anamwali.
8. (a) Mophiphiritsira, kodi ndimotani kuti kuwodzera ndi kugona kwa anamwali kunachitika? (b) Kodi Mkwati anadza ku kachisi kaamba ka chifuno chotani, ndipo chifukwa ninji kumeneku kunayambukira kagulu ka mkwatibwi?
8 M’kulankhula kophiphiritsira, anamwali anawodzera ndi kugona. Kulalikidwa kwapoyera kwa mbiri yabwino ya ulamuliro ulinkudza wa Kristu wa zaka chikwi kaamba ka kudalitsira anthu onse kwakukulukulu kunalekeka. Kuyambira m’chaka chomalizira cha Nkhondo Yadziko I, nyengo yowopsa ya chiweruzo inayamba kwa anamwali ophiphiritsira amenewo. Zimenezi zinali chifukwa chakuti Mfumu yolamulira Yesu Kristu anali itadza ku kachisi wauzimu. Atafika kumeneko, inayamba makonzedwe a chiweruzo kuti iyeretse oikidwa kupereka utumiki pa kachisi wa Yehova Mulungu. (Malaki 3:1-3) Imeneyi inali nthaŵi ya kuvumbulutsidwa kwake pamene, monga Mkwati wakumwamba, nthaŵi inafika yakuti ilandire mamembala ovomerezedwa a kagulu ka mkwatibwi amene panthaŵiyo anali atafa kale.
9. Kodi ndiliti pamene inali nthaŵi ya kugalamutsidwira kuntchito ya kagulu ka anamwali, ndipo chifukwa ninji?
9 Mu 1919, pambuyo pa kumasulidwa kwa mamembala odziŵika asanu ndi atatu a Watch Tower Bible and Tract Society ku kuikidwa m’ndende mosalungama, inali nthaŵi yokwanira yakuti kagulu ka anamwali kokhalabe ndi moyo padziko lapansi kadzutsidwe kutulo tawo ta kusachita ntchito. Ntchito yopereka kuunika padziko lonse lapansi inali mtsogolo. Inali nthaŵi yawo, okhala ndi nyali zounikiridwa, kukomana ndi Mkwati, amene anali atadza ku kachisi wauzimu. Zimenezi zinali choncho kotero kuti anthu ambiri amitundu yonse afike ku “nyumba ya Yehova” imene inali itakwezedwa pamwamba pa mapiri, kunena kwake titero.—Yesaya 2:1-4.
Kukonza Nyali Zawo
10. Kodi mafuta amene anatengedwa kuchokera m’nsupa za anamwali ochenjera anaphiphiritsira chiyani?
10 Ochenjera a kagulu ka anamwali anali atadza ndi nsupa zamafuta ounikira m’nthaŵi yofunika. Iwo sanazengeleze m’kudzadza nyali zawo. Mafuta onga madzi ounikira anaphiphiritsira Mawu opereka chidziŵitso a Yehova ndi mzimu wake woyera. Motero, kodi mafuta amene anachotsedwa m’nsupa ndi anamwali ochenjera anaphiphiritsira chiyani? Mzimu wa Yehova umene unatsala umene umaunikira Mawu ake olembedwa ndi umene otsalira odzozedwa a ophunzira obadwa ndi mzimu a Mkwati anali nawo mwa iwo eni pamene ntchito ya pambuyo pa nkhondo ya padziko lonse lapansi ya kuunikira ponena za Ufumu wakumwamba inaikidwiratu kuyamba.
11. Kodi nchiyani chimene chinali nsupa zophiphiritsira zimene zinali ndi mafuta?
11 Zotengera zinaphiphiritsira anamwali ochenjera enieniwo monga okhala ndi mafuta ounikira ophiphiritsira. Zimenezi sizimatanthauza kuti kagulu ka anamwali kanayamba kudzozedwa panthaŵiyo ndi mzimu wa Yehova. Ayi, anamwali samadzidzoza okha ndi mzimu wake. Kamadzozedwa ndi Iye!—Yesaya 61:1, 2; Luka 4:16-21.
12. (a) Kodi ndiulosi wotani wa Yoweli umene unali pafupi kukwaniritsidwa pa anamwali ochenjera? (b) Kodi ndiliti pamene nthaŵi inafika yakuti iwo alole kuunika kuŵale kudzera mwa nyali zawo?
12 Kuchirikiza kugaŵiridwa kwawo ntchito yaikulu ya kuunikira dziko ponena za “Ufumu wakumwamba,” anamwali ochenjera analandira chiyanjo cha kukwaniritsidwa kwa Yoweli 2:28, 29 pa iwo. Nayi njira imene mtumwi Petro akugwira nayo mawu mavesi amenewo: “Ndipo kudzali m’masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha mzimu wanga pathupi lirilonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzawona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto.” (Machitidwe 2:17) Chotero kuyambira 1919 kumkabe mtsogolo ochenjera a kagulu ka anamwali ophiphiritsirawo anali kudzatenga zounikira zawo, nyali zawo zophiphiritsira—iwo eni. Iwo anachita zimenezi kotero kuti agaŵire kuunika kwa onse amene anali chikhalirebe m’mdima wauzimu. Chifukwa cha mtundu wa miyoyo imene amakhala ndipo mosonkhezeredwa ndi Mawu a Mulungu ndi mzimu, iwo amakhala ‘miuni m’dziko.’ (Afilipi 2:15) Motero iwo anayamba kutsatira mapazi a Mkwati amene anachita makonzedwe a kutengera mamembala onse a kagulu ka mkwatibwi kwa iye mwini mu Ufumu wakumwamba pambuyo pa imfa yawo padziko lapansi.—Mateyu 5:14-16.
Zotulukapo za Kupusa Kwauzimu
13. Kodi ndimotani mmene anamwali ochenjera anayankhira pempho la anamwali opusa?
13 Tsopano, bwanji, za kagulu ka anamwali opusa? Yesu akupitirizabe kunena kuti: “Opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zirinkuzima. Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.”—Mateyu 25:8, 9.
14. Kodi nchifukwa ninji anamwali amene anakana kugaŵana mafuta awo anali ochenjera ndipo osati adyera?
14 Okana kugaŵana ndi opusawo sanali adyera, anali ochenjera. Iwo anali kuumirira ku kukwaniritsidwa kwa chifuno chawo choyambirira, chabwino, cha kuunikira malo ozungulira amdima mmalo mwa Mkwati. Iwo mwanjira iriyonse sanali okakamizika kugonjera, kuchepetsa mlingo wawo wa mzimu woyera wa Yehova kuti athandize amene anali opusa mwauzimu. Opusa amenewo sanadzikonzekeretse kuloŵa mofulumira m’mwaŵi wautumiki wowatsegukira mu 1919.
15. (a) Pamene nyengo ya mtendere inatseguka, kodi ndani pakati pa kagulu ka anamwali amene anayamba kusonyeza zikhoterero za kupusa kwauzimu? (b) Kodi nchifukwa ninji anamwali ochenjera anali osakhoza kuthandiza anamwali opusa mwauzimu?
15 Pamene nyengo ya mtendere inali kuyamba, ena a odzinenera kukhala atsamwali odzipatulira, obatizidwa anayamba kusonyeza kupusa kwauzimu. Pambuyo pa imfa ya prezidenti woyamba wa Watch Tower Society, Charles Taze Russell, iwo sanasonkhezeredwe mokwanira ndi kupita patsogolo kwauzimu kwa chipangizo chowoneka ndi maso cha Yehova Mulungu motsogozedwa ndi prezidenti wake watsopano, J. F. Rutherford. Kwenikweni mitima yawo siinali yogwirizana ndi njira imene zinthu zinali kuchitidwira. Iwo anasonyeza kupanda chiyamikiro ndi njira imene Yehova anali kuchitira ndi anthu ake. Motero, awo amene anali ofanana ndi anamwali ochenjera sakanakhoza kuloŵetsa mkhalidwe weniweni wa kupereka chichirikizo chochokera mu mtima kwa opusa ameneŵa amene anali kudzilekanitsa mowonjezerekawonjezereka.
16. Kodi kupusa kwauzimu kwa anamwali opusa kunawonekera motani?
16 Motero kupusa kwauzimu kunawonekera poyera. Motani? Mwa kulephera kukhala ndi mafuta ophiphiritsira panthaŵi zovutitsa pamene kuunika kwauzimu kunali kufunika kwakukulu pamene kupita patsogolo kwatsopano kunali kuchitika, kusonyeza kukhalako kwa Mkwati. Mwanjira yophiphiritsira inali nthaŵi yakuti munthuyo atuluke kukakomana naye ndi nyali yake itaunikidwa moŵala. Koma mmalo mwake, ofanana ndi anamwali opusa amenewo, amene nyali zawo zinali kuzima, anadzilekanitsa ndi ochenjera.
17. Kodi ndikutayikiridwa kosakhoza kukonzeka kotani kumene ophiphiritsiridwa ndi anamwali opusa amakhala nako, monga momwe kwasonyezedwera pa Mateyu 25:10?
17 Ha ndikutayikiridwa kosakonzeka chotani nanga kumene kumachitika pamene munthu wodzinenera kukhala woŵerengeredwa pakati pa kagulu ka anamwali atayikiridwa ndi mwaŵi ndi mpata wosakhoza kubwezeredwa wa kuchingamira Mkwati wauzimu, Yesu Kristu! Kutayikiridwa kotero kumakhala pakati pa anamwali opusa amakono, monga momwe kwasonyezedwera ndi mawu owonjezereka a fanizo la Yesu: “Pamene iwo anali kumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analoŵa naye pamodzi mu ukwati; ndipo anatseka pakhomo.”—Mateyu 25:10.
18. (a) Kodi ndimwaŵi wotani umene anamwali opusa a m’zaka za zana lino samakhala nawo? (b) Kodi nchifukwa ninji opusa amatsimikizira kukhala ochedwa kwambiri kukhala ndi phande m’chisangalalo cha ukwati ndi kuloŵa m’phwando?
18 Ha ndichokunama nacho chomvetsa chisoni chotani nanga chimene anamwali opusa amakono amakunama nacho! M’nyengo ya mdima wa ndiwe yani imeneyi ya mbiri yonse ya anthu, iwo amalephera kukhala ndi phande m’ntchito ya kupereka kuunika kwa awo okhala mu mdima wauzimu ndi mthunzi wa imfa pa “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse”! (Chivumbulutso 16:14) Popeza kuli kwakuti nyali zawo zophiphiritsira zinalibe mafuta ounikira chikhulupiriro chawo, iwo anachoka ndipo anafunikira kuyenda mu mdima wa pakati pa usiku. Chifukwa cha chimenechi sanayenerere kutsatira mapazi a Mkwati m’dzoma lachisangalalo lodzera pakhomo ndi kufika pa phwando lounikiridwa moŵala ngwee. Iwo ataya kudziŵika kwawo monga otsatira ake amene ali mu mzera wa kukwatiŵa kwa iye mu Ufumu wakumwamba. Iwo sanapezedwe ali “okonzekera” panthaŵi yoikidwiratu. Ha iwo akugaŵira chitsanzo cha chenjezo chotani nanga!
19. Kodi ndichokumana nacho chotani chimene chikutiyembekezera chifukwa cha kulondola nkhani imeneyi kufikira mapeto ake?
19 Chowonadi chomvetsa chisoni chimenechi chasonyezedwa mowonekera bwino m’mbali yotsirizira ya fanizo loperekedwa ndi Yesu Kristu, Mkwatiyo, makamaka kwa ife amene tikukhala mu “mapeto a dongosolo la zinthu.” Chotero tiyeni tsopano tilondole mopitiriza nkhaniyo! Kuunika kobweretsa chisangalalo kukutiyembekezera ngati titero, monga momwe tidzawonera m’chaputala chotsatira.
[Chithunzi patsamba 45]
Ofanana ndi anamwali opusa sadzaloŵa m’phwando laukwati