CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 25
“Khalanibe Maso”
Ngakhale kuti fanizo la anamwali 10 limanena za otsatira odzozedwa a Khristu, mfundo zake zimakhudza Akhristu onse. (w15 3/15 12-16) Iye anati, “Khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.” (Mat. 25:13) Kodi mungakwanitse kufotokoza bwinobwino fanizoli?
Mkwati (vesi 1)—Yesu
Anamwali ochenjera omwe anakonzekera (vesi 2)—Akhristu odzozedwa omwe ndi okonzeka kugwira ntchito yawo mokhulupirika ndipo adzawala ngati zounikira mpaka m’nthawi yamapeto. (Afil. 2:15)
Mawu ofuula akuti: “Mkwati uja wafika!” (vesi 6)—Chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu
Anamwali opusa (vesi 8)—Akhristu odzozedwa omwe anapita kukachingamira mkwati koma analephera kukhalabe maso ndipo analephera kukhalabe okhulupirika
Anamwali ochenjera anakana kugawana mafuta awo ndi anamwali opusa (vesi 9)—Pambuyo poti Yehova wadinda chidindo chomaliza Akhristu odzozedwa, zidzakhala zosatheka kuti odzozedwa okhulupirikawa athandize osakhulupirika aja
“Mkwati anafika” (vesi 10)—Yesu adzabwera kudzapereka chiweruzo chakumapeto kwa chisautso chachikulu
Anamwali ochenjera analowa limodzi ndi mkwati m’nyumba imene munali phwando laukwati, ndipo chitseko chinatsekedwa (vesi 10)—Yesu adzasonkhanitsa odzozedwa okhulupirika n’kupita nawo kumwamba, koma osakhulupirika sadzalandira nawo mphoto imeneyi