-
‘Kapolo Wokhulupirika’ ndi Bungwe Lake LolamuliraNsanja ya Olonda—1990 | March 15
-
-
13 M’fanizo lofanana nalo, fanizo la matalente, Yesu analongosola kuti patapita nthaŵi yaitali, mbuyeyo anadza kudzaŵerengera ndi akapolo ake. Kwa akapolo amene anakhala okhulupirika, mbuyeyo anati: “Unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m’chikondwero cha mbuye wako.“ Koma ponena za kapolo wosakhulupirika, iye analengeza kuti: “Kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho. Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake ku mdima wakunja.”—Mateyo 25:21-23, 29, 30.
14. Kodi Yesu anayembekezera chiyani kwa akapolo ake odzozedwa ndi mzimu?
14 Patapita nthaŵi yaitali—chifupifupi zaka manzana 19—Kristu anavekedwa ulamuliro waufumu mu 1914, pamapeto pa “nthaŵi zawo za anthu akunja.” (Luka 21:24) Mwamsanga pambuyo pake, iye “anabwera . . . naŵerengera nawo pamodzi” akapolo ake, Akristu odzozedwa ndi mzimu. (Mateyu 25:19) Kodi Yesu anayembekezanji kwa iwo aliyense payekha ndi onse pamodzi? Ntchito ya mdindoyo inapitiriza monga mmene inaliri chiyambire zaka za zana loyamba. Kristu anaikiza matalente kwa munthu payekha—“kwa iwo onse monga mwa nzeru zawo.” Chotero, Yesu anayembekezera zotulukapo zosiyanasiyana. (Mateyu 25:15) Lamulo la pa 1 Akorinto 4:2 likugwira ntchito pano, limene limati: “Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.” Kugwiritsira ntchito matalentewo kunatanthauza kuchita mokhulupirika monga atumiki a Mulungu, kupanga ophunzira ndi kuwapatsa chowonadi chauzimu.—2 Akorinto 5:20.
-
-
‘Kapolo Wokhulupirika’ ndi Bungwe Lake LolamuliraNsanja ya Olonda—1990 | March 15
-
-
21. (a) Kodi Kristu anapeza yani akugaŵira chakudya chauzimu, ndipo ndimotani mmene anawafupira iwo? (b) Kodi nchiyani chimene chinayembekezera kapolo wokhulupirika ndi Bungwe lake Lolamulira?
21 Mu 1918, pamene Yesu Kristu anayendera awo odzinenera kukhala akapolo ake, iye anapeza gulu la mitundu yonse la Akristu likufalitsa zowonadi za Baibulo zogwiritsidwa ntchito ponse paŵiri mkati ndi kunja kwa mpingo mu ntchito yolalikira. Mu 1919 zinachitikadi monga mmene Kristu aneneneratu: “Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero. Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.” (Mateyo 24:46, 47) Akristu owona ameneŵa analoŵa m’chikondwero cha Mbuye wawo. Pokhala atasonyeza kukhala ‘okhulupirika pa zinthu zazing’ono,’ anaikidwa ndi Mbuyeyo “pa zinthu zambiri.” (Mateyu 25:21) Kapolo wokhulupiririka ndi Bugwe lake Lolamulira anali m’malo mwake, wokonzekera kaamba ka ntchito yowonjezereka. Tiyenera kukhala achimwemwe chotani nanga kuti mmenemu ndi mmene zinaliri, popeza kuti Akristu okhulupirika akupindula molemera ndi ntchito yodzipereka ya kapolo wokhulupiririka ndi Bungwe lake Lolamulira!
-