-
Anamwali Anzeru ndi OpusaNsanja ya Olonda—1990 | April 15
-
-
Kuchedwa kotalika kwa mkwati kumeneko kumasonyeza kuti kukhalapo kwa Kristu monga Mfumu yolamulira kuli patali mtsogolo. Pomalizira pake akubwera ku mpando wake wachifumu m’chaka cha 1914. Mkati mwa usiku wautali iye asanafike, anamwali onse akugona tulo. Koma iwo sakukanidwa kaamba ka chimenechi. Kukanidwa kwa anamwali opusa kuli kaamba ka kukhala kwawo opanda mafuta m’supa zawo. Yesu akufotokoza mmene anamwaliwo akugalamukira mkwatiyo asanafike:
“Pakati pa usiku panali kufuula, Onani, mkwati! tulukani kukakomana naye. Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zawo. Ndipo opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zirikuzima. Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.”
-
-
Anamwali Anzeru ndi OpusaNsanja ya Olonda—1990 | April 15
-
-
Pambuyo pa kufika kwa Kristu mu Ufumu wake wakumwamba, kagulu ka anamwali ochenjera ka Akristu odzozedwa enieni kanagalamukira ku mwaŵi wawo wapadera wa kuwunikira m’dziko lino lamdima m’chitamando cha kubweranso kwa Mkwati. Koma aja ochitiridwa chithunzi ndi anamwali opusa anali osakonzekera kupereka chitamando cholonjera chimenechi. Chotero pamene nthaŵi ifika, Kristu sakuwatsegulira khomo lopita ku phwando laukwati kumwamba. Iye akuwasiya kunja ku mdima wadziko wa ndiwe yani, kuti awonongeke limodzi ndi onse ochita kusayeruzika. Yesu akumaliza kuti: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake.” Mateyu 25:1-13.
-